Yesaya 19:1-25

  • Uthenga wokhudza Iguputo (1-15)

  • Aiguputo adzadziwa Yehova (16-25)

    • Mu Iguputo mudzakhala guwa lansembe la Yehova (19)

19  Uwu ndi uthenga wokhudza Iguputo:+ Taonani! Yehova wakwera mtambo wothamanga ndipo akubwera mu Iguputo. Milungu yopanda pake ya ku Iguputo idzanjenjemera pamaso pake,+Ndipo mitima ya anthu a ku Iguputo idzachita mantha kwambiri.   “Ndidzachititsa kuti Aiguputo ayambane ndi Aiguputo anzawo.Ndipo azidzamenyana okhaokhaAliyense adzamenyana ndi mʼbale wake komanso munthu woyandikana naye.Mzinda udzamenyana ndi mzinda unzake ndipo ufumu udzamenyana ndi ufumu unzake.   Anthu a mu Iguputo adzadabwa kwambiriNdipo ine ndidzasokoneza mapulani awo.+ Iwo adzafunsira kwa milungu yopanda pake,Kwa anthu amatsenga, kwa olankhula ndi mizimu ndiponso kwa olosera zamʼtsogolo.+   Ndidzapereka Iguputo mʼmanja mwa mbuye wankhanzaNdipo mfumu yankhanza idzawalamulira,”+ akutero Ambuye woona, Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.   Madzi amʼnyanja adzauma,Mtsinje udzakhala wopanda madzi ndipo udzauma.+   Mitsinje idzanunkha.Ngalande za ku Iguputo zochokera mumtsinje wa Nailo zidzaphwa ndipo zidzauma. Bango ndi mlulu* zidzawola.+   Zomera zamʼmphepete mwa mtsinje wa Nailo, kumene mtsinje wa Nailo wakathera,Komanso malo onse amʼmphepete mwa mtsinjewo odzalidwa mbewu,+ adzauma.+ Zomera zamʼmphepete mwa mtsinjewo zidzauma ndipo zidzauluzika ndi mphepo.   Asodzi adzalira,Anthu oponya mbedza mumtsinje wa Nailo adzalira,Ndipo chiwerengero cha anthu amene amaponya maukonde awo mʼmadzi chidzachepa.   Anthu amene amagwiritsira ntchito fulakesi* wopalapala pa ntchito yawo+Komanso anthu owomba nsalu* zoyera adzachititsidwa manyazi. 10  Anthu ake owomba nsalu adzavutika maganizo.Anthu onse aganyu adzamva chisoni. 11  Akalonga a ku Zowani+ ndi opusa. Alangizi anzeru kwambiri a Farao, amapereka malangizo osathandiza.+ Koma zoona mungamuuze Farao kuti: “Ine ndine mbadwa ya anthu anzeru,Ndine mbadwa ya mafumu akale”? 12  Ndiye kodi anthu ako anzeruwo ali kuti?+ Akuuze, ngati akudziwa zimene Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wakonza zokhudza Iguputo. 13  Akalonga a ku Zowani achita zopusa.Akalonga a ku Nofi*+ apusitsidwa.Atsogoleri a mafuko ake asocheretsa Iguputo. 14  Yehova waika mzimu wachisokonezo mʼdzikolo.+Atsogoleri awo asocheretsa Iguputo pa chilichonse chimene akuchita,Ngati munthu woledzera amene akuterereka mʼmasanzi ake. 15  Ndipo Iguputo sadzakhala ndi ntchito iliyonse yoti achite.Sadzakhala ndi ntchito yoti mutu kapena mchira komanso mphukira ndi udzu* zichite. 16  Pa tsiku limenelo Aiguputo adzakhala ngati akazi ndipo adzanjenjemera ndi kuchita mantha, chifukwa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba adzatambasula dzanja loopsa kuti awapatse chilango.+ 17  Dziko la Yuda lidzakhala chinthu chochititsa mantha kwa Iguputo. Iwo akadzangomva wina akutchula dzikolo, adzachita mantha chifukwa cha zimene Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wasakha kuti awachitire.+ 18  Pa tsiku limenelo padzakhala mizinda 5 mʼdziko la Iguputo yolankhula chilankhulo cha ku Kanani+ ndiponso yolumbira kuti idzakhala yokhulupirika kwa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. Mzinda umodzi udzatchedwa Mzinda wa Chiwonongeko. 19  Pa tsiku limenelo, pakatikati pa dziko la Iguputo padzakhala guwa lansembe la Yehova, ndipo mʼmalire mwake mudzakhala chipilala cha Yehova. 20  Zimenezi zidzakhala chizindikiro ndi umboni kwa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba mʼdziko la Iguputo. Iwo adzalirira Yehova chifukwa cha anthu amene akuwapondereza, ndipo iye adzawatumizira mpulumutsi wamkulu amene adzawapulumutse. 21  Yehova adzadziwika bwino kwa Aiguputo, ndipo Aiguputowo adzamudziwa Yehova pa tsiku limenelo. Iwo adzapereka nsembe ndi mphatso ndipo adzachita lonjezo kwa Yehova nʼkulikwaniritsa. 22  Yehova adzalanga Iguputo.+ Adzamulanga kenako nʼkumuchiritsa. Iwo adzabwerera kwa Yehova ndipo iye adzamva kuchonderera kwawo nʼkuwachiritsa. 23  Pa tsiku limenelo, padzakhala msewu waukulu+ wochokera ku Iguputo kupita ku Asuri. Anthu a ku Asuri adzapita ku Iguputo ndipo anthu a ku Iguputo adzapita ku Asuri. Aiguputo adzatumikira Mulungu limodzi ndi Asuri. 24  Pa tsiku limenelo, anthu a ku Isiraeli adzakhala gulu lachitatu, ataphatikizana ndi Aiguputo komanso Asuri,+ amenewa adzakhala madalitso padziko lapansi, 25  chifukwa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba adzakhala atawadalitsa nʼkuwauza kuti: “Adalitsike Aiguputo anthu anga, Asuri ntchito ya manja anga komanso Aisiraeli omwe ndi cholowa changa.”+

Mawu a M'munsi

“Mlulu” ndi zomera zitalizitali zimene zimakonda kumera mʼmadambo.
“Fulakesi” ndi mbewu imene ankalima ku Iguputo ndipo ankaigwiritsa ntchito popanga ulusi wowombera nsalu.
Mʼchilankhulo choyambirira, “anthu owomba nsalu pogwiritsa ntchito chowombela nsalu.”
Kapena kuti, “Memfisi.”
Mabaibulo ena amati, “nthambi ya kanjedza kapena bango.”