Kalata Yoyamba Yopita kwa Atesalonika 2:1-20

  • Utumiki wa Paulo ku Tesalonika (1-12)

  • Atesalonika analandira mawu a Mulungu (13-16)

  • Paulo ankalakalaka kuona Atesalonika (17-20)

2  Kunena zoona, inuyo mukudziwa abale, kuti ulendo wathu wobwera kwa inu sunali wopanda phindu.+  Chifukwa ngakhale kuti poyamba tinavutika komanso kuchitiridwa zachipongwe ku Filipi,+ monga mmene mukudziwira, tinalimba mtima mothandizidwa ndi Mulungu wathu kuti tikuuzeni uthenga wabwino wa Mulungu+ pa nthawi imene anthu ankatitsutsa kwambiri.*  Zimene tikukulimbikitsani kuti muchite sizikuchokera mʼmaganizo olakwika kapena odetsedwa ndipo sitikuzinena mwachinyengo.  Koma Mulungu wavomereza kuti tipatsidwe ntchito yolalikira uthenga wabwino. Choncho sitikulankhula nʼcholinga chosangalatsa anthu, koma Mulungu amene amafufuza mitima yathu.+  Ndipotu mukudziwa kuti sitinayambe talankhulapo mawu okuyamikirani mwachinyengo, kapena kuchita zachiphamaso ndi zolinga zadyera.+ Mulungu ndi mboni yathu.  Komanso sitinkafuna ulemerero wochokera kwa anthu, kaya kuchokera kwa inu kapena kwa anthu ena, ngakhale kuti monga atumwi a Khristu+ tikanatha kupempha kuti mutilipirire zinthu zina kuti mutithandize.  Mʼmalomwake, tinakusonyezani chikondi komanso kukoma mtima ngati mmene mayi woyamwitsa amachitira posamalira ana ake mwachikondi.  Choncho popeza timakukondani kwambiri,+ tinkafunitsitsa* kukuuzani uthenga wabwino wa Mulungu komanso kupereka miyoyo yathu yeniyeniyo+ kuti tikuthandizeni.  Ndithudi abale, mukukumbukira kuti tinayesetsa kugwira ntchito mwakhama ndi mphamvu zathu zonse. Tinkagwira ntchito usiku ndi masana kuti aliyense wa inu asatilipirire kanthu kalikonse pofuna kutithandiza,+ pamene tinkalalikira uthenga wabwino wa Mulungu kwa inu. 10  Pamene tinali ndi inu okhulupirira, tinali okhulupirika, tinkachita zinthu zachilungamo ndiponso tinalibe chifukwa chotinenezera. Inuyo komanso Mulungu ndinu mboni zathu. 11  Inu mukudziwa bwino kuti aliyense wa inu tinkamudandaulira, kumulimbikitsa komanso kumulangiza+ ngati mmene bambo+ amachitira ndi ana ake. 12  Tinkachita zimenezi nʼcholinga choti mupitirize kuyenda mʼnjira imene Mulungu amafuna.+ Iye ndi amene akukuitanani kuti mulowe mu Ufumu wake+ ndi kulandira ulemerero.+ 13  Ndithudi, nʼchifukwa chake ifenso timathokoza Mulungu mosalekeza,+ chifukwa pamene munalandira mawu a Mulungu amene munamva kwa ife, simunawalandire monga mawu a anthu, koma mmene alilidi, monga mawu a Mulungu. Mawu amenewa akugwiranso ntchito mwa inu okhulupirira. 14  Chifukwa inu abale munatsanzira mipingo ya Mulungu yogwirizana ndi Khristu Yesu imene ili ku Yudeya. Tikutero chifukwa munayamba kuvutitsidwa ndi anthu akwanu,+ ngati mmene iwowonso akuvutitsidwira ndi Ayuda. 15  Iwo anafika popha Ambuye Yesu+ komanso aneneri ndipo ife anatizunza.+ Kuwonjezera pamenepo, iwo sakusangalatsa Mulungu, koma akuchita zinthu zimene sizingapindulitse anthu onse. 16  Iwo akuchita zimenezi pamene akuyesa kutiletsa kulalikira kwa anthu a mitundu ina zimene angachite kuti adzapulumuke.+ Pochita zimenezi, nthawi zonse akuwonjezera machimo awo. Koma tsopano mkwiyo wake wawafikira.+ 17  Koma pamene tinakakamizika kusiyana ndi inu abale, kwa nthawi yochepa (pamasomʼpamaso osati mumtima mwathu), tinayesetsa kwambiri kuti tikuoneni pamasomʼpamaso* chifukwa ndi zimene tinkalakalaka kwambiri. 18  Choncho tinkafuna kubwera kwa inu ndipo ineyo Paulo ndinayesa kuti ndibwere, osati kamodzi kokha koma kawiri, koma Satana anatchinga njira yathu. 19  Kodi chiyembekezo chathu kapena chimwemwe chathu nʼchiyani? Kodi mphoto* imene tidzainyadire pamaso pa Ambuye wathu Yesu, pa nthawi ya kukhalapo kwake nʼchiyani? Kodi si inuyo?+ 20  Ndithudi, inu ndinu ulemerero wathu komanso chimwemwe chathu.

Mawu a M'munsi

Mabaibulo ena amati, “nthawi imene tinkavutika kwambiri.”
Kapena kuti, “tinali osangalala.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “tione nkhope zanu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “chisoti chachitsulo chooneka ngati nkhata.”