Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

N’chifukwa Chiyani Ndikufunika Kumathandiza Ena?

N’chifukwa Chiyani Ndikufunika Kumathandiza Ena?

 Mfundo ziwiri zofunika zimene anthu ambiri sadziwa

 Mfundo yoyamba: Mukamathandiza anthu, inunso anthu ena amakuthandizani.

 Anthu amaona ndithu kuti ndinu wowolowa manja. Zimenezi zimachititsa kuti nawonso akhale owolowa manja kwa inu. Pa mfundo imeneyi Baibulo limanena kuti:

 •  “Khalani opatsa ndipo inunso anthu adzakupatsani. . . . Pakuti muyezo umene mukuyezera ena, iwonso adzakuyezerani womwewo.”​—Luka 6:​38.

 •  Palemba lomweli, Baibulo lina limati: “Zinthu zimene mumachitira anthu ena, inunso adzakuchitirani zomwezo.”​—Luka 6:​38, Contemporary English Version.

 Mfundo yachiwiri: Mukamathandiza ena mumakhala wosangalala.

 Mukamachitira zabwino ena, zimakuthandizani kuti musamadzione ngati wosafunika ndiponso mumakhala ndi chimwemwe mumtima. Baibulo limanena kuti:

 •  “Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.”​—Machitidwe 20:35.

 •  “Koma ukakonza phwando, uziitana anthu osauka, otsimphina, olumala, ndi akhungu. Ukatero udzakhala wodala, chifukwa alibe choti adzabweze kwa iwe.”​—Luka 14:​13, 14.

 Achinyamata amene amathandiza ena

 Pali achinyamata ambiri amene amathandiza ena. Taonani zitsanzo izi:

 “Nthawi zina ndimafuna kungokhala n’kumaonera TV. Koma ndikaganizira kuti bambo ndi mayi anga akamabwera kuntchito akhala atatopa, ndimayamba kugwira ntchito za pakhomo monga kutsuka mbale ndi kukonza m’nyumba. Ndimawakonzeranso tiyi chifukwa makolo anga amamukonda kwambiri. Mayi anga akangolowa m’nyumba amafikira kunena kuti, ‘Eee koma ndiye m’nyumba muno mukuoneka bwino bwanji! Zikomo kwambirinso potikonzera tiyi. Ndathokoza mwana wanga.’ Nthawi zonse ndimasangalala kwambiri ndikachitira bambo ndi mayi anga zinthu zabwino ngati zimenezi.”​—Casey.

 “Makolo anga akhala akundithandiza pa chilichonse chimene ndimafunikira pa moyo wanga. Choncho chaka chathachi galimoto yawo itawonongeka, ndinawapatsa ndalama zoti aikonzetsere ngakhale kuti ndimapeza ndalama zochepa. Iwo anayesetsa kukana ndalamazo komabe ndinawakakamiza. Ndimaona kuti pali zambiri zimene ndiyenera kuwachitira kuposa zimenezi ndipo nthawi iliyonse ndikawathandiza, ndimasangalala kwambiri.”​—Holly.

 Kodi mukudziwa? Achinyamata ambiri a Mboni za Yehova amasangalala akathandiza ena powauza uthenga wa m’Baibulo. Ndipotu ena afika posamukira m’mayiko ena kumene anthu ambiri akufunikira kumva uthenga wa m’Baibulo.

 “Ndinasamuka ku United States n’kumakakhala ku Mexico kuti ndizikaphunzitsa anthu Baibulo. Nthawi zambiri sindikwanitsa kuthandiza anthu ndi ndalama kapena zinthu zina chifukwa ndilibe zinthu zambiri. Koma ndazindikira kuti anthu amayamikira kwambiri ndikamagwiritsa ntchito mphamvu ndi nthawi yanga kuwaphunzitsa Baibulo, kuposa ndikawapatsa ndalama.”​—Evan.

 Kodi ndingathandize ena m’njira ziti?

 Kodi inunso mukufuna kusangalala chifukwa chothandiza ena? Onani zinthu zingapo zimene mungachite.

 Pothandiza anthu a m’banja lanu mungachite izi:

 •  Kukonza m’nyumba ndi kutsuka mbale popanda kuuzidwa

 •  Kuphika chakudya

 •  Kulembera makolo anu khadi loyamikira zimene amakuchitirani

 •  Kuthandiza m’bale wanu homuweki

 Pothandiza anthu omwe si a m’banja lanu mungachite izi:

 •  Kutumiza khadi kwa munthu amene akudwala

 •  Kusesa kapena kutchetcha panja pa nyumba ya munthu wachikulire

 •  Kukacheza ndi munthu amene sangathe kuchoka pakhomo chifukwa cha mavuto ena

 •  Kugulira mphatso munthu amene akukumana ndi mavuto

 Zimene zingakuthandizeni: Ganizirani zinthu zina zimene inuyo mungachite kuti muthandize ena. Mukatero yesetsani kukhala ndi cholinga choti muthandize munthu m’modzi mlungu uno. Mungasangalale kwambiri kuposa mmene mukuganizira ngati mutachita zimenezi.

 “Ukathandiza ena, umasangalala kwambiri. Umaona kuti wachita chinachake chofunika komanso anthu ena amayamikira. Umazindikiranso kuti zimene umachita pothandiza ena zimakhala zosangalatsa osati zotopetsa. Sumaona n’komwe kuti unawononga chilichonse pothandiza ena chifukwa chimwemwe chimene umapeza chimakhala chochuluka kwambiri.”​—Alana.