Yesaya 13:1-22

  • Uthenga wokhudza Babulo (1-22)

    • Tsiku la Yehova lili pafupi (6)

    • Amedi adzaukira Babulo (17)

    • MʼBabulo simudzakhalanso anthu (20)

13  Uwu ndi uthenga wokhudza Babulo,+ umene Yesaya+ mwana wa Amozi anaona mʼmasomphenya:   “Imikani chizindikiro+ paphiri la miyala yokhayokha. Afuulireni! Akodoleni ndi dzanja lanu,Kuti adzalowe pamakomo a anthu olemekezeka.   Ine ndapereka lamulo kwa anthu amene ndawasankha.*+ Ndaitana asilikali anga kuti adzasonyeze mkwiyo wanga.Iwo amasangalala komanso kunyada.   Tamverani! Mʼmapiri mukumveka phokoso la gulu la anthu.Phokosolo likumveka ngati la anthu ambiri, Tamverani! Kukumveka phokoso losonyeza kuti maufumu asokonezeka,Phokoso la mitundu ya anthu imene yasonkhanitsidwa pamodzi.+ Yehova wa magulu ankhondo akumwamba akusonkhanitsira asilikali kunkhondo.+   Iwo akubwera kuchokera kudziko lakutali,+Kuchokera kumalo akutali kwambiri pansi pa thambo,Yehova akubwera ndi zida zamkwiyo wake,Kuti awononge dziko lonse lapansi.+   Lirani mofuula, chifukwa tsiku la Yehova lili pafupi. Lidzabwera ngati chiwonongeko chochokera kwa Wamphamvuyonse.+   Nʼchifukwa chake manja onse adzangoti lobodo,Ndipo mtima wa munthu aliyense udzasungunuka ndi mantha.+   Anthu apanikizika.+ Nsautso ndi zowawa zawagweraNgati mkazi amene akubereka. Akuyangʼanana mwamantha,Ndipo nkhope zawo zikuonekeratu kuti ali ndi nkhawa.   Taonani! Tsiku la Yehova likubwera,Tsikulo ndi lankhanza, laukali ndiponso lamkwiyo woyaka moto,Likubwera kuti lidzachititse dziko kukhala chinthu chochititsa mantha,+Ndiponso kuti lidzawononge anthu ochimwa amʼdzikolo. 10  Chifukwa nyenyezi zakumwamba ndi magulu awo*+Sizidzaonetsa kuwala kwawo.Dzuwa lidzachita mdima potuluka,Ndipo mwezi sudzaonetsa kuwala kwake. 11  Ndidzaimba mlandu anthu okhala padziko lapansi chifukwa cha zoipa zawo,+Ndiponso anthu oipa chifukwa cha zolakwa zawo. Ndidzathetsa kunyada kwa anthu odzikuzaNdidzatsitsa kudzikuza kwa olamulira ankhanza.+ 12  Ndidzachititsa kuti anthu azisowa kwambiri kuposa golide woyengedwa bwino,+Ndiponso ndidzachititsa kuti anthu azisowa kwambiri kuposa golide wa ku Ofiri.+ 13  Choncho ndidzachititsa kuti kumwamba kunjenjemere,Ndipo dziko lapansi lidzagwedezeka nʼkuchoka mʼmalo mwake+Chifukwa cha ukali wa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, pa tsiku limene mkwiyo wake udzayake. 14  Mofanana ndi insa imene ikuthamangitsidwa ndiponso mofanana ndi ziweto zimene zilibe wozisonkhanitsa pamodzi,Aliyense adzabwerera kwa anthu ake.Aliyense adzathawira kudziko lake.+ 15  Aliyense amene adzapezedwe adzabayidwa,Ndipo aliyense amene adzagwidwe adzaphedwa ndi lupanga.+ 16  Ana awo adzaphwanyidwaphwanyidwa iwo akuona,+Katundu wamʼnyumba zawo adzalandidwa,Ndipo akazi awo adzagwiriridwa. 17  Ndidzachititsa Amedi kuti awaukire,+Amene saona siliva ngati kanthuNdipo sasangalala ndi golide. 18  Mauta awo adzaphwanyaphwanya anyamata.+Iwo sadzamvera chisoni chipatso cha mimbaKapena kuchitira chifundo ana. 19  Babulo, amene ndi waulemerero kwambiri* kuposa maufumu onse,+Chinthu chokongola chimene Akasidi amachinyadira,+Adzakhala ngati Sodomu ndi Gomora pa nthawi imene Mulungu anawononga mizindayi.+ 20  MʼBabulo simudzakhalanso anthu,Ndipo sadzakhalanso malo oti anthu nʼkukhalamo ku mibadwo yonse.+ Kumeneko Mluya sadzakhomako tenti yakeNdipo abusa sadzagonekako ziweto zawo. 21  Nyama zamʼchipululu zidzagona kumeneko.Nyumba zawo zidzadzaza ndi akadzidzi. Nthiwatiwa zizidzakhala kumeneko,+Ndipo mbuzi zakutchire* zizidzadumphadumpha kumeneko. 22  Nyama zakutchire zizidzalira munsanja zake,Ndipo mimbulu izidzalira mʼnyumba zake zachifumu zokongola. Nthawi yoti apatsidwe chilango yayandikira, ndipo zimenezi zichitika posachedwa.”+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “kwa anthu anga opatulika.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndi makesili awo,” mwina kutanthauza mlalangʼamba wa Oriyoni ndi milalangʼamba ina imene uli nayo pafupi.
Kapena kuti, “yemwe ndi chokongoletsera maufumu.”
Mabaibulo ena amati, “ziwanda zooneka ngati mbuzi.”