February

Lamlungu, February 1

February

Munthu amalemekezeka akapewa mkangano, koma aliyense wopusa amafulumira kuyambitsa mkangano.—Miy. 20:3.

Abale amene amasonyeza makhalidwe abwino amathandiza kwambiri mumpingo. Munthu wololera amalimbikitsa mtendere. Kuti mukhale ololera, muyenera kumamvetsera ena komanso kukhala okonzeka kuyendera maganizo awo. Ngati muli pa zokambirana, kodi mumakhala wokonzeka kuyendera mfundo zimene ambiri akuona kuti n’zoyenera ngati sizikuphwanya mfundo za m’Baibulo? Simuyenera kukhala munthu womva zake zokha. Munthu wololera amazindikira ubwino wokhala ndi alangizi ambiri. (Gen. 13:​8, 9; Miy. 15:22) M’malo mokhala wankhanza kapena wokonda kukangana, ayenera kukhala wofatsa komanso wochita zinthu mosamala. Munthu wokonda mtendere amayamba ndi iyeyo kuchita zinthu mwamtendere ngakhale zinthu zitavuta kwambiri. (Yak. 3:​17, 18) Mukamalankhula mokoma mtima, mukhoza kufewetsa mitima ya anthu ena ngakhalenso otsutsa.—Ower. 8:​1-3; Miy. 25:15; Mat. 5:​23, 24. w24.11 23 ¶13

Iye adzatumiza angelo ndipo adzasonkhanitsa osankhidwa ake kuchokera kumphepo 4, kuchokera kumalekezero a dziko lapansi kukafika kumalekezero amumlengalenga.—Maliko 13:27.

Ngakhale kuti Khristu anatifera “kamodzi kokha basi,” pali zambiri zimene akuchita potithandiza. (Aroma 6:10) Kodi ndi zinthu ziti zimene akuchita? Iye akugwirabe ntchito kuti atipatse zinthu zabwino zimene zimatheka chifukwa cha dipo. Mwachitsanzo, iye amagwira ntchito mwakhama monga Mfumu, Mkulu wa Ansembe komanso mutu wa mpingo. (1 Akor. 15:25; Aef. 5:23; Aheb. 2:17) Iye akuyang’anira ntchito yosonkhanitsa odzozedwa komanso a khamu lalikulu ndipo adzamaliza kuchita zimenezi chisautso chachikulu chisanathe. (Mat. 25:32) Yesu amaonetsetsanso kuti atumiki ake okhulupirika akulandira chakudya chauzimu chokwanira m’masiku otsiriza ano. (Mat. 24:45) Ndipo mu Ulamuliro wa Zaka 1,000, iye adzapitiriza kutithandiza. Apatu Yehova anapereka Mwana wake ndi mtima wonse kuti atithandize. w25.01 24 ¶12

Kuonedwa olungama chifukwa cha kukoma mtima kwake kwakukulu kumene wakusonyeza powamasula ndi dipo lolipiridwa ndi Khristu Yesu, kuli ngati mphatso yaulere.—Aroma 3:24.

Yehova amatikhululukira ndi mtima wonse ndipo nkhaniyo imathera pomwepo. Zimenezi zimatithandiza kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Atate wathu wakumwambayu. Tizikumbukira kuti kukhululuka kwa Yehova ndi mphatso. Iye amatipatsa mphatsoyi chifukwa cha chikondi komanso kukoma mtima kwake kwakukulu. Samatikhululukira chifukwa chakuti ndi ufulu wathu kuti atikhululukire. Timayamikira kwambiri Yehova chifukwa chakuti iye ndi Mulungu amene ‘amakhululuka ndi mtima wonse.’ (Sal. 130:4; Aroma 4:8) Koma kuti Yehova atikhululukire timafunika kuchita kanthu kena kofunika kwambiri. Yesu ananena kuti: “Ngati simukhululukira anthu machimo awo, Atate wanu sadzakukhululukiraninso machimo anu.” (Mat. 6:​14, 15) Choncho tiyenera kutsanzira Yehova n’kumakhululukiranso anthu ena. w25.02 13 ¶18-19

Mulungu adzaukitsa olungama ndi osalungama omwe.Mac. 24:15.

Taganizirani za anthu a ku Sodomu ndi Gomora. Loti yemwe anali munthu wolungama, ankakhala pakati pawo. Koma kodi tikudziwa ngati Loti analalikira kwa anthu onsewo? Ayi. N’zoona kuti iwo anali oipa koma kodi onsewo ankadziwa kuti izi n’zabwino ndipo izi n’zoipa? Kumbukirani kuti gulu la amuna a mumzindawo linkafuna kugwiririra alendo a Loti. Baibulo limanena kuti pachigulupo “panali anyamata komanso achikulire.” (Gen. 19:4; 2 Pet. 2:7) Ndiye kodi tingatsimikize kuti Yehova Mulungu yemwe ndi wachifundo, anaweruza kuti anthu onsewo afe ndipo asadzaukitsidwe? Yehova anatsimikizira Abulahamu kuti mumzindawo munalibe anthu olungama ngakhale 10. (Gen. 18:32) Iwo anali osalungama choncho Yehova anawaweruza mwachilungamo powawononga chifukwa cha zimene ankachita. Ndiye kodi tinganene motsimikiza kuti palibe aliyense wa anthu amenewo, adzakhale m’gulu la “osalungama” omwe adzaukitsidwe? Ayi, sitingatero. w24.05 2 ¶3; 3 ¶8

Nthawi zonse muziika Ufumu ndi mfundo zolungama za Mulungu pamalo oyamba pa moyo wanu, ndipo iye adzakupatsani zinthu zina zonsezi.—Mat. 6:33.

Mavuto a zachuma, achititsa anthu ena kukagwira ntchito kutali ndi banja lawo, koma zotsatira zake sizimakhala zabwino. Mukamasankha ntchito, musamangoganizira ndalama zimene mungapeze. Koma muziganiziranso mmene zingakhudzire ubwenzi wanu ndi Yehova. (Luka 14:28) Mungadzifunse kuti: ‘N’chiyani chingachitikire banja langa ngati nditapita kutali? Kodi ndizikwanitsa kupezeka pamisonkhano komanso mu utumiki?’ Ngati muli ndi ana muyeneranso kudzifunsa funso lofunika ili: ‘Ngati nditachoka, kodi ndingalere bwanji ana anga “powapatsa malangizo komanso kuwaphunzitsa mogwirizana ndi zimene Yehova amanena?”’ (Aef. 6:4) Muziyendera maganizo a Mulungu osati a achibale kapena anzanu amene salemekeza mfundo za m’Malemba. w25.03 29 ¶12

Tisakhalenso ana.Aef. 4:14.

Munthu amene sakukula mwauzimu, akhoza kukhulupirira mosavuta zinthu zachinyengo zimene zimafalitsidwa komanso mabodza ndipo angapusitsidwenso ndi ampatuko. Iye akhoza kumachitira nsanje anthu ena, kukangana nawo, kapena kukwiya msanga ndipo nthawi zambiri akhoza kuchita zoipa ngati wayesedwa. (1 Akor. 3:3) Malemba amayerekezera kukula mwauzimu ndi mmene mwana amakulira n’kukhala munthu wamkulu. (Aef. 4:15) Mwana sadziwa zinthu zambiri choncho amafunika kutsogoleredwa. Mwachitsanzo, mayi akhoza kugwira mkono wa mwana wake wamng’ono kuti adumphe msewu. Koma mwana uja akamakula, mayi akhoza kumulola kuti adutse yekha koma angamamukumbutse kuti aziyang’ana mbali zonse asanadutse. Ndiyeno mwanayo akakula amachita zinthu ngati zimenezi payekha. Mofanana ndi zimenezi, Mkhristu wolimba mwauzimu akafuna kusankha zochita, amaganizira mfundo za m’Baibulo kuti adziwe maganizo a Yehova pa nkhaniyo ndipo amachita zinthu zoyenera. w24.04 3 ¶5-6

Inu Yehova, ndi ndani amene angakhale mlendo mutenti yanu?—Sal. 15:1.

Kwa zaka zambiri, anzake a Yehova anali kumwamba kokha komwe iye amakhala. Pambuyo pake analenga anthu padzikoli omwe anakhalanso alendo mutenti yake. Ena mwa alendo akewa anali Inoki, Nowa, Abulahamu komanso Yobu. Atumiki okhulupirikawa amafotokozedwa kuti anali anzake a Mulungu kapena kuti anthu omwe anayenda “ndi Mulungu woona.” (Gen. 5:24; 6:9; Yobu 29:4; Yes. 41:8) Kwa zaka zambiri, Yehova wakhala akuitana anzake kuti akhale alendo ake. (Ezek. 37:​26, 27) Ulosi wa Ezekieli umasonyeza kuti Mulungu amafunitsitsa kuti atumiki ake okhulupirika akhale naye pa ubwenzi wabwino. Iye amalonjeza kuti adzachita nawo “pangano lamtendere.” Ulosiwu umanena za nthawi imene anthu omwe ali ndi chiyembekezo chodzapita kumwamba ndi omwe ali ndi chiyembekezo chodzakhala padzikoli, adzagwirizane n’kukhala “gulu limodzi” la nkhosa mutenti yake yophiphiritsa. (Yoh. 10:16) Nthawi imeneyo ndi inoyi. w24.06 2 ¶2, 4; 3 ¶5

Tinalimba mtima mothandizidwa ndi Mulungu wathu.—1 Ates. 2:2.

Anthu a Yehovafe timayesetsa kukhala kumbali ya Ufumu wa Mulungu. Koma kuchita zimenezi kumafuna kuti tikhale olimba mtima. (Mat. 6:33) Mwachitsanzo, m’dziko loipali timafunika kukhala olimba mtima kuti tizitsatira mfundo za makhalidwe abwino za Yehova komanso kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu. Timafunikanso kulimba mtima kuti tisalowerere ndale m’dzikoli, limene anthu ake ndi osagwirizana. (Yoh. 18:36) Atumiki ambiri a Yehova akukumana ndi mavuto azachuma, amazunzidwa ndipo ena amaikidwa m’ndende chifukwa chokana kulowerera ndale kapena kulowa usilikali. Timalimbikitsidwa komanso kupeza mphamvu tikamaganizira zitsanzo za anthu omwe molimba mtima anatsimikiza kukhala kumbali ya ulamuliro wa Yehova. Mwachitsanzo, Mfumu yathu Khristu Yesu anakanitsitsa kulowerera ndale m’dziko la Satanali. (Mat. 4:​8-11; Yoh. 6:​14, 15) Nthawi zonse ankadalira Yehova kuti amupatse mphamvu. w24.07 3 ¶4; 4 ¶7

Anathyola chipatso cha mtengowo nʼkudya. Kenako anatenga zina nʼkukapatsa mwamuna wake pa nthawi imene anali limodzi, ndipo nayenso anadya.—Gen. 3:6.

Yehova anachititsa kuti nkhaniyi ilembedwe n’cholinga choti izitithandidza. Imatithandiza kumvetsa chifukwa chake iye amadana kwambiri ndi uchimo. Uchimo umachititsa kuti titalikirane ndi Atate wathu komanso umabweretsa imfa. (Yes. 59:2) N’chifukwa chake Satana yemwe anayambitsa mavutowa, amakonda uchimo komanso kulimbikitsa anthu kuti azichimwa. Iye ayenera kuti ankaganiza kuti kuchimwitsa Adamu ndi Hava kwasokoneza cholinga cha Mulungu chokhudza anthu. Koma sankadziwa kukula kwa chikondi cha Yehova. Mulungu sanasinthe cholinga chomwe anali nacho chokhudza ana a Adamu ndi Hava. Iye amakonda kwambiri anthu choncho mwamsanga anawapatsa chiyembekezo. (Aroma 8:​20, 21) Yehova ankadziwa kuti ena mwa ana a Adamuwo adzasankha kumukonda komanso kumumvera. Choncho pokhala Atate komanso Mlengi wawo, iye adzawamasula ku uchimo ndiponso kuwathandiza kuti akhale naye pa ubwenzi. w24.08 3 ¶3-4

Muzitha kusankha zinthu zimene ndi zofunikadi kwambiri.—Afil. 1:10.

Anthu a Yehova ambiri amatanganidwa kugwira ntchito kuti azipeza zofunika pa moyo wawo ndi wa banja lawo. (1 Tim. 5:8) Akhristu ambiri amasamalira achibale awo okalamba kapena amene akudwala. Komanso tonsefe timafunika nthawi yambiri yosamalira thanzi lathu. Kuwonjezera pa zonsezi, timapatsidwa zochita kumpingo. Ndipo ntchito ina yofunika kwambiri yomwe timafunika kugwira nawo ndi yolalikira. Kuwerenga Baibulo ndi chimodzi mwa ‘zinthu zofunika kwambiri’ kwa Akhristufe choncho tiyenera kuyesetsa kuti tiziliwerenga. Ponena za munthu wosangalala, salimo loyamba limanena kuti: “Amakonda kwambiri chilamulo cha Yehova, ndipo amawerenga ndi kuganizira mozama chilamulocho masana ndi usiku.” (Sal. 1:​1, 2) Izi zikutanthauza kuti tiyenera kumapeza nthawi yowerenga Baibulo. Koma kodi nthawi yabwino yoliwerenga ndi iti? Aliyense angasankhe nthawi yomwe ili yabwino kwa iyeyo. Mwachidule, tingati ndi nthawi imene mukhoza kukwanitsa kumawerenga nthawi zonse. w24.09 3 ¶5-6

Aliyense ayenera kunyamula katundu wake.Agal. 6:5.

Kodi Mkhristu wolimba mwauzimu samafunikira kuthandizidwa ndi wina aliyense? Ayi. Nthawi zina anthu olimba mwauzimu amafunikiranso kuthandizidwa. Munthu amene ndi mwana mwauzimu angayembekezere kuti anthu ena azimuuza kapena kumusankhira zochita pa nkhani zimene anafunika kusankha yekha. Pomwe Mkhristu wolimba mwauzimu akapempha anthu ena anzeru kapena odziwa zambiri kuti amuthandize, amadziwa kuti Yehova amayembekezera kuti aliyense ayenera “kunyamula katundu wake.” Anthu akuluakulu amaoneka mosiyana. Mofanana ndi zimenezi, Akhristu olimba mwauzimu amasiyananso pa nkhani ya makhalidwe monga nzeru, kulimba mtima, kupatsa komanso kuganizira ena. Kuwonjezera pamenepo, Akhristu awiri olimba mwauzimu akakumana ndi zinthu zofanana akhoza kusankha zinthu zosiyana koma zonse zili zogwirizana ndi mfundo za m’Malemba. Izi zimachitika makamaka pa nkhani zokhudza chikumbumtima. Chifukwa chozindikira mfundo imeneyi, iwo saweruza ena akaona kuti asankha mosiyana. Chimene amafuna kwambiri n’kukhalabe ogwirizana.—Aroma 14:10; 1 Akor. 1:10. w24.04 4 ¶7-8

Nkhawa zitandichulukira, munanditonthoza komanso kundisangalatsa.—Sal. 94:19.

Kodi mungatani ngati mumadziona kuti ndinu wosafunika? Muziwerenga komanso kuganizira malemba amene amasonyeza kuti Yehova amakuonani kuti ndinu wamtengo wapatali. Ngati mwalephera kukwaniritsa cholinga chinachake kapenanso kukhumudwa chifukwa chakuti simukuchita zambiri ngati ena, musamadziweruze mopitirira malire. Yehova sayembekezera kuti muzichita zimene simungakwanitse. (Sal. 103:​13, 14) Ngati munachitiridwa zinazake zoipa, musamadziimbe mlandu kuti inuyo ndi amene munachititsa. Simumayenera kuchitiridwa zinthu ngati zimenezo. Muzikumbukira kuti Yehova adzaweruza amene amachita zoipa, osati amene amachitiridwa zoipa. (1 Pet. 3:12) Musamakayikire kuti Yehova angagwiritse ntchito inuyo pothandiza ena. Iye wakupatsani mwayi wogwira naye limodzi ntchito yolalikira. (1 Akor. 3:9) Zimene zinachitika pa moyo wanu zingakuthandizeni kuti muzisonyeza chifundo kwa ena komanso kumvetsa mmene akumvera. Choncho mungachite zambiri powathandiza. w24.10 7-8 ¶6-7

Kodi Mulungu sadzaonetsetsa kuti chilungamo chachitika kwa osankhidwa ake, amene amafuulira kwa iye masana ndi usiku, pamene akuwalezera mtima? Ndithu ndikukuuzani, iye adzaonetsetsa kuti chilungamo chachitika kwa iwo mwamsanga.—Luka 18:​7, 8.

Popeza ‘Yehova amakonda chilungamo,’ zimamukhudza anthu ena akamachitira atumiki ake zopanda chilungamo. (Sal. 37:28) Yesu anatitsimikizira kuti Yehova “adzaonetsetsa kuti chilungamo chachitika . . . mwamsanga” komanso pa nthawi yoyenera. Posachedwa, iye adzathetsa mavuto onse ndi zopanda chilungamo zamtundu uliwonse. (Sal. 72:​1, 2) Pamene tikuyembekezera nthawi imene Yehova adzabweretse chilungamo, iye amatithandiza kupirira tikakumana ndi zopanda chilungamozo. (2 Pet. 3:13) Iye amatiphunzitsa mmene tingachitire zinthu mwanzeru. Kudzera mwa Mwana wake, iye amatipatsa chitsanzo chabwino cha mmene tingachitire tikakumana ndi zinthu zoterezi. Komanso amatipatsa malangizo othandiza omwe tingatsatire. w24.11 2-3 ¶3-4

Muwapatse chakudya.—Mat. 14:16.

Zimene Yesu ananena zoti apatse anthu chakudya zinali zovuta chifukwa panali amuna pafupifupi 5,000. Tikaphatikiza akazi ndi ana, ndiye kuti payenera kuti panali anthu pafupifupi 15,000 oti awadyetse. (Mat. 14:21) Andireya anati: “Pali kamnyamata pano kamene kali ndi mitanda 5 ya mkate wa balere ndi tinsomba tiwiri. Koma nanga zimenezi zingakwanire chigulu cha anthu chonsechi?” (Yoh. 6:9) Mikate ya balere ndi imene anthu ambiri ankadya ndipo nsombazo ziyenera kuti zinali zouma komanso zothira mchere. Koma chakudya chimene mnyamatayo anali nacho chinali chosakwanira kwa gulu lonselo. Pofuna kuthandiza anthuwo, Yesu anawauza kuti akhale pa udzu m’magulu. (Maliko 6:​39, 40; Yoh. 6:​11-13) Kenako timawerenga kuti Yesu anapemphera kwa Atate wake pothokoza chifukwa cha chakudyacho. Zinali zomveka kuti Yesu athokoze Mulungu chifukwa ndi amene amapereka chakudya. Apatu Yesu anapereka chitsanzo chabwino kwa tonsefe kuti tizipemphera kaye tisanayambe kudya. Kenako Yesu anapereka chakudyacho kwa ophunzira ake kuti agawire anthuwo. Iwo anadya n’kukhuta mpaka chakudya china chinatsala. w24.12 2-3 ¶3-4

Tamandani Yehova Mulungu wanu.1 Mbiri 29:20.

Yesu ali padzikoli, ankapereka ulemerero kwa Atate wake posonyeza kuti ndi amene ankamupatsa mphamvu kuti azichita zinthu zodabwitsa. (Maliko 5:​18-20) Zimene Yesu ankalankhula zokhudza Atate wake komanso mmene ankachitira zinthu ndi ena, zinkapereka ulemerero kwa Yehova. Pa nthawi ina Yesu ankaphunzitsa ku sunagoge. Pagulu la anthu amene ankawaphunzitsawo panali mayi wina yemwe anali atavutitsidwa ndi chiwanda kwa zaka 18. Chiwandacho chinachititsa kuti apindike msana moti sankathanso kuweramuka. Zinalitu zomvetsa chisoni kwambiri. Yesu anamumvera chisoni ndipo anamuyandikira n’kumalankhula mokoma mtima kuti: “Mayi, mwamasuka ku matenda anu.” Kenako anamugwira ndipo mayiyo anaimirira moongoka “n’kuyamba kutamanda Mulungu,” Mayiyo anakhalanso wamphamvu. (Luka 13:​10-13) Mofanana ndi mayiyu, tili ndi zifukwa zomveka zopatsira Yehova ulemerero. w25.01 2-3 ¶3-4

Mutikhululukire machimo athu.—Luka 11:4.

Kodi n’zotheka kudzapezanso zonse zimene Adamu ndi Hava anataya? Zingatheke koma osati patokha. (Sal. 49:​7-9) Popanda kuthandizidwa ndi Yehova sitingakhale ndi chiyembekezo chodzakhalanso ndi moyo kapena kudzaukitsidwa. Ndipotu bwenzi tikungofa popanda chiyembekezo chilichonse ngati zinyama. (Mlal. 3:19; 2 Pet. 2:12) Atate wathu wachikondi Yehova, watipatsa mphatso yomwe yalipira ngongole ya uchimo imene tinatengera kwa Adamu. Pofotokoza zimenezi Yesu ananena kuti: “Mulungu anakonda kwambiri dziko moti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense womukhulupirira asawonongedwe koma akhale ndi moyo wosatha.” (Yoh. 3:16) Kuwonjezera pamenepa, mphatsoyi imatithandizanso kuti tikhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Tingapindule ndi mphatso yamtengo wapataliyi, komanso kuti machimo athu omwe ali ngati ngongole angakhululukidwe. w25.02 3 ¶3-6

[Saulo] kenako anapita kukabatizidwa.—Mac. 9:18.

Kodi n’chiyani chinathandiza Saulo kuti abatizidwe? Yesu atalankhula ndi Saulo kuchokera kumwamba, Saulo anasiya kuona. (Mac. 9:​3-9) Kwa masiku atatu iye sankadya ndipo ayenera kuti ankaganizira zimene zinamuchitikirazo. Apa Saulo anali atatsimikiza kuti Yesu ndi Mesiya ndiponso kuti otsatira ake ndi amene anali m’chipembedzo choona. Tingaphunzire zambiri kuchokera kwa Saulo. Iye akanatha kulola kuti kunyada kapena kuopa anthu kumulepheretse kubatizidwa. Koma iye sanalole kuti zimenezi zichitike. Ankafunitsitsa kukhala Mkhristu ngakhale kuti ankadziwa kuti adzazunzidwa. (Mac. 9:​15, 16; 20:​22, 23) Atabatizidwa, iye anapitiriza kudalira Yehova kuti azimuthandiza kupirira mayesero osiyanasiyana. (2 Akor. 4:​7-10) Inunso mukabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova, muzikumana ndi mayesero omwe angayese chikhulupiriro chanu. Koma Yehova ndi Khristu adzakuthandizani kuti mupitirizebe kukhala okhulupirika.—Afil. 4:13. w25.03 4 ¶8-9

Sikuti ndikungothamanga osadziwa kumene ndikupita.1 Akor. 9:26.

Kuwerenga Baibulo ndi cholinga chabwino kwambiri chimene tingakhale nacho. Koma pamafunika zambiri kuti tizipindula tikamawerenga Mawu a Mulungu. Taganizirani chitsanzo ichi: Zomera zambiri zimafuna mvula. Koma ngati mvula yambiri itagwa pa nthawi yochepa, nthaka ingadzadze madzi. Zikatero mvula yambiri imakhala yosathandiza. Pamafunika nthawi kuti madzi alowe munthaka n’kusungika kuti zomera zigwiritse ntchito. Ifenso tiyenera kupewa kuwerenga Baibulo mofulumira kwambiri mpaka kufika polephera kuganizira zomwe tikuwerengazo, kuzikumbukira komanso kuzigwiritsa ntchito. (Yak. 1:24) Kodi nthawi zina mumaona kuti mumawerenga Baibulo mofulumira kwambiri? Ngati ndi choncho, kodi muyenera kuchita chiyani? Muyenera kuchepetsa liwiro. Muziyesetsa kuganizira zimene mukuwerenga kapena zimene mwawerenga. Kuchita zimenezi si kovuta. Mukhoza kuwonjezera nthawi imene mumaphunzira kuti muzipeza nthawi yoganizira zimene mwawerenga. w24.09 4 ¶7-9

Muzimvera amene akukutsogolerani.Aheb. 13:17.

Akalandira malangizo, akulu ayenera kuwawerenga mosamala n’kuyesetsa mmene angathere kuti awatsatire. Kuwonjezera pa kupatsidwa malangizo a mmene angachititsire misonkhano komanso kupemphera, amapatsidwanso malangizo a mmene angasamalirire nkhosa za Khristu. Akulu amene amatsatira malangizo a gulu amathandiza kuti amene akuyang’aniridwawo azimva kuti ndi otetezeka komanso amakondedwa. Tikalandira malangizo ochokera kwa akulu tiyenera kuwatsatira ndi mtima wonse. Tikatero timathandiza akuluwo kuti azigwira bwino ntchito yawo. Baibulo limatilimbikitsa kuti tizimvera komanso kugonjera amene akutitsogolera. (Aheb. 13:​7, 17) N’chifukwa chiyani zimenezi zimakhala zovuta nthawi zina? Chifukwa chakuti abale amenewa si angwiro. Koma tikamaganizira kwambiri zimene amalakwitsa osati zimene amachita bwino, timakhala tikuthandiza adani athu. Kodi timawathandiza bwanji? Timayamba kukayikira gulu la Mulungu. w24.04 10 ¶11-12

Adzalekanitsa anthu.—Mat. 25:32.

Kodi anthu onse omwe adzafe pa nthawi ya chisautso chachikulu sadzakhala ndi chiyembekezo chodzaukitsidwa? Malemba amafotokoza momveka bwino kuti anthu otsutsa omwe Yehova ndi gulu lake la nkhondo adzawawononge pa Aramagedo sadzaukitsidwa. (2 Ates. 1:​6-10) Koma bwanji za anthu amene adzafe pa nthawiyo chifukwa cha ukalamba, matenda, ngozi kapena kuphedwa ndi anthu anzawo? (Mla. 9:11; Zek. 14:13) Kodi ena mwa anthuwa angadzakhale m’gulu la “osalungama” omwe adzaukitsidwe m’dziko latsopano? (Mac. 24:15) Sitikudziwa. Koma tikudziwa zambiri zimene zidzachitike m’tsogolo. Mwachitsanzo, tikudziwa kuti pa Aramagedo, anthu adzaweruzidwa potengera mmene ankachitira zinthu ndi abale ake a Khristu. (Mat. 25:40) Ndipo amene adzaweruzidwe kuti ndi nkhosa, ndi amene anathandiza odzozedwa komanso Khristu.—Chiv. 12:17. w24.05 10-11 ¶9-11

Litamandike Thanthwe langa. Mulungu amene amandipulumutsa alemekezeke.Sal. 18:46.

Baibulo limanena kuti nthawi tikukhalayi ndi “nthawi yapadera komanso yovuta.” (2 Tim. 3:1) Kuwonjezera pa mavuto amene aliyense amakumana nawo m’dzikoli, anthu a Yehova amatsutsidwa komanso kuzunzidwa. N’chiyani chingatithandize kuti tizitumikirabe Yehova ngakhale pamene tikukumana ndi mavutowa? Chinthu chimodzi chimene chimatithandiza ndi kudziwa kuti Yehova ndi “Mulungu wamoyo.” (Yer. 10:10; 2 Tim. 1:12) Yehova amaona mavuto amene timakumana nawo ndipo nthawi zonse amafunitsitsa kutithandiza. (2 Mbiri 16:9; Sal. 23:4) Kukumbukira kuti Mulungu ndi wamoyo kungatithandize kulimbana ndi vuto lililonse limene tingakumane nalo. w24.06 20 ¶1-2

Njira ya olungama ili ngati kuwala kwamphamvu kwa mʼmawa kumene kumawonjezereka mpaka kunja kutawala kwambiri.—Miy. 4:18.

Tiyenera kupitiriza kukhulupirira gulu la Yehova. Ngati pakufunika kusintha zimene timakhulupirira pa mfundo zinazake za m’Baibulo kapenanso njira imene timagwirira ntchito za Ufumu, anthu amene amatitsogolera sazengereza kusintha. Iwo amachita zimenezi chifukwa amafunitsitsa kusangalatsa Yehova. Iwo amayesetsanso kusankha zochita pogwiritsa ntchito Mawu a Mulungu chifukwa m’Baibulo ndi momwe muli mfundo zimene Akhristu onse amatsatira. Mtumwi Paulo analangiza kuti: “Gwiritsitsabe chitsanzo cha mawu olondola.” (2 Tim. 1:13) Mawu akuti “chitsanzo cha mawu olondola,” amatanthauza mfundo za m’Baibulo zimene Akhristu amakhulupirira. (Yoh. 17:17) Chilichonse chimene timakhulupirira chimachokera pa mfundo zimenezi. Gulu la Yehova latiphunzitsa kuti tizigwiritsitsa mfundozi. Tikamachita zimenezi tidzadalitsidwa. w24.07 11-12 ¶12-13

Yehova . . . akukulezerani mtima chifukwa sakufuna kuti munthu aliyense adzawonongedwe, koma akufuna kuti anthu onse alape.—2 Pet. 3:9.

Popeza ankadziwa mmene munthu amamvera akalapa n’kukhululukidwa, mtumwi Petulo akanatha kuphunzitsa ena zokhudza nkhanizi. Pa nthawi ina pambuyo pa Chikondwerero cha Pentekosite, Petulo anakambira nkhani gulu la Ayuda yofotokoza kuti iwo anapha Mesiya. Koma mwachikondi iye anawalimbikitsa kuti: “Lapani ndi kutembenuka kuti machimo anu afafanizidwe, ndiponso kuti nyengo zotsitsimutsa zibwere kuchokera kwa Yehova.” (Mac. 3:​14, 15, 17, 19) Apa Petulo anasonyeza kuti kulapa kumamuthandiza munthu wochimwa kuti atembenuke, kutanthauza kuti asiye zoipa zimene amaganiza kapena kuchita, n’kuyamba kuchita zabwino zimene zingasangalatse Mulungu. Mtumwiyu anasonyezanso kuti Yehova amakhululuka kotheratu, zomwe zimakhala ngati wafufuta machimowo. N’zolimbikitsatu kudziwa kuti tikalapa machimo athu ngakhale atakhala akuluakulu, Yehova amatikhululukira. w24.08 12 ¶14

Musamakonde ndalama.—Aheb. 13:5.

Tikhoza kupewa mtima wokonda chuma ngati timakhulupirira kwambiri kuti mapeto a dzikoli ali pafupi. Ndipotu anthu ‘adzataya siliva wawo m’misewu’ chifukwa adzazindikira kuti “siliva wawo kapena golide wawo sadzatha kuwapulumutsa pa tsiku limene Yehova adzasonyeze mkwiyo wake waukulu.” (Ezek. 7:19) M’malo mofuna kukhala ndi ndalama zambiri, tizichita zinthu zimene zingatithandize kuti tizipeza zinthu zofunika kwambiri, uku tikutumikira Yehova. Izi zikuphatikizapo kupewa ngongole zosafunika kapenanso kutanganidwa ndi kusamalira zinthu zambiri zimene tili nazo. Tidzapewanso kukonda kwambiri zinthu zimene tili nazo kale. (Mat. 6:​19, 24) Pamene mapeto a dzikoli akuyandikira, chikhulupiriro chathu chingayesedwe pa nkhani ya chuma komanso zinthu zina. w24.09 11 ¶13-14

Amene akuganiza kuti waima bwinobwino asamale kuti asagwe.—1 Akor. 10:12.

Anthufe tikhoza kusiyiratu makhalidwe ena oipa. Koma tikhoza kumavutikabe ndi mtima wofuna kuchita zoipa. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mtumwi Petulo. Chifukwa choopa anthu iye anakana Yesu katatu. (Mat. 26:​69-75) Koma pamene analankhula molimba mtima pamaso pa Khoti Lalikulu la Ayuda, zinkaoneka ngati anasiya kuchita mantha. (Mac. 5:​27-29) Koma pa nthawi ina patapita zaka zingapo, iye anasiya kudya ndi Akhristu a mitundu ina “chifukwa ankaopa anthu odulidwawo.” (Agal. 2:​11, 12) Apa tingati anayambiranso kuopa anthu. N’kutheka kuti vuto lake la manthali linali lisanatheretu. Mwina ifenso tingamalimbane ndi vuto linalake mobwerezabwereza Chomwe chingatithandize ndi kutsatira malangizo a Yesu pa nkhani ya mayesero. Iye anati: “Khalani maso.” (Mat. 26:41) Ngakhale pa nthawi imene mukuona kuti ndinu olimba mwauzimu, muzipitiriza kupewa zinthu zimene zingachititse kuti mulowe m’mayesero. Muzipitiriza kuchita zinthu zimene zinakuthandizani kuti mugonjetse vutolo.—2 Pet. 3:14. w24.07 18-19 ¶17-19

Anapereka amuna kuti akhale mphatso.—Aef. 4:8.

Yesu ndi wowolowa manja kuposa munthu aliyense. Ali padziko lapansi anagwiritsa ntchito mphamvu zimene anali nazo pothandiza ena. (Luka 9:​12-17) Iye anatipatsa mphatso yaikulu kwambiri potifera. (Yoh. 15:13) Yesu wakhala akutipatsanso zinthu zambiri kungochokera pamene anaukitsidwa n’kubwerera kumwamba. Iye analonjeza kuti adzapempha Atate wake kuti atipatse mzimu woyera kuti uzidzatiphunzitsa komanso kutilimbikitsa ndipo ndi zimene wachita. (Yoh. 14:16, 17, mawu a m’munsi; 16:13) Amatiphunzitsanso pa ntchito yophunzitsa anthu Baibulo yomwe ikuchitika padziko lonse pogwiritsa ntchito misonkhano yampingo. (Mat. 28:​18-20) Mtumwi Paulo analemba kuti Yesu atapita kumwamba, “anapereka amuna kuti akhale mphatso.” (Aef. 4:​7, 8) Paulo anafotokoza kuti Yesu anapereka amuna amenewa kuti azithandiza mpingo. (Aef. 1:​22, 23; 4:​11-13) Amuna amenewa si angwiro, choncho amalakwitsa zinthu zina. (Yak. 3:2) Koma Ambuye wathu Yesu Khristu amawagwiritsabe ntchito kuti azitithandiza ndipo ndi mphatso zimene watipatsa. w24.10 18 ¶1-2

Kuzindikira kudzakuteteza.—Miy. 2:11.

Davide anauza mwana wake kuti ngati angamvere Yehova, zinthu zidzamuyendera bwino. N’zomvetsa chisoni kuti patapita nthawi, Solomo anayamba kulambira milungu ina. Yehova anasiya kumukonda ndipo anasiya kumupatsa nzeru zoti azilamulira anthu mwachilungamo. (1 Maf. 11:​9, 10; 12:4) Kodi tikuphunzirapo chiyani? Zinthu zimatiyendera bwino tikakhala omvera. (Sal. 1:​1-3) N’zoona kuti Yehova sanatilonjeze kutipatsa chuma ndi ulemerero ngati Solomo. Koma tikamamumvera, iye adzatipatsa nzeru zomwe zingatithandize kuti tizisankha bwino zochita. (Miy. 2:​6, 7; Yak. 1:5) Mfundo zake zingatithandize pa nkhani zokhudza ntchito, maphunziro, zosangalatsa komanso ndalama. Tikamatsatira malangizo ake tidzakhala naye pa ubwenzi komanso tidzapeza moyo wosatha. (Miy. 2:​10, 11) Tingapezenso anzathu abwino. Komanso tingapeze malangizo amene angatithandize kukhala ndi banja losangalala. w24.11 10-11 ¶11-12

Muzifufuza zinthu zonse nʼkutsimikizira zimene zili zabwino ndipo gwirani mwamphamvu zabwinozo.1 Ates. 5:21.

Makolo ayenera kugwiritsa ntchito mwayi uliwonse kuti akambirane ndi mwana wawo zokhudza kukhulupirira Mulungu kapena Baibulo. Angachite zimenezi pamene apita kumalo osungirako zinthu zakale. Mungagwiritse ntchito zinthu zakalezo pothandiza mwana wanu kuona kuti Baibulo ndi lolondola. Kodi mwana wanu amadziwa kuti dzina la Mulungu limapezeka pamwala wina wa ku Moabu womwe wakhalapo zaka pafupifupi 3,000? Mwala umenewu uli kumalo osungirako zinthu zakale ku Likulu Lapadziko Lonse la Mboni za Yehova ku Warwick ku New York. Mwala umenewu umasonyeza kuti Mfumu Mesa ya ku Mowabu inagalukira Isiraeli. Zimene ndi zogwirizana ndi zimene Baibulo limanena. (2 Maf. 3:​4, 5) Ngati mwana wanu ataona umboni woti Baibulo ndi lolondola, chikhulupiriro chake chikhoza kulimba. w24.12 14 ¶4; 15 ¶6