December

Lachiwiri, December 1

December

Anatseguliratu maganizo awo kuti amvetse tanthauzo la Malemba.—Luka 24:45.

Ophunzira a Yesu ankadziwa Mawu a Mulungu ndipo ankawatsatira pa moyo wawo. (Yoh. 17:6) Komabe iwo anasokonezeka pomwe iye anaphedwa ngati chigawenga pamtengo wozunzikirapo. Yesu anazindikira kuti iwo ankakayikira chifukwa chakuti sankamvetsa zinthu, osati chifukwa chakuti anali ndi mtima woipa. (Luka 9:​44, 45; Yoh. 20:9) Choncho iye anawathandiza kumvetsa Malemba. Taonani mmene anachitira zimenezi kwa ophunzira awiri omwe ankapita ku Emau. Yesu pocheza nawo sanangofikira kuwauza kuti iye waukitsidwa. M’malomwake, anayamba ndi kuwafunsa mafunso. N’chifukwa chiyani anachita zimenezi? N’kutheka kuti iye ankafuna kuti afotokoze zimene zinali m’maganizo ndi mumtima mwawo, ndipo iwo anafotokozadi. Iwo anamufotokozera kuti ankayembekezera kuti Yesu apulumutsa Aisiraeli ku ulamuliro wopondereza wa Aroma. (Luka 24:​18-27) Yesu anagwiritsa ntchito Malemba powathandiza kumvetsa zimene zinachitika. Madzulo a tsiku limenelo, Yesu anathandizanso ophunzira ena kumvetsa mfundo zimenezi.—Luka 24:​33-48. w24.10 14 ¶9-10

Sindichita chilichonse mongoganiza ndekha. Koma zimene ndimalankhula zimakhala zogwirizana ndendende ndi zimene Atate anandiphunzitsa.Yoh. 8:28.

Yesu anaphunzira kwa Atate ake akumwamba zoyenera kuchita komanso kulankhula. Potengera chitsanzo cha Yesu, gulu la Yehova limagwiritsa ntchito Mawu a Mulungu pophunzitsa anthu kuti adziwe zoyenera ndi zosayenera komanso popereka malangizo. (2 Tim. 3:​16, 17) Nthawi zonse timakumbutsidwa kuti tiziwerenga Mawu a Mulungu komanso kuwatsatira. Timapindula kwambiri tikamaphunzira Baibulo pogwiritsa ntchito mabuku athu. Mwachitsanzo, timatha kuyerekezera zimene Baibulo limaphunzitsa ndi malangizo amene gulu limatipatsa. Tikaona kuti malangizo amene timalandira ndi ochokera m’Malemba timayamba kukhulupirira kwambiri gulu la Yehova. (Aroma 12:2) Yesu ankalalikira “uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.” (Luka 4:​43, 44) Iye analamulanso ophunzira ake kuti azilalikira za Ufumu wa Mulungu. (Luka 9:​1, 2; 10:​8, 9) Masiku ano, anthu onse amene ali m’gulu la Yehova amalalikira uthenga wa Ufumu posatengera kumene amakhala. w24.04 9 ¶5-7

Zonse zimene mwatilamula tichita, ndipo kulikonse kumene mungatitumize tipita.Yos. 1:16.

Muzikhulupirira malangizo ochokera kugulu la Mulungu. Kale Yehova anagwiritsa ntchito Mose kenako Yoswa popereka malangizo kwa Aisiraeli. (Yos. 1:17) Aisiraeli ankadalitsidwa akamaona anthu amenewa ngati oimira Yehova Mulungu. Patapita zaka zambiri, mpingo wa Chikhristu unakhazikitsidwa ndipo atumwi 12 ndi amene ankapereka malangizo. (Mac. 8:​14, 15) Kenako m’gulu la anthu opereka malangizowa munalinso akulu a ku Yerusalemu. Chifukwa chotsatira malangizo a amuna okhulupirikawa, “anthu m’mipingo anapitiriza kukhala ndi chikhulupiriro cholimba ndipo chiwerengero chinkawonjezeka tsiku ndi tsiku.” (Mac. 16:​4, 5) Masiku anonso timadalitsidwa tikamatsatira malangizo ochokera kugulu la Yehova. w24.07 10 ¶10

Ndapeza Davide mwana wa Jese, munthu wapamtima panga.—Mac. 13:22.

Yehova ankakonda kwambiri Mfumu Davide. Iye anafika pomutchula kuti “munthu wapamtima panga.” Koma Davide anachita machimo akuluakulu monga chigololo komanso kupha munthu. Malinga ndi Chilamulo cha Mose, Davide ankayenera kuphedwa. (Lev. 20:10; Num. 35:31) Koma mokoma mtima Yehova anamuthandiza kuti alape. Iye anamutumizira mneneri wake Natani ngakhale kuti Davide anali asanasonyeze kulapa kulikonse. Natani anagwiritsa ntchito fanizo limene linamufika pamtima Davide. Atazindikira kuti wakhumudwitsa Yehova, Davide analapa. (2 Sam. 12:​1-14) Pambuyo pake analemba salimo losonyeza kudzimvera chisoni ndi zomwe anachita. (Sal. 51, timawu tapamwamba) Salimoli lakhala likutonthoza anthu ambiri ochimwa komanso kuwalimbikitsa kuti alape. Timayamikira kwambiri kuti Yehova anathandiza mtumiki wake wokondedwa Davide kuti alape. w24.08 10 ¶9

Muzindikire chifuniro cha Mulungu, chabwino, chovomerezeka ndi changwiro.—Aroma 12:2.

Ambiri angavomereze kuti kulera ana ndi ntchito yaikulu. Ngati ndinu kholo ndipo muli ndi mwana wamng’ono tikukuthokozani chifukwa choyesetsa kumuthandiza kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba. (Deut. 6:​6, 7) Mwana wanu akamakula adzayamba kufunsa mafunso ena ovuta okhudza zimene timakhulupirira komanso mfundo za m’Baibulo zokhudza makhalidwe abwino. Poyamba, mukhoza kumada nkhawa ndi mafunso amene mwana wanu akufunsa. Mwinanso mukhoza kuyamba kuona kuti chikhulupiriro chake chayamba kuchepa. Koma zoona n’zakuti mwana akamakula ayenera kumafunsa mafunso n’cholinga chakuti azitsimikizira zimene amakhulupirira. (1 Akor. 13:11) Choncho simuyenera kuchita mantha. Akamafunsa mafunso muziona kuti umenewo ndi mwayi womuthandiza kuti aziganiza bwino. w24.12 14 ¶1-2

Ndife anthu okhala ndi chikhulupiriro chomwe chingatithandize kudzapeza moyo.—Aheb. 10:39.

Akhristu a Chiheberi ankafunika kukhala ndi chikhulupiriro cholimba kuti apulumuke chisautso chomwe chinkabwera ku Yudeya. (Aheb. 10:​37, 38) Yesu anachenjeza otsatira ake kuti adzathawire kumapiri akadzaona mzinda wa Yerusalemu utazunguliridwa ndi asilikali. Akhristu onse ankayenera kutsatira malangizowa kaya ankakhala mumzindawo kapena ayi. (Luka 21:​20-24) Kale asilikali akabwera kudzaukira, anthu ankathawira mumzinda wokhala ndi mpanda, ngati mmene zinalili ndi mzinda wa Yerusalemu. Choncho kuthawira kumapiri kukanaoneka ngati kusaganiza bwino ndipo zikanafunika kuti munthu akhale ndi chikhulupiriro cholimba. Akhristu a Chiheberi ankafunikanso kukhulupirira kwambiri anthu amene Yesu ankawagwiritsa ntchito potsogolera mpingo. Anthu amene ankatsogolerawo, ayenera kuti anapereka malangizo omwe akanathandiza Akhristuwo kudziwa nthawi yoyenera kuthawa komanso mmene akanachitira zimenezo.—Aheb. 13:17. w24.09 10 ¶9-10

Anapereka amuna kuti akhale mphatso.—Aef. 4:8.

Ali padzikoli Yesu anagwira bwino ntchito imene Atate wake anamupatsa. (Yoh. 17:4) Koma Yesu analibe maganizo akuti, ‘Zinthu zingayende bwino ngati nditamachita ndekha.’ Iye anaphunzitsa ena kuti azigwira bwino ntchitoyi. Anapatsa ophunzira ake ntchito yosamalira nkhosa za Mulungu komanso kutsogolera pa ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa anthu. Yesu anapereka malangizo kwa ophunzira ake mosapita m’mbali koma mokoma mtima. Ena ankakayikira zinthu zina ndipo anawadzudzula. (Luka 24:​25-27; Yoh. 20:27) Iye anawathandiza kuti aziona ntchito yolalikira kukhala yofunika kwambiri kuposa ntchito zina. (Yoh. 21:15) Anawakumbutsanso kuti asamaganizire kwambiri mwayi wa utumiki umene ena apatsidwa m’gulu la Yehova. (Yoh. 21:​20-22) Anawathandizanso kukonza maganizo olakwika omwe anali nawo okhudza Ufumu ndipo anawalimbikitsa kuti aziganizira kwambiri zolalikira uthenga wa Ufumu.—Mac. 1:​6-8. w24.10 15-16 ¶13-14

Olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo mpaka kalekale.—Sal. 37:29.

Kumvera kumapulumutsa moyo. Mofanana ndi Aisiraeli omwe anali atatsala pang’ono kulowa m’Dziko Lolonjezedwa, ifenso tatsala pang’ono kulowa m’dziko limene Mulungu analonjeza. Posachedwapa tiona iye akusintha dzikoli kukhala Paradaiso. (Yes. 35:1; Luka 23:43) Satana ndi ziwanda zake adzachotsedwa. (Chiv. 20:​2, 3) Zipembedzo zabodza sizidzasocheretsanso anthu. (Chiv. 17:16) Sipadzapezekanso maboma opondereza anthu. (Chiv. 19:​19, 20) M’paradaiso simudzapezekanso anthu oukira. (Sal. 37:​10, 11) Kulikonse anthu azidzatsatira malamulo olungama a Yehova, omwe amalimbikitsa mgwirizano ndi mtendere. Choncho anthu azidzakondana komanso kukhulupirirana. (Yes. 11:9) Tikuyembekezeratu zinthu zabwino kwambiri. Kuwonjezera pamenepo, ngati tizimvera Yehova tidzapitiriza kukhala m’Paradaiso mpaka kalekale.—Yoh. 3:16. w24.11 9 ¶7

Uthenga wabwino uwu wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni kwa anthu amitundu yonse.—Mat. 24:14.

Ulosiwu umene uli mulemba lalero ukukwaniritsidwa kwambiri masiku ano kuposa kale. Uthenga wa Ufumu ukufalitsidwa m’zilankhulo zoposa 1,000 ndipo webusaiti yathu ya jw.org ikuthandiza anthu ambiri padziko lonse kuti amve uthenga wabwino. Koma Yesu anauzanso ophunzira ake kuti sadzamaliza “kuzungulira mizinda yonse” kapena kuti kulalikira kwa munthu wina aliyense iye asanabwere. (Mat. 10:23; 25:​31-33) Mawu a Yesuwa akukwaniritsidwanso masiku ano. Anthu ambiri akukhala m’madera amene ntchito yathu ndi yoletsedwa. Komanso ana mahandiredi akubadwa pa miniti iliyonse. Timachita zonse zomwe tingathe kuti tilalikire uthenga wabwino kwa anthu a “fuko lililonse, chilankhulo chilichonse ndi mtundu uliwonse.” (Chiv. 14:6) Koma zoona ndi zakuti sitingathe kuuza munthu aliyense uthenga wabwino mapeto asanafike. w24.05 10 ¶6-7

Sakhalanso kuti ndi awiri, koma thupi limodzi.—Mat. 19:6.

Yesu ankalankhula mawu olimbikitsa komanso otsitsimula kwa ena. Iye sankalankhula mwaukali kwa ophunzira ake. (Luka 8:​47, 48) Apatu iye anapereka chitsanzo chabwino kwambiri kwa amuna a Chikhristu. Yesu analangiza amuna kuti azikhala okhulupirika kwa akazi awo. Iye anagwiritsa ntchito mawu amene Atate wake ananena akuti mwamuna ayenera ‘kudziphatika kwa mkazi wake.’ (Mat. 19:​4-6) Mawu a Chigiriki omwe anawamasulira kuti “kudziphatika” angatanthauze “kumata ndi guluu.” Choncho mwamuna ndi mkazi, ayenera kumagwirizana kwambiri ngati amatidwa pamodzi ndi guluu. Ngati iwo atasiyanitsidwa, awiri onsewa adzamva kupweteka. Mwamuna amene amagwirizana chonchi ndi mkazi wake sangaonere zolaula zilizonse. Iye amatembenuka mwamsanga kuti ‘asayang’ane zopanda pake.’ (Sal. 119:37) Zimakhala ngati wapangana ndi maso ake kuti asayang’ane mosirira akazi ena.—Yobu 31:1. w25.01 10 ¶12-13

Mulungu wathu . . . adzamukhululukira ndi mtima wonse.—Yes. 55:7.

Anthu akamanena kuti akhululuka amakhala akutanthauza zinthu zosiyanasiyana. Mmene Yehova amatikhululukira anthu ochimwafe, n’zosiyana kwambiri ndi mmene timakhululukirana tokhatokha. Palibe amene angathe kukhululuka ngati mmene Yehova amachitira. Ponena za Yehova wolemba masalimo anati: “Inu mumakhululuka ndi mtima wonse, kuti anthu azikuopani.” (Sal. 130:4) Choncho Yehova ‘amakhululuka ndi mtima wonse.’ Iye ndi chitsanzo chabwino chosonyeza zimene kukhululuka kumatanthauza. M’mavesi ena, olemba Baibulo anagwiritsa ntchito mawu a Chiheberi ofotokoza za kukhululuka amene amagwiritsidwa ntchito ponena za Yehova yekha, osati anthu. Yehova akakhululukira munthu amafufuta machimo onse a munthuyo ndipo amakhala nayenso pa ubwenzi ngati poyamba. Timayamikira kuti Yehova amatikhululukira ndi mtima wonse komanso mobwerezabwereza. w25.02 8 ¶1-3

Anatilamula kuti tilalikire kwa anthu ndi kupereka umboni wokwanira.—Mac. 10:42.

Sikuti anthu akamvetsera uthenga wathu m’pamene tinganene kuti zinthu zatiyendera bwino mu utumiki. N’chifukwa chiyani tikutero? Tikutero chifukwa timakhala titachita zimene Yehova komanso Mwana wake amafuna kuti tizichita, zomwe ndi kuchitira umboni. Ngakhale tisapeze anthu oti tiwalalikire kapena palibe amene wamvetsera uthenga wathu, timakhalabe osangalala chifukwa timadziwa kuti tasangalatsa Atate wathu wakumwamba. ( Miy. 27:11) Tingasangalalenso wofalitsa wina akapeza munthu wachidwi mu utumiki. Nsanja ya Olonda ina inayerekezera ntchito yathu yolalikira ndi kufufuza mwana wotayika. Anthu ambiri angagwire nawo ntchito yomufufuza m’malo osiyanasiyana. Mwanayo akapezeka, anthu onsewo amasangalala osati munthu amene wamupeza yekhayo. Mofanana ndi zimenezi, nayonso ntchito yolalikira timaigwira ngati gulu. Aliyense mumpingo amagwira nawo ntchito yofufuza anthu ndipo aliyense amasangalala munthu mmodzi akayamba kusonkhana. w24.04 18 ¶13-14

Anthu onse amene anali ndi maganizo abwino amene akanawathandiza kukapeza moyo wosatha anakhala okhulupirira.—Mac. 13:48.

Tikuyembekezeratu zinthu zosangalatsa kwambiri patsogolopa. Ndi Madalitso a Yehova, tikuyembekezera kuona anthu ambiri akuphunzira choonadi chisautso chisanayambe. Tasangalalanso kudziwa kuti ngakhale pachisautso chachikulu tingadzaone anthu ambiri akuchoka m’dziko loipa la Satanali n’kuyamba kutamanda nafe limodzi Yehova. Padakali pano tili ndi ntchito yambiri yoti tigwire. Tili ndi mwayi wogwira nawo ntchito yomwe sidzachitikanso yolengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu padziko lonse. Pa nthawi imodzimodziyo tiyenera kupitiriza kuchenjeza anthu zomwe zichitike. Anthu akufunika adziwe kuti mapeto a dziko loipali ali pafupi kwambiri. Chifukwa chokonda uthenga wabwino, anthu komanso koposa zonse kukonda Yehova Mulungu ndi dzina lake, tipitiriza kulalikira mofunitsitsa, mwachangu komanso mwakhama mpaka Yehova atanena kuti “Basi mwamaliza!” w24.05 19 ¶14-16

Muzichita zinthu modzichepetsa, chifukwa Mulungu sasangalala ndi anthu odzikuza. Koma odzichepetsa amawasonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu.—1 Pet. 5:5.

Pa usiku wake womaliza, Yesu anaphunzitsa Petulo ndi atumwi anzake mfundo yofunika kwambiri yokhudza kudzichepetsa. Atumwiwo ayenera kuti anadabwa kwambiri kuona Yesu akugwira ntchito imene nthawi zambiri inkagwiridwa ndi wantchito wapanyumba. Yesu anavula malaya ake akunja, kumanga chopukutira m’chiuno mwake, kuika madzi m’beseni n’kuyamba kuwasambitsa mapazi. (Yoh. 13:​4, 5) Ziyenera kuti zinamutengera nthawi kuti asambitse mapazi a atumwi onse 12, kuphatikizapo Yudasi, yemwe anali atatsala pang’ono kumupereka. Koma modzichepetsa, Yesu anamaliza kugwira ntchitoyi. Kenako moleza mtima Yesu ananena kuti: “Kodi mukudziwa chifukwa chake ndasambitsa mapazi anu? Inu mumanditchula kuti ‘Mphunzitsiʼ komanso ‘Ambuye,’ mumalondola, chifukwa ndinedi Mphunzitsi komanso Ambuye. Choncho ngati ine amene ndi Ambuye komanso Mphunzitsi, ndasambitsa mapazi anu, inunso mukuyenera kusambitsana mapazi.”—Yoh 13:​12-14. w25.03 10 ¶9-11

Mumanditsogolera ndi malangizo anu, ndipo pambuyo pake mudzandipatsa ulemerero.—Sal. 73:24.

M’dzikoli, kupitiriza kukhala pa ubwenzi ndi Yehova si kophweka. Anthu ambiri savomereza kuti Mulungu aliko. Ndipo nthawi zambiri anthu amene satsatira mfundo za Mulungu amaoneka ngati zinthu zikuwayendera bwino. Tikamaona zimenezi zikuchitika chikhulupiriro chathu chingayesedwe. Ngakhale kuti sitingafike pokayikira kuti Mulungu alikodi, tingayambe kukayikira ngati angatithandize. Amene analemba Salimo 73 anayambanso kukayikira zimenezi. Ankaona kuti anthu amene ankanyalanyaza malamulo a Mulungu zinthu zinkawayendera bwino. Choncho anayamba kukayikira ngati kutumikira Yehova kuli ndi phindu lililonse. (Sal. 73:​11-13) Kodi n’chiyani chinathandiza wolemba masalimo kuti ayambenso kuona zinthu moyenera? Iye anaganizira zimene zingachitikire anthu amene aiwala Yehova. (Sal. 73:​18, 19, 27) Anaganiziranso madalitso omwe anthu amene akutumikira Mulungu amapeza. Ifenso tiziganizira madalitso amene Yehova watipatsa. w24.06 25 ¶16-17

Musamakonde ndalama.Aheb. 13:5.

Kale anthu ena ankadyera abale awo osauka masuku pamutu powalipiritsa chiwongola dzanja pa ndalama zimene anawabwereka. Komanso oweruza ena ankalandira ziphuphu ndipo ankaweruza anthu osalakwa mopanda chilungamo. Yehova amadana ndi zinthu ngati zimenezi. (Ezek. 22:12) Tingachite bwino kumadzifufuza mmene timaonera nkhani ya ndalama. Dzifunseni kuti: ‘Kodi nthawi zonse ndimangoganizira za ndalama komanso zimene ndingagule? Kodi ndikabwereka ndalama, ndimachedwa kubweza poganiza kuti amene wandibwereka ndalamayo sakuzifuna? Kodi kukhala ndi ndalama kumandichititsa kuti ndizidziona ngati wofunika koma n’kumalephera kuthandiza ena? Kodi ndimaona kuti abale ndi alongo ena ndi okonda ndalama chabe chifukwa choti ali ndi ndalamazo? Kodi ndimakonda kucheza ndi anthu olemera n’kumapewa anthu osauka?’ Tingathe kupitirizabe kukhala anzake a Yehova tikamapewa kukonda ndalama. Tikamachita zimenezi Yehova sadzatisiya.—w24.06 12-13 ¶17-18

Ndimakana kuyenda mʼnjira iliyonse yoipa, kuti ndisunge mawu anu.—Sal. 119:101.

Kuti tipewe mayesero, tiyenera kumalakalaka zinthu zoyenera. Tikaphunzira ‘kudana ndi choipa n’kumakonda chabwino’ tidzatsimikiza mtima kuti tizichita zoyenera n’kumapewa zinthu zimene zingachititse kuti tichimwe. (Amosi 5:15) Kulakalaka zinthu zoyenera kudzatithandiza kuti tisatengeke tikakumana ndi mayesero amene sitimayembekezera kapenanso ovuta kuwapewa. Tiyenera kumatanganidwa ndi zinthu zokhudza kulambira. Tikakhala pamisonkhano kapena mu utumiki zimakhala zovuta kuti tiyesedwe. M’malomwake timalimbikitsidwa kukhala ndi mtima wofuna kusangalatsa Yehova. (Mat. 28:​19, 20; Aheb. 10:​24, 25) Tikamawerenga, kuphunzira komanso kuganizira mozama Mawu a Mulungu timayamba kukonda zabwino ndipo timadana ndi zoipa. (Yos. 1:8; Sal. 1:​2, 3; 119:97) Kumbukirani kuti Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Mupitirize kupemphera kuti musalowe mʼmayesero.” (Mat. 26:41) Tikatero Yehova amatithandiza ndipo ifeyo timafunitsitsa kumusangalatsa.—Yak. 4:8. w24.07 17-18 ¶14-16

Ndidzakupatsa nzeru komanso kukulangiza njira yoti uyendemo. Ndidzakupatsa malangizo ndi kukuyangʼanira.—Sal. 32:8.

Anthu amene akuphunzitsa anzawo ayenera kutsanzira mmene Yehova amaperekera nzeru. Kumbukirani kuti Yehova amapereka nzeru mowolowa manja. Ifenso timaphunzitsa ena ndi mtima wonse zimene tikudziwa. Tisamaope kuphunzitsa ena zinthu poopa kuti adzatilanda malo. Si bwinonso kuganiza kuti, ‘Ndinaphunzira ndekha, nayenso aphunzire yekha.’ Mtima umenewo ndi wosafunika pakati pa anthu a Mulungu. M’malomwake, timachita zonse zomwe tingathe kuti tiwaphunzitse chilichonse chomwe tikudziwa, ngati kuti ‘tikuwapatsa miyoyo yathu yeniyeniyo.’ (1 Ates. 2:8) Timayembekezera kuti “nawonso adzakhala oyenerera kuphunzitsa ena.” (2 Tim. 2:​1, 2) Tikatero timathandiza ena kuti akhale owolowa manja komanso osangalala. w24.09 29 ¶12-13

Ndife thupi limodzi mwa Khristu ndipo ndife ziwalo zolumikizana.—Aroma 12:5.

Ngati mukuona kuti mulibe luso linalake lapadera, musataye mtima. Chifukwa n’zosakayikitsa kuti muli ndi makhalidwe ena omwe angathandize anthu mumpingo. Kuwerenga malangizo a Paulo a pa 1 Akorinto 12:​12-30 komanso kuipempherera nkhaniyo, kungakuthandizeni. Mawu a Paulo amasonyeza kuti inuyo, mofanana ndi mtumiki wa Yehova aliyense, ndinu wofunika mumpingo. Muzichita zonse zomwe mungathe potumikira Yehova komanso abale ndi alongo anu. Dziwani kuti akulu adzakupatsani zochita mogwirizana ndi zimene mungathe. (Aroma 12:​4-8) Akhristu onse amafunika kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova n’kumasangalala chifukwa chopatsa ena zinthu komanso kukhala chitsanzo chabwino kwa ena. w24.11 17¶12-13

[Iye] anayamba kupemphera kwa Yehova uku akulira kwambiri.—1 Sam. 1:10.

Hana ankakumana ndi mavuto omwe ankachititsa kuti alire. Limodzi mwa mavutowo linali lakuti anali m’banja la mitala ndipo mkazi mnzake dzina lake Penina ankamunyoza. Kuwonjezera pamenepo Hana anali wosabereka, pomwe Penina anali ndi ana. (1 Sam. 1:​1, 2) Ndiye Penina ankanyoza Hana chifukwa choti analibe ana. Hana zinkamupweteka kwambiri mumtima moti “ankalira ndipo sankadya” komanso “anali wokhumudwa kwambiri.” (1 Sam. 1:​6, 7, 10) Kodi n’chiyani chinamuthandiza Hana? Chimodzi mwa zinthu zomwe zinamuthandiza ndi kupita kuchihema komwe anthu ankalambirako Mulungu. Ali kumeneko, iye anayamba kupempha Yehova kuti: ‘Muone kuvutika kwa ine kapolo wanu nʼkundikumbukira.’ (1 Sam. 1:11) Yehova anaona mavuto ake, anamva kulira kwake komanso anamudalitsa pomupatsa mwana.—1 Sam. 1:​19, 20; 2:21. w24.12 21 ¶5-7

Ana a anthu ndi amene ankandisangalatsa kwambiri.—Miy. 8:31.

Dipo limatiphunzitsa kuti Yesu amakonda kwambiri anthu, makamaka otsatira ake. (Yoh. 13:1) Mwachitsanzo, Yesu ankadziwa kuti zina zomwe adzakumane nazo pa utumiki wake zidzakhala zovuta kwambiri, makamaka imfa yake. Komabe, Yesu anachita zonsezi, osati chifukwa chakuti ndi zimene Yehova anamutuma kudzachita, koma chifukwa chakuti ankakonda anthu. Choncho iye ankaika mtima wake wonse pa ntchito yolalikira, kuphunzitsa ndi kutumikira ena. Ngakhale pa tsiku limene anaphedwa, Yesu anasambitsa mapazi a atumwi ake, kuwapatsa malangizo komanso kuwauza mawu olimbikitsa. (Yoh. 13:​12-15) Kenako Yesu ali pamtengo wozunzikirapo, anathandiza chigawenga kukhala ndi chiyembekezo komanso anakonza zoti mayi ake azisamaliridwa. (Luka 23:​42, 43; Yoh 19:​26, 27) Apa Yesu anasonyeza kuti amakonda anthu, osati potifera pokha, koma pa moyo wake wonse. w25.01 23 ¶11

Analandira chilango kuti ife tikhale pamtendere, ndipo chifukwa cha mabala ake ifeyo tinachiritsidwa.—Yes. 53:5.

Baibulo limagwiritsa ntchito fanizo pofuna kutithandiza kumvetsa ufulu umene timakhala nawo Yehova akatikhululukira ndi mtima wonse. Chifukwa chakuti ndife ochimwa ndipo timalakalaka zoipa, tili ngati “akapolo a uchimo.” Koma Yehova akatikhululukira timakhala ngati akapolo amene ‘amasulidwa ku uchimo.’ (Aroma 6:​17, 18; Chiv. 1:5) Tikadziwa kuti Yehova watikhululukira timakhala osangalala ngati kapolo amene wamasulidwa. Pogwiritsa ntchito nsembe ya Mwana wake, mophiphiritsa, Yehova amatichiritsa. (1 Pet. 2:24) Dipo limathandiza kuti tikhalenso pa ubwenzi wabwino ndi Yehova, womwe unasokonekera chifukwa cha matenda oopsa. Mofanana ndi munthu amene amasangalala akachiritsidwa matenda aakulu, ifenso timasangalala tikachiritsidwa mwauzimu n’kukhalanso pa ubwenzi ndi Yehova chifukwa chakuti watikhululukira. w25.02 11 ¶16; 13 ¶17

Mukapitiriza kuchita zimenezi, simudzalephera ngakhale pangʼono.—2 Pet. 1:10.

Mufanizo la matalente, Yesu ananena kuti akapolo awiri anali okhulupirika kwa mbuye wawo ndipo mmodzi anali wosakhulupirika. (Mat. 25:​14-30) Akapolo awiri okhulupirika akuimira Akhristu odzozedwa okhulupirika. Mbuye wawo yemwe ndi Yesu, amawaitana kuti ‘asangalale limodzi naye.’ Iwo amalandira mphoto yawo yakumwamba pa kuuka koyamba. (Mat. 25:​21, 23; Chiv. 20:5b) Zimene zinachitikira kapolo waulesi zimapereka chenjezo kwa odzozedwa onse. N’chifukwa chiyani tikutero? Iwo ayenera kukhala akhama. Mufanizo la matalente, monganso mmene zilili mufanizo la anamwali, Yesu sankalosera kuti odzozedwa adzakhala aulesi. M’malomwake ankangofotokoza zimene zingachitike ngati iwo atasiya kukhala akhama. Iwo angalephere kukhala “pakati pa anthu amene Mulungu wawaitana ndi kuwasankha” ndipo sangaloledwe kulowa mu Ufumu wakumwamba. w24.09 22 ¶10; 23 ¶12-13

Muzitha kusankha zinthu zimene ndi zofunikadi kwambiri.—Afil. 1:10.

Tonsefe timafuna kuti tizipeza zinthu zofunika pa moyo wathu komanso wa anthu a m’banja lathu. (Mlal. 7:12; 1 Tim. 5:8) M’pake kuti tikamasankha ntchito timaganizira ndalama zomwe tingamalandire. Koma ngati munthu atamangoganizira zimenezi zokha, akhoza kukhala munthu amene akuyenda motsogoleredwa ndi zimene akuona. Ngati tili ndi chikhulupiriro tidzaganizira mmene ntchito yomwe tingasankhe ingakhudzire ubwenzi wathu ndi Yehova. Tingadzifunse kuti: ‘Kodi ntchitoyi ichititsa kuti ndizichita zimene Yehova amadana nazo?’ (Miy. 6:​16-19) ‘Kodi isokoneza kulambira kwanga komanso izichititsa kuti ndizisiyana ndi banja langa kwa nthawi yaitali?’ Ngati ndi choncho, sizingakhale bwino kuvomera ntchitoyo ngakhale kuti ntchito zikusowa. Chifukwa chakuti tili ndi chikhulupiriro, zimene tingasankhe ziyenera kusonyeza kuti tikukhulupirira kuti Yehova adzatisamalira.—Mat. 6:33; Aheb. 13:5. w25.03 21 ¶5-6

Muzikomerana mtima, muzisonyezana chifundo chachikulu komanso muzikhululukirana ndi mtima wonse.—Aef. 4:32.

Nthawi zonse tiziyesetsa kuona abale ndi alongo athu ngati mmene Yehova amawaonera. Tingachite zimenezi poona makhalidwe abwino amene ali nawo osati oipa, omwe pakapita nthawi amawasiya. Tingathetse kusamvana kulikonse mwachikondi. Ndiyeno anthu amene amafuna kuchitiridwa zimenezi adzakopeka n’kulowa m’paradaiso wauzimu. Tidzapitiriza kuyamikira Yehova mpaka kalekale chifukwa cha paradaiso amene watikonzerayu. Aliyense amene akufuna kukhala ndi moyo wabwino, kutsitsimulidwa, kukhala wosatekeseka ndiponso wotetezeka ayenera kulowa m’paradaisoyu ndipo sayenera kutulukamo. Komabe tiyenera kukhala osamala chifukwa Satana amafunitsitsa kutichotsamo. (1 Pet. 5:8; Chiv. 12:9) Tisalole kuti iye achite zimenezo. Tiyeni tizichita zonse zomwe tingathe kuti paradaiso wauzimuyu akhalebe woyera, wokongola komanso wamtendere. w24.04 24-25 ¶18-19

Muziika Ufumu . . . pamalo oyamba.—Mat. 6:33.

Makolo, mungathe kuthandiza ana anu kuti azitumikira Yehova ndi mtima wawo wonse. Zolankhula komanso zochita zanu zizisonyeza kuti zinthu zokhudza kulambira monga kuphunzira Baibulo, kupezeka pamisonkhano komanso kugwira ntchito yolalikira ndi zofunika kwambiri kuposa chilichonse. Kupanda kutero, anawo akhoza kumangoona ngati ndi a Mboni za Yehova chifukwa chakuti akungotsatira makolo awo. Zotsatira zake n’zakuti sangamaike pamalo oyamba kulambira koona mwinanso akhoza kungosiyiratu kulambira Yehova. Kodi munthu amene wasiya kutumikira Yehova sangadzakhalenso naye pa ubwenzi? Ayi, chifukwa akhoza kulapa n’kuyambiranso kumulambira m’njira yoyenera. Kuti zimenezi zitheke, ayenera kudzichepetsa n’kulola kuti athandizidwe ndi akulu. (Yak. 5:14) N’zoona kuti angafunike kuchita khama, koma khamalo limapindula chifukwa amayambiranso kukhala pa ubwenzi ndi Yehova. w24.07 24-25 ¶18-19

Thawani chiwerewere.—1 Akor. 6:18.

Kodi mungatani kuti chibwenzi chanu chikhale cholemekezeka? Chikondi chanu chikamakula, mumayambanso kutengeka kwambiri ndi mnzanuyo. Ndiye kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuti musachite makhalidwe oipa? Muzipewa kukhala awiriwiri, kumwa mowa kwambiri komanso kukambirana nkhani zosayenera zokhudza kugonana. (Aef. 5:3) Zinthu zimenezi zingachititse kuti mukhale ndi chilakolako cha kugonana komanso kuti kudziletsa kukhale kovuta. Mungachite bwino kumakambirana pafupipafupi zimene mungachite kuti chibwenzi chanu chikhale cholemekezeka. (Miy. 22:3) Pakamapita nthawi, njira zina zosonyezerana chikondi zikhoza kukhala zoyenera. Komabe mukayamba kukhala ndi chilakolako chofuna kugonana, mukhoza kuvutika kusankha zinthu mwanzeru. (Nyimbo 1:2; 2:6) Komanso njira zina zosonyezerana chikondi zikhoza kuchititsa kuti mulephere kudziletsa n’kuchita zosayenera. (Miy. 6:27) Choncho chibwenzi chanucho chisanafike patali muzikambirana n’kugwirizana njira zoyenera kusonyezerana chikondi mogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo.—1 Ates. 4:​3-7. w24.05 29 ¶10-11

Mukati ‘Indeʼ akhaledi inde, ndipo mukati ‘Ayiʼ akhaledi ayi.—Mat. 5:37.

Timafuna kuti anthu ena azitidalira makamaka pa nthawi ya mavuto. (Miy. 17:17) Kodi tingatani kuti tikhale anthu odalirika? Tiyenera kuyesetsa kusonyeza makhalidwe abwino nthawi zonse. Mwachitsanzo, tiziyesetsa kukwaniritsa zimene talonjeza komanso kuyesetsa kusunga nthawi. Akulu odalirika amathandiza kwambiri mpingo. Kodi iwo amachita bwanji zimenezi? Ofalitsa sada nkhawa akadziwa kuti akhoza kulankhula ndi mkulu nthawi ina iliyonse, makamaka woyang’anira kagulu kawo. Ofalitsa amamvanso kuti amakondedwa akadziwa kuti akulu ndi okonzeka kuwathandiza. Ndipo akulu akamapereka malangizo ochokera m’Baibulo komanso mabuku athu osati maganizo awo, abale ndi alongo amawakhulupirira. Abale ndi alongo amakhulupiriranso mkulu amene saulula nkhani zachinsinsi komanso amene amachita zimene walonjeza. w24.06 30 ¶14-15

Mudzawapatsa mtendere wosatha, chifukwa amadalira inu.—Yes. 26:3.

Masiku ano sitingayembekezere kuti Yehova atichotsera mavuto athu onse koma tingamudalire kuti atithandiza. (Sal. 41:3) Iye angagwiritse ntchito mzimu woyera kuti atipatse mphamvu, nzeru komanso mtendere wa mumtima kuti tizipirira. (Miy. 18:14; Afil. 4:13) Amatilimbikitsanso potipatsa chiyembekezo chakuti adzathetsa matenda onse. (Yes. 33:24) Yehova anasunga m’Baibulo mawu amene amatikhazika mtima pansi tikakumana ndi mavuto osiyanasiyana. (Aroma 15:4) Mlongo wina wa ku West Africa atapezeka ndi khansa, ankangokhalira kulira. Iye anati: “Lemba lomwe linandilimbikitsa kwambiri ndi la Yesaya 26:3. . . . Vesili limanditsimikizira kuti Yehova angandithandize kupeza mtendere wa mumtima womwe ungandithandize kudziwa zochita ndikakumana ndi mayeserowo.” Mukakumana ndi vuto lalikulu ndipo mukusowa mtengo wogwira, kodi pali lemba limene limakulimbikitsani? w24.12 24 ¶17-18

Ali chapatali ndithu, bambo akewo anamuona ndipo anagwidwa ndi chifundo. Kenako anamuthamangira nʼkumukumbatira ndipo anamukisa mwachikondi.—Luka 15:20.

Akulu amayesetsa kuthandiza anthu amene asochera. Iwo amafuna kuti nkhosa zotayika zibwerere kwa Yehova. (Luka 15:​22-24, 32) Kumwamba kumakhala chisangalalo chachikulu munthu wochimwa akabwerera, chimodzimodzinso padziko lapansi. (Luka 15:7) N’zoonekeratu kuti Yehova salekerera anthu osalapa. Komabe sawatayiratu, amafuna kuti iwo abwerere. Maganizo a Yehova kwa anthu ochimwa afotokozedwa pa Hoseya 14:​4, pomwe amati: “Ndidzathetsa kusakhulupirika kwawo. Ndidzawakonda mwa kufuna kwanga, chifukwa ndasiya kuwakwiyira.” Mawu amenewa ayenera kuthandiza akulu kuti aziona chizindikiro chilichonse chosonyeza kuti munthu wayamba kulapa. Mawuwa akutsimikiziranso anthu amene anasiya Yehova kuti iye amawakonda ndipo akufuna kuti abwerere mwamsanga. w24.08 28 ¶8-9

Sonyezani kuti ndinu oyamikira.—Akol. 3:15.

Zoona n’zakuti si nthawi zonse pomwe anthu amayamikira zimene tachita. Nthawi zina tingapereke nthawi, mphamvu ndi zinthu zathu koma pambuyo pake n’kudabwa kuti munthu sakuyamikira zimene tamuchitira. Ngati izi zitatichitikira, kodi tingatani kuti tisakwiye n’kupitirizabe kukhala osangalala? Tizikumbukira kuti sikuti timasangalala chifukwa cha zimene munthu amachita tikamupatsa zinthu. (Mac. 20:35) Tikhoza kumasangalalabe ngakhale zitaoneka kuti munthuyo sakuyamikira. Maganizo athu azikhala pa kutsanzira Yehova. Iye amapereka zinthu zabwino kwa anthu kaya iwo ayamikira kapena ayi. (Mat. 5:​43-48) Yehova amalonjeza kuti tikamapereka zinthu “osayembekezera kulandira kalikonse” ndiye kuti ‘mphoto yathu idzakhala yaikulu.’ (Luka 6:35) Mawu akuti “kalikonse” akhoza kutanthauzanso zimene ena angachite posonyeza kuyamikira. Kaya atiyamikira kapena ayi, nthawi zonse Yehova adzatibwezera chifukwa cha zabwino zimene timachitira ena komanso chifukwa ‘chopereka mosangalala.’—Miy. 19:17; 2 Akor. 9:7. w24.09 29 ¶14-16