October

Lachinayi, October 1

October

Ine ndidzayembekezera Yehova.—Mika 7:7.

Nthawi zambiri timalandira malangizo okhudza kulambira kwathu kuchokera kwa akulu, oyang’anira dera, ofesi ya nthambi kapena Bungwe Lolamulira. Koma nthawi zina sitingamvetse chifukwa chake tapatsidwa malangizo enaake. Zikatero tikhoza kumangoona mavuto amene angabwere chifukwa cha malangizowo. Tikhozanso kumaganizira kwambiri zimene abale omwe apereka malangizowo amalakwitsa. Tikakhala ndi chikhulupiriro sitikayikira kuti Yehova akutsogolera gulu lake ndipo akudziwa mmene zinthu zilili. Choncho timakhala okonzeka kumvera mosanyinyirika. (Aheb. 13:17) Timazindikira kuti kumvera kwathu kumathandiza kuti mpingo ukhale wogwirizana. (Aef. 4:​2, 3) Ngakhale kuti abale amene amatitsogolera si angwiro, timakhulupirira kuti Yehova adzatidalitsa tikakhala omvera. (1 Sam. 15:22) Pa nthawi yake, iye adzakonza kalikonse koyenera kukonzedwa. w25.03 23-24 ¶13-14

Mulungu . . . ndi Woulula zinsinsi.—Dan. 2:28.

Tikukhala mu nthawi yosangalatsa kwambiri. Tsiku lililonse timaona maulosi a m’Baibulo akukwaniritsidwa. Mwachitsanzo, tikuona “mfumu yakumpoto” ndi “mfumu yakum’mwera” akukangana polimbirana ulamuliro. (Dan. 11:40) Tikuonanso uthenga wabwino ukulalikidwa padziko lonse ndipo anthu mamiliyoni akusankha kutumikira Mulungu. (Yes. 60:22; Mat. 24:14) Timalandiranso chakudya chauzimu chochuluka “pa nthawi yoyenera.” (Mat. 24:​45-47) Yehova akupitiriza kutithandiza kuti timvetse bwino zinthu zofunika zomwe zichitike posachedwapa. (Miy. 4:18) Sitikukayikira kuti pamene chisautso chachikulu chizidzayamba, tidzakhala tikudziwa zonse zofunikira kuti tikhalebe okhulupirika pa nthawi yovutayi. Komabe tiyenera kuzindikira kuti pali zinthu zina zokhudza m’tsogolo zomwe sitikudziwa. w24.05 8 ¶1-2

Iye sanena miseche ndi lilime lake.—Sal. 15:3.

Wolemba masalimo anatchulanso zokhudza miseche. Kodi miseche n’chiyani? Mwachidule ndi kunena zinthu zabodza zimene zingawononge mbiri ya munthu wina. Salimo 15:3 limatikumbutsanso kuti mlendo m’nyumba ya Yehova sachitira anzake zoipa ndipo sanyoza ena. (Sal. 15:1) Kodi munthu angachitire bwanji ena zoipa? Tingachitire ena zoipa pofalitsa zinthu zabodza zokhudza iwowo. Mwachitsanzo: (1) mlongo wasiya utumiki wa nthawi zonse, (2) banja lina silikutumikiranso pa Beteli kapena (3) m’bale sakutumikiranso ngati mkulu kapena mtumiki wothandiza. Kodi ndi bwino kungoganiza zimene zachititsa kusinthako n’kumauza ena zimene tikuganizazo? Pakhoza kukhala zifukwa zimene zachititsa zomwe ifeyo sitikuzidziwa. Kumbukirani kuti mlendo mutenti ya Yehova, “sachitira mnzake choipa chilichonse, ndipo sanyoza anzake.” w24.06 11 ¶11-13

Ndimaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse. Chifukwa iye ali kudzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.—Sal. 16:8.

Kuti tiziopa kwambiri Yehova, tiyenera kukhala ofunitsitsa kuti tizimusangalatsa pa chilichonse chomwe timasankha kuchita. Mukamawerenga nkhani za m’Baibulo muzidzifunsa kuti, ‘Kodi ineyo ndikanakhalapo, ndikanasankha kuchita chiyani?’ Mwachitsanzo, yerekezerani kuti munkamva pamene atsogoleri amafuko 10 a Aisiraeli ankalankhula pambuyo pokayendera dziko limene Yehova analonjeza kuti adzawapatsa. Kodi mukanakhulupirira zimene ankanena n’kuyamba kuopa anthu, kapena kukonda kwanu Yehova kukanakuchititsani kuchita zinthu zomusangalatsa? Aisiraeli onse sanakhulupirire choonadi chimene Yoswa ndi Kalebe ankalankhula. Zotsatira zake n’zakuti onse anataya mwayi wokalowa m’Dziko Lolonjezedwa.—Num. 14:​10, 22, 23. w24.07 10 ¶7

Yehova ndi amene amayesa mitima.Miy. 17:3.

Gomeri yemwe anali mkazi wa Hoseya anachita chigololo ndipo anamusiya n’kupita kwa mwamuna wina. Kodi Mulungu anamuona kuti iye sangasinthe? Yehova yemwe amatha kudziwa zomwe zili mumtima mwa munthu anauza Hoseya kuti: “Pita ukayambenso kukonda mkazi amene akukondedwa ndi mwamuna wina ndipo akuchita chigololo. Ukamukonde ngati mmene Yehova amakondera Aisiraeli, ngakhale kuti iwo amalambira milungu ina.” (Hos. 3:1; Miy. 16:2) Dziwani kuti mkazi wa Hoseya anali asanasiye kuchita tchimo lalikululi. Koma Yehova anauza Hoseya kuti apite kwa mkaziyo, kumukhululukira ndi kumutenganso monga mkazi wake. Mofanana ndi zimenezi, Yehova sanasiye kukonda anthu ake omwe anali osamvera. Ngakhale kuti iwo ankachita machimo akuluakulu, iye ankawakondabe komanso anapitiriza kuwathandiza kuti alape n’kusintha zochita zawo. Zimenezi zikutanthauza kuti Yehova, yemwe “amayesa mitima,” angathandizebe munthu yemwe akupitiriza kuchita tchimo lalikulu kuti alape. w24.08 10 ¶7

Chilamulo chimangochitira chithunzi zinthu zabwino zimene zikubwera.—Aheb. 10:1

Ayuda, omwe anadzakhala Akhristu, anakumana ndi mavuto aakulu. Pa nthawi ina iwo anali mtundu wosankhidwa ndi Mulungu. Mzinda wa Yerusalemu unali likulu la Ufumu wa Mulungu padziko lapansi ndipo kachisi anali likulu la kulambira koyera. Ayuda onse okhulupirika ankatsatira Chilamulo cha Mose chimene atsogoleri awo achipembedzo ankaphunzitsa. Zimene ankaphunzitsazo zinkakhudza nkhani ya zakudya, mdulidwe komanso mmene ankayenera kuchitira zinthu ndi anthu a mitundu ina. Koma Yesu atafa, Yehova sankavomerezanso nsembe zimene Ayuda ankapereka. Zimenezi zinali zovuta kwambiri kwa Akhristu a Chiyuda omwe poyamba ankatsatira Chilamulo. (Aheb. 10:​1, 4, 10) Ngakhalenso Akhristu olimba mwauzimu ngati mtumwi Petulo anavutika kuti asinthe zinthu zina. (Mac. 10:​9-14; Agal. 2:​11-14) Chifukwa chakuti ankakhulupirira mfundo zatsopano, Akhristuwo ankazunzidwa ndi atsogoleri achipembedzo a Chiyuda. w24.09 9 ¶4

Muzikumbukira amene akukutsogolerani. Amenewa anakuphunzitsani mawu a Mulungu.Aheb. 13:7.

Yehova akapereka ntchito kwa anthu amayembekezera kuti aigwire mwadongosolo. (1 Akor. 14:33) Mwachitsanzo, Mulungu amafuna kuti uthenga wabwino ulalikidwe padziko lonse lapansi kumene kuli anthu. (Mat. 24:14) Yehova anasankha Yesu kuti azitsogolera ntchito imeneyi. Ndipo Yesu akuonetsetsa kuti ntchitoyi izigwiridwa mwadongosolo. Mu nthawi ya atumwi pamene mipingo inkakhazikitsidwa, akulu ankaikidwa kuti azipereka malangizo komanso azitsogolera. (Mac. 14:23) Ku Yerusalemu kunali bungwe limene linapangidwa ndi atumwi ndi akulu ndipo linkapereka malangizo amene mipingo yonse inkayenera kutsatira. (Mac. 15:2; 16:4) Chifukwa chomvera malangizo amene ankapatsidwa, “anthu m’mipingo anapitiriza kukhala ndi chikhulupiriro cholimba ndipo chiwerengero chinkawonjezeka tsiku ndi tsiku.”—Mac. 16:5. w24.04 8 ¶1

Mariya wa ku Magadala anapita kwa ophunzirawo ndipo anawauza kuti: “Ambuye ndawaona ine!”—Yoh. 20:18.

M’mawa pa Nisani 16, amayi ena okhulupirika anapita kumanda a Yesu. (Luka 24:​1, 10) Tiyeni tione zimene zinachitikira mmodzi wa amayiwa dzina lake Mariya wa ku Magadala. Mariya atafika anapeza kuti m’mandamo munalibe kanthu. Iye anathamanga kukauza Petulo ndi Yohane ndipo anawalondola pomwe iwo ankapita kumandako. Petulo ndi Yohane atatsimikizira kuti m’mandamo mulibe kanthu anabwerera kunyumba, koma Mariya anatsala komweko n’kumalira. Iye sankadziwa kuti Yesu akumuona. Yesu anakhudzidwa kwambiri ataona mayi wokhulupirikayo akulira. Choncho anaonekera kwa Mariya ndipo anachita chinthu china chomwe chinamulimbikitsa kwambiri. Yesu analankhula naye ndipo anamutuma kuti akauze abale ake kuti iye waukitsidwa.—Yoh. 20:​17, 18. w24.10 13 ¶7

Ndidzachita zizindikiro ndi zodabwitsa zochuluka mʼdziko la Iguputo.—Eks. 7:3.

Mose anali mneneri, woweruza, mtsogoleri komanso wolemba mbiri. Iye anatsogolera Aisiraeli kuchoka ku ukapolo ku Iguputo ndipo anaona Yehova akuchita zinthu zambiri zodabwitsa. Yehova anamugwiritsa ntchito kuti alembe mabuku 5 oyambirira a m’Baibulo, Salimo 90, komanso mwina Salimo 91. Zikuonekanso kuti iye ndi amene analemba buku la Yobu. Atatsala pang’ono kufa, ali ndi zaka 120, Mose anasonkhanitsa Aisiraeli onse n’kuwakumbutsa zimene anaona Yehova akuwachitira. Iwo anaona zizindikiro ndi zodabwitsa zambiri zimene Yehova anachita ndiponso mmene anaweruzira Aiguputo. (Eks. 7:4) Iwo anayenda pa Nyanja Yofiira madzi atagawikana ndipo anaona Yehova akuwononga magulu ankhondo a Farao. (Eks. 14:​29-31) Yehova anawateteza komanso kuwasamalira m’chipululu. (Deut. 8:​3, 4) Ndiyeno atsala pang’ono kulowa m’Dziko Lolonjezedwa, Mose anaona kuti uwu unali mwayi wake womaliza kuti awalimbikitse. w24.11 8-9 ¶3-4

Ngati wina atadya chakudya chimenechi adzakhala ndi moyo wosatha. Ndipotu chakudya chimene ndidzapereke kuti dzikoli lipeze moyo, ndi mnofu wangawu.—Yoh. 6:51.

Zimene Yesu anauza atumwi ake pa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye zikusiyana ndi zimene anauza gulu la anthu ku Galileya. Zimene analankhula ku Galileyako zinali zokhudza anthu ambiri. Pamene Yesu anali ku Galileya mu 32 C.E., ankalankhula ndi Ayuda omwe ankafuna kuti awapatse chakudya. Koma iye anawauza za zinthu zina zofunika kwambiri kuposa chakudya. Anawauza zinthu zomwe zingawathandize kudzapeza moyo wosatha. Yesu anawauza anthuwo kuti anthu omwe anamwalira adzaukitsidwa ndipo adzakhala ndi moyo wosatha. Apa sankanena za anthu ochepa ngati mmene anachitira pa nthawi ya Chakudya Chamadzulo cha Ambuye. Ku Galileya iye ankanena za madalitso amene anthu onse akhoza kupeza. w24.12 11 ¶10-11

Amuna, pitirizani kukonda akazi anu.—Akol. 3:19.

Yehova amadana ndi munthu aliyense wachiwawa. (Sal. 11:5) Iye amadana kwambiri ndi mwamuna amene amazunza mkazi wake. (Mal. 2:16) Ngati mwamuna amazunza mkazi wake amasokoneza ubwenzi wake ndi Mulungu. Yehova sangayankhe mapemphero ake. (1 Pet. 3:7) Amuna ena amazunza akazi awo powalankhula mwachipongwe komanso mwaukali. Koma Yehova amadana ndi ‘kupsa mtima, mkwiyo, kulalata komanso mawu achipongwe.’ (Aef. 4:​31, 32) Mwamuna amene amalankhula mwachipongwe ndi mkazi wake amasokoneza banja lake komanso ubwenzi wake ndi Mulungu. (Yak. 1:26) N’chimodzimodzinso ndi mwamuna amene amaonera zolaula. Nayenso amasokoneza ubwenzi wake ndi Yehova komanso salemekeza mkazi wake. Yehova amayembekezera kuti zochita komanso zoganiza za mwamuna zizisonyeza kuti ndi wokhulupirika kwa mkazi wake. Yesu ananena kuti mwamuna amene amayang’ana mkazi wina momusirira wachita naye kale chigololo “mumtima mwake.”—Mat. 5:​28, 29. w25.01 9 ¶6-8

Munthu amaonedwa kuti ndi wolungama . . . chifukwa chokhulupirira Yesu Khristu basi.—Agal. 2:16.

Kuonedwa kuti ndi wolungama kumatanthauza kuti milandu yako yathetsedwa, ndipo zimene unalakwitsa zafufutidwa. Yehova akachita zimenezi, amakhala akutsatirabe mfundo zake zachilungamo. Sikuti amationa kuti ndife olungama chifukwa chakuti tachita zinazake. Ndiponso sikuti amakhala akulekerera machimo athu. Koma chifukwa choti timakhulupirira zimene wachita pophimba machimo athu komanso kupereka dipo, Yehova amatikhululukira. (Aroma 3:24) Kodi timapindula bwanji Yehova akamationa kuti ndife olungama? Anthu amene anasankhidwa kuti akalamulire ndi Yesu kumwamba amaonedwa kale kuti ndi olungama monga ana a Mulungu. (Tito 3:7; 1 Yoh. 3:1) Machimo awo anakhululukidwa. Iwo alibe mbiri iliyonse yoti anapalamula mlandu ndipo ndi oyenera kulowa mu Ufumu. (Aroma 8:​1, 2, 30) Amene akuyembekezera kudzakhala padziko lapansi, amaonedwa kuti ndi olungama monga anzake a Mulungu ndipo machimo awo amakhululukidwa.—Yak. 2:​21-23. w25.02 5 ¶17; 7 ¶18

Zimene umaganiza si maganizo a Mulungu, koma maganizo a anthu.—Mat. 16:23.

Taganizirani zimene zinachitika pa nthawi ina pamene mtumwi Petulo analephera kukhala ndi maganizo a Yehova. Yesu anali atauza atumwi ake kuti akuyenera kupita ku Yerusalemu ndipo akaperekedwa m’manja mwa atsogoleri achipembedzo, akazunzidwa ndipo pamapeto pake akaphedwa. (Mat. 16:21) Ziyenera kuti zinamuvuta Petulo kukhulupirira kuti Yehova angalole kuti Yesu, yemwe anali chiyembekezo cha Isiraeli, komanso Mesiya wolonjezedwa, aphedwe. (Mat. 16:16) Choncho Petulo anamutengera Yesu pambali n’kumuuza kuti: “Dzikomereni mtima Ambuye. Musalole kuti zimenezi zikuchitikireni ngakhale pang’ono.” (Mat. 16:22) Popeza kuti Petulo sankaganiza ngati Yehova pa nkhaniyi, sanali ndi maganizo ofanana ndi a Yesu. N’kutheka kuti Petulo anali ndi zolinga zabwino, koma Yesu anakana kutsatira malangizo ake. Pamenepatu pali phunziro kwa ife. Sichinali cholinga cha Yehova kuti Yesu adzakhale ndi moyo popanda kukumana ndi mavuto alionse. Pa nthawiyi Petulo anaphunzira mfundo yofunika kwambiri yakuti ayenera kukhala ndi maganizo a Yehova. w25.03 9 ¶5-6

Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka. Iye amapulumutsa anthu amene akudzimvera chisoni mumtima mwawo.—Sal. 34:18.

Kodi mtima ukukupwetekani chifukwa chakuti munthu amene munkamudalira wakukhumudwitsani kapena wachita zinthu zosakhulupirika? Kaya munthu wakukhumudwitsani bwanji, Atate wanu wakumwamba amakukondanibe. Ngati ena achita zosakhulupirika tingalimbikitsidwe ndi mawu a Davide a mulemba lalero. Buku lina linanena kuti anthu amene “akudzimvera chisoni mumtima mwawo” angakhalenso anthu amene “amaona kuti m’tsogolomu mulibe chabwino chilichonse.” Kodi Yehova amathandiza bwanji anthu amene amamva choncho? Mofanana ndi kholo lachikondi lomwe limatonthoza mwana wake akakhala ndi nkhawa, Yehova amakhala nafe pafupi. Iye amatisonyeza chifundo ndipo amakhala wokonzeka kutithandiza tikakhumudwa chifukwa cha kusakhulupirika kwa ena. Iye ndi wokonzeka kulimbikitsa anthu a mtima wosweka komanso amene akudzimvera chisoni mumtima mwawo.—Yes. 65:17. w24.12 23 ¶13-14

Mphoto imene mudzalandire . . . kwa Yehova.—Akol. 3:24.

Masiku ano akulu amadziwa kuti Yehova amaona komanso kuyamikira ntchito yabwino imene amagwira. Kuwonjezera pa kusamalira nkhosa za Mulungu, kuphunzitsa komanso kulalikira, akulu ambiri amathandizanso pantchito monga zomangamanga ndiponso kupereka thandizo pakachitika ngozi. Akulu enanso ali m’Magulu Oyendera Odwala kapena Makomiti Olankhulana ndi Achipatala. Akulu amene amadzipereka kugwira ntchito zimenezi amadziwa kuti Yehova ndiye mwiniwake wa mpingo. Iwo amagwira ntchito zawo modzipereka ndipo amakhulupirira kwambiri kuti Mulungu adzawapatsa mphoto chifukwa cha zimene amachita. (Akol. 3:​23, 24) N’zosatheka kuti aliyense akhale mkulu. Koma tonsefe tingathe kumupatsa chinachake Yehova. Mulungu wathu amayamikira tikamayesetsa kumutumikira mwakhama. Iye amaona tikamapereka zinthu zathu pothandiza pa ntchito yapadziko lonse, ngakhale zitakhala zochepa. Ndiponso amasangalala tikamanyalanyaza zolakwa za ena n’kuwakhululukira. Dziwani kuti Yehova amayamikira zimene mumachita. Amakukondani chifukwa cha zimene mumachitazo ndipo adzakupatsani mphoto.—Luka 21:​1-4. w24.06 23 ¶12-13

Musalole kuti mtima wanu upatukire kunjira zake. Musasochere nʼkuyamba kuyenda mʼnjira zake.—Miy. 7:25.

Nkhani imene Solomo analemba imasonyeza zimene zingachitikire mtumiki wa Yehova aliyense. Iye angathe kuchita tchimo lalikulu n’kumaona kuti zachitika “mwadzidzidzi.” Kapenanso angathe kunena kuti zangochitika. Koma ataganizira bwinobwino zimene zinachitika, akhoza kupeza kuti pali zina zomwe anachita mosaganiza bwino zomwe zachititsa kuti achite tchimolo. Zinthu zimenezi zingaphatikizepo zosangalatsa zosayenera, kucheza ndi anthu a makhalidwe oipa kapena kupezeka m’malo okayikitsa, kaya malo enieni kapena pa intaneti. N’kuthekanso kuti mwina anasiya kupemphera, kuwerenga Baibulo, kupezeka pamisonkhano kapenanso kugwira ntchito yolalikira. Choncho mofanana ndi wachinyamata wa m’buku la Miyambo, tchimo lake silingakhale kuti langochitika mwadzidzidzi. Kodi tikuphunzirapo chiyani? Sitiyenera kungopewa tchimo, koma tiyeneranso kupewa zinthu zimene zingachititse kuti tichite tchimolo. Solomo anamveketsa bwino mfundo imeneyi.—Mat. 5:​29, 30. w24.07 16 ¶10-11

Tili ndi chuma chimenechi mʼziwiya zadothi.—2 Akor. 4:7.

Kodi chuma chimenechi n’chiyani? Ndi ntchito yolalikira za Ufumu yomwe ndi yopulumutsa miyoyo. (2 Akor. 4:1) Nanga ziwiya zadothi n’chiyani? Zikuimira atumiki a Mulungu omwe amauza ena uthenga wabwino. M’nthawi ya Paulo, amalonda ankagwiritsa ntchito mitsuko yadothi ponyamula zinthu zofunika monga chakudya, vinyo komanso ndalama. Mofanana ndi zimenezi, Yehova watipatsa uthenga wabwino womwe ndi wamtengo wapatali. Mothandizidwa ndi Yehova, tingathe kupeza mphamvu zomwe timafunikira kuti tipitirize kulalikira uthenga wabwino mokhulupirika. Nthawi zina tikhoza kumaopa anthu kapenanso kuopa kuti akana uthenga wathu. Kodi tingalimbane bwanji ndi vutoli? Taganizirani pemphero limene atumwi anapereka atalamulidwa kuti asiye kulalikira. M’malo mochita mantha n’kusiya, iwo anapempha Yehova kuti awathandize kuti apitirize kulankhula molimba mtima. Yehova anayankha pemphero lawo nthawi yomweyo. (Mac. 4:​18, 29, 31) Inunso nthawi zina mukayamba kuopa anthu, muzimupempha kuti akuthandizeni kuti muzikonda kwambiri anthu n’cholinga choti musaope kuwauza uthenga wabwino. w24.04 16 ¶8-9

Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe.—Mat. 6:9.

Kukonda Yehova kumatilimbikitsanso kuti tiziyeretsa dzina lake. Zimenezi zikutanthauza kuti timafunitsitsa kuuza ena kuti zinthu zoipa zomwe Satana amanena zokhudza Yehova si zoona. (Gen. 3:​1-5; Yobu 2:4; Yoh. 8:44) Tikamalalikira, timafunitsitsa kuuza anthu onse omwe angamvetsere zoona zenizeni zokhudza Yehova. Timafuna kuti aliyense adziwe kuti khalidwe lake lalikulu ndi chikondi, amalamulira mwachilungamo ndiponso kuti posachedwapa Ufumu wake uthetsa mavuto onse n’kubweretsa mtendere ndi chimwemwe kwa anthu. (Sal. 37:​10, 11, 29; 1 Yoh. 4:8) Tikamauza anthu zinthu ngati zimenezi zokhudza Yehova, timakhala tikuyeretsa dzina lake. Timasangalalanso chifukwa timadziwa kuti tikuchita zinthu mogwirizana ndi dzina lathu. w24.05 18 ¶12

Ukakonza phwando, uziitana anthu osauka, otsimphina, olumala ndi osaona. Ukatero udzakhala wosangalala chifukwa alibe choti adzakubwezere. Mulungu adzakubwezera anthu olungama akamadzaukitsidwa.—Luka 14:​13, 14.

Abale, mungasonyeze kuti ndinu “wochereza” mukamachitira zabwino anthu ena, kuphatikizapo amene si anzanu apamtima. (1 Pet. 4:9) Pofotokoza za munthu wochereza, buku lina linanena kuti: “Chitseko cha nyumba yake komanso cha mtima wake, chimakhala chotsegula ngakhale kwa anthu osawadziwa.” Mungachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi mbiri yanga pa nkhani yolandira alendo ndi yotani?’ (Aheb. 13:​2, 16) Munthu wochereza amagawana zimene ali nazo ndi alendo kuphatikizapo osauka komanso anthu amene amatumikira Yehova mwakhama monga oyang’anira madera ndiponso amene abwera kudzakamba nkhani kuchokera kumipingo ina.—Gen. 18:​2-8; Miy. 3:27; Mac. 16:15; Aroma 12:13. w24.11 21 ¶6

Anamwali amene anali atakonzeka aja analowa naye limodzi mʼnyumba imene munali phwando laukwati.Mat. 25:10.

Mufanizo la anamwali, Yesu anafotokoza za anamwali 10 omwe anapita kukachingamira mkwati. (Mat. 25:​1-4) Iwo ankafuna kuperekeza mkwatiyo kuphwando la ukwati wake. Yesu anafotokoza kuti anamwali 5 anali “ochenjera” pomwe 5 enawo anali “opusa.” Anamwali ochenjerawo anali okonzeka kudikira mkwatiyo ngakhale mpaka usiku. Anatenga nyale kuti asakhale mumdima ndipo anatenganso mafuta owonjezera kuti mwina mkwati angachedwe kubwera. Choncho iwo anakonzekera kuti nyale zawo zisazime. (Mat. 25:​6-10) Mkwatiyo atafika anamwali ochenjerawo analowa naye limodzi m’nyumba yaphwando. Mofanana ndi zimenezi, Akhristu odzozedwa omwe asonyeza kuti ndi okonzeka, ali tcheru komanso ndi okhulupirika mpaka kubwera kwa Khristu, adzaonedwa kuti ndi oyenera kulowa ndi mkwati, yemwe ndi Yesu, mu Ufumu wakumwamba.—Chiv. 7:​1-3. w24.09 21 ¶6

Ndinaona khamu lalikulu la anthu. . ochokera mʼdziko lililonse.—Chiv. 7:9.

Timalimbikitsidwa kugwira mwakhama ntchito yolalikira tikamaona mmene ikuthandizira anthu padziko lonse. Chaka chilichonse anthu mamiliyoni amabwera ku Chikumbutso komanso amayamba kuphunzira Baibulo. Anthu enanso masauzande ambiri amabatizidwa n’kuyamba kugwira nafe ntchito yolalikira. Sitikudziwa kuti ndi anthu ochuluka bwanji omwe angamvetsere uthenga wathu, koma tikudziwa kuti Yehova akupitiriza kusonkhanitsa khamu lalikulu lomwe lidzapulumuke pa chisautso chachikulu. (Chiv. 7:​9, 14) Mwiniwake wa munda akuonabe kuti padakali zokolola zambiri, choncho tili ndi zifukwa zabwino zotichititsa kupitiriza kulalikira. (Luka 10:2) Nthawi zonse ophunzira a Yesu ankadziwika chifukwa cha khama lawo polalikira. Anthu ataona kulimba mtima kwa atumwi polalikira, “anazindikira kuti ankayenda ndi Yesu.” (Mac. 4:13) Ifenso anthu akamaona kulimba mtima kwathu polalikira azizindikira kuti tikutsanzira Yesu. w25.03 18 ¶15; 19 ¶17-18

Inu Yehova, munthu ndi ndani kuti muzimuganizira?—Sal. 144:3.

Baibulo limasonyeza kuti Yehova amaganizira anthu amene amaoneka ngati osafunika kwa anthu ena. Mwachitsanzo, Yehova anatuma mneneri Samueli kuti akadzoze mmodzi mwa ana a Jese kuti akhale mfumu ya Isiraeli. Jese anaitana ana ake 7 kuti akakumane ndi Samueli koma sanaitane Davide, yemwe anali wamng’ono kwambiri. Koma Davideyo ndi amene Yehova anamusankha. (1 Sam. 16:​6, 7, 10-12) Yehova anaona zimene zinali mumtima mwa Davide ndipo anazindikira kuti anali munthu wokonda Mulungu. Yehova wasonyeza kale kuti amakuganizirani. Mwachitsanzo, amakupatsani malangizo ogwirizana ndi zimene mukufunikira. (Sal. 32:8) Zimenezi sizikanatheka akanakhala kuti samakudziwani bwino. (Sal. 139:1) Mukayamba kugwiritsira ntchito malangizo a Yehova n’kuona mmene akukuthandizirani, simukayikira kuti iye amakukondani. (1 Mbiri 28:9; Mac. 17:​26, 27) Yehova amaona zonse zomwe mumachita kuti muzimutumikira. Amaonanso makhalidwe abwino omwe muli nawo ndipo amafuna kuti mukhale mnzake.Yer. 17:10. w24.10 25-26 ¶7-9

Anawamvera chisoni, chifukwa anali ngati nkhosa zimene zilibe mʼbusa.—Maliko 6:34.

N’zosachita kufunsa kuti mumakonda Yehova ndipo mumafuna kutumikira ena. Koma mwina mulibe mtima wofuna kukhala mtumiki wothandiza. Ndiye kodi mungatani kuti mukhale ndi mtima wofuna kutumikira ena? Muziganizira chimwemwe chimene mungapeze chifukwa chotumikira abale ndi alongo anu. Paja Yesu anati: “Kupatsa kumatichititsa kukhala osangalala kwambiri kuposa kulandira.” (Mac. 20:35) Ndipotu izi ndi zimene iye ankachita. Iye ankasangalala chifukwa chotumikira ena. Chitsanzo ndi nkhani yopezeka pa Maliko 6:​31-34. Pa nthawiyi, Yesu ndi ophunzira ake anatopa ndipo ankapita kwaokha kuti akapume. Koma gulu la anthu linafika kumeneko mwamsanga n’kumayembekezera kuti Yesu awaphunzitse. Iye akanatha kukana kuwaphunzitsa. Ndipotu paja iye ndi ophunzira ake “analibe nthawi yoti apume ngakhalenso yoti adye chakudya.” Apo ayi, akanatha kungowaphunzitsa zochepa n’kuwauza kuti azipita. Koma chifukwa chokonda anthu, “anayamba kuwaphunzitsa” mpaka ‘nthawi inatha.’—Maliko 6:35. w24.11 16 ¶9-10

Mudzapeza mphoto chifukwa cha ntchito yanu.—2 Mbiri 15:7.

Makolo, muzilimbikitsa mwana wanu kuti azifunafuna mipata youza ena choonadi cha m’Baibulo. (Aroma 10:10) Mungayerekezere khama limene mwana wanu amafunika kuti aziuza ena zimene amakhulupirira ndi khama limene limafunika kuti munthu aphunzire kugwiritsa ntchito chida chinachake choimbira. Poyamba angafunike kuphunzira nyimbo yosavuta. Pakapita nthawi angayambe kuimba nyimbo ngakhale zovuta. Mofanana ndi zimenezi, Mkhristu wachinyamata angayambe ndi nkhani yosavuta pouza ena zimene amakhulupirira. Mwachitsanzo, iye angafunse mnzake wa kusukulu kuti: “Kodi ukudziwa kuti akatswiri opanga zinthu amatengera zinthu za m’chilengedwe? Ndikufuna ndikuonetse kavidiyo aka komwe ndi kosangalatsa.” Pambuyo pomuonetsa imodzi mwa mavidiyo akuti Kodi Zinangochitika Zokha? anganene kuti: “Kodi ndi ndani amene akuyenera kulemekezedwa pakati pa akatswiri amene amapanga zinthu potengera zinthu zam’chilengedwe ndi mwiniwake amene anapanga zinthu zachilengedwezo?” Kugwiritsa ntchito njira yosavuta imeneyi kungathandize mnzake wa kusukuluyo kukhala ndi chidwi chofuna kuphunzira zambiri. w24.12 19 ¶17-18

Uchimo unalowa mʼdziko kudzera mwa munthu mmodzi ndipo uchimowo unabweretsa imfa.—Aroma 5:12.

Kuti atipulumutse ku uchimo ndi imfa, Yehova anakonza zoti Yesu apereke dipo. Koma kodi nsembe ya munthu mmodzi wangwiro ikanapulumutsa bwanji anthu mamiliyoni ambiri? Mtumwi Paulo anafotokoza kuti: “Popeza kusamvera kwa munthu mmodziyo [Adamu] kunachititsa kuti ambiri akhale ochimwa, kumvera kwa munthu mmodziyu [Yesu] kudzachititsanso kuti ambiri akhale olungama.” (Aroma 5:19; 1 Tim. 2:6) Tingati kusamvera kwa munthu mmodzi yemwe anali wangwiro, kunachititsa kuti tikhale akapolo a uchimo ndi imfa. Choncho panafunikanso munthu mmodzi womvera yemwe ndi wangwiro kuti tipulumutsidwe. Kodi Yehova sakanatha kungolola ana omvera a Adamu kuti akhale ndi moyo wosatha? Mwina anthufe tingaganize kuti imeneyi ikanakhala njira yabwino yothetsera vutoli. Koma zimenezi si zogwirizana ndi chilungamo cha Yehova. Popeza Yehova ndi wachilungamo, sakanangolekerera kusamvera mwadala kwa Adamu. w25.01 21 ¶3-4

Tikuyenda motsogoleredwa ndi chikhulupiriro, osati motsogoleredwa ndi zooneka ndi maso.—2 Akor. 5:7.

Pa nthawi ina, mtumwi Paulo ankadziwa kuti anali atatsala pang’ono kuphedwa. Komabe ankasangalala podziwa kuti wachita zonse zimene ankafunika kuchita pa moyo wake. Poganizira zimenezi, iye ananena kuti: “Ndathamanga pa mpikisanowu mpaka pamapeto. Ndakhalabe ndi chikhulupiriro.” (2 Tim. 4:​6-8) Paulo ankasankha zochita mwanzeru pa utumiki wake ndipo sankakayikira kuti Yehova akusangalala naye. Nafenso tiyenera kumasankha zinthu mwanzeru kuti Yehova azisangalala nafe. Kodi tingachite bwanji zimenezi? Pofotokoza za iyeyo komanso Akhristu ena okhulupirika, Paulo ananena kuti: “Tikuyenda motsogoleredwa ndi chikhulupiriro, osati motsogoleredwa ndi zooneka ndi maso.” M’Baibulo, nthawi zina mawu akuti “kuyenda” amatanthauza zimene munthu amasankha kuchita pa moyo wake. Munthu yemwe amayenda motsogoleredwa ndi chikhulupiriro amadalira Yehova ndipo amasankha zinthu mogwirizana ndi zimene Yehovayo amafuna. Zimene amachita zimasonyeza kuti samakayikira kuti Mulungu adzamudalitsa, komanso kuti zinthu zidzamuyendera bwino akamatsatira malangizo a Yehova opezeka m’Mawu ake.—Sal. 119:66; Aheb. 11:6. w25.03 20 ¶1-2

Khalani munthu watsopano posintha kwambiri maganizo anu.—Aroma 12:2.

Mzimu wa Mulungu wathandiza anthu ambiri omwe poyamba anali ndi makhalidwe ngati a zinyama kuti asinthe. (Yes. 65:25) Iwo anayesetsa kusiya makhalidwe oipa omwe anali nawo kale. (Aef. 4:​22-24) Komabe anthu a Mulungu si angwiro, choncho amalakwitsabe zinthu zina. Ngakhale zili choncho, Yehova akuthandiza “anthu a mitundu yonse” kuti akhale ogwirizana ndipo zotsatira zake n’zakuti amakondana komanso ali pamtendere. (Tito 2:11) Izi ndi zodabwitsa zimene Mulungu yekha, yemwe ndi wamphamvu zonse, angakwanitse kuchita. Mawu ake amakwaniritsidwa nthawi zonse. (Yes. 55:​10, 11) Panopa paradaiso wauzimu alipo kale. Yehova wakonza ubale wapadera kwambiri. Anthu ake amakhala mwamtendere komanso motetezeka ngakhale kuti ali m’dziko lodzadza ndi chiwawa. (Sal. 72:7) Pa chifukwa chimenechi, timafuna kuthandiza anthu ambiri mmene tingathere kuti alowe m’banja lauzimuli. Tingachite zimenezi pogwira ntchito yophunzitsa anthu.—Mat. 28:​19, 20. w24.04 23 ¶13, 15

Ife tili ndi maganizo a Khristu.—1 Akor. 2:16.

Yesu ankakonda Atate wake ndi mtima wonse. Iye ankadziwa zimene Mulungu ankafuna kuti achite ndipo anali wokonzeka kuchita zinthu mogwirizana ndi zimenezo ngakhale kuti zikanachititsa kuti akumane ndi mavuto. Popeza kuti ankaganizira kwambiri zosangalatsa Atate wake, Yesu sanalole kuti chilichonse chimulepheretse kukwaniritsa cholinga chakechi. Petulo ndi atumwi anzake anali ndi mwayi wokhala ndi Yesu ndipo anaphunzira mmene Yesuyo ankaganizira. Pamene Petulo ankalemba kalata yake yoyamba youziridwa analimbikitsa Akhristu kuti adzikonzekeretse pokhala ndi maganizo amene Khristu anali nawo. (1 Pet. 4:1) Pamene Petulo ananena kuti nanunso “konzekerani,” anagwiritsa ntchito mawu omwe m’chilankhulo choyambirira amafotokoza za msilikali yemwe wanyamula zida zake pokonzekera nkhondo. Choncho Akhristu akamatsanzira mmene Yesu amaganizira, amakhala kuti atenga chida champhamvu chomwe chingawathandize kulimbana ndi uchimo komanso dziko lolamulidwa ndi Satanali.—2 Akor. 10:​3-5; Aef. 6:12. w25.03 8-9 ¶1-3

Maganizo amumtima mwa munthu ali ngati madzi akuya, koma munthu wozindikira ndi amene amawatunga.Miy. 20:5.

Kodi muyenera kudziwanso zinthu zina ziti zokhudza munthu amene muli naye pa chibwenzi? Musanafike pokondana kwambiri, mungafunike kukambirana zinthu zina zofunika monga zolinga zimene mnzanuyo ali nazo. Kodi mungatani kuti mumudziwe bwino mnzanuyo? Mungachite zimenezi pomalankhulana momasuka komanso moona mtima, kufunsa mafunso ndiponso kumvetsera. (Yak. 1:19) Kuti zimenezi zitheke, mwina mungakonze zochitira limodzi zinthu zina ngati kudyera limodzi, kukayenda kumalo opezeka anthu ambiri komanso kulalikira limodzi. Kuwonjezera pamenepo, muzikonza zochita zinthu zomwe zingakuthandizeni kudziwa mmene mnzanuyo amachitira zinthu pa nthawi zosiyanasiyana komanso akakhala ndi anthu osiyanasiyana monga anzanu ndi achibale anu. w24.05 27-28 ¶6-7

Muzitsanzira Mulungu, monga ana ake okondedwa.—Aef. 5:1.

M’tsogolomu, tidzakumana ndi mayesero amene adzafuna kuti tizidalira Yehova kuposa kale. Nkhani za m’Baibulo komanso zokhudza atumiki a Yehova a masiku ano zingatithandize kuona mmene Mulungu wasonyezera kuti ali ngati thanthwe pothandiza atumiki ake. Tiziganizira mozama nkhani zimenezi. Tikatero tiziona kuti Yehova ndi Thanthwe lathu. Komanso tidzalimbikitsa kwambiri abale ndi alongo athu. Mwachitsanzo, Yesu anapatsa Simoni dzina lakuti Kefa (limene kumasulira kwake ndi “Petulo”) ndipo limatanthauza “Mwala.” (Yoh. 1:42) Zimenezi zinasonyeza kuti iye adzalimbikitsa anthu ena mumpingo ndiponso kuwathandiza kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. Akulu mumpingo amayerekezeredwa ndi “mthunzi wa thanthwe lalikulu.” Mawu amenewa akusonyeza mmene amatetezera anthu mumpingo. (Yes. 32:2) Tonsefe, kaya ndi abale kapena alongo, tikhoza kulimbikitsa anthu mumpingo tikamatsanzira makhalidwe a Yehova. w24.06 28 ¶10-11

Yehova . . . amafuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha basi.—Deut. 4:24.

Yehova ankaona kuti mafumu omwe ankamulambira m’njira yoyenera ndi okhulupirika. Mafumu ambiri amene Yehova anawaweruza kuti anali osakhulupirika anasiya kutsatira Chilamulo cha Yehova n’kuyamba kulambira mafano. (1 Maf. 21:​25, 26; 2 Mbiri 12:1) N’chifukwa chiyani Yehova ankaona kuti nkhani yokhudza kulambira ndi yofunika kwambiri? Chifukwa chimodzi n’chakuti mafumuwa anali ndi udindo waukulu wotsogolera anthu a Mulungu kuti azimulambira m’njira yoyenera. Komanso kulambira mafano kumachititsa kuti ena azichita machimo akuluakulu komanso zopanda chilungamo. (Hos. 4:​1, 2) Kuwonjezera pamenepo, mafumuwo komanso anthuwo anali mtundu wodzipereka kwa Yehova. N’chifukwa chake Baibulo limayerekezera kulambira kwawo mafano ndi chigololo. (Yer. 3:​8, 9) Munthu amene wachita chigololo amakhala kuti walakwira kwambiri mwamuna kapena mkazi wake. Mofanana ndi zimenezi mtumiki wodzipereka wa Yehova yemwe amalambira mafano amakhala kuti wamulakwira kwambiri Yehova.—Deut. 4:23. w24.07 22-23 ¶12-15