Chichewa
August
https://assetsnffrgf-a.akamaihd.net/assets/ct/d71826a198/images/syn_placeholder_sqr.png
es26 tsamba 77-87

August

Loweruka, August 1

August

Kudzakhala chisautso chachikulu chimene sichinachitikepo kuchokera pachiyambi cha dziko mpaka lero.—Mat. 24:21.

Timapemphera kuti anthu ambiri amve uthenga wathu wochenjezawu n’kusankha kumatumikira Yehova panopa. Koma bwanji za anthu amene sakufuna kumvera chenjezoli? N’kutheka kuti Yehova angadzapulumutse anthu omwe adzasinthe maganizo awo pambuyo poona kuwonongedwa kwa Babulo Wamkulu. Ngati ndi choncho, ndiye kuti n’zofunika kwambiri kuti panopa tipitirize kuwachenjeza. Zimene tingawauze, angadzazikumbukire pa nthawiyo. (Yerekezerani ndi Ezekieli 33:33.) Mwina angadzakumbukire zimene tinawauza n’kusankha kuyamba kutumikira Mulungu nthawi isanathe. Mofanana ndi woyang’anira ndende wa ku Filipi, yemwe anasintha maganizo pambuyo pa “chivomerezi champhamvu,” n’kutheka kuti ena omwe panopa samvetsera uthenga wathu, angadzasinthe maganizo awo pambuyo poona zomwe zidzachitike Babulo Wamkulu akamadzawonongedwa.—Mac. 16:​25-34. w24.05 17 ¶9-10

Khristu ndiye kutha kwa Chilamulo.Aroma 10:4.

Tikuphunzira mfundo yofunika pa mawu amene Paulo analembera Akhristu a Chiheberi. Ena mwa Akhristuwa sanapitirize kukula mwauzimu. Iwo ‘anayambanso kufuna mkaka osati chakudya [chauzimu] chotafuna.’ (Aheb. 5:12) Iwo sanaphunzire komanso kuvomereza mfundo zatsopano zimene Yehova ankawaphunzitsa kudzera mumpingo. (Miy. 4:18) Mwachitsanzo, Akhristu ambiri a Chiyuda ankalimbikitsabe Chilamulo cha Mose ngakhale kuti chilamulocho chinali chitathetsedwa zaka 30 m’mbuyomo chifukwa cha nsembe ya Khristu. (Tito 1:10) Aliyense amene angawerenge kalata imene Paulo analembera Akhristu a Chiheberi akhoza kuvomereza kuti m’bukuli muli chakudya chauzimu chotafuna. Mfundozi ndi zimene iwo ankafunikira kuti azikhulupirira kuti njira yolambirira ya Akhristu ndi yapamwamba. Zikanawathandizanso kuti azilalikira molimba mtima.—Aheb. 10:​19-23. w24.04 6 ¶15

Mulungu adzaukitsa olungama ndi osalungama omwe.Mac. 24:15.

Kungochokera pamene Adamu ndi Hava anakhala kumbali ya Satana poukira Yehova Mulungu, anthu mabiliyoni ambiri akhala akufa. Ndiye kodi n’chiyani chidzachitikire anthu onsewa? Anthu ochepa, okwana 144,000 omwe ndi otsatira okhulupirika a Khristu, adzaukitsidwa n’kupatsidwa moyo wosafa kumwamba. (Chiv. 14:1) Amuna ndi akazi okhulupirika amene ankakonda Yehova, adzakhala m’gulu la anthu ‘olungama amene adzaukitsidwe’ ndipo adzapatsidwa moyo wosatha padziko lapansi ngati angakhale okhulupirika mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu komanso akadzayesedwa komaliza. (Dan. 12:13; Aheb. 12:1) Komanso mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 , anthu “osalungama” kuphatikizapo amene sanatumikirepo Yehova, kapena amene “ankachita zoipa,” adzapatsidwa mwayi woti asinthe njira zawo n’kukhala okhulupirika. (Yoh. 5:29; Luka 23:​42, 43) Koma pali anthu ena oipa kwambiri omwe Yehova anasankha kuti asadzaukitsidwe n’komwe.—Luka 12:​4, 5w24.05 2 ¶3; 5 ¶15; 6 ¶17

Amandilemekeza ndi milomo yawo yokha, koma mitima yawo aiika kutali ndi ine.Yes. 29:13.

Kuti munthu avomerezedwe ndi Yehova ayenera “kulankhula zoona mumtima mwake.” (Sal. 15:2) Apa sikuti akungotanthauza kupewa kunama. Yehova amafuna kuti nthawi zonse tizikhala oona mtima. (Aheb. 13:18) Zimenezi ndi zofunika “chifukwa Yehova amanyansidwa ndi munthu wachiphamaso, koma anthu owongoka mtima amakhala nawo pa ubwenzi wolimba.” (Miy. 3:32) Anthu amene ‘amalankhula zoona mumtima mwawo,’ samayerekezera kukhala omvera akakhala pagulu n’kumaphwanya malamulo a Mulungu akakhala kwaokha. Amapewa kuchita zinthu mwachiphamaso. Munthu wachiphamaso amayamba kukayikira ngati malamulo a Yehova alidi anzeru. (Yak. 1:​5-8) Munthu wotereyo samvera Yehova pa zinthu zimene iyeyo amaziona kuti ndi zing’onozing’ono. Akaona kuti sanakumane ndi mavuto chifukwa cha kusamverako, amalimba mtima n’kumapitirizabe kuphwanya malamulo a Mulungu ndipo kulambira kwake kumakhala kwachinyengo. (Mlal. 8:11) Koma ife timafuna kukhala oona mtima pa zinthu zonse. w24.06 10 ¶7-8

Khalani olimba, mutamanga kwambiri choonadi mʼchiuno mwanu ngati lamba.—Aef. 6:14.

Anthu a Yehova amakonda choonadi chopezeka m’Mawu a Mulungu. Zimene timawerenga m’mawu akewo zimalimbitsa chikhulupiriro chathu. (Aroma 10:17) Timakhulupirira kuti Yehova wakhazikitsa mpingo wa Chikhristu kuti ‘uzilimbikitsa ndi kuteteza choonadi.’ (1 Tim. 3:15) Satana amafunitsitsa kuti tisiye kukhulupirira Baibulo komanso malangizo amene timalandira kuchokera kugulu la Mulungu. (Aef. 4:14) Posachedwapa, Mdyerekezi adzagwiritsa ntchito mabodza pofuna kusokoneza anthu a mitundu yonse kuti atsutsane ndi Yehova. (Chiv. 16:​13, 14) Tikudziwanso kuti Satana ayesetsa kwambiri kuti asokoneze anthu a Yehova. (Chiv. 12:9) Choncho tingachite bwino kudziphunzitsa kuti tizisiyanitsa choonadi ndi mfundo zabodza, n’kumamvera choonadicho. (Aroma 6:17; 1 Pet. 1:22) Kuchita zimenezi n’kumene kungathandize kuti tidzapulumuke pa chisautso chachikulu. w24.07 8 ¶1-3

Lamulo limene ndikukupatsani leroli si lovuta kwa inu kulitsatira, ndipo silili poti simungathe kulipeza.Deut. 30:11.

Yehova atasankha Aisiraeli kuti akhale mtundu wake, anachita nawo pangano ndipo iwo analonjeza kuti azimumvera. Akamamvera malamulo ake, iye ankawateteza komanso kuwadalitsa. Koma akapanda kumumvera, mwina posankha kulambira milungu ina, iye ankasiya kuwadalitsa ndipo ankakumana ndi mavuto. Ngakhale zinali choncho, zinali zotheka kuti Mulungu ayambirenso kuwakonda. Iwo akanatha ‘kubwerera kwa Yehova Mulungu wawo komanso kumvera mawu ake.’ (Deut. 30:​1-3, 17-20) M’mawu ena tingati iwo akanatha kulapa. Ndipo Yehova akanatha kukhalanso nawo pa ubwenzi n’kuyambiranso kuwadalitsa. Anthu a Yehova ankamuchimwira mobwerezabwereza. Izi zinachititsa kuti azikumana ndi mavuto. Koma Yehova sanatope nawo anthu ake osamverawa. Mobwerezabwereza, ankawatumizira aneneri n’cholinga choti alape ndi kubwerera kwa iye.—2 Maf. 17:​13, 14. w24.08 9 ¶4-5

Mpingo umene unali ku Yerusalemu unayamba kuzunzidwa koopsa.—Mac. 8:1.

Akhristu a Chiheberi omwe ankakhala ku Yerusalemu ndi ku Yudeya anakumana ndi mavuto aakulu pambuyo poti Yesu waphedwa. Mpingo wa Chikhristu utakhazikitsidwa, Akhristuwo anayamba kuzunzidwa kwambiri. Kenako patapita zaka 20, otsatira a Khristu ankakumana ndi mavuto a zachuma, mwina chifukwa cha njala yomwe inagwa m’dzikolo. (Mac. 11:​27-30) Koma cha m’ma 61 C.E., Akhristu sankazunzidwa kwambiri poyerekezera ndi zimene akanakumana nazo m’tsogolo. Pa nthawi imeneyi iwo analandira kalata youziridwa ya Paulo, yomwe inali ya pa nthawi yake. Kalata yopita kwa Aheberiwa inali ya pa nthawi yake chifukwa mtendere womwe Akhristuwo anali nawo unali wosakhalitsa. Paulo anapereka malangizo kwa Akhristuwo omwe akanawathandiza kupirira mayesero amene amayembekezeka kukumana nawo. w24.09 8 ¶1-2

[Iwo] amandilimbikitsa kwambiri.—Akol. 4:11.

Tikamakumana ndi mavuto, zimene abale ndi alongo amachita zimasonyeza kuti Yehova amatikonda. Iwo angatilimbikitse potimvetsera mwachifundo, kapenanso kukhala nafe pa nthawi imene tikukumana ndi mavutoyo. Angatiwerengere vesi linalake lolimbikitsa kapenanso kupemphera nafe. (Aroma 15:4) Nthawi zina m’bale kapena mlongo angatikumbutse maganizo a Yehova, zomwe zingathandize kuti mtima wathu ukhale m’malo. Akhristu anzathu angatithandizenso m’njira zina monga kutipatsa chakudya pa nthawi imene tili ndi nkhawa. Kuti ena atithandize tiyenera kuwafotokozera mavuto athu. (Miy. 17:17) Paokha sangadziwe mmene tikumvera komanso zimene tikufunikira. (Miy. 14:10) Choncho muzikhala wokonzeka kufotokozera anzanu amene ndi odalirika. Muziwauza zimene zingakuthandizeni. Mungathe kuuza mkulu mmodzi kapena awiri omwe mumamasuka nawo. Alongo ena amaona kuti zimawathandiza akafotokozera mlongo wina wolimba mwauzimu. w24.10 10 ¶15-16

Aliyense wovomereza Mwana komanso kumukhulupirira akhale ndi moyo wosatha.—Yoh. 6:40.

Anthu ambiri amakhala osamala ndi zimene amadya komanso amachita masewera olimbitsa thupi pafupipafupi kuti akhale athanzi. Komabe iwo amadziwa kuti kuchita zimenezi sikungawathandize kuti asakalambe kapena kufa. Choncho iwo amaganiza kuti n’zosatheka kukhala ndi moyo mpaka kalekale. Ngakhale zili choncho, Yesu anafotokoza kuti n’zotheka kudzapeza “moyo wosatha.” Chitsanzo ndi zimene ananena pa Yohane 3:16 ndi 5:24. Tsiku lina Yesu anachita zodabwitsa pomwe anadyetsa gulu la anthu mkate ndi nsomba. Zimenezi zinalidi zodabwitsa, koma zodabwitsa kwambiri ndi zimene ananena tsiku lotsatira. Gulu la anthu linamutsatira ku Kaperenao pafupi ndi nyanja ya Galileya komwe iye anawauza kuti akufa adzaukitsidwa komanso adzakhala ndi moyo wosatha. (Yoh. 6:​39, 40) Mawu a Yesuwa akusonyeza kuti anthu ambiri omwe anamwalira adzaukitsidwa ndipo inuyo limodzi ndi anthu amene mumawakonda mudzakhala ndi moyo mpaka kalekale. w24.12 8 ¶1-2

Inunso amuna, . . . muziwapatsa ulemu chifukwa akazi ali ngati chiwiya chosachedwa kusweka.—1 Pet. 3:7.

Lipoti laposachedwapa la Bungwe Loona za Umoyo Padziko Lonse linasonyeza kuti amuna ambiri amamenya akazi awo, kuwalankhula mawu achipongwe kapena kuwazunza m’njira zina. Amalemekeza akazi awo akakhala pagulu koma n’kumakawazunza akapita kunyumba. N’chifukwa chiyani amuna ena amazunza akazi awo? Mwina analeredwa ndi bambo wankhanza choncho amaganiza kuti palibe vuto kuchitira ena nkhanza. Ena amayendera chikhalidwe cholakwika choti “mwamuna weniweni” ayenera kusonyeza mphamvu kuti azilemekezedwa ndipo amuna ena sanaphunzitsidwe kudziletsa. Pomwe amuna ena amakhala ndi maganizo olakwika okhudza akazi komanso kugonana chifukwa choonera zolaula. Kuwonjezera pamenepa, malipoti akusonyeza kuti mliri wa COVID-19 wawonjezera mavuto amenewa. Komabe zimenezi si zifukwa zomveka zochititsa kuti amuna azichitira nkhanza akazi awo. w25.01 8 ¶2-3

Popeza Khristu anavutika pa nthawi imene anali munthu, nanunso konzekerani pokhala ndi maganizo ofanana ndi amene Khristu anali nawo.—1 Pet. 4:1.

“Muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, moyo wanu wonse, mphamvu zanu zonse ndi maganizo anu onse.” (Luka 10:27) Apa Yesu anasonyeza kuti limeneli linali lamulo lofunika kwambiri m’Chilamulo cha Mose. Onani kuti kukonda Yehova kumaphatikizapo mtima wathu, womwe ukuimira zimene timakonda, mmene timamvera komanso mmene timaganizira. Kumaphatikizaponso kudzipereka kwa Yehova ndi mtima wathu wonse komanso mphamvu zathu zonse. Komabe kukonda Yehova kumaphatikizaponso maganizo athu, omwe akuimira mmene timaonera nkhani zosiyanasiyana. N’zoona kuti sitingamvetse mokwanira mmene Yehova amaganizira. Komabe tingathe kumvetsa mmene Mulungu amaganizira pophunzira “maganizo a Khristu,” chifukwa Yesu amatsanzira ndendende mmene Atate wake amaganizira.—1 Akor. 2:16. w25.03 8 ¶1

Kudzera mwa mwana wakeyu, tinamasulidwa ndi dipo la magazi ake, inde, takhululukidwa machimo athu, mogwirizana ndi kukoma mtima kwake kwakukulu.—Aef. 1:7.

Popeza Yesu anali wangwiro, ankafanana ndi mmene Adamu analili asanachimwe. (1 Akor. 15:45) Imfa ya Yesu inaphimba tchimo la Adamu, ndipo inabwezeretsa zimene Adamu anataya. (Aroma 5:19) Choncho Yesu anakhala “Adamu womalizira.” Sipakufunikanso munthu wina wangwiro kuti abwere kudzalipira zimene Adamu anataya. Yesu anafa “kamodzi kokha kuti akhale nsembe yothandiza anthu mpaka kalekale.” (Aheb. 7:27; 10:12) Kodi kuphimba machimo n’kosiyana bwanji ndi dipo? Kuphimba machimo ndi zimene Mulungu wachita kuti anthu akhale nayenso pa ubwenzi wabwino. Pomwe dipo ndi malipiro amene amaperekedwa kuti machimo a anthu aphimbidwe. Malipiro amenewa akuimiridwa ndi magazi amtengo wapatali a Yesu omwe anakhetsedwa chifukwa cha ife.—Aheb. 9:14. w25.02 5 ¶12-13

Mulungu ndi wokhulupirika ndipo sadzalola kuti muyesedwe kufika pamene simungapirire, koma pamene mukukumana ndi mayeserowo iye adzapereka njira yopulumukira kuti muthe kuwapirira.—1 Akor. 10:13.

Kukhulupirira kuti Yehova alikodi kungatithandize kuti tiziona moyenera mayesero amene timakumana nawo. N’chifukwa chiyani tikutero? Tikutero chifukwa timayamba kuona mavuto amene tikukumana nawo monga mbali ya nkhani yaikulu yomwe ilipo pakati pa Yehova ndi Satana. Mdyerekezi amanena kuti tikakumana ndi mavuto tingasiye kutumikira Yehova. (Yobu 1:​10, 11; Miy. 27:11) Koma tikakwanitsa kupirira mavutowo, timasonyeza kuti timakonda Yehova ndipo timatsutsa bodza la Mdyerekezi. Kodi inuyo mukutsutsidwa ndi akuluakulu a boma, mukukumana ndi mavuto a zachuma, anthu sakumvetsera uthenga wabwino kapena mukukumana ndi mayesero ena? Muzikumbukira kuti zimene mukukumana nazo zingakupatseni mwayi woti musangalatse mtima wa Yehova. Muzikumbukiranso kuti Mulungu sadzalola kuti muyesedwe mpaka kufika poti simungathe kupirira. Iye adzakupatsani mphamvu kuti mupirire. w24.06 22 ¶9

Munthu aliyense amayesedwa ndi chilakolako chake chimene chimamukopa ndi kumukola.—Yak. 1:14.

Kodi mumadziwa zinthu zimene zingakuyeseni inuyo mosavuta? Simuyenera kumadzinamiza n’kumanyalanyaza zofooka zanu kapena kumaganiza kuti ndinu wolimba kwambiri moti simungachite zoipa. (1 Yoh. 1:8) Ndipotu Paulo ananena kuti ngakhale anthu “amene ndi oyenerera mwauzimu” akhoza kuyesedwa ngati sangakhale maso. (Agal. 6:1) Choncho tiyenera kukhala oona mtima n’kumazindikira zofooka zathu. (2 Akor. 13:5) Kodi tiyenera kuchita chiyani tikazindikira zinthu zimene zingachititse kuti tiyesedwe mosavuta? Tizichita khama kuti tizipewa zinthu zimenezo. Mwachitsanzo, mizinda yakale yomwe inkakhala ndi mipanda inkatetezedwa kwambiri pageti chifukwa ndi pamene adani akanadzera mosavuta kuti aukire. Mofanana ndi zimenezi, tiyenera kudziwa bwino zofooka zathu n’cholinga choti tizitha kupewa mayesero.—1 Akor. 9:27. w24.07 15 ¶5-7

[Pitirizani] kubala zipatso pantchito iliyonse yabwino ndi kuwonjezera kumudziwa Mulungu molondola.Akol. 1:10.

Ntchito yabwino imene ikutchulidwa mulemba lalero ikuphatikizapo kulalikira uthenga wabwino. Choncho tikamawerenga Mawu a Mulungu komanso kuwaganizira mozama timayamba kukhulupirira kwambiri Yehova ndiponso timayamba kuona kuti kuuza ena uthenga wabwino n’kofunika kwambiri. Kuti tizipindula kwambiri ndi Mawu a Mulungu, tiyenera kupewa kuthamanga powerenga, kuphunzira komanso kuganizira zimene tikuwerengazo. Tizidzipatsa nthawi yokwanira. Tikapeza lemba limene sitikulimvetsa, tisamangolidutsa. M’malomwake, tizigwiritsa ntchito Watch Tower Publications Index kapena Buku la Mboni za Yehova Lofufuzira Nkhani kuti tidziwe mmene afotokozera lembalo. Tikamakhala ndi nthawi yokwanira pophunzira, tidzayamba kukhulupirira kwambiri kuti Mawu a Mulungu ndi olondola. (1 Ates. 5:21) Ndipo tikamawakhulupirira kwambiri m’pamenenso timasangalala kuuza ena zomwe taphunzira. w24.04 15 ¶4-5

Ndinakulemberani nʼcholinga choti ndidziwe ngati mulidi omvera pa zinthu zonse.—2 Akor. 2:9.

Davide anati Yehova ndi “wabwino” ndipo ndi “wokonzeka kukhululuka.” (Sal. 86:5) Mika analemba kuti: “Kodi pali Mulungu winanso wofanana ndi inu, amene amakhululukira zolakwa ndi machimo?” (Mika 7:18) Ndipo Yesaya ananena kuti: “Munthu woipa asiye njira yake ndipo wopweteka anzake asiye maganizo ake. Iye abwerere kwa Yehova ndipo adzamuchitira chifundo. Abwerere kwa Mulungu wathu, chifukwa adzamukhululukira ndi mtima wonse.” (Yes. 55:7) Kuti anthu a mumpingo wa ku Korinto atsanzire Yehova, anauzidwa kuti alandire munthu wochimwa amene analapa komanso kumutsimikizira kuti amamukonda. Potsatira malangizo amenewo, mpingo unasonyeza kuti unalidi ‘womvera pa zinthu zonse.’ Ngakhale kuti panali patangopita miyezi yochepa kuchokera pamene anachotsedwa, munthuyo analapa. Choncho panalibe chifukwa chochedwera kumubwezeretsa mumpingo. w24.08 17-18 ¶12-13

Mmodzi adzatengedwa ndipo winayo adzasiyidwa.—Mat. 24:40.

Tikukhala munthawi imene tikuyembekezera kuti zinthu zisintha kwambiri. Posachedwapa Yesu aweruza anthu onse okhala padzikoli. Iye anafotokoza zimene zichitike tsiku lachiweruzo lisanafike. Anapatsa ophunzira ake ‘chizindikiro cha kukhalapo kwake ndi cha mapeto a nthawi ino.’ (Mat. 24:3) Ulosiwu umapezeka m’machaputala 24 ndi 25 a buku la Mateyu komanso mu Maliko 13 ndi Luka 21. Yesu anapereka mafanizo atatu othandiza komanso otichenjeza: Fanizo la nkhosa ndi mbuzi, la anamwali ochenjera ndi opusa komanso la matalente. Fanizo lililonse limatithandiza kumvetsa mmene zochita za munthu aliyense zidzakhudzire chiweruzo chomwe adzalandire. w24.09 20 ¶1-2

Zonse zimene mukuchita, muzizichita mwachikondi.—1 Akor. 16:14.

Yesu Khristu ndi chitsanzo chabwino kwambiri. Iye ankachita zinthu chifukwa chokonda Atate wake komanso anthu. Chikondi chimenechi chinkamulimbikitsa kugwira ntchito mwakhama ngakhale ntchito zooneka ngati zonyozeka. (Mat. 20:28; Yoh. 13:​5, 14, 15) Abale, ngati inunso mumachita zinthu chifukwa cha chikondi, Yehova adzakudalitsani kuti mukwaniritse zolinga zanu zauzimu monga kukhala mtumiki wothandiza. (1 Pet. 5:5) M’dzikoli, anthu amasirira anthu amene amafuna kukhala apamwamba. Koma si mmene zilili m’gulu la Yehova. M’bale amene amachita zinthu chifukwa cha chikondi ngati Yesu, salakalaka malo apamwamba, mphamvu kapena udindo. Munthu amene amafuna kukhala wapamwamba akapatsidwa udindo mumpingo, sangamalole kugwira ntchito zooneka ngati zonyozeka pothandiza anthu a Yehova. Atha kumaona kuti ntchito zimenezo si zoyenera kwa iyeyo.—Yoh. 10:12. w24.11 15 ¶6-7

Mzimu woyera wakuikani kuti muziyangʼanira.—Mac. 20:28.

Padziko lonse, pakufunikira abale oti atumikire m’maudindo osiyanasiyana. (Aef. 4:8) Ngati ndinu m’bale wobatizidwa, kodi ‘mungathe kuthandiza’ abale ndi alongo? (Miy. 3:27) Kodi mukufuna mutakhala mtumiki wothandiza? Kodi mungayesetse kuti muzitumikira abale anu monga mkulu? Kodi mungasinthe zinthu zina n’cholinga choti mukalowe nawo Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu? Sukulu imeneyi ikhoza kukuthandizani kuti Yesu akugwiritseni ntchito kwambiri. Ngati mukuganiza kuti ndinu wosayenerera, muyenera kuipempherera nkhaniyi kwa Yehova. Muzimupempha kuti akupatseni mzimu woyera kuti muzitha kugwira ntchito iliyonse imene mwapatsidwa. (Luka 11:13) Zimene Yesu wachita posankha “amuna” ena kuti azitumikira mumpingo ndi umboni wakuti akutitsogolera masiku otsiriza ano. (Mat. 28:20) Timayamikira kuti tili ndi Mfumu yachikondi, yopatsa komanso imene imatiganizira. Mfumuyi yatipatsa anthu oyenerera kuti azitithandiza. w24.10 23 ¶16-17

Zinthu zakale sizidzakumbukiridwanso.—Yes. 65:17.

Koma bwanji za zinthu zonse zomwe zimachititsa anthu a Mulungu kuti azimva kupweteka komanso azivutika? Posachedwapa zimenezi ‘zidzaiwalika ndipo zidzabisidwa kuti [Mulungu] asazionenso.’ (Yes. 65:16) Yehova adzachotsa mavuto onse ndipo pakapita nthawi sitidzakumbukiranso ululu wonse womwe tinkamva chifukwa cha mavutowo. Ngakhale panopa mitima yathu imakhala m’malo tikapezeka kumisonkhano komwe timakaiwala mavuto omwe tikukumana nawo m’dziko loipali. Timathandiza kuti onse mumpingo azikhala osatekeseka tikamasonyeza makhalidwe monga chikondi, chimwemwe, mtendere, kukoma mtima komanso kufatsa, amene ndi makhalidwe omwe timakhala nawo mothandizidwa ndi mzimu wa Mulungu. (Agal. 5:​22, 23) Ndi mwayitu waukulu kukhala m’gulu la Mulungu. Anthu onse amene akupitiriza kukhala m’paradaiso wauzimu adzaona kukwaniritsidwa kwa lonjezo la Mulungu lokhudza “kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano.” w24.04 22 ¶9-10

Umakhala msampha munthu akathamangira kufuula kuti, “Nʼzoyera!” Koma pambuyo polonjeza nʼkuyamba kuganiziranso bwino zimene walonjezazo.—Miy. 20:25.

Nthawi yomwe anthu ali pa chibwenzi ikhoza kukhala yosangalatsa. Koma kuwonjezera pamenepa, ndi nthawi yofunika kwambiri yomwe ingathandize anthu kuona ngati angadzakwatirane. Pa tsiku la ukwati wawo, anthu okwatiranawo amalumbira pamaso pa Yehova kuti azikondana komanso kulemekezana kwa moyo wawo wonse. Tisanalumbire pa nkhani iliyonse, tiyenera kuiganizira kaye mofatsa. Ndi mmenenso zilili pa nkhani ya lumbiro la ukwati. Kukhala pa chibwenzi kumathandiza awiriwo kuti adziwane bwino komanso kuti asankhe zinthu mwanzeru. Akhoza kusankha kukwatirana kapena kuthetsa chibwenzicho. Ngati asankha kuthetsa chibwenzi sizitanthauza kuti chibwenzicho sichinawathandize. M’malomwake, chinakwaniritsa cholinga chake chifukwa chinawathandiza kuti adziwe zoyenera kusankha. Koma nkhani yokhala pa chibwenzi tiyenera kumaiona moyenera. N’chifukwa chiyani tikutero? Ngati munthu yemwe sali pa banja ali ndi maganizo oyenera, sangachite chibwenzi ndi munthu yemwe akudziwiratu kuti sadzakwatirana naye. w24.05 26-27 ¶3-4

Usachite manyazi ndi ntchito yolalikira za Ambuye wathu.—2 Tim. 1:8.

Nthawi zina Akhristu achinyamata amaopa kufotokozera ena zimene amakhulupirira. Mwina iwo angachite mantha anthu m’kalasi akayamba kufotokoza kuti zinthu zinachita kusintha. Mwina angamachite mantha chifukwa chakuti aphunzitsi awo amafotokoza ngati kuti zinthu zinachitadi kusintha. Ndiye ngati ndinu kholo kodi mungatani kuti muthandize mwana wanu kuti asamaope kufotokoza zomwe amakhulupirira? Muzitsimikizira kuti sayenera kuchita manyazi chifukwa chakuti amakhulupirira kuti zinthu zinachita kulengedwa. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa palinso asayansi ambiri amene amakhulupirira kuti zamoyo sizinachite kusintha. Iwo amaona umboni woti pali winawake wanzeru amene analenga zinthu zodabwitsa zam’chilengedwe. Choncho iwo sagwirizana ndi zimene zimaphunzitsidwa kusukulu zakuti zamoyo zinachita kusintha. Mwana wanu akhoza kulimbitsa chikhulupiriro chake akamaganizira zifukwa zimene zinachititsa abale ndi alongo ena kukhulupirira kuti zamoyo zinachita kulengedwa. w24.12 18 ¶14-15

Yesu anasangalala kwambiri mwa mzimu woyera.—Luka 10:21.

Yesu sankakayikira kuti anthu ena adzamvetsera uthenga wabwino. Zimenezi zinamuthandiza kuti azisangalala ndi utumiki wake. Mwachitsanzo, chakumapeto kwa chaka cha 30 C.E., Yesu anaona kuti anthu ambiri anali okonzeka kumvetsera uthenga wabwino ndipo anawayerekezera ndi munda umene mbewu zake zakhwima. (Yoh. 4:35) Patangopita chaka chimodzi iye anauza ophunzira ake kuti: “Pali zinthu zambiri zofunika kukolola.” (Mat. 9:​37, 38) Pasanapite nthawi yaitali anabwerezanso kuti: “Pali zinthu zambiri zofunika kukolola . . . pemphani Mwiniwake wa munda kuti atumize antchito kukakolola.” (Luka 10:2) Yesu sanasiye kukhulupirira kuti anthu amvetsera uthenga wabwino ndipo ankasangalala iwo akachita zimenezo. Iye anaphunzitsa ophunzira ake kuti azionabe uthenga umene ankalalikira kukhala wofunika. Zimenezi zikanawalimbikitsa kuti apitirize kuchita khama. w25.03 18-19 ¶15-16

Mulungu wanga ndi thanthwe langa lothawirako.—Sal. 94:22.

Yehova ndi malo othawirako. Mofanana ndi thanthwe lalikulu lomwe munthu angabisaleko mphepo yamkuntho, Yehova amatiteteza pa nthawi yomwe tikukumana ndi mavuto. Amatiteteza kuti mavutowo asawononge ubwenzi wathu ndi iye. Amatilonjezanso kuti adzathetsa chilichonse chimene chimatidetsa nkhawa komanso mavuto onse. (Ezek. 34:​25, 26) Njira imodzi imene tingapitire kwa Yehova ngati thanthwe lathu, ndi kupemphera kwa iye. Tikapemphera, Yehova amatipatsa “mtendere” wake womwe umateteza maganizo ndi mtima wathu. (Afil. 4:​6, 7) Yehova nthawi zonse amakhala wokonzeka kuti atithandize. Tiyenera kumudalira chifukwa iye ndi “Thanthwe lamuyaya.” (Yes. 26:​3, 4) Iye adzakhalapo nthawi zonse kuti akwaniritse malonjezo ake, ayankhe mapemphero athu ndiponso azitithandiza. Tingadalirenso Yehova chifukwa chakuti amakhala wokhulupirika kwa anthu amene amamutumikira. (2 Sam. 22:26) Iye sadzaiwala zimene timachita ndipo adzatipatsa mphoto.—Aheb. 6:10; 11:6. w24.06 27 ¶4-6

Uteteze mtima wako . . . chifukwa mumtimamo ndi mmene muli akasupe a moyo.—Miy. 4:23.

Zosangalatsa zosayenera zingachititse kuti tisamatumikire Mulungu ndi mtima wonse. Tikazindikira kuti pali zinazake zomwe zikuchititsa kuti chikondi chathu kwa Yehova chiyambe kuchepa, tizichitapo kanthu mwamsanga. (Mat. 5: 29, 30) Tisamalole kuti mtima wathu ukhale wogawanika. Tikhoza kumadzinamiza n’kumaona kuti ngati tikuchita zambiri potumikira Yehova, palibe chimene chingachititse kuti tichite zoipa. Tiyerekeze kuti kunja kuli chimphepo komanso fumbi. Ndiye inu mwakonza bwinobwino m’nyumba mwanu. Kodi mungasiye mawindo ndi zitseko zili zotsegula kuti fumbi lizilowa m’nyumbamo? Ayi. Mfundo yake ndi yakuti timafunika kuchita zambiri osati kungodya chakudya chauzimu chomwe chimatithandiza kuti tikhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Tiyeneranso kutseka chitseko, kunena kwake titero, kuti fumbi la m’dzikoli kapena zinthu zimene Mulungu amadana nazo zisalowe mumtima mwathu n’kuugawanitsa.—Aef. 2:2. w24.07 21 ¶6-7

Pitirizani kukonda adani anu ndi kupempherera amene akukuzunzani.—Mat. 5:44.

Yesu anachitiridwa zinthu zochititsa manyazi komanso zankhanza kwambiri ndipo sitingamvetse ululu umene anamva. Koma iye sanagonje chifukwa cha zinthu zopanda chilungamo zimene anamuchitira. M’malo motemberera asilikali omwe anamukhomerera pamtengo, iye anapemphera kuti: “Atate, akhululukireni, chifukwa sakudziwa zimene akuchita.” (Luka 23:34) Tikapempherera anthu amene atilakwira, zimatithandiza kuti tisiye kusunga chakukhosi kapena kukwiya. Komanso zimatithandiza kuti tiziwaona moyenera. M’dziko loipali, tizikumanabe ndi zinthu zopanda chilungamo. Ndiye kaya tikumana ndi zotani, tiyeni tisasiye kupemphera kwa Yehova kuti atithandize. Tizitsanziranso mmene Yesu anachitira zinthu atachitiridwa zopanda chilungamo ndipo tipitirize kutsatira mfundo za m’Baibulo. Tikamachita zimenezi, Yehova adzatidalitsa.—1 Pet. 3:​8, 9w24.11 6 ¶16; 7 ¶17, 19

Inu si Mulungu amene amasangalala ndi zoipa, palibe munthu woipa amene angakhale ndi inu.—Sal. 5:4.

Yehova si Mulungu wolekerera machimo. (Sal. 5:​4-6) Iye amafuna kuti tizimvera mfundo zake zolungama zomwe zimapezeka m’Baibulo. N’zoona kuti Yehova sayembekezera kuti anthu omwe si angwiro azichita zinthu mosalakwitsa kalikonse. (Sal. 130:​3, 4) Pa nthawi imodzimodziyo, iye salekerera ‘anthu osaopa Mulungu omwe amatenga kukoma mtima kwake kwakukulu kukhala chifukwa chochitira khalidwe lopanda manyazi.’ (Yuda 4) Ndipotu Baibulo limanena za ‘kuwonongedwa kwa anthu osaopa Mulungu’ pa nkhondo yake ya Aramagedo. (2 Pet. 3:7; Chiv. 16:16) Koma Yehova safuna kuti aliyense adzawonongedwe. Baibulo limafotokoza momveka bwino kuti Mulungu “akufuna kuti anthu onse alape.” (2 Pet. 3:9) Akulu amatsanzira Yehova akamathandiza moleza mtima anthu omwe achita tchimo kuti asinthe njira zawo n’kukhalanso naye pa ubwenzi. w24.08 26 ¶1-2

Mumatambasula dzanja lanu nʼkukwaniritsa zolakalaka za chamoyo chilichonse.—Sal. 145:16.

Mofanana ndi Yehova, ifenso tingapatse ena zinthu chifukwa chowakonda. Mwachitsanzo, kodi mukudziwa Mkhristu wina yemwe akufunika chakudya kapena zovala? Yehova angagwiritse ntchito inuyo kuti mumuthandize kupeza zimene akufunikira. Anthu a Yehova amadziwika kuti amathandizana pakagwa mavuto. Mwachitsanzo, pa nthawi ya mliri wa COVID-19, abale ndi alongo ankapereka chakudya, zovala komanso zinthu zina kwa anthu amene akuvutika. Ndipo ambiri ankapereka ndalama zothandiza pa ntchito ya padziko lonse. Izi zinathandiza kuti gulu lizipereka chithandizo padziko lonse. Abale ndi alongo anachita mogwirizana ndi lemba la Aheberi 13:​16, lomwe limati: “Musaiwale kuchita zabwino ndi kugawira ena zomwe muli nazo, chifukwa Mulungu amasangalala ndi nsembe zoterozo.” w24.09 27 ¶6-7

Muzitha kusankha zinthu zimene ndi zofunikadi kwambiri.—Afil. 1:10.

Taganizirani chitsanzo ichi. Mukufufuza ntchito yomwe ingakuthandizeni kuti muzisamalira banja lanu. Ndiye papezeka ntchito ziwiri. Mukuganizira mfundo zonse monga mtundu wa ntchitoyo, nthawi yomwe muziigwira komanso mtunda umene mungamayende ndi zina. Ntchito zonsezo ndi zoti Mkhristu angagwire. Komabe inuyo mukukonda ntchito imodzi chifukwa cha mtundu wake komanso malipiro ake. Ngakhale zili choncho, pali mfundo zinanso zimene muyenera kuziganizira musanasankhe zochita. Mwachitsanzo, kodi ntchitoyo iziwombana ndi nthawi yanu ya kumisonkhano? Kodi izikutherani nthawi yomwe mumafunikira kucheza ndi banja lanu ndiponso kulithandiza kuti likhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova? Kuganizira mafunso amenewa kungakuthandizeni kudziwa kuti “zinthu zimene ndi zofunikadi kwambiri,” ndi zokhudza kulambira kwanu komanso kusamalira banja lanu kuposa kupeza ndalama zambiri. Mukatero mungasankhe zochita zimene zingachititse kuti Yehova akudalitseni. w25.01 17 ¶11-13

Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka.—Sal. 34:18.

Ngakhale ena akuchitireni zopanda chilungamo, musamakayikire kuti Yehova amakukondani komanso amakuonani kuti ndinu wamtengo wapatali. Ngati ‘mukudzimvera chisoni mumtima’ muzikumbukira kuti Yehova anaona zabwino mumtima mwanu ndipo anakukokerani kwa iye. (Yoh. 6:44) Nthawi zonse iye ndi wokonzeka kukuthandizani chifukwa amakukondani kwambiri. Chitsanzo cha Yesu chingatithandize kudziwa mmene Yehova amamvera. Ali padziko lapansi, Yesu ankakomera mtima komanso kuchitira chifundo anthu omwe ankaonedwa ngati osafunika. (Mat. 9:​9-12) Mwachitsanzo, mayi wina yemwe ankadwala matenda aakulu atagwira chovala chake pokhulupirira kuti achira, Yesu anamulimbikitsa komanso kumuyamikira chifukwa cha chikhulupiriro chake. (Maliko 5:​25-34) Yesu anatengera makhalidwe a Atate wake. (Yoh. 14:9) Choncho musamakayikire kuti Yehova amakuonani kuti ndinu wamtengo wapatali ndiponso amaona makhalidwe anu abwino, kuphatikizapo chikhulupiriro ndi chikondi chanu kwa iye. w24.10 7 ¶4-5

Sungani misozi yanga mʼthumba lanu lachikopa.—Sal. 56:8.

Pa moyo wake, Davide ankakumana ndi mavuto osiyanasiyana omwe ankamuchititsa kulira. Anthu ena ankadana naye ndipo ena omwe ankawakhulupirira anamukhumudwitsa. (1 Sam. 19:​10, 11; 2 Sam. 15:​10-14, 30) Pa nthawi ina iye analemba kuti: “Ndafooka chifukwa cha kuusa moyo kwanga. Usiku wonse ndimanyowetsa bedi langa ndi misozi, ndimalira ndipo misozi imadzaza pabedi panga.” (Sal. 6:6) Ngakhale kuti Davide anakumana ndi mavuto ambiri, sankakayikira kuti Yehova amamukonda. Iye analemba kuti: “Chifukwa Yehova adzamva mawu a kulira kwanga.” (Sal. 6:8) Mawu a mulemba lalero amasonyeza bwino mmene Yehova amatikondera. Davide ankamva ngati kuti Yehova akusunga misozi yake m’botolo kapena akuilemba m’buku. Davide sankakayikira kuti Yehova ankaona komanso kukumbukira mavuto ake. Ankakhulupirira kuti Atate wake wachikondi akudziwa zimene akukumana nazo komanso mmene zikumukhudzira. w24.12 22 ¶11-12