Kalata Yoyamba ya Yohane 1:1-10

  • Mawu opatsa moyo (1-4)

  • Muziyenda mʼkuwala (5-7)

  • Tiyenera kuvomereza machimo (8-10)

1  Tikukulemberani zokhudza amene analipo kuyambira pachiyambi, yemwe amabweretsa mawu opatsa moyo,+ amene tinamumva ndiponso kumuona ndi maso athu, amene tamuyangʼanitsitsa mwachidwi komanso kumukhudza ndi manja athu.  (Ife taona ndipo tikuchitira umboni+ ndi kukuuzani za moyo wosatha+ umene unachokera kwa Atate ndipo unaonetsedwa kwa ife.)  Zimene taziona komanso kuzimva, tikukuuzani+ kuti inunso mugwirizane nafe. Ndipotu ndife ogwirizana ndi Atate ndiponso Mwana wake Yesu Khristu.+  Choncho tikulemba zimenezi kuti tikhale osangalala kwambiri.  Ife tamva uthenga kuchokera kwa iye ndipo tikuulengeza kwa inu. Uthenga wake ndi wakuti, Mulungu ndiye kuwala+ ndipo kwa iye kulibe mdima ngakhale pangʼono.  Ngati tikunena kuti, “Ndife ogwirizana naye,” koma tikupitiriza kuyenda mumdima, ndiye kuti tikunama ndipo sitikuchita zinthu mogwirizana ndi choonadi.+  Komatu ngati tikuyenda mʼkuwala mofanana ndi mmenenso iye alili mʼkuwala, ndiye kuti ndife ogwirizana ndipo magazi a Yesu, yemwe ndi Mwana wake, akutiyeretsa ku machimo onse.+  Tikamanena kuti, “Tilibe uchimo,” ndiye kuti tikudzinamiza+ ndipo mumtima mwathu mulibe choonadi.  Mulungu ndi wokhulupirika ndiponso wolungama, choncho tikavomereza machimo athu, adzatikhululukira komanso kutiyeretsa ku ntchito zonse zoipa.+ 10  Tikamanena kuti, “Sitinachimwe,” zili ngati tikunena kuti Mulungu ndi wabodza, ndipo mumtima mwathu mulibe mawu ake.

Mawu a M'munsi