Deuteronomo 30:1-20

  • Kubwerera kwa Yehova (1-10)

  • Malamulo a Yehova si ovuta kwambiri (11-14)

  • Kusankha moyo kapena imfa (15-20)

30  “Mawu onsewa akadzakwaniritsidwa pa inu, madalitso ndi matemberero amene ndaika pamaso panu,+ ndipo mukadzawakumbukira*+ muli ku mitundu yonse kumene Yehova Mulungu wanu adzakubalalitsireni,+  inu nʼkubwerera kwa Yehova Mulungu wanu+ komanso kumvera mawu ake ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, mogwirizana ndi zonse zimene ndikukulamulani lero, inuyo ndi ana anu,+  Yehova Mulungu wanu adzabweza kwawo anthu a mtundu wanu amene anagwidwa nʼkupita kudziko lina,+ ndipo adzakuchitirani chifundo+ nʼkukusonkhanitsaninso pamodzi kuchokera pakati pa anthu onse kumene Yehova Mulungu wanu anakubalalitsirani.+  Ngakhale anthu a mtundu wanu amene anabalalitsidwawo atadzakhala kumalekezero kwa thambo, Yehova Mulungu wanu adzakusonkhanitsani nʼkukubweretsani kuchokera kumeneko.+  Yehova Mulungu wanu adzakubweretsani mʼdziko limene makolo anu analitenga kuti likhale lawo, ndipo lidzakhala lanu. Iye adzachititsa kuti zinthu zikuyendereni bwino ndipo adzakuchulukitsani kwambiri kuposa makolo anu.+  Yehova Mulungu wanu adzayeretsa* mitima yanu ndi mitima ya ana anu,+ kuti muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse komanso moyo wanu wonse ndipo mudzakhala ndi moyo.+  Ndiyeno Yehova Mulungu wanu adzabweretsa matemberero onsewa pa adani anu, amene ankadana nanu komanso kukuzunzani.+  Kenako inu mudzabwerera nʼkumvera mawu a Yehova komanso kutsatira malamulo ake onse amene ndikukupatsani lero.  Yehova Mulungu wanu adzachititsa kuti zinthu zikuyendereni bwino kwambiri pa ntchito iliyonse ya manja anu.+ Adzachulukitsa ana anu, ziweto zanu ndi zokolola zanu, chifukwa Yehova adzasangalalanso kuchititsa kuti zinthu zikuyendereni bwino, ngati mmene anachitira ndi makolo anu.+ 10  Chifukwa pa nthawiyo mudzamvera mawu a Yehova Mulungu wanu ndi kusunga malamulo komanso malangizo ake amene analembedwa mʼbuku ili la Chilamulo, ndipo mudzabwerera kwa Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse komanso moyo wanu wonse.+ 11  Lamulo limene ndikukupatsani leroli si lovuta kwa inu kulitsatira, ndipo silili poti simungathe kulipeza.*+ 12  Silili kumwamba kuti munene kuti, ‘Ndani adzapite kumwamba kuti akatitengere lamulolo kuti ife tidzalimve nʼkulitsatira?’+ 13  Ndiponso silili tsidya lina la nyanja kuti munene kuti, ‘Ndani adzawoloke kupita tsidya lina la nyanja kuti akatitengere lamulolo kuti ife tidzalimve nʼkulitsatira?’ 14  Chifukwa mawu a chilamulowo ali pafupi kwambiri ndi inu, ali mʼkamwa mwanu ndi mumtima mwanu+ kuti muwatsatire.+ 15  Taonani, ine ndikuika pamaso panu lero moyo ndi zinthu zabwino, imfa ndi zinthu zoipa.+ 16  Mukadzamvera malamulo a Yehova Mulungu wanu amene ndikukupatsani lero, pokonda Yehova Mulungu wanu,+ kuyenda mʼnjira zake ndi kusunga malamulo ake, malangizo ake ndi zigamulo zake, mudzakhala ndi moyo,+ mudzachulukana ndipo Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani mʼdziko limene mukupita kukalitenga kuti likhale lanu.+ 17  Koma mtima wanu ukatembenukira kwina+ ndipo simukumvera, moti mwakopeka nʼkugwadira milungu ina ndi kuitumikira,+ 18  ndikukuuzani lero kuti mudzatheratu.+ Simudzakhala nthawi yaitali mʼdziko limene mukupita kukalitenga kuti likhale lanu mutawoloka Yorodano. 19  Lero ndaika moyo ndi imfa, dalitso ndi temberero pamaso panu.+ Kumwamba ndi dziko lapansi ndi mboni pa zochita zanu. Choncho inuyo ndi mbadwa zanu+ musankhe moyo kuti mukhalebe ndi moyo.+ 20  Musankhe moyo pokonda Yehova Mulungu wanu,+ kumvera mawu ake ndi kukhala okhulupirika kwa iye,+ chifukwa iye ndi amene amapereka moyo ndipo angakuthandizeni kuti mukhale ndi moyo kwa nthawi yaitali mʼdziko limene Yehova analumbira kuti adzalipereka kwa makolo anu, Abulahamu, Isaki ndi Yakobo.”+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “mukadzawabweretsanso mumtima mwanu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “adzachita mdulidwe.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “silili patali.”