January
Lachinayi, January 1
Pa nkhani yomvetsa zinthu khalani anthu akuluakulu.—1 Akor. 14:20.
Kubadwa kwa mwana kumakhala chimodzi mwa zinthu zosangalatsa kwambiri kwa makolo ake. Ngakhale kuti makolo amakonda kwambiri mwana wawo wakhanda, safuna kuti azingokhalabe choncho mpaka kalekale. Ndipotu angadandaule kwambiri ngati mwanayo sakukula. Mofanana ndi zimenezi, Yehova amasangalala tikayamba kutsatira Yesu, koma iye safuna kuti tizingokhala ana mwauzimu. (1 Akor. 3:1) M’malomwake amafuna kuti tikhale Akhristu aakulu mwauzimu. M’Baibulo, mawu amene anamasuliridwa kuti anthu “akuluakulu,” angatanthauzenso anthu okhwima kapena “olimba mwauzimu.” (1 Akor. 2:6) Mofanana ndi mwana amene amapitiriza kukula mpaka atakhala wamkulu, ifenso tiyenera kupitiriza kukula mwauzimu mpaka titakhala Akhristu olimba. Koma ngakhale titafika pamenepo sitiyenera kusiya kupita patsogolo.—1 Tim. 4:15. w24.04 2 ¶1, 3
Tenti yanga idzakhala pakati pawo. Ine ndidzakhala Mulungu wawo.—Ezek. 37:27.
Kodi Yehova ali ngati ndani kwa inuyo? Mwina mungayankhe kuti, ‘Yehova ndi Atate wanga, Mulungu wanga komanso mnzanga.’ Palinso mayina ena audindo omwe mungagwiritse ntchito ponena za Yehova. Komabe, kodi munayamba mwaganizirapo kuti mungakhalenso mlendo wake? Mfumu Davide anayerekezera ubwenzi womwe umakhalapo pakati pa Yehova ndi atumiki ake okhulupirika ndi ubwenzi umene umakhalapo pakati pa munthu ndi alendo amene wawaitana. Iye anafunsa kuti: “Inu Yehova, ndi ndani amene angakhale mlendo mutenti yanu? Ndi ndani amene angakhale m’phiri lanu lopatulika?” (Sal. 15:1) Mawu ouziridwa amenewa akusonyeza kuti tikhoza kukhala alendo a Yehova kapena kuti anzake. Yehova asanayambe kulenga zinthu zonse anali yekha. Koma kenako pa nthawi ina, iye analandira Mwana wake woyamba kubadwa mutenti yake yophiphiritsa. Yehova anasangalala kwambiri kulandira mlendo wakeyu. Baibulo limanena kuti Yehova “ankasangalala kwambiri” ndi Mwana wake. Nayenso mlendo wake woyambayu, ‘ankakhala wosangalala pamaso pake [Yehova] nthawi zonse.’—Miy. 8:30. w24.06 2 ¶1-3
Zadoki [anali] mnyamata wamphamvu ndi wolimba mtima.—1 Mbiri 12:28.
Yerekezerani kuti mukuona gulu la anthu oposa 340,000 omwe asonkhana kuti amuike Davide kukhala mfumu ya Isiraeli. Kwa masiku atatu, m’dera la mapiri pafupi ndi ku Heburoni kukumveka phokoso la kulankhulana kwa anthu, kuseka komanso nyimbo zotamanda. (1 Mbiri 12:39) Pagulu la anthulo pali wachinyamata wina dzina lake Zadoki yemwe sanali wodziwika kwa anthu ambiri. Koma Yehova anafuna kuti tidziwe zoti iye anali pagululi. (1 Mbiri 12:22, 26-28) Zadoki anali wansembe amene ankagwira ntchito ndi Abiyatara yemwe anali mkulu wa ansembe. Zadoki anali wamasomphenya yemwe ankatha kuzindikira zimene Mulungu akufuna ndipo anapatsidwa nzeru zapadera. (2 Sam. 15:27) Iye anali munthu wolimba mtima. M’masiku otsiriza ano, Satana akuukira kwambiri anthu a Mulungu. (1 Pet. 5:8) Tiyenera kukhala olimba mtima pamene tikuyembekezera kuti Yehova awononge Satana ndi dziko loipali. (Sal. 31:24) Tikamachita zimenezi tingatsanzire kulimba mtima kwa Zadoki. w24.07 2 ¶1-3
Zaka zonse zimene Adamu anakhala ndi moyo zinakwana 930, kenako anamwalira.—Gen. 5:5.
Yehova atalenga mwamuna ndi mkazi oyamba ankafuna kuti iwo azisangalala. Anawapatsa malo okongola okhala, mphatso ya banja komanso ntchito yosangalatsa yoti azigwira. Iwo ankafunika kubereka ana n’kudzadza dziko lonse lapansi komanso kulikonza kuti likhale lokongola ngati munda wa Edeni. Koma anangowapatsa lamulo limodzi. Ndipo anawachenjeza kuti ngati mwadala sangamvere lamulolo adzafa. Timadziwa zimene zinachitika pambuyo pake. Mngelo yemwe sankawakonda komanso yemwe sankakonda Mulungu, anawanyengerera kuti achimwe. Adamu ndi Hava anachita zomwe mngelo woipayo ankafuna. Chifukwa choti analephera kukhulupirira Atate wawo wachikondi, iwo anachimwa. Ndipotu mmene tikudziwira, zimene Yehova ananena zinachitika. Kuchokera tsiku limenelo iwo anayamba kukumana ndi zotsatirapo zake, zomwe ndi kukalamba ndipo pamapeto pake anafa.—Gen. 1:28, 29; 2:8, 9, 16-18; 3:1-6, 17-19, 24. w24.08 3 ¶3
Muzichita zimene mawu amanena.—Yak. 1:22.
Yehova ndi Mwana wake wokondedwa amafuna kuti tizisangalala. Wolemba Salimo 119:2 ananena kuti: “Osangalala ndi anthu amene amasunga zikumbutso zake, amene amamufunafuna ndi mtima wawo wonse.” Yesu ananenanso kuti: “Osangalala ndi anthu amene akumva mawu a Mulungu nʼkuwasunga.” (Luka 11:28) Monga anthu amene timalambira Yehova, timakhala osangalala tikamawerenga Mawu a Mulungu nthawi zonse ndiponso tikamayesetsa kutsatira zimene timaphunzira. (Yak. 1:22-25) Chimenechi ndi chinthu chofunika kwambiri kuti tizisangalatsa Yehova. (Mlal. 12:13) Tikamagwiritsa ntchito zimene timawerenga m’Mawu a Mulungu timakhala ndi mabanja abwino komanso timagwirizana ndi Akhristu anzathu. N’kutheka kuti inunso mwaona kale kuti zimenezi ndi zoona. Kuwonjezera pamenepo, timapewa mavuto amene anthu omwe satsatira mfundo za Yehova amakumana nawo. Timagwirizana ndi zimene Mfumu Davide inanena. Atanena za malamulo ndi zigamulo za Yehova, Davide anamaliza nyimbo yake ndi mawu akuti: “Munthu wosunga zigamulozo amapeza mphoto yaikulu.”—Sal. 19:7-11. w24.09 2 ¶1-3
Iye amachiritsa anthu osweka mtima, ndipo amamanga mabala awo.—Sal. 147:3.
Kodi Yehova amaona zimene zikuchitikira atumiki ake padzikoli? Inde. Iye amadziwa tikamasangalala kapena tikakhumudwa. (Sal. 37:18) Amasangalala akaona kuti tikuyesetsa mmene tingathere kuti tizimutumikira ngakhale pamene tili ndi nkhawa. Kuwonjezera pamenepo, iye amakhalanso wokonzeka kutithandiza komanso kutilimbikitsa. Lemba la Salimo 147:3 limati Yehova ‘amamanga mabala’ a anthu osweka mtima. Apa lembali likufotokoza mmene Yehova amasamalirira mwachikondi anthu omwe ali ndi nkhawa. Ndiye kodi tingatani kuti tizipindula ndi zimene Yehova amachita potisamalira? Taganizirani chitsanzo ichi: Dokotala waluso angachite zambiri pothandiza munthu amene wavulala kuti achire. Komabe kuti munthuyo achire, amafunika kutsatira mosamala malangizo a dokotalayo. Yehova, kudzera m’Mawu ake amalankhula ndi anthu amene ali ndi nkhawa komanso kuwapatsa malangizo ake achikondi. w24.10 6 ¶1-2
Zonsezi anazisesa padziko lapansi.—Gen. 7:23.
M’mbuyomu, mabuku athu akhala akufotokoza zimene zidzachitikire anthu omwe Yehova anawaweruza kuti ndi osalungama. Tinkanena kuti palibe chiyembekezo choti anthu amene Yehova anawawononga adzaukitsidwa. Baibulo limafotokoza nthawi zingapo pamene Yehova anapereka chiweruzo kwa anthu osalungama. Mwachitsanzo, anthu ambirimbiri anafa pa nthawi ya Chigumula. Yehova analamulanso anthu ake kuti akawononge mitundu 7 ya anthu a m’Dziko Lolonjezedwa. Pa nthawi inanso, mngelo wa Yehova anapha asilikali a Asuri 185,000, usiku umodzi. (Deut. 7:1-3; Yes. 37:36, 37) Pa nkhani zonsezi, Baibulo silifotokoza zambiri zomwe zingatipangitse kuganiza kuti Yehova anaweruza kuti anthu amenewa awonongedwe ndipo asadzaukitsidwe. Sitikudziwa mmene Yehova anaweruzira munthu aliyense payekha komanso ngati anthu omwe anaphedwawo anali ndi mwayi wophunzira za iye komanso kulapa. w24.05 3 ¶5-7
Pitirizani kugonjetsa choipa pochita chabwino.—Aroma 12:21.
Yesu ananena fanizo la mkazi wina wamasiye yemwe anapempha woweruza kuti amuthandize mwachilungamo. Nkhaniyi iyenera kuti inafika pamtima ophunzira a Yesu chifukwa chakuti pa nthawiyo anthu wamba sankachitiridwa zachilungamo. (Luka 18:1-5) Nkhaniyi ingatithandizenso chifukwa pafupifupi tonsefe tinachitiridwapo zinthu zopanda chilungamo. Masiku ano zinthu zopanda chilungamo, kusankhana mitundu komanso kuponderezana ndi zofala, choncho sitidabwa anthu ena akatichitira zopanda chilungamo. (Mlal. 5:8) Akhristufe sitimayembekezera kuti m’bale kapena mlongo angatichitire zimenezi, koma izi zikhoza kuchitika. Mosiyana ndi anthu amene amatizunza kapena kutsutsa choonadi, abale ndi alongo athu samafuna kutichitira zopanda chilungamo. Kungoti iwowo si angwiro. Tingaphunzire zambiri pa zimene Yesu anachita atachitiridwa zopanda chilungamo ndi otsutsa. Ngati timaleza mtima ndi otsutsa omwe amatichitira zopanda chilungamo, tiyeneranso kumaleza mtima ndi Akhristu anzathu. w24.11 2 ¶1-2
Kodi mitanda ya mkate yodyetsa anthu onsewa tingakaigule kuti?—Yoh. 6:5.
Kale mkate unali chakudya chomwe anthu ambiri ankadya. (Gen. 14:18; Luka 4:4) Mkate unali wofunika kwambiri moti nthawi zina Baibulo limagwiritsa ntchito mawu akuti “mkate” ponena za chakudya. (Mat. 6:11; Mac. 20:7) Pa maulendo ena awiri amene Yesu anachita zodabwitsa anagwiritsanso ntchito mkate. (Mat. 16:9, 10) Imodzi mwa nkhanizi imapezeka mu Yohane chaputala 6. Atumwi atamaliza kulalikira, anakwera boti limodzi ndi Yesu n’kupita tsidya lina la Nyanja ya Galileya kuti akapume. (Maliko 6:7, 30-32; Luka 9:10) Iwo anapita kudera lina lopanda anthu ku Betisaida. Koma pasanapite nthawi yaitali gulu la anthu linafika. Yesu sanawanyalanyaze. M’malomwake iye anayamba kuwaphunzitsa zokhudza Ufumu komanso kuchiritsa odwala. Kutayamba kuda, iwo anayamba kuganizira mmene anthuwo angapezere chakudya. N’kutheka kuti ena anali ndi chakudya chochepa koma ambiri ankafunika kupita kumidzi kukagula chakudya.—Mat. 14:15. w24.12 2 ¶1-2
Mphatso imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha kudzera mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.—Aroma 6:23.
Makolo athu oyambirira, Adamu ndi Hava, anali angwiro ndipo ankakhala m’Paradaiso. (Gen. 1:27; 2:7-9) Iwo akanatha kukhala ndi moyo wosangalala mpaka kalekale. Koma kenako zinthu zinasintha. Iwo anathamangitsidwa m’munda wa Edeni ndipo anataya mwayi wokhala ndi moyo mpaka kalekale. Ndiye kodi Adamu anasiyira chiyani ana ake? Baibulo limati: “Uchimo unalowa mʼdziko kudzera mwa munthu mmodzi [Adamu] ndipo uchimowo unabweretsa imfa. Choncho imfayo inafalikira kwa anthu onse chifukwa onse anachimwa.” (Aroma 5:12) Cholowa chomwe Adamu anatisiyira ndi uchimo, womwe umabweretsa imfa. Uchimo umenewo uli ngati ngongole yaikulu imene palibe munthu amene angathe kubweza. (Sal. 49:8) Yesu anayerekezera machimo ndi “ngongole.” (Mat. 6:12; Luka 11:4) Tikachimwa timakhala ngati tili ndi ngongole kwa Yehova. Timayenera kulipira ngongole ya machimo athu. Ngati sitingalipire ngongoleyo, ingathetsedwe pokhapokha ngati titafa.—Aroma 6:7. w25.02 2-3 ¶2-3
Ine ndachititsa kuti iwo adziwe dzina lanu.—Yoh. 17:26.
Timaona kuti ndi mwayi waukulu kuuza ena choonadi chokhudza Ufumu wa Mulungu. Koma si aliyense amene ali ndi mwayi wogwira ntchito imeneyi. Mwachitsanzo, Yesu ali padziko lapansi sanalole kuti mizimu yoipa izilalikira za iye. (Luka 4:41) Masiku ano, munthu asanayambe kulalikira ndi anthu a Yehova amafunika kukwaniritsa zinthu zofunikira. Timasonyeza kuti timayamikira mwayi umenewu tikamalalikira kulikonse komanso pa nthawi iliyonse. Mofanana ndi Yesu, cholinga chathu ndi kudzala ndi kuthirira mbewu za choonadi m’mitima ya anthu. (Mat. 13:3, 23; 1 Akor. 3:6) Potengera chitsanzo cha Yesu, gulu la Yehova limachita zonse zimene lingathe pothandiza anthu kuti adziwe dzina la Mulungu. Baibulo la Dziko Latsopano lathandiza kwambiri pa nkhaniyi pobwezeretsa dzina la Mulungu pamalo ake oyenera. Baibuloli, lonse kapena mbali yake, likupezeka m’zilankhulo zoposa 270. w24.04 9 ¶8-9
Mwamuna wake amaimirira nʼkumutamanda.—Miy. 31:28.
Amuna ena omwe akusangalala m’banja lawo amayesetsa kuti tsiku lililonse azichita chinachake chomwe chingasonyeze kuti amakonda akazi awo. (1 Yoh. 3:18) Mwamuna akhoza kusonyeza kuti amakonda mkazi wake m’njira zing’onozing’ono monga kumugwira dzanja kapena kumuhaga. Atha kumutumizira uthenga monga wakuti, “Ndakusowa” kapena kumufunsa kuti, “Zikuyenda?” Nthawi zinanso akhoza kumulembera mawu osankhidwa bwino pakhadi. Mwamuna akamachita zinthu ngati zimenezi amalemekeza mkazi wake ndipo banja lawo limakhala lolimba. Mwamuna amene amalemekeza mkazi wake amamulimbikitsa. Njira ina yolimbikitsira mkazi ndi kumuyamikira pa zonse zomwe amachita. (Akol. 3:15) Mwamuna akamayamikira mkazi wake kuchokera pansi pa mtima, mkaziyo amamva bwino. Amamva kuti ndi wotetezeka, amakondedwa komanso amalemekezedwa. w25.01 11 ¶15; 13 ¶16
Ine Yehova ndine Mulungu wanu, . . . amene ndimakutsogolerani mʼnjira imene mukuyenera kuyenda.—Yes. 48:17.
Salimo 15 limamaliza ndi mawu akuti: “Munthu aliyense amene amachita zimenezi, sadzagwedezeka.” Apa wolemba masalimoyu ankafotokoza chifukwa chake Yehova amafuna kuti tizichita zonse zimene zatchulidwa mu Salimoli. Iye amafuna kuti tizisangalala. Choncho amatipatsa malangizo omwe amatithandiza kupeza madalitso komanso kukhala otetezeka. Alendo a Yehova akuyembekezera zinthu zabwino kwambiri. Odzozedwa okhulupirika adzalandira “malo ambiri okhalamo” omwe Yesu wawakonzera kumwamba. (Yoh. 14:2) Omwe ali ndi chiyembekezo chodzakhala padziko lapansi akuyembekezera kudzaona kukwaniritsidwa kwa malonjezo omwe ali pa Chivumbulutso 21:3. Kunena zoona, timaona kuti ndi mwayi waukulu kukhala anzake a Yehova komanso alendo mutenti yake mpaka kalekale.—Sal. 15:1-5. w24.06 13 ¶19-20
M’patseni Yehova ulemerero woyenera dzina lake.—Sal. 96:8.
M’Baibulo, mawu akuti “ulemerero” angatanthauze chilichonse chimene chingapangitse winawake kuti akhale wochititsa chidwi. Yehova anasonyeza ulemerero wake wodabwitsa Aisiraeli atangomasulidwa kumene ku ukapolo ku Iguputo. Yerekezerani kuti mukuona Aisiraeli ambirimbiri atasonkhana m’mbali mwa phiri la Sinai kuti akumane ndi Mulungu wawo. Mtambo wakuda waphimba phirilo. Kenako mwadzidzidzi chivomerezi champhamvu, chokhala ngati phiri likuphulika chikugwedeza pomwe iwo aima. Komanso pali kung’anima ndi kulira kwa mabingu ndiponso kulira kogonthetsa m’khutu kwa lipenga. (Eks. 19:16-18; 24:17; Sal. 68:8) Aisiraeli ayenera kuti anachita chidwi ndi mmene Yehova anasonyezera ulemerero wake. Masiku ano timapereka ulemerero kwa Yehova tikamauza anthu zokhudza mphamvu zake komanso makhalidwe ake abwino. Timaperekanso ulemerero kwa Mulungu tikamamulemekeza chifukwa cha zimene watithandiza kuchita.—Yes. 26:12. w25.01 2 ¶2-3
Yehova ndi amene wandituma.—Num. 16:28.
Pa nthawi ina Aisiraeli ali pa ulendo wokalowa m’Dziko Lolonjezedwa, amuna ena otchuka ankatsutsa Mose komanso udindo umene Yehova anamupatsa. Iwo ananena kuti: “Gulu lonseli [osati Mose yekha] ndi loyera, ndipo Yehova ali pakati pawo.” (Num. 16:1-3) N’zoona kuti Mulungu ankaona kuti ‘gulu lonselo’ linali loyera, koma Yehova anali atasankha Mose kuti azitsogolera anthu ake. Potsutsana ndi Mose, anthu oukirawa ankatsutsana ndi Yehova. M’malo moganizira zimene Yehova ankafuna, iwo ankaganizira kwambiri zimene iwowo ankafuna. Ankafuna kuti akhale ndi mphamvu zambiri komanso kutchuka. Mulungu anapha anthu amene ankatsogolera pa kuukirako komanso anthu masauzande ambiri amene anali kumbali yawo. (Num. 16:30-35, 41, 49) Masiku anonso, timadziwa kuti Yehova sasangalala ndi anthu amene salemekeza malangizo ochokera kugulu lake. w24.07 11 ¶11
Masomphenyawa akudikira nthawi yake yoikidwiratu.—Hab. 2:3.
Tikukhala m’nthawi imene anthu ambiri amakana komanso kunyoza chenjezo la m’Baibulo lonena za mapeto a dziko loipali. (2 Pet. 3:3, 4) Ngakhale kuti pali zambiri zimene sitikuzidziwa, tiyenera kukhulupirira kwambiri kuti mapeto adzafika pa nthawi yoyenera komanso kuti Yehova adzatisamalira. Tiyeneranso kumakhulupirira kwambiri “kapolo wokhulupirika komanso wanzeru,” amene Yehova akumugwiritsa ntchito potipatsa malangizo masiku ano. (Mat. 24:45) Chisautso chachikulu chikadzayamba tingadzalandire malangizo otithandiza kuti tipulumuke. Panopa m’pamene tiyenera kumakhulupirira kwambiri malangizo amene anthu omwe akutsogolera gulu la Yehova amatipatsa. Ngati panopa zimativuta kuwamvera, tisamayembekezere kuti tidzawakhulupirira komanso kuwamvera pa nthawi ya chisautso chachikulu. w24.09 11 ¶11-12
Muzindikire chifuniro cha Mulungu, chabwino, chovomerezeka ndi changwiro.—Aroma 12:2.
Makolo a Chikhristu amazindikira kuti kukhulupirira Mulungu si zimene mwana amatengera pobadwa. Pakapita nthawi, iye akhoza kumadzifunsa mafunso ngati awa: ‘Ndingadziwe bwanji kuti kuli Mulungu? Kodi zimene Baibulo limanena ndi zoona?’ Ndipotu Baibulo limatilimbikitsa kuti ‘tizigwiritsa ntchito luso la kuganiza,’ komanso ‘tizifufuza zinthu zonse nʼkutsimikizira.’ (Aroma 12:1; 1 Ates. 5:21) Ndiye kodi mungathandize bwanji mwana wanu kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba? Muzithandiza mwana wanu kupeza umboni wotsimikizira kuti zimene Baibulo limaphunzitsa ndi zoona. Mwana wanu akamafunsa mafunso muzipezerapo mwayi womuthandiza mmene angapezere mayankho pogwiritsa ntchito zinthu zofufuzira monga Watch Tower Publications Index komanso Buku la Mboni za Yehova Lofufuzira Nkhani. M’buku lofufuzira nkhanili, pansi pa mutu wakuti “Baibulo,” angayang’ane pa kamutu kakuti “Kuuziridwa ndi Mulungu” kuti apeze umboni wakuti Baibulo ndi “Mawu a Mulungu” osati chabe buku labwino lolembedwa ndi anthu.—1 Ates. 2:13. w24.12 14-15 ¶4-5
[Zinthu zimenezi] uziphunzitse kwa anthu okhulupirika ndipo nawonso adzakhala oyenerera kuphunzitsa ena.—2 Tim. 2:2.
Kodi akulu angatsanzire bwanji Yesu? Iwo ayenera kuphunzitsa amuna kuphatikizapo achinyamata kuti adzakhale ndi maudindo aakulu. Akulu samayembekezera kuti amene akuwaphunzitsawo sazilakwitsa kalikonse. Iwo ayenera kupereka malangizo kwa achinyamata kuti adziwe zambiri, akhale odzichepetsa, okhulupirika komanso ofunitsitsa kutumikira ena. (1 Tim. 3:1; 1 Pet. 5:5) Yesu anapatsa ophunzira ake ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa anthu. Ophunzirawo ayenera kuti ankaona kuti sangakwanitse kugwira ntchitoyo. Koma Yesu sankakayikira kuti iwo akwanitsa ndipo anawauza zimenezo. Yesu anasonyeza kuti amawakhulupirira kwambiri powauza kuti: “Mofanana ndi mmene Atate ananditumira, inenso ndikukutumani.”—Yoh. 20:21. w24.10 16 ¶15; 17 ¶17
Davide . . . , munthu wapamtima panga.—Mac. 13:22.
Davide anali mfumu yabwino komanso yokhulupirika kwa Yehova. Iye a nali woimba, wandakatulo, msilikali komanso mneneri. Davide anakumana ndi mayesero ambiri. Kwa zaka zambiri iye ankakhala moyo wothawathawa pomwe Mfumu Sauli inkafuna kumupha. Atakhala mfumu, Davide anathawanso pamene mwana wake Abisalomu ankafuna kumulanda ufumu. Ngakhale kuti anakumana ndi mavuto amenewa ndiponso ankalakwitsa zinthu zina, Davide anakhalabe wokhulupirika kwa Mulungu kwa moyo wake wonse. Yehova ananena kuti Davide anali “munthu wapamtima [pake].” Choncho malangizo a Davide ndi othandiza kwambiri. (1 Maf. 15:5) Taganizirani malangizo omwe Davide anapereka kwa mwana wake Solomo yemwe anadzakhala mfumu m’malo mwake. Yehova anasankha Solomo kuti apitirize kulimbikitsa kulambira koyera komanso kuti amange kachisi yemwe akanalemekeza Mulungu. (1 Mbiri 22:5) Pogwira ntchitoyi, Solomo akanakumana ndi mavuto. Ndiye kodi Davide anamupatsa malangizo otani? Davide anauza mwana wake kuti ngati angamvere Yehova, zinthu zidzamuyendera bwino.—1 Maf. 2:2, 3. w24.11 10 ¶9-11
Lola kuti Yehova akutsogolere panjira yako, uzimudalira ndipo iye adzakuthandiza.—Sal. 37:5.
Mwamuna amene amazunza kapena kulankhula mwachipongwe mkazi wake ayenera kuchita zinthu zina kuti akonze ubwenzi wake ndi Yehova komanso ndi mkaziyo. Choyamba, iye ayenera kuzindikira kuti ali ndi vuto lalikulu. Palibe chilichonse chimene chimabisika kwa Yehova. (Sal. 44:21; Mlal. 12:14; Aheb. 4:13) Chachiwiri, iye ayenera kusiya kuzunza mkazi wake ndiponso kusinthiratu khalidwe lake. (Miy. 28:13) Chachitatu, ayenera kupepesa mkazi wake komanso kupempha Yehova kuti amukhululukire. (Mac. 3:19) Ayeneranso kupempha Yehova kuti amuthandize kukhala ndi mtima wofuna kusintha komanso kuti akhale wodziletsa pa zimene amaganiza, kulankhula ndiponso kuchita. (Sal. 51:10-12; 2 Akor. 10:5; Afil. 2:13) Cha 4, iye ayenera kuchita zinthu mogwirizana ndi mapemphero ake podana ndi zachiwawa zilizonse komanso mawu achipongwe. (Sal. 97:10) Cha 5, ayenera kupempha thandizo kwa abusa achikondi mumpingo. (Yak. 5:14-16) Cha 6, iye ayenera kukhala ndi pulani yomuthandiza kuti asadzayambirenso khalidwe loipalo. w25.01 11 ¶14
Ukuchedweranji? Nyamuka ubatizidwe.—Mac. 22:16.
Kodi mumakonda Yehova Mulungu yemwe amakupatsani mphatso iliyonse yabwino, kuphatikizapo moyo? Kodi mumafuna kumusonyeza kuti mumamukonda? Njira yabwino imene mungachitire zimenezo ndi kudzipereka kwa iye n’kusonyeza kwa ena kuti munadzipereka pobatizidwa m’madzi. Mukachita zimenezo mumasonyeza kuti mwalowa m’banja la Yehova. Zotsatira zake n’zakuti Yehova yemwe ndi Atate wanu komanso mnzanu, adzakutsogolerani komanso kukusamalirani chifukwa ndinu wake. (Sal. 73:24; Yes. 43:1, 2) Kudzipereka komanso kubatizidwa kumakupatsaninso mwayi wokhala ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wosatha. (1 Pet. 3:21) Kodi pali chinachake chomwe chikukulepheretsani kubatizidwa? Ngati ndi choncho, dziwani kuti simuli nokha. Pali anthu enanso ambiri omwe ankafunika kusintha khalidwe ndi kaganizidwe kawo kuti ayenerere kubatizidwa. Panopa amatumikira Yehova mwakhama komanso mosangalala. w25.03 2 ¶1-2
Inu mumakhululuka ndi mtima wonse.—Sal. 130:4.
M’Baibulo machimo amawayerekezera ndi katundu wolemera. Pofotokoza za machimo ake Mfumu Davide anati: “Zolakwa zanga zakwera kupitirira mutu wanga. Sindingathe kuzisenza chifukwa zikulemera kwambiri ngati katundu wolemera.” (Sal. 38:4) Koma Yehova amakhululukira anthu amene alapa. (Sal. 25:18; 32:5) Mawu a Chiheberi amene anawamasulira kuti “kukhululuka” angatanthauze “kuchotsa” kapena “kunyamula.” Choncho Yehova ali ngati munthu wamphamvu yemwe mophiphiritsa amatichotsera machimo omwe amalemera paphewa lathu. Fanizo lina limasonyeza mmene Yehova amanyamulira machimo athu n’kukawasiya kutali ndi ife. Lemba la Salimo 103:12, limatiuza kuti: “Mofanana ndi mmene kotulukira dzuwa kwatalikirana ndi kolowera dzuwa, Mulungu waikanso zolakwa zathu kutali ndi ife.” Kum’mawa ndi kotalikirana kwambiri ndi kumadzulo. Malo awiriwa sangakumane. Zimenezi zikutanthauza kuti Yehova amaika machimo athu kutali kwambiri ndi ife. Zimenezi zikutitsimikizira kuti Yehova amatikhululukira ndi mtima wonse. w25.02 9 ¶5-6
Mukamapereka mphatso zachifundo, musamalize lipenga.—Mat. 6:2.
Yesu atabwerera kumwamba, mtumwi Petulo anachita chozizwitsa pomwe anachiritsa munthu yemwe anabadwa ali wolumala. (Mac 1:8, 9; 3:2, 6-8) Zimene zinachitikazi zinachititsa kuti anthu ambiri asonkhane pamalowo. (Mac 3:11) Kodi Petulo akanasankha kuti ulemerero upite kwa iyeyo poganizira kuti anakulira m’chikhalidwe chomwe chimaona kuti kutchuka ndi udindo n’zofunika kwambiri? Ayi, modzichepetsa Petulo sanalole kutamandidwa. M’malomwake anapereka ulemerero kwa Yehova ndi Yesu ponena kuti: “M’dzina [la Yesu] komanso chifukwa choti timakhulupirira dzina lakelo, munthu amene mukumuona ndiponso kumudziwayu wachira.” (Mac 3:12-16) Tingatengere chitsanzo cha Petulo pokhala odzichepetsa. Timachitira ena zabwino chifukwa chakuti timakonda Yehova ndi anthu, osati chifukwa chakuti timafuna kuti ena atione. Timasonyeza kuti ndife odzichepetsadi ngati timasangalala potumikira Yehova ndi abale athu, ngakhale ena asamaone zimene tikuchita.—Mat. 6:1-4. w25.03 10-11 ¶11-12
Nthawi zonse uzisamala ndi zimene umachita komanso zimene umaphunzitsa.—1 Tim. 4:16.
Kukonda Yehova komanso anzathu kungatichititse kuti tizikonda kwambiri ntchito yolalikira. (Mat. 22:37-39) Tangoganizirani mmene Yehova amasangalalira akationa tikugwira ntchitoyi komanso mmene anthu amasangalalira akayamba kuphunzira Baibulo. Muzikumbukiranso kuti anthu amene amvetsera uthengawu n’kuyamba kutumikira Yehova, adzapulumuka. (Yoh. 6:40) Kodi simungathe kuchoka pakhomo pazifukwa zina? Ngati ndi choncho, ganizirani zimene mungachite kuti musonyeze kuti mumakonda Yehova komanso anthu. Pa nthawi ya mliri wa COVID-19, Samuel ndi Dania sankachoka pakhomo. Pa nthawi yovuta yonseyi, iwo ankalalikira pogwiritsa ntchito telefoni, makalata ndiponso ankachititsa maphunziro a Baibulo pa Zoom. Ngakhale kuti Samuel ndi Dania sankatha kuchita zambiri ngati kale, ankayesetsa kuchita zomwe angathe ndipo ankasangalala. w24.04 18 ¶15-16
Kodi ndi ndani amene angapeze mkazi wamakhalidwe abwino? Ndi wamtengo wapatali kuposa miyala ya korali.—Miy. 31:10.
Ngakhale kuti ukwati si umene umapangitsa munthu kuti akhale wosangalala, Akhristu ambiri omwe sali pa banja, achikulire ndi achichepere omwe, amafuna kudzapeza munthu wokwatirana naye. Komabe musanayambe chibwenzi, muyenera kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova, kudzidziwa bwino komanso kukhala wokonzeka kusamalira banja. (1 Akor. 7:36) Ndi bwino kudziwa makhalidwe a munthu amene mukufuna musanayambe chibwenzi. Kupanda kutero, mukhoza kusiya munthu amene ndi woyenerera n’kuyamba chibwenzi ndi munthu amene si woyenerera kwa inu. N’zoona kuti munthu aliyense amene mukufuna kukwatirana naye, ayenera kukhala Mkhristu wobatizidwa. (1 Akor. 7:39) Koma si Mkhristu aliyense wobatizidwa yemwe angakhale wokuyenerani. Choncho mungachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi zolinga zanga ndi zotani? Kodi ndi makhalidwe ati amene ndimaona kuti ndi ofunika kwa munthu amene ndikufuna kudzakwatirana naye? Kodi zimene ndimayembekezera n’zotheka?’ w24.05 20 ¶1; 21 ¶3
Muzikomerana mtima.—Aef. 4:32.
Ngati muli pa chibwenzi, kodi mungatani ngati nthawi zambiri pamakhala mavuto komanso kusagwirizana? Kodi zimenezi zingasonyeze kuti si inu oyenererana? Osati kwenikweni. Anthu onse omwe ali pa chibwenzi kapena pa banja, nthawi zina amasemphana maganizo. Koma ngati anthuwo amalolerana komanso kulemekezana akhozabe kukhala ndi banja lolimba. Choncho zimene mumachita pothetsa mavuto panopa zingakuthandizeni kudziwa ngati mudzakhale ndi banja labwino kapena ayi. Muzidzifunsa kuti: ‘Kodi pakakhala vuto timakambirana modekha komanso mwaulemu? Kodi timavomereza mosavuta zinthu zomwe sitichita bwino n’kumayesetsa kuzikonza? Kodi timafulumira kupepesa, kulolera komanso kukhululuka?’ (Aef. 4:31) Komabe ngati pa chibwenzi nthawi zambiri simugwirizana ndipo mumangokhalira kukangana, n’zokayikitsa kuti zinthu zingadzasinthe mukadzakwatirana. Ngati mwazindikira kuti munthuyo si wokuyenerani, kuthetsa chibwenzicho kungakhale kothandiza kwa nonsenu. w24.05 29 ¶12
Atamandike Yehova Thanthwe langa, amene amaphunzitsa manja anga kumenya nkhondo.—Sal 144:1.
Tikhoza kukhala chitsanzo chabwino kwa anthu ena ngati sitisintha pochita zoyenera ndiponso kutsatira mfundo za m’Baibulo posankha zochita. Tikamayesetsa kulimbitsa chikhulupiriro chathu komanso kudziwa zinthu zambiri, timakhazikika m’choonadi. Sitivutika kusankha zochita ndipo sititengeka mosavuta ndi ziphunzitso zabodza komanso maganizo a m’dzikoli. (Aef. 4:14; Yak. 1:6-8) Tingathenso kuthandiza anthu amene akukumana ndi mayesero. (1 Ates. 3:2, 3) Akulu ayenera kukhala osachita zinthu mopitirira malire, oganiza bwino, ochita zinthu mwadongosolo ndiponso ololera. Amuna amenewa amathandiza anthu mumpingo kukhala odekha, komanso kukhulupirira kwambiri Yehova ‘pogwira mwamphamvu mawu okhulupirika.’ (Tito 1:9; 1 Tim. 3:1-3) Chitsanzo cha akulu komanso maulendo awo aubusa, zimathandiza ofalitsa kuti nthawi zonse azipezeka pamisonkhano, azilowa mu utumiki komanso aziphunzira paokha. Abale ndi alongo akakumana ndi mavuto amene akuwadetsa nkhawa, akulu ayenera kuwathandiza kuti aziganizira kwambiri za Yehova ndiponso zolinga zake. w24.06 31 ¶16-18
Lapani, chifukwa Ufumu wakumwamba wayandikira.—Mat. 4:17.
Ali padziko lapansi Yesu anaphunzitsa anthu kuti Atate wake ndi wokonzeka kutikhululukira tikachimwa. Taganizirani za fanizo la mwana wolowerera. Mwanayo anasankha kuchoka pakhomo pa makolo ake n’kumakachita zoipa. Koma pambuyo pake “nzeru zitamubwerera,” anabwerera kwawo. Ndiye kodi bambo ake anatani? Yesu ananena kuti mwanayo “ali chapatali ndithu, bambo akewo anamuona ndipo . . . anamuthamangira nʼkumukumbatira ndipo anamukisa mwachikondi.” Mwanayo anapempha bambo akewo kuti amutenge ngati wantchito wawo, koma bambowo anamutchula kuti “mwana wangayu,” kusonyeza kuti ankamuonabe kuti ndi mwana wawo. Bambowo anati: “Anatayika koma wapezeka.” (Luka 15:11-32) Mosakayikira Yesu asanabwere padzikoli, ankaona Atate wake akusonyeza chifundo kwa anthu olapa ambirimbiri. Fanizo la Yesuli limatilimbikitsa ndipo limatitsimikizira kuti Atate wathu Yehova ndi wachifundo. w24.08 11 ¶11-12
Khalani oganiza bwino.—1 Pet. 4:7.
Mkhristu woganiza bwino amayesetsa kusankha zochita potengera maganizo a Yehova. Mkhristu wotereyu amadziwa kuti kukhala pa ubwenzi ndi Yehova, n’kofunika kwambiri kuposa chilichonse. Iye sayenera kudziganizira kuposa mmene ayenera kudziganizirira, chifukwa amadziwa kuti sakudziwa zonse. Ndipo amasonyeza kuti amadalira Mulungu popemphera kwa iye nthawi zonse. Timazindikira kuti tiyenera kumapemphera kwa Yehova kuti azitithandiza, ngakhale zitakhala kuti tili ndi maluso enaake apadera. Timapempheranso kwa Yehova makamaka pamene tikufunika kusankha zinthu zofunika kwambiri ndipo timakhulupirira kuti iye akudziwa zomwe ndi zabwino kwambiri kwa ife. Timayamikira kwambiri kuti Yehova anatilenga m’njira imene tingathe kutsanzira makhalidwe ake. (Gen. 1:26) N’zoona kuti sitingathe kumutsanzira ndendende.—Yes. 55:9. w25.03 11 ¶13; 13 ¶17-18
[Chikondi] chimayembekezera zinthu zonse komanso chimapirira zinthu zonse.—1 Akor. 13:7.
Tizipewa kukayikira zolinga za ena. Ngati wina sanasonyeze kuyamikira zimene tachita, tingadzifunse kuti: ‘Kodi ndi wosayamikadi, kapena wangoiwala kuyamikira?’ N’kutheka kuti pali zimene zachititsa kuti asayamikire m’njira imene timaganizira. Ena amakhala akuyamikira mumtima koma amalephera kusonyeza kuyamikirako. Ena angamachite manyazi akathandizidwa makamaka ngati m’mbuyomo iwowo ndi amene ankathandiza ena. Kaya zinthu zili bwanji, chikondi ndi chimene chingatithandize kuti tisamakayikire zolinga za Akhristu anzathu n’kupitirizabe kukhala osangalala. (Aef. 4:2) Tizikhala oleza mtima. Pa nkhani ya kuwolowa manja, Mfumu Solomo inalemba kuti: “Ponya mkate wako pamadzi chifukwa pakapita masiku ambiri udzaupezanso.” (Mlal. 11:1) Lembali likusonyeza kuti anthu ena akhoza kuyamikira zimene tawachitira patapita nthawi yaitali, kapena kuti “masiku ambiri.” w24.09 30 ¶18-19
Anthu amene ali ndi chizolowezi chochita tchimo, uziwadzudzula pamaso pa onse kuti ena onsewo akhale ndi mantha.—1 Tim. 5:20.
Nthawi zina chilengezo chimaperekedwa mumpingo chonena kuti munthu wadzudzulidwa. Zikatero tingathe kupitiriza kuchita naye zinthu podziwa kuti analapa ndipo anasiya zoipa zimene ankachita. Iye amakhalabe mbali ya mpingo ndipo amafunika kulimbikitsidwa pocheza ndi Akhristu anzake. (Aheb. 10:24, 25) Koma umu si mmene zimakhalira munthu akachotsedwa mumpingo. Timasiya kugwirizana naye “ngakhale kudya naye munthu wotereyu.” (1 Akor. 5:11) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti tizimunyalanyaziratu? Ayi. N’zoona kuti sitingamacheze naye. Koma Akhristu akhoza kugwiritsa ntchito chikumbumtima chawo posankha kuti aitanire munthu amene wachotsedwa kumisonkhano makamaka ngati wochotsedwayo ndi wachibale kapena anali mnzawo. w24.08 30 ¶13-14

