Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kupewa Kuonerera Zolaula?

N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kupewa Kuonerera Zolaula?

 Kodi mungakwanitse kupewa kuonera zolaula?

Ngati mumagwiritsa ntchito Intaneti, dziwani kuti tsiku lina mudzakumana ndi zinthu zolaula. Mtsikana wina wazaka 17 dzina lake Hayley ananena kuti: “Masiku ano zolaulazo zikhoza kukupeza zokha moti sipofunika kumazifufuza.”

Ngakhale munthu amene amayesetsa kupewa kuonera zolaula akhoza kukopeka kuti aonere. Mnyamata wina wazaka 18 dzina lake Greg ananena kuti: “Ndinatsimikiza kuti sindidzaonera zolaula koma tsiku lina ndinaonera. Munthu sunganeneretu kuti sungaonere zolaula.”

Masiku ano n’zosavuta kupeza zinthu zolaula kuposa kale. Popeza anthu ambiri akumakonda kutumizirana mameseji a zinthu zolaula, achinyamata ambiri amapanga okha zinthu zolaula n’kumazifalitsa.

Mfundo yofunika kwambiri: Masiku ano zinthu zolaula ndi zofala kwambiri kuposa nthawi imene makolo kapena agogo anu anali achinyamata. Kodi inuyo mungakwanitse kupewa kuonera zolaula?​—Salimo 97:10.

Inde mungakwanitse ngati mutasankha kutero. Koma choyamba mukuyenera kudziwa kuipa koonera zolaula. Tiyeni tione kaye zinthu zina zimene anthu amanena pa nkhaniyi komanso zoona zake.

 Zimene anthu ena amanena komanso zoona zake za nkhaniyi

Zimene anthu ena amanena: Kuonera zolaula kulibe vuto lililonse.

Zoona zake: Zinthu zolaula zimadetsa maganizo anu mofanana ndi mmene fodya angadetsere mapapo anu. Komanso zimapeputsa mphatso ya kugonana yomwe Mulungu anaipereka kuti izigwirizanitsa mwamuna ndi mkazi okwatirana. (Genesis 2:24) Ndipo n’kupita kwa nthawi, zolaula zikhoza kukupangitsani kuti musamathe kusiyanitsa zinthu zabwino ndi zoipa. Mwachitsanzo, akatswiri ena amanena kuti amuna amene amakonda kuonera zolaula akhoza kumaona kuti si vuto kuchitira nkhanza akazi.

Baibulo limanena kuti anthu ena “sakuthanso kuzindikira makhalidwe abwino.” (Aefeso 4:19) Chikumbumtima chawo chinasiya kugwira ntchito moti sadandaula ngakhale pang’ono akamachita zoipa.

Zimene anthu ena amanena: Kuonera zolaula kungathandize munthu kudziwa zokhudza kugonana.

Zoona zake: Kuonera zinthu zolaula kumapangitsa munthu kukhala ndi mtima wadyera. Munthuyo amayamba kuona kuti anthu analengedwa kuti azigonana nawo basi. N’zosadabwitsa kuti pa kafukufuku wina, anapeza kuti anthu amene amakonda kuonera zolaula sakhutira ndi kugonana akalowa m’banja.

Baibulo limauza Akhristu kuti azipewa “kugonana, chikhumbo choipa, ndi kusirira kwa nsanje.” Kuonera zolaula kumalimbikitsa munthu kuchita zinthu zonsezi.—Akolose 3:5.

Zimene anthu ena amanena: Anthu amene amapewa kuonera zolaula amakokomeza zinthu poganiza kuti zilizonse zokhudza kugonana ndi zoipa.

Zoona zake: Anthu amene amapewa kuonera zolaula amakhala ndi maganizo oyenera pa nkhani yokhudza kugonana. Amaona kuti kugonana ndi mphatso imene Mulungu anaipereka kwa mwamuna ndi mkazi okwatirana kuti azikondana komanso kugwirizana kwambiri. Anthu amene amakhala ndi maganizo amenewa amasangalala ndi mphatso yogonana akalowa m’banja.

Baibulo linanena mosapita m’mbali zokhudza kugonana. Mwachitsanzo, limauza amuna okwatira kuti: “Usangalale ndi mkazi wapaunyamata wako . . . Nthawi zonse uzikhala wokondwa kwambiri ndi chikondi chake.”—Miyambo 5:18, 19.

 Zimene mungachite kuti mupewe kuonerera zolaula

Kodi mungatani ngati mutaona kuti mukukopeka kwambiri kuti muonere zolaula? Nkhani yakuti “Zimene Mungachite Kuti Mupewe Kuonerera Zolaula” ingakuthandizeni.

Dziwani kuti mungakwanitse kupewa kuonera zolaula. Mukhozanso kuphunzira zimene mungachite kuti musiye kuonera zolaula ngati munayamba kale kuonera. Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kwambiri.

Taonani zimene zinachitikira Calvin, amene anayamba kuonera zolaula ali ndi zaka 13. Iye ananena kuti: “Ndinkadziwa kuti n’kulakwa kuonera zolaula koma zinkandivuta kuzipewa. Ndipo ndinkati ndikaonera, ndinkakhumudwa kwambiri. Kenako bambo anga anadziwa za vuto langali ndipo anandithandiza. Iwo atandithandiza, ndinapepukidwa kwambiri.”

Panopa Calvin anasiya kuonera zolaula. Iye ananena kuti: “Ndimaona kuti ndinalakwitsa kwambiri kuyamba kuonera zolaula chifukwa ngakhale ndinasiya, mpaka pano zinthuzo zimabwerabe m’maganizo mwanga. Nthawi zina ndimalakalakabe nditaonera zinthu zolaula. Zikatere ndimayamba kuganizira zoti panopa ndine wosangalala, ndine woyera komanso ndili ndi tsogolo labwino chifukwa ndikuchita zimene Yehova amafuna.”