Yesaya 49:1-26

  • Ntchito ya mtumiki wa Yehova (1-12)

    • Kuwala kwa mitundu ya anthu (6)

  • Uthenga wotonthoza wopita kwa Isiraeli (13-26)

49  Ndimvereni zilumba inu,Ndipo mvetserani, inu mitundu yakutali.+ Yehova anandiitana ndisanabadwe.*+ Kuyambira nthawi imene ndinali mʼmimba mwa mayi anga, anatchula dzina langa.   Iye anachititsa kuti mʼkamwa mwanga mukhale ngati lupanga lakuthwa.Wandibisa mumthunzi wa dzanja lake.+ Anandisandutsa muvi wonola bwino.Anandibisa mʼkachikwama kake koikamo mivi.   Anandiuza kuti: “Iwe Isiraeli ndiwe mtumiki wanga.+Kudzera mwa iwe ndidzaonetsa ulemerero wanga.”+   Koma ine ndinati: “Ndangovutika pachabe. Mphamvu zanga zangopita pachabe, pa zinthu zopanda pake. Ndithu, Yehova ndi amene amandiweruza,*Ndipo Mulungu wanga ndi amene adzandipatse malipiro anga.”*+   Ndiyeno Yehova amene anandipanga ndili mʼmimba kuti ndikhale mtumiki wake,Wandiuza kuti nditenge Yakobo nʼkumubwezera kwa iye,Nʼcholinga choti Isiraeli asonkhanitsidwe kwa iye.+ Ine ndidzalemekezedwa pamaso pa YehovaNdipo Mulungu wanga adzakhala mphamvu yanga.   Ndiyeno iye anati: “Sikuti wangokhala mtumiki wangaKuti ubwezeretse mafuko a YakoboNdiponso kuti Aisiraeli amene ali otetezeka uwabwezere kwawo. Koma ndakuperekanso kuti ukhale kuwala kwa anthu a mitundu ina,+Kuti chipulumutso changa chifike kumalekezero a dziko lapansi.”+  Yehova, Wowombola Isiraeli, Woyera wake,+ wauza amene amanyozedwa kwambiri,+ amene mtundu wa anthu umadana naye, mtumiki wa olamulira kuti: “Mafumu adzaona nʼkuimirira,Ndipo akalonga adzagwada pansiChifukwa cha Yehova yemwe ndi wokhulupirika,+Woyera wa Isiraeli, amene wakusankha.”+   Yehova wanena kuti: “Pa nthawi yosonyeza kukoma mtima kwanga, ndinakuyankha.+Ndipo pa tsiku la chipulumutso ndinakuthandiza.+Ndinkakuteteza kuti ndikupereke ngati pangano kwa anthu,+Kuti ndikonzenso dzikolo,Kuti anthuwo atengenso cholowa chawo chimene chinali bwinja,+   Kuti ndiuze akaidi kuti, ‘Tulukani!’+ Ndiponso amene ali mumdima+ kuti, ‘Bwerani poyera kuti anthu akuoneni!’ Iwo adzadya msipu mʼmphepete mwa msewu,Ndipo mʼmphepete mwa njira zonse zimene zimadutsidwadutsidwa* mudzakhala malo awo odyeramo msipu. 10  Iwo sadzakhala ndi njala ndipo sadzamva ludzu,+Komanso sadzamva kutentha kapena kupsa ndi dzuwa.+ Chifukwa amene amawachitira chifundo adzawatsogolera+Ndipo adzapita nawo kumene kuli akasupe amadzi.+ 11  Ndidzachititsa kuti mapiri anga onse akhale njira,Ndipo misewu yanga yonse idzakhala pamalo okwera.+ 12  Taonani! Anthu akuchokera kutali,+Ena akuchokera kumpoto ndi kumadzulo.Komanso ena akuchokera kudziko la Sinimu.”+ 13  Fuulani mosangalala kumwamba inu ndipo sangalala iwe dziko lapansi.+ Mapiri asangalale ndipo afuule mosangalala.+ Chifukwa Yehova watonthoza anthu ake+Ndipo wachitira chifundo anthu ake ovutika.+ 14  Koma Ziyoni ankangonena kuti: “Yehova wandisiya+ ndipo Yehova wandiiwala.”+ 15  Kodi mayi angaiwale mwana wake woyamwaKapena kulephera kuchitira chifundo mwana wochokera mʼmimba mwake? Ngakhale amayi amenewa ataiwala, ine sindingakuiwale.+ 16  Taona! Ndalemba dzina lako mʼmanja mwanga. Makoma ako ali pamaso panga nthawi zonse. 17  Ana ako abwerera mofulumira. Anthu amene anakugwetsa nʼkukuwononga adzachoka kwa iwe. 18  Kweza maso ako uone zonse zimene zikuchitika mokuzungulira. Onse akusonkhana pamodzi.+ Akubwera kwa iwe. Yehova wanena kuti: “Pali ine Mulungu wamoyo,Onsewo udzadzikongoletsa nawo ngati zokongoletsera,Ndipo udzawavala ngati ndiwe mkwatibwi. 19  Ngakhale kuti malo ako anawonongedwa komanso kusakazidwa ndipo dziko lako linali mabwinja,+Tsopano anthu amene adzakhale mmenemo malo adzawachepera moti adzakhala mopanikizana,+Ndipo anthu amene anakumeza+ adzakhala kutali.+ 20  Ana ako amene unabereka ana ena onse atamwalira, adzakuuza kuti,‘Malowa atichepera. Tipezereni malo oti tizikhalamo.’+ 21  Ndipo mumtima mwako udzanena kuti,‘Kodi bambo amene wandiberekera anawa ndi ndani,Popeza ine ndine mayi woferedwa ana ndiponso amene anasiya kubereka,Mayi amene anatengedwa kupita kudziko lina kuti akakhale mkaidi? Ndi ndani amene walera ana amenewa?+ Inetu ndinangosiyidwa ndekhandekha,+Ndiye ana amenewa achokera kuti?’”+ 22  Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Taona! Ineyo ndidzakwezera dzanja langa mitundu ya anthu,Ndipo anthu a mitundu ina ndidzawakwezera chizindikiro.+ Iwo adzakubweretsera ana ako aamuna atawanyamula mʼmanja,*Ndipo ana ako aakazi adzawanyamula paphewa.+ 23  Mafumu adzakhala okusamalira,+Ndipo ana awo aakazi adzakhala okuyamwitsira ana ako. Iwo adzakugwadira mpaka nkhope zawo pansi+Ndipo adzanyambita fumbi lakumapazi ako.+Choncho iwe udzadziwa kuti ine ndine Yehova.Anthu amene amandikhulupirira sadzachita manyazi.”+ 24  Kodi anthu amene agwidwa kale angalandidwe mʼmanja mwa munthu wamphamvu,Kapena kodi anthu amene agwidwa ndi wolamulira wankhanza angapulumutsidwe? 25  Koma Yehova akunena kuti: “Ngakhale anthu amene agwidwa ndi munthu wamphamvu adzalandidwa,+Ndipo amene anagwidwa ndi wolamulira wankhanza adzapulumutsidwa.+ Ndidzalimbana ndi aliyense amene akulimbana nawe,+Ndipo ana ako ndidzawapulumutsa. 26  Amene akukuzunza ndidzawachititsa kuti adye mnofu wawo womwe,Ndipo adzaledzera ndi magazi awo omwe ngati kuti amwa vinyo wotsekemera. Anthu onse adzadziwa kuti ine ndine Yehova,+Mpulumutsi wako+ ndiponso Wokuwombola,+Mulungu Wamphamvu wa Yakobo.”+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “ndili mʼmimba.”
Kapena kuti, “Yehova adzandichitira chilungamo.”
Kapena kuti, “mphoto yanga.”
Mabaibulo ena amati, “Ndipo mʼmapiri onse opanda kanthu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “pachifuwa.”