September

Lachiwiri, September 1

September

Pitirizani kudziyesa kuti muone ngati mukadali ndi chikhulupiriro.2 Akor. 13:5.

Sikuti tizingoyesetsa kuti tikule mwauzimu koma tiziyesetsanso kuti tikhalebe aakulu mwauzimu. Kuti zimenezi zitheke tiyenera kupewa kudzidalira. (1 Akor. 10:12) Tifunika “kupitiriza kudziyesa” kuti tione ngati tikupitabe patsogolo. M’kalata yake yopita kwa Akhristu a ku Kolose, mtumwi Paulo anatsindika kufunika kokhalabe olimba mwauzimu. Ngakhale kuti iwo anali aakulu kale mwauzimu, Paulo anawachenjeza kuti asapusitsidwe ndi nzeru za anthu. (Akol. 2:​6-10) Epafura, yemwe zikuoneka kuti ankawadziwa bwino anthu a mumpingomo, ankawapempherera nthawi zonse kuti “apitirize kukhala olimba mwauzimu.” (Akol. 4:12) Kodi tikuphunzirapo chiyani? Paulo ndi Epafura ankadziwa kuti pamafunika khama komanso kuthandizidwa ndi Mulungu kuti munthu akhalebe wolimba mwauzimu. Iwo ankafuna kuti Akhristu a ku Kolose akhalebe olimba mwauzimu ngakhale kuti ankakumana ndi mavuto. w24.04 6-7 ¶16-17

Yehova ali nafe. Musawaope.—Num. 14:9.

Kuopa Yehova moyenera kumatithandiza kuti tizimukonda kwambiri moti sitingachite chilichonse chimene chingamukhumudwitse. Timafunitsitsa kuphunzira kuti tizitha kusiyanitsa pakati pa zoyenera ndi zosayenera ndiponso pakati pa choonadi ndi mfundo zabodza n’cholinga choti tizisangalatsa Yehova. (Miy. 2:​3-6; Aheb. 5:14) Tikamaopa kwambiri anthu kuposa Mulungu tikhoza kupatutsidwa pa choonadi. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi atsogoleri amafuko 12 amene anapita kukaona dziko limene Mulungu analonjeza kuti adzapereka kwa Aisiraeli. Atsogoleri 10 ankaopa kwambiri Akanani kuposa mmene ankakondera Yehova. Iwo anauza Aisiraeli anzawo kuti: “Sitingathe kukalimbana nawo anthuwo, chifukwa ndi amphamvu kuposa ifeyo.” (Num. 13:​27-31) N’zoona kuti malinga n’kuona kwa anthu, Akanani anali amphamvu kuposa Aisiraeli. Koma ponena kuti Aisiraeli sakanatha kugonjetsa adani awo ndiye kuti sankaganizira za Yehova. w24.07 9 ¶5-6

Ndinu Woweruza wa dziko lonse lapansi. Ndiye kodi simuchita chilungamo?—Gen. 18:25.

Kodi tingakhale otsimikiza kuti nthawi zonse Yehova amaweruza anthu mwachilungamo? Inde. Abulahamu ankadziwa kuti Yehova ndi “Woweruza wa dziko lonse lapansi” yemwe ndi wangwiro, wanzeru komanso wachifundo. Iye waphunzitsa bwino Mwana wake ndipo wamupatsa udindo wonse woweruza. (Yoh. 5:22) Iye pamodzi ndi Mwana wakeyu amadziwa zimene zili mumtima mwa munthu. (Mat. 9:4) Choncho akamadzaweruza munthu aliyense adzachita zinthu ‘mwachilungamo.’ Tiyeni tisamakayikire ngakhale pang’ono kuti Yehova amadziwa zonse. Timadziwa kuti iye ndi woyenera kuweruza osati ifeyo. (Yes. 55:​8, 9) Choncho nkhani yonse yoweruzayi timaisiya m’manja mwa iyeyo ndi Mwana wake. Ndipo Mwana wakeyu ndi Mfumu imene imatsanzira Atate wake posonyeza chilungamo ndi chifundo.Yes. 11:​3, 4w24.05 7 ¶18-19

Yehova amanyansidwa ndi munthu wachiphamaso, koma anthu owongoka mtima amakhala nawo pa ubwenzi wolimba.—Miy. 3:32.

Tingathe kuona ubwino wokhala oona mtima tikaganizira zimene zinachitika Yesu atakumana koyamba ndi Natanayeli. Filipo atamubweretsa Natanayeli kwa Yesu, panachitika chinthu china chochititsa chidwi. Ngakhale kuti Yesu anali asanakumanepo ndi Natanayeli, iye ananena kuti: “Onani Mwisiraeli ndithu, amene mwa iye mulibe chinyengo.” (Yoh. 1:47) Yesu anaona kuti Natanayeli anali woona mtima kwambiri. Mofanana ndi tonsefe, Natanayeli sanali wangwiro koma ankayesetsa kupewa chinyengo. Yesu anachita chidwi ndi zimenezi ndipo anayamikira Natanayeli. Mfundo zambiri za mu Salimo 15 zimakhudza mmene timachitira zinthu ndi anzathu. Salimo 15:3 limanena kuti mlendo mutenti ya Yehova “sanena miseche ndi lilime lake, sachitira mnzake choipa chilichonse, ndipo sanyoza anzake.” Kugwiritsa ntchito mawu athu molakwika kungavulaze ena.—Yak. 1:26. w24.06 10 ¶7, 9; 11 ¶10

Ambuye, ngakhale ziwanda zimatigonjera tikagwiritsa ntchito dzina lanu.—Luka 10:17.

Tikakonzekera bwino utumiki zimakhala zosavuta kuti tilankhule ndi anthu. Yesu anathandiza ophunzira ake kuti akonzekere asanawatume kuti akalalikire. (Luka 10:​1-11) Popeza anagwiritsa ntchito zimene Yesu anawaphunzitsa, ophunzirawo anasangalala kwambiri chifukwa cha zimene anakwanitsa kuchita. Kodi tingakonzekere bwanji utumiki? Tiyenera kuganizira mmene tingafotokozere mfundo za choonadi mogwira mtima m’mawu athuathu. Tingachitenso bwino kuganizira zinthu ziwiri kapena zitatu zimene anthu a m’gawo lathu amakonda kunena n’kukonzekera mmene tingawayankhire. Ndiyeno tikamalankhula ndi anthu mtima wathu ukhoza kukhala m’malo, tikhoza kumasekerera komanso kukhala aubwenzi. w24.04 16 ¶6-7

Ndinu woyenera, inu Yehova Mulungu wathu kulandira ulemerero, ulemu ndi mphamvu chifukwa munalenga zinthu zonse.Chiv. 4:11.

Chifukwa chachikulu chomwe timalalikirira uthenga wabwino n’chakuti timakonda Yehova Mulungu komanso dzina lake loyera. Timaona kuti kulalikira ndi njira yotamandira Mulungu wathu yemwe timamukonda. Timagwirizana ndi zimene angelo ananena, kuti Yehova Mulungu ndi woyenera kulandira ulemerero, ulemu ndi mphamvu kuchokera kwa atumiki ake omwe amamulambira mokhulupirika. Timamupatsa ulemerero ndi ulemu tikamauza ena umboni wosatsutsika wakuti iye ndi “amene analenga zinthu zonse” komanso kuti tili ndi moyo chifukwa cha iye. Timamupatsa mphamvu zathu tikamagwiritsa ntchito nthawi, mphamvu komanso zinthu zathu polalikira mmene tingathere mogwirizana ndi mmene zinthu zilili pa moyo wathu. (Mat. 6:33; Luka 13:24; Akol. 3:23) Mwachidule, timakonda kuuza ena za Mulungu wathu yemwe timamukonda. Timalimbikitsidwanso kuuza ena za dzina lake komanso zimene limatanthauza. w24.05 17 ¶11

Amapereka mphoto kwa anthu amene amamufunafuna ndi mtima wonse.—Aheb. 11:6.

Yehova amatipatsa mtendere komanso amatithandiza kukhala osangalala ndipo adzatipatsa moyo wosatha m’tsogolo. Timakhulupirira kwambiri kuti iye amafunitsitsa kutipatsa mphoto ndipo ali ndi mphamvu yochitira zimenezo. Tikamamukhulupirira kwambiri, timapitiriza kumutumikira ndi mtima wonse ngati mmene atumiki ake akale ankachitira. Izi ndi zimenenso Timoteyo anachita. (Aheb. 6:​10-12) Timoteyo ankakhulupirira kwambiri kuti Mulungu wamoyo adzamupatsa mphoto. (1 Tim. 4:10) N’chifukwa chake iye ankachita khama potumikira Mulungu. Kodi iye ankachita bwanji zimenezi? Mtumwi Paulo anamulimbikitsa kuti ayesetse kukhala mphunzitsi wabwino pa ntchito yolalikira komanso mumpingo. Iye ankafunikanso kukhala chitsanzo chabwino kwa Akhristu anzake, achinyamata ndi achikulire omwe. Anapatsidwanso ntchito yovuta yomwe inkaphatikizapo kupereka malangizo amphamvu koma achikondi kwa anthu omwe angafunikire malangizowo. (1 Tim. 4:​11-16; 2 Tim. 4:​1-5) Timoteyo sankakayikira kuti Yehova adzamupatsa mphoto.—Aroma 2:​6, 7w24.06 22-23 ¶10-11

Yehova ankachenjeza Aisiraeli ndi Ayuda kudzera mwa aneneri ake onse.2 Maf. 17:13.

Nthawi zonse Yehova ankagwiritsa ntchito aneneri pofuna kuchenjeza komanso kuthandiza anthu ake kuti asinthe. Mwachitsanzo, kudzera mwa Yeremiya, Mulungu ananena kuti: “Bwerera Isiraeli wopanduka iwe. Sindidzakuyangʼana mokwiya chifukwa ndine wokhulupirika . . . Sindidzakhala wokwiya mpaka kalekale. Koma vomerezani kuti ndinu olakwa chifukwa mwapandukira Yehova.” (Yer. 3:​12, 13) Kudzera mwa Yoweli, Yehova anati: “Bwererani kwa ine ndi mtima wonse.” (Yow. 2:​12, 13) Anauzanso Yesaya kuti alengeze kuti: “Dziyeretseni. Chotsani zochita zanu zoipa pamaso panga. Lekani kuchita zoipa.” (Yes. 1:​16-19) Ndiponso kudzera mwa Ezekieli, Yehova anafunsa kuti: “Kodi ine ndimasangalala ndi imfa ya munthu wochimwa? Kodi zimene ine ndimafuna si zoti munthu wochimwayo alape n’kupitiriza kukhala ndi moyo? Inetu sindisangalala ndi imfa ya munthu aliyense, . . . choncho siyani kuchita zoipa kuti mupitirize kukhala ndi moyo.” (Ezek. 18:​23, 32) Yehova amasangalala akaona kuti anthu alapa chifukwa iye amafuna kuti iwo apitirize kukhala ndi moyo mpaka kalekale. w24.08 9 ¶5-6

Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu, ndipo ndi othandiza.—2 Tim. 3:16.

Anthu onse a Mulungu amalandira chakudya chauzimu, malangizo komanso chitetezo chimene amafunikira. Chitsanzo chosonyeza kuti Yehova alibe tsankho masiku ano ndi chakuti amathandiza anthu padziko lonse kuti apeze Baibulo. Malemba opatulika analembedwa m’zilankhulo zitatu: Chiheberi, Chiaramu ndi Chigiriki. Kodi anthu amene amalankhula bwino zilankhulo zoyambirirazi ndi amene amakhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova kuposa ena? Ayi si choncho. (Mat. 11:25) Yehova satiitana kuti tikhale alendo ake chifukwa choti tinaphunzira kwambiri kapena timadziwa zilankhulo zoyambirira za Baibulo. Choncho iye amalola kuti anthu padziko lonse adziwe nzeru zake, kaya ndi ophunzira kapena ayi. Baibulo lomwe ndi Mawu ake lamasuliridwa m’zilankhulo zambiri ndipo anthu padziko lonse angathe kupindula ndi zimene limaphunzitsa komanso angadziwe zimene angachite kuti akhale anzake.—2 Tim. 3:​16, 17. w24.06 6-7 ¶13-15

Mzinda [wa Yerusalemu] watsala pangʼono kuwonongedwa.—Luka 21:20.

Kuwonongedwa kwa mzinda wa Yerusalemu komwe Yesu ananeneratu kunali kutatsala pang’ono kuchitika. Ngakhale zinali choncho, Akhristuwo akanatha kugwiritsa ntchito nthawi imeneyo podzikonzekeretsa komanso kuyesetsa kuti akhale ndi makhalidwe monga chikhulupiriro ndi kupirira. (Aheb. 10:25; 12:​1, 2) Posachedwapa tikumana ndi chisautso chachikulu kwambiri kuposa chimene Akhristu a Chiheberi ankayembekezera. (Mat. 24:21; Chiv. 16:​14, 16) Choncho tiyeni tikambirane malangizo amene Yehova anapereka kwa Akhristuwo omwe angatithandizenso masiku ano. Mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu anzake kuti aziphunzira komanso kuganizira mozama Mawu a Mulungu. (Aheb. 5:14–6:1) Pogwiritsa ntchito Malemba a Chiheberi, Paulo anafotokozera abale akewo kuti njira yolambirira ya Akhristu inali yapamwamba kuposa ya Ayuda. Paulo ankadziwa kuti kudziwa bwino komanso kumvetsa mfundo za choonadi kukanathandiza Akhristuwo kuti azindikire komanso kupewa kupusitsidwa ndi mfundo zabodza. w24.09 8-9 ¶2-3; 10 ¶6

Nʼzoonadi, Ambuye auka kwa akufa.—Luka 24:34.

N’chifukwa chiyani ophunzira a Yesu ankafunika kulimbikitsidwa? Ena anasiya nyumba, mabanja komanso mabizinezi awo n’cholinga choti azitsatira Yesu. (Mat. 19:27) Pomwe enanso ankazunzidwa chifukwa chokhala ophunzira ake. (Yoh. 9:22) Iwo analolera kusintha moyo wawo komanso kuvutika chifukwa ankakhulupirira kuti Yesu ndi Mesiya wolonjezedwa. (Mat. 16:16) Koma Yesu ataphedwa, iwo anakhumudwa chifukwa choona kuti zimene ankayembekezera zalephereka. Yesu ankaona kuti zinali zomveka kuti ophunzira ake akhale ndi chisoni ndipo sunali umboni wakuti anali ofooka mwauzimu. Choncho tsiku limene anaukitsidwa anayamba kulimbikitsa anzakewo. Mwachitsanzo, iye anaonekera kwa Mariya wa ku Magadala pomwe ankalira pamanda ake. (Yoh. 20:​11, 16) Anaonekeranso kwa ophunzira awiri ku Emau. Komanso anaonekera kwa mtumwi Petulo. w24.10 13 ¶5-6

Muzikhala okonzeka kuyankha aliyense amene wakufunsani za chiyembekezo chanu.—1 Pet. 3:15.

Makolo, muzithandiza mwana wanu kuti azitha kufotokozera ena chifukwa chake amakhulupirira kuti kuli Mlengi. Zingakhale zothandiza kuphunzira ndi mwana wanuyo nkhani zopezeka pa jw.org zakuti, “Zimene Achinyamata Amadzifunsa—Kodi Zinthu Zinachita Kulengedwa?” Ndiyeno mungakambirane ndi mwana wanuyo zifukwa zimene iyeyo akuona kuti zingathandize ena kudziwa kuti zinthu zinachita kulengedwa. Mulimbikitseni kuti azigwiritsa ntchito mfundo zosavuta ngati ena akufuna kuti akambirane naye. Mwachitsanzo, mnzake wakusukulu anganene kuti: “Ndimangokhulupirira zokhazo zimene ndaziona, ndipo sindinaonepo Mulungu.” Mkhristu wachinyamatayo angayankhe kuti: “Tiyerekeze kuti ukuyenda m’nkhalango kumalo kumene kulibeko anthu ndipo wapeza chitsime chabwinobwino. Kodi ungaganize chiyani? Ngati chitsimecho chikukupatsa umboni woti pali winawake wanzeru amene anachipanga, ndiye kuli bwanji zinthu zonse za m’chilengedwezi?” w24.12 18 ¶16

Kodi si paja okalamba amakhala ndi nzeru, ndipo amene akhala moyo wautali si paja amamvetsa zinthu?—Yobu 12:12.

Tonsefe timafunikira malangizo kuti tizisankha zochita mwanzeru. Tingapeze malangizowa kwa akulu komanso Akhristu olimba mwauzimu. Ngati otipatsa malangizowo ali achikulire, tisamafulumire kuganiza kuti malangizo awo ndi achikale. Yehova amafuna kuti tiziphunzira zinthu kuchokera kwa achikulirewo. Iwo akhala ndi moyo kwa nthawi yaitali kuposa ife, zomwe zachititsa kuti adziwe zinthu zambiri, azimvetsa zinthu komanso akhale ndi nzeru. Kale, Yehova ankagwiritsa ntchito achikulire okhulupirika pofuna kulimbikitsa komanso kutsogolera anthu ake. Mwachitsanzo, iye anagwiritsa ntchito anthu ngati Mose, Davide komanso mtumwi Yohane. Iwo anakhala ndi moyo pa nthawi zosiyanasiyana ndipo zochitika pa moyo wawo zinalinso zosiyana kwambiri. Pamene moyo wawo unkapita kumapeto, iwo anapereka malangizo anzeru kwa achinyamata. Aliyense wa amuna okhulupirikawa anatsindika kufunika komvera Mulungu. Yehova anachititsa kuti mawu awo anzeru alembedwe n’cholinga choti azitithandiza masiku ano. Kaya ndife achinyamata kaya achikulire, kuphunzira malangizo a amuna amenewa kungatithandize.—Aroma 15:4; 2 Tim. 3:16. w24.11 8 ¶1-2

Mukapanda kudya mnofu wa Mwana wa munthu ndi kumwa magazi ake, simudzapeza moyo.—Yoh. 6:53.

Kale mu nthawi ya Nowa, Mulungu analetsa anthu kuti asamadye magazi. (Gen. 9:​3, 4) Yehova anabwerezanso lamuloli m’Chilamulo chimene anapereka kwa Aisiraeli. Aliyense wodya magazi ankayenera ‘kuphedwa.’ (Lev. 7:27) Yesu ankamvera malamulo omwe Mulungu anapereka m’Chilamulo. (Mat. 5:​17-19) Choncho zinali zosamveka kuti iye auze Ayudawo kuti adye mnofu kapena kumwa magazi ake. N’zoonekeratu kuti Yesu anagwiritsa ntchito mawu ophiphiritsa ngati mmene anachitira polankhula ndi mayi wa Chisamariya pomwe anati: ‘Madzi amene ndidzamupatsewo . . . adzamupatsa moyo wosatha.’ (Yoh. 4:​7, 14) Yesu sankatanthauza kuti mayiyo adzapeza moyo wosatha pongomwa madzi enieni. Mofanana ndi zimenezi iye sankatanthauza kuti anthu omwe ankalankhula nawo ku Kaperenao adzapeza moyo wosatha ngati atadya mnofu wake weniweni komanso kumwa magazi ake. w24.12 9 ¶4-6

Mupereke matupi anu ngati nsembe yamoyo, yoyera ndiponso yovomerezeka kwa Mulungu, yomwe ndi utumiki wopatulika pogwiritsa ntchito luso la kuganiza.—Aroma 12:1.

Akhristu ayenera kupewa maganizo olakwika okhudza akazi. Chifukwa chiyani? Tikutero chifukwa zimene munthu amachita zimayamba ndi kuganiza. Mtumwi Paulo anachenjeza Akhristu odzozedwa ku Roma kuti ‘asamatengere nzeru za nthawi ino.’ (Aroma 12:​1, 2) Pamene Paulo ankalemba kalatayi mpingo wa ku Roma unali utakhalapo kwa nthawi yaitali. Koma mawu a Paulowa akusonyeza kuti ena mumpingowo ankayendera maganizo komanso chikhalidwe cha m’dzikoli. N’chifukwa chake anawalimbikitsa kuti asinthe maganizo ndi khalidwe lawo. Malangizo amenewa ndi othandizanso kwa amuna a Chikhristu masiku ano. N’zomvetsa chisoni kuti ena atengera maganizo a m’dzikoli ndipo amachitira nkhanza akazi awo. w25.01 9 ¶4

Wetani gulu la nkhosa za Mulungu zomwe zili mʼmanja mwanu, monga oyangʼanira.—1 Pet. 5:2.

Akulu amakhala otanganidwa kwambiri masiku ano. Iwo amagwira ntchito yolalikira. (2 Tim. 4:5) Amatsogolera mwakhama ntchitoyi, kuonetsetsa kuti ikuchitika mugawo la mpingo wawo komanso kutiphunzitsa kuti tiziigwira bwino. Iwo amagwiranso ntchito ngati oweruza achifundo komanso opanda tsankho. Mkhristu akachita tchimo lalikulu, akulu amamuthandiza kuti akonzenso ubwenzi wake ndi Yehova koma pa nthawi imodzimodziyo, amaonetsetsa kuti mpingo ukhale woyera. (1 Akor. 5:​12, 13; Agal. 6:1) Akulu amadziwika kuti ndi abusa. (1 Pet. 5:​1-3) Amakonzekera komanso kukamba nkhani pamisonkhano, kudziwa bwino aliyense mumpingo komanso kuchita maulendo a ubusa. Kuwonjezera pa ntchito zimenezi, akulu ena amathandiza pa ntchito zomanga ndi kukonza Nyumba za Ufumu, kukonzekera misonkhano ikuluikulu ndiponso kukhala m’Makomiti Olankhulana ndi Achipatala komanso Magulu Oyendera Odwala. Akulu amagwira ntchito mwakhama kuti atithandize. w24.10 20 ¶9

Monga zilili kuti anthu onse amafa chifukwa cha Adamu, anthu onse adzapatsidwanso moyo kudzera mwa Khristu.—1 Akor. 15:22.

M’Baibulo, mawu akuti “kuwombola” amatanthauza kumasula kapena kukhululuka chifukwa chakuti dipo laperekedwa. Mtumwi Petulo anafotokoza zimenezi ponena kuti: “Mukudziwa inu kuti zinthu zimene zinakumasulani [m’chilankhulo choyambirira, “zinakuwombolani”] ku moyo wanu wopanda phindu umene munatengera kuchokera kwa makolo anu, sizinali zinthu zotha kuwonongeka monga siliva kapena golide. Koma munamasulidwa ndi magazi amtengo wapatali a Khristu, omwe ndi ofanana ndi magazi a nkhosa yopanda chilema komanso yopanda mawanga.” (1 Pet. 1:​18, 19) Chifukwa cha nsembe ya dipo tikhoza kumasulidwa ku ukapolo wa uchimo ndi imfa. (Aroma 5:21) Choncho tiyenera kuyamikira kwambiri Yehova ndi Yesu chifukwa chotimasula pogwiritsa ntchito magazi amtengo wapatali, kapena kuti moyo wa Yesu. w25.02 5 ¶15-16

Wosangalala ndi munthu amene nthawi zonse amasamala zochita zake.—Miy. 28:14.

Kodi tingatani kuti tizipewa mayesero? Tiyeni tione zimene tingaphunzire kwa wachinyamata wotchulidwa pa Miyambo chaputala 7. Iye anagona ndi mkazi wachiwerewere. Vesi 22 limatiuza kuti “mwadzidzidzi,” wachinyamatayo anayamba kulondola mkaziyo. Koma mavesi a m’mbuyo amasonyeza kuti iye anachitanso zinthu zina zomwe mwapang’onopang’ono zinamufikitsa poti achite tchimo. Kodi ndi zinthu ziti zomwe zinachititsa kuti achite tchimo? Choyamba, iye “ankadutsa mumsewu pafupi ndi mphambano” yolowera kunyumba ya mkazi wachiwerewereyo. Kenako anayamba kulowera kunyumba ya mkaziyo. (Miy. 7:​8, 9) Iye atamuona mkaziyo sanatembenuke n’kubwerera. M’malomwake analola kuti mkaziyo amukise komanso anamumvetsera pomwe ankafotokoza kuti anakapereka nsembe zamgwirizano. Mwina ankamuuza zimenezi pofuna kumuchititsa mnyamatayo kuti aziona kuti iye si munthu woipa. (Miy. 7:​13, 14, 21) Wachinyamatayo akanapewa zinthu zimenezi, akanatetezeka ndipo sakanachita tchimo. w24.07 16 ¶8-9; 19 ¶19

Mukhululukireni ndi mtima wonse ndiponso kumutonthoza.—2 Akor. 2:7.

Yehova salekerera machimo akuluakulu pakati pa anthu ake. Iye saona kuti anthu ochimwa omwe sakulapa ayenera kuchitiridwa chifundo kuti apitirizebe kukhala mumpingo limodzi ndi atumiki ake okhulupirika. Yehova ndi wachifundo koma si wolekerera ndipo mfundo zake sizisintha. (Yuda 4) Ndipotu kulekerera munthu wosalapa sichingakhale chifundo chifukwa zingavulaze anthu ena onse mumpingo. (Miy. 13:20; 1 Akor. 15:33) Ngakhale zili choncho, timadziwa kuti Yehova safuna kuti wina aliyense adzawonongedwe. Iye amafuna kupulumutsa anthu ngati n’kotheka. Amasonyeza chifundo kwa anthu amene alapa ndipo amafuna kuti akhale nawonso pa ubwenzi. (Ezek. 33:11; 2 Pet. 3:9) Choncho pamene munthu wa ku Korinto analapa n’kusiya njira yake yoipa, Yehova anagwiritsa ntchito mtumwi Paulo pouza mpingowo kuti umukhululukire n’kumulandiranso mumpingo. w24.08 17 ¶7; 18-19 ¶14-15

Nthawi iliyonse imene munachitira zimenezo mmodzi wa abale anga aangʼono awa, munachitiranso ine.—Mat. 25:40.

Mufanizo la nkhosa ndi mbuzi, Yesu anafotokoza kuti adzaweruza anthu potengera mmene anachitira pothandiza abale ake odzozedwa. (Mat. 25:​31-46) Pa nthawi ya “chisautso chachikulu,” iye adzapereka chiweruzochi Aramagedo isanachitike. (Mat. 24:21) Mofanana ndi mmene m’busa amalekanitsira nkhosa ndi mbuzi, Yesu adzalekanitsa anthu amene anathandiza mokhulupirika otsatira ake odzozedwa ndi anthu omwe sanawathandize. Ulosi wa m’Baibulo umasonyeza kuti, monga Woweruza wosankhidwa ndi Yehova, Yesu adzaweruza mwachilungamo. (Yes. 11:​3, 4) Iye amaona zochita, zoganiza ndi zolankhula za anthu komanso mmene anachitira zinthu ndi abale ake odzozedwa. (Mat. 12:​36, 37) Yesu adzadziwa amene ankathandiza abale ake odzozedwa komanso kugwira nawo ntchito yolalikira. Njira yaikulu imene a nkhosa zina amathandizira abale ake a Khristu, ndi kugwira nawo ntchito yolalikira. w24.09 20-21 ¶3-4

Muzifufuza zinthu zonse nʼkutsimikizira.—1 Ates. 5:21.

Tingatsimikizire kuti zimene timakhulupirira ndi zoona poziyerekezera ndi zimene Baibulo limanena. Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti wachinyamata akukayikira zoti Yehova amamukonda. Kodi iye ayenera kungokhulupirira kuti basi samukondadi? Ayi, m’malomwake ayenera kufufuza maganizo a Yehova pa nkhaniyo kuti atsimikizire. Tikamawerenga Mawu a Mulungu zimakhala ngati tikumva Yehova akutilankhula. Koma timafunika kuchita khama kuti tipeze maganizo a Yehova pa funso limene tili nalo. Tikamawerenga, tiyenera kuganizira kwambiri zimene zikutidetsa nkhawazo. Tingafufuze zambiri pa nkhaniyo pogwiritsa ntchito zinthu zothandiza pophunzira zimene gulu la Yehova latipatsa. (Miy. 2:​3-6) Tingapemphe Yehova kuti atithandize pa nthawi imene tikufufuzayo kuti tidziwe maganizo ake. Kenako tingafufuze mfundo za m’Baibulo zomwe zingatithandize pa nkhani yathuyo. w24.10 25 ¶4-5

[Chikondi] sichisamala zofuna zake zokha.—1 Akor. 13:5.

Yehova samadalitsa aliyense amene amachita zinthu chifukwa cha kunyada. (1 Akor. 10:​24, 33; 13:4) Nthawi zina ngakhale ophunzira a Yesu ankafuna maudindo pa zifukwa zolakwika. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Yakobo ndi Yohane. Iwo anapempha Yesu kuti adzawapatse malo apamwamba mu Ufumu wake. Yesu sanawayamikire kuti iwo anachita bwino kupempha zimenezi. M’malomwake iye anauza atumwi onse 12 kuti: “Aliyense amene akufuna kuti akhale wamkulu pakati panu akuyenera kukhala mtumiki wanu ndipo amene akufuna kuti akhale woyamba pakati panu akuyenera kukhala kapolo wa onse.” (Maliko 10:​35-37, 43, 44) Abale amene amakhala ndi mtima wofuna kutumikira ena, amathandiza kwambiri mumpingo.—1 Ates. 2:8. w24.11 15-16 ¶7-8

Alangizi akachuluka zinthu zimayenda bwino.—Miy. 15:22.

Tikamasankha zochita, kukonda ena kudzatilimbikitsa kuti tiziganizira “zopindulitsanso ena” komanso tikhale odzichepetsa. (1 Akor. 10:​23, 24, 32; 1 Tim. 2:​9, 10) Tikatero tidzasankha zinthu zomwe zimasonyeza kuti timakonda komanso kulemekeza ena. Mukamasankha zochita pa nkhani zofunika kwambiri, muziganiziranso zomwe mungachite kuti muzikwaniritse. Yesu anatiphunzitsa kuti ‘tiziwerengera’ mtengo wake. (Luka 14:28) Choncho muziganizira kuchuluka kwa nthawi komanso zinthu zina zomwe zingafunikire kuti zimene mwasankhazo zitheke. Nthawi zina mungafunike kukambirana ndi banja lanu kuti mudziwe mmene aliyense angathandizirepo pa zimene mwasankhazo. N’chifukwa chiyani kuchita zimenezi kuli kofunika? Zingakuthandizeni kudziwa ngati zimene mwasankhazo zikufunika kukonza pena ndi pena kapenanso ngati pali njira ina yabwino kwambiri. Ndiponso mukamakambirana ndi anthu a m’banja lanu n’kumamvetsera maganizo awo, iwo amakhala okonzeka kukuthandizani kuti zimene mwasankha ziyende bwino. w25.01 18-19 ¶14-15

Kondwerani ndipo muzisangalala.—Yes 65:18.

Yesaya anafotokoza chifukwa chake tiyenera ‘kukondwera ndiponso kusangalala’ m’paradaiso wauzimu. Yehova ndi amene wakonza paradaisoyu. (Yes. 65:​18, 19) N’chifukwa chake akutigwiritsa ntchito kuti tithandize anthu kuti atuluke m’mabungwe a m’dzikoli omwe sakuthandiza anthu kuti akhale pa ubwenzi ndi iye, n’kulowa m’paradaiso wauzimu wokongolayu. Timasangalala chifukwa cha madalitso amene timapeza chifukwa chokhala m’choonadi ndipo izi zimatilimbikitsa kuti tiziuza ena zokhudza madalitsowa. (Yer. 31:12) Timayamikiranso chiyembekezo chimene tili nacho chifukwa chokhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova ndipo timakhala osangalala. Baibulo limalonjeza kuti ‘tidzamanga nyumba nʼkumakhalamo, ndipo tidzadzala minda ya mpesa nʼkudya zipatso zake.’ Anthu “sadzagwira ntchito mwakhama pachabe” chifukwa ‘adzadalitsidwa ndi Yehova.’ Iye akutilonjeza kuti tidzakhala ndi moyo wabwino ndiponso otetezeka. Iye amadziwa zimene aliyense akufunikira ndipo ‘adzakwaniritsa zolakalaka za chamoyo chilichonse.’—Yes. 65:​20-24; Sal. 145:16. w24.04 22-23 ¶11-12

Mulungu ndi thanthwe langa lolimba ndi malo anga othawirako.—Sal. 62:7.

Yehova amakhala Thanthwe lathu tikamamudalira ndi mtima wonse. Timakhulupirira kuti zinthu zimatiyendera bwino tikamamumvera ngakhale pa nthawi yovuta. (Yes. 48:​17, 18) Tikamaona akutithandiza m’pamenenso timamukhulupirira kwambiri. Timakhulupirira kuti Yehova yekha ndi amene angatithandize kupirira mavuto ngakhale atakhala aakulu kwambiri. Mofanana ndi thanthwe lalikulu, Yehova amakhala chimodzimodzi nthawi zonse. Iye sasintha makhalidwe ake komanso cholinga chake. (Mal. 3:6) Adamu ndi Hava atakana kumumvera mu Edeni, Yehova sanasinthe cholinga chake. Mogwirizana ndi zimene Mtumwi Paulo analemba, Yehova “sangadzikane.” (2 Tim. 2:13) Zimenezi zikutanthauza kuti kaya pachitike zotani, kaya anthu ena achite zotani, Yehova sadzasintha makhalidwe ake, cholinga chake komanso mfundo zake. Popeza Yehova sasintha, timadziwa kuti iye adzatithandiza pa nthawi yovuta, komanso adzakwaniritsa malonjezo ake m’tsogolo.—Sal. 62:​6, 7w24.06 27-28 ¶7-8

Munthu wobisika mumtima . . . ndi wamtengo wapatali pamaso pa Mulungu.—1 Pet. 3:4.

Ngati muli pa chibwenzi, n’chiyani chingakuthandizeni kusankha kuti mukwatirane ndi munthuyo kapena ayi? Yesetsani kuti mudziwane bwino. Muyenera kuti munadziwapo zinthu zina zokhudza munthuyo musanayambe chibwenzi. Koma pa nthawiyi mumakhala ndi mwayi woti mudziwenso “munthu wobisika mumtima.” Zimenezi zikuphatikizapo kudziwa zokhudza ubwenzi wake ndi Yehova, makhalidwe ake komanso mmene amaganizira. Pakapita nthawi, muyenera kupeza mayankho a mafunso ngati akuti: ‘Kodi munthu ameneyu ndi woyenera kuti ndidzakwatirane naye?’ (Miy. 31:​26, 27, 30; Aef. 5:33; 1 Tim. 5:8) ‘Kodi tikhoza kumakondanadi komanso kupatsana zonse zomwe aliyense amafunikira? Kodi ndizidzakwanitsa kunyalanyaza zimene amalakwitsa?’ (Aroma 3:23) Pamene mukuyesetsa kudziwana bwino, muzikumbukira kuti chofunika kwambiri si kufanana pa chilichonse, koma kuona ngati mungakwanitse kukhalabe ndi munthuyo ngakhale kuti mumasiyana pa zinthu zina. w24.05 27 ¶5

Ndachimwira Yehova.—2 Sam. 12:13.

Mfumu Davide inachita tchimo lalikulu. Koma mneneri Natani atamudzudzula chifukwa cha tchimo lakelo, Davide anadzichepetsa n’kulapa. (Sal. 51:​3, 4, 17, timawu tapamwamba) Mfumu Hezekiya nayonso inachimwira Yehova. (2 Mbiri 32:25) Koma mofanana ndi Davide, Hezekiya anadzichepetsa n’kulapa. (2 Mbiri 32:26) Zotsatira zake n’zakuti Yehova ankamuona monga mfumu yokhulupirika yomwe ‘inkachita zoyenera.’ (2 Maf. 18:3) Kodi tikuphunzirapo chiyani? Tiyenera kulapa machimo athu n’kuyesetsa kuti tisawabwerezenso. Nanga kodi tizitani akulu akatipatsa malangizo pa zinthu zooneka ngati zazing’ono? Tisamaone ngati akuluwo komanso Yehova satikonda. Ngakhale mafumu abwino a ku Isiraeli ankafunikanso kupatsidwa malangizo komanso kudzudzulidwa. (Aheb. 12:6) Choncho tikamapatsidwa malangizo, tiyenera (1) kuwalandira modzichepetsa, (2) kusintha pamene pakufunika kutero, komanso (3) kupitiriza kutumikira Yehova ndi mtima wonse. Tikalapa machimo athu Yehova adzatikhululukira.—2 Akor. 7:​9, 11. w24.07 21 ¶8; 22 ¶9, 11

Mʼchotseni munthu woipayo pakati panu.—1 Akor. 5:13.

Wochimwa amachotsedwa mumpingo akakana kusintha ngakhale kuti akulu anamuthandiza mobwerezabwereza kuti alape. (2 Maf. 17:​12-15) Zochita zake zimasonyeza kuti iye wasankha kukana kutsatira mfundo za Yehova. (Deut. 30:​19, 20) Chilengezo chimaperekedwa kumpingo chonena kuti iye salinso wa Mboni za Yehova. Cholinga cha chilengezochi si kuchititsa manyazi munthuyo. Koma chimaperekedwa kuti anthu mumpingo atsatire malangizo a m’Malemba oti ‘asiye kugwirizana’ ndi munthuyo “ngakhalenso kudya naye.” (1 Akor. 5:​9-11) Pali chifukwa chabwino chimene Mulungu anaperekera malangizowa. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Zofufumitsa zapangʼono zimafufumitsa mtanda wonse wa ufa wokandakanda.” (1 Akor. 5:6) Ngati munthu wosalapa sakuchotsedwa mumpingo zochita zake zingafooketse ena omwe akuyesetsa kutsatira mfundo zolungama za Yehova.—Miy. 13:20; 1 Akor. 15:33. w24.08 27 ¶3-4

Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kuchokera kwa Mulungu amene amandipatsa mphamvu zimene ndikufunikira.—Afil. 4:13.

Sitingathe kupatsa munthu mphamvu koma tikhoza kugwiritsa ntchito mphamvu zathu kuti timuthandize. Mwachitsanzo, ngati pali Mkhristu amene ndi wachikulire kapena amene akudwala, tingamuthandize ntchito zapakhomo kapena kukamugulira zinthu. Kapenanso tikhoza kugwira nawo ntchito yoyeretsa kapena kukonza Nyumba ya Ufumu. Muzikumbukiranso kuti mawu ndi amphamvu. Kodi pali winawake amene mukudziwa kuti angamve bwino mutamuyamikira kuchokera pansi pa mtima? Kodi mukudziwa munthu wina amene akufunika kulimbikitsidwa? Ngati ndi choncho, mungachite bwino kulankhula ndi munthuyo. Mungachite zimenezo popita kukalankhula naye, kumuimbira foni, kumulembera khadi, imelo kapena kumutumizira meseji. Sikuti mufunika kulankhula mwaluso kwambiri. Mawu ochepa koma ochokera pansi pa mtima akhoza kuthandiza Mkhristu mnzanuyo kuti akhalebe wokhulupirika kapena kuti ayambe kumva bwino pa mavuto amene akukumana nawo.—Miy. 12:25; Aef. 4:29. w24.09 28 ¶8-10

Ngati munthu akuyesetsa kuti akhale woyangʼanira, akufuna ntchito yabwino.1 Tim. 3:1.

Ngati mwakhala mukutumikira ngati mtumiki wothandiza kwa kanthawi, muyenera kuti mwayesetsa kukhala ndi makhalidwe ambiri omwe amafunika kuti munthu akhale mkulu. Kodi mungayesetse kuti mugwire nawo “ntchito yabwino” imeneyi? Kodi akulu amagwira ntchito zotani? Amatsogolera pa ntchito yolalikira, amachita khama kuphunzitsa ndi kuchita maulendo aubusa komanso amalimbikitsa mpingo ndi mawu ndiponso zochita zawo. N’chifukwa chake Baibulo limatchula amuna akhamawa kuti ndi “mphatso.” (Aef. 4:8) Kodi m’bale angatani kuti akhale mkulu? Zimene zimafunika kuti munthu akhale mkulu n‘zosiyana kwambiri ndi zimene zimafunika kuti munthu apeze ntchito yolembedwa. M’dzikoli munthu amatha kulembedwa ntchito bola ngati ali ndi luso la ntchitoyo. Mosiyana ndi zimenezi, kuti mukhale mkulu pamafunika zambiri, osati kungokhala ndi luso lophunzitsa kapena kulalikira. Mumafunika kukhala ndi makhalidwe omwe afotokozedwa pa 1 Timoteyo 3:1-7 ndi Tito 1:​5-9. w24.11 20 ¶1-3