Kalata Yoyamba Yopita kwa Akorinto 1:1-31

  • Mawu oyamba (1-3)

  • Paulo anayamikira Mulungu chifukwa cha Akorinto (4-9)

  • Anawalangiza kuti akhale ogwirizana (10-17)

  • Khristu ndi mphamvu komanso nzeru ya Mulungu (18-25)

  • Kudzitama mwa Yehova (26-31)

1  Ine Paulo, woitanidwa kukhala mtumwi+ wa Khristu Yesu mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu, pamodzi ndi Sositene mʼbale wathu,  ndikulembera mpingo wa Mulungu umene uli ku Korinto.+ Ndikulembera inu amene mwayeretsedwa mwa Khristu Yesu,+ amene mwaitanidwa kuti mukhale oyera, pamodzi ndi onse amene ali kulikonse omwe akuitana pa dzina la Ambuye wathu, Yesu Khristu,+ Ambuye wawo ndiponso wathu.  Kukoma mtima kwakukulu ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate wathu ndi Yesu Khristu Ambuye wathu zikhale nanu.  Nthawi zonse ndimathokoza Mulungu wanga chifukwa cha inu, poona kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu kumene anakusonyezani kudzera mwa Khristu Yesu.  Chifukwa chogwirizana naye, ndinu olemera mʼzinthu zonse, ndipo wakuthandizani kukhala ndi luso la kulankhula ndiponso kudziwa zinthu zonse,+  popeza umboni wonena za Khristu+ wakhazikika pakati panu.  Palibe mphatso imene mukuperewera pamene mukuyembekezera mwachidwi kuululidwa kwa Ambuye wathu Yesu Khristu.+  Komanso Mulungu adzakulimbitsani mpaka pamapeto, kuti musakhale ndi chifukwa chokunenezerani mʼtsiku la Ambuye wathu Yesu Khristu.+  Mulungu amene anakuitanani kuti mukhale ogwirizana ndi Mwana wake Yesu Khristu, Ambuye wathu, ndi wokhulupirika.+ 10  Tsopano ndikukudandaulirani abale, mʼdzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti nonse muzilankhula mogwirizana ndipo pakati panu pasakhale kugawanika,+ koma mukhale ogwirizana kwambiri pokhala ndi mtima umodzi ndi maganizo amodzi.+ 11  Chifukwa anthu ena a mʼbanja la Kuloe andiuza za inu, abale anga, kuti pakati panu pali kugawanika. 12  Ndikutanthauza kuti, ena mwa inu akumanena kuti: “Ine ndine wa Paulo,” ena akuti, “Ine ndine wa Apolo,”+ enanso akuti, “Ine ndine wa Kefa,”* pamene ena akuti, “Ine ndine wa Khristu.” 13  Kodi Khristu wakhala wogawanika? Kodi Paulo anapachikidwa pamtengo wozunzikirapo* kuti inu mupulumutsidwe? Kapena kodi munabatizidwa mʼdzina la Paulo? 14  Ndikuthokoza Mulungu kuti sindinabatize aliyense wa inu kupatulapo Kirisipo+ ndi Gayo,+ 15  moti wina sanganene kuti munabatizidwa mʼdzina langa. 16  Nʼzoona kuti ndinabatizanso anthu a mʼbanja la Sitefana.+ Koma za enawo, sindikudziwa ngati ndinabatizapo aliyense. 17  Khristu sananditume kuti ndizibatiza anthu, koma kuti ndizilengeza uthenga wabwino,+ osati mwa luso la kulankhula,* kuopera kuti mtengo wozunzikirapo* wa Khristu ungakhale wopanda ntchito. 18  Nkhani yokhudza mtengo wozunzikirapowo* ndi chinthu chopusa kwa anthu amene akupita kukawonongedwa,+ koma kwa ife amene tikupulumutsidwa, imeneyi ndi mphamvu ya Mulungu.+ 19  Chifukwa Malemba amati: “Ndidzathetsa nzeru za anthu anzeru ndipo ndidzakana* kuchenjera kwa anthu anzeru.”+ 20  Kodi wanzeru ali kuti? Mlembi* ali kuti? Katswiri wa mtsutso wa nthawi* ino ali kuti? Kodi Mulungu sanapange nzeru zadzikoli kukhala zopusa? 21  Mwa nzeru zake, Mulungu sanalole kuti dziko ligwiritse ntchito nzeru zake+ pomudziwa.+ Mʼmalomwake, Mulungu anaona kuti ndi bwino kupulumutsa okhulupirira kudzera mu uthenga umene anthu ena amauona kuti ndi wopusa.+ 22  Ayuda amafuna kuona zizindikiro+ ndipo Agiriki amafunafuna nzeru. 23  Koma ife timalalikira za Khristu amene anaphedwa popachikidwa pamtengo wozunzikirapo.* Ayuda amaona kuti zimenezi nʼzokhumudwitsa ndipo anthu a mitundu ina amaona kuti nʼzopusa.+ 24  Ngakhale zili choncho, Ayuda ndi Agiriki amene anaitanidwa amaona kuti Khristu ndi mphamvu ya Mulungu ndiponso nzeru za Mulungu.+ 25  Chifukwa chinthu cha Mulungu chimene anthu amachiona kuti nʼchopusa, nʼchanzeru kuposa anthu. Ndipo chinthu cha Mulungu chimene anthu amachiona kuti nʼchofooka, nʼchamphamvu kuposa anthu.+ 26  Mukuona mmene anakuitanirani abale, kuti si ambiri amene anthu amawaona kuti ndi anzeru+ omwe anaitanidwa, si ambiri amphamvu amene anaitanidwa, si ambiri a mʼmabanja olemekezeka.+ 27  Koma Mulungu anasankha zopusa za dziko kuti achititse manyazi anthu anzeru, ndipo Mulungu anasankha zinthu zofooka za dziko kuti achititse manyazi zinthu zamphamvu.+ 28  Mulungu anasankhanso zinthu zonyozeka za dziko ndi zinthu zimene anthu amaziona ngati zachabechabe, zinthu zimene palibe, kuti achititse zinthu zimene zilipo kukhala zopanda mphamvu.+ 29  Anachita zimenezi kuti pasapezeke munthu wodzitama pamaso pa Mulungu. 30  Koma inu ndinu ogwirizana ndi Khristu Yesu chifukwa cha Mulunguyo. Yesuyo amatisonyeza nzeru za Mulungu ndiponso chilungamo cha Mulungu.+ Kudzera mwa Yesu, anthu akhoza kuyeretsedwa,+ ndipo kudzera mwa dipo* akhoza kumasulidwa,+ 31  kuti zigwirizane ndi zimene Malemba amanena zoti: “Amene akudzitama, adzitame mwa Yehova.”*+

Mawu a M'munsi

Amatchedwanso Petulo.
Kapena kuti, “polankhula mochenjera.”
Kapena kuti, “ndidzakankhira pambali.”
Kutanthauza katswiri wa Chilamulo.