Yesaya 46:1-13

  • Mafano a Ababulo sangafanane ndi Mulungu wa Isiraeli (1-13)

    • Yehova amaneneratu zamʼtsogolo (10)

    • Mbalame yodya nyama yochokera kotulukira dzuwa (11)

46  Beli wawerama+ ndipo Nebo wagwada. Mafano awo anyamulidwa ndi nyama, nyama zonyamula katundu.+Mafanowo ali ngati katundu wolemera kwa nyama zotopa.   Milungu imeneyi imawerama komanso kugwada pa nthawi imodzi.Singapulumutse katunduyo,*Ndipo nayonso imatengedwa kupita ku ukapolo.   “Inu anyumba ya Yakobo ndimvetsereni, komanso inu nonse otsala a mʼnyumba ya Isiraeli,+Inu amene ndakuthandizani kuyambira pamene munabadwa ndiponso kukunyamulani kuyambira pamene munatuluka mʼmimba.+   Ngakhale mudzakalambe, ine ndidzakhala chimodzimodzi.+Ngakhale tsitsi lanu lidzachite imvi, ine ndidzapitiriza kukunyamulani. Ndidzakunyamulani, kukuthandizani komanso kukupulumutsani ngati mmene ndakhala ndikuchitira.+   Kodi mungandifananitse kapena kundiyerekezera ndi ndani?+Kodi munganene kuti ndine wofanana ndi ndani?+   Pali anthu amene amakhuthula golide mʼzikwama zawo.Amayeza siliva pasikelo. Iwo amalemba ganyu mmisiri wa zitsulo ndipo amapanga mulungu ndi zinthu zimenezi.+ Kenako anthuwo amayamba kumuweramira ndi kumulambira.*+   Iwo amamunyamula pamapewa awo.+Amamutenga nʼkukamuika pamalo ake ndipo mulunguyo amangoima pomwepo. Sasuntha pamene amuikapo.+ Anthuwo amamuitana mofuula, koma sayankha.Sangapulumutse munthu amene ali pamavuto.+   Kumbukirani zimenezi ndipo mulimbe mtima. Muziganizire mumtima mwanu, anthu ochimwa inu.   Kumbukirani zinthu zoyambirira zimene zinachitika kalekale,Kuti ine ndine Mulungu ndipo palibenso wina. Ine ndine Mulungu ndipo palibe aliyense wofanana ndi ine.+ 10  Kutatsala nthawi yaitali, ndimaneneratu zimene zidzachitike,Ndipo kale kwambiri ndinaneneratu zinthu zimene zidzachitike mʼtsogolo.+ Ine ndimanena kuti, ‘Zolinga zanga zidzachitikadi,+Ndipo ndidzachita chilichonse chimene ndikufuna.’+ 11  Ine ndikuitana mbalame yodya nyama kuchokera kotulukira dzuwa,*+Ndikuitana munthu kuchokera kudziko lakutali kuti adzachite zolinga zanga.+ Ineyo ndalankhula ndipo ndidzazichita. Ndakonza kuti zimenezi zichitike komanso ndidzazichita.+ 12  Ndimvereni inu anthu osamva,*Inu amene muli kutali ndi chilungamo. 13  Ine ndabweretsa pafupi chilungamo changa.Chilungamocho sichili kutali,Ndipo chipulumutso changa sichidzachedwa.+ Ndidzapereka chipulumutso mu Ziyoni, ndipo Isiraeli ndidzamʼpatsa ulemerero wanga.”+

Mawu a M'munsi

Katundu ameneyu ndi mafano amene anyamulitsa nyama.
Mʼchilankhulo choyambirira, “kumugwadira.”
Kapena kuti, “kumʼmawa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “a mtima wamphamvu.”