Yesaya 14:1-32

  • Isiraeli adzakhala mʼdziko lake (1, 2)

  • Kunyozedwa kwa mfumu ya Babulo (3-23)

    • Wonyezimira adzagwa kuchokera kumwamba (12)

  • Dzanja la Yehova lidzaphwanya Asuri (24-27)

  • Uthenga wokhudza Filisitiya (28-32)

14  Yehova adzachitira chifundo Yakobo+ ndipo adzasankhanso Isiraeli.+ Iye adzachititsa kuti akhazikike* mʼdziko lawo,+ alendo adzagwirizana nawo ndipo adzakhala limodzi ndi nyumba ya Yakobo.+  Anthu a mitundu ina adzawatenga nʼkubwerera nawo kwawo ndipo nyumba ya Isiraeli idzatenga anthuwo kuti akhale antchito awo aamuna ndi aakazi+ mʼdziko la Yehova. Iwo adzagwira anthu amene anawagwira nʼkupita nawo kudziko lina ndipo azidzalamulira anthu amene ankawagwiritsa ntchito mokakamiza.  Tsiku limene Yehova adzakupatseni mpumulo ku ululu wanu nʼkuthetsa chipwirikiti komanso ukapolo wanu wowawa,+  mudzanena mwambi uwu wonyoza mfumu ya Babulo: “Amene ankagwiritsa ntchito anzake mokakamiza uja wawonongedwa! Kuponderezedwa kuja kwatha ndithu!+   Yehova wathyola ndodo ya anthu oipa,Ndodo ya anthu olamulira.+   Wathyola ndodo ya amene ankakwapula mwaukali komanso mosalekeza anthu a mitundu ina,+Amene anagonjetsa mitundu ya anthu mokwiya powazunza mosalekeza.+   Tsopano dziko lonse lapansi lapuma, palibenso chosokoneza. Anthu akufuula mosangalala.+   Ngakhale mitengo ya junipa* yasangalala ndi zimene zakuchitikira,Limodzi ndi mitengo ya mkungudza ya ku Lebanoni. Mitengoyi ikunena kuti, ‘Kuyambira pamene unaphedwa,Palibenso munthu wodula mitengo amene anabwera kudzatidula.’   Ngakhale Manda* amene ali pansi agwedezekaKuti akumane nawe ukamabwera. Chifukwa cha iwe, Mandawo adzutsa akufa,Adzutsa atsogoleri* onse opondereza apadziko lapansi. Amachititsa mafumu onse a mitundu ya anthu kunyamuka pamipando yawo yachifumu. 10  Onsewo akulankhula nawe kuti,‘Kodi iwenso wafooka ngati ife? Kodi wafanana ndi ife? 11  Kunyada kwako kwatsikira ku Manda*Limodzi ndi phokoso la zoimbira zako za zingwe.+ Mphutsi zayalana pansi pako ngati bedi,Ndipo nyongolotsi zasanduka chofunda chako.’ 12  Wagwa kuchokera kumwamba,Wonyezimirawe, iwe mwana wa mʼbandakucha! Wadulidwa nʼkugwera padziko lapansi,Iwe amene unagonjetsa mitundu ya anthu!+ 13  Iweyo wanena mumtima mwako kuti, ‘Ndikwera kumwamba.+ Ndikweza mpando wanga wachifumu pamwamba pa nyenyezi za Mulungu,+Ndipo ndikhala paphiri lokumanapoKumapeto kwenikweni kwa madera akumpoto.+ 14  Ndikwera pamwamba kupitirira nsonga za mitambo.Ndidzipanga kukhala wofanana ndi Wamʼmwambamwamba.’ 15  Koma mʼmalomwake adzakutsitsira ku Manda,*Pansi penipeni pa dzenje. 16  Okuona adzakuyangʼana modabwa.Adzakuyangʼanitsitsa nʼkunena kuti,‘Kodi munthu amene ankagwedeza dziko lapansi uja ndi ameneyu,Amene ankachititsa kuti maufumu anjenjemere,+ 17  Amene anachititsa dziko lapansi kukhala ngati chipululu,Nʼkugonjetsa mizinda yake,+Amene sanalole kuti akaidi ake azipita kwawo?’+ 18  Mafumu ena onse a mitundu ya anthu,Onsewo anaikidwa mʼmanda molemekezeka,Aliyense mʼmanda* ake. 19  Koma iweyo watayidwa popanda kuikidwa mʼmanda,Ngati mphukira* imene anthu amanyansidwa nayo,Imene ili pakati pa anthu akufa ophedwa ndi lupanga,Amene amatsikira kumiyala yamʼdzenje,Ngati mtembo wopondedwapondedwa. 20  Sudzaikidwa mʼmanda limodzi ndi mafumuwo,Chifukwa unawononga dziko lako lomwe,Unapha anthu ako omwe. Mayina a ana a anthu ochita zoipa sadzatchulidwanso. 21  Konzekerani kupha ana akeChifukwa cha zolakwa za makolo awo,Kuti asakhalenso ndi mphamvu nʼkuyamba kulamulira dziko lapansiKomanso kudzaza dzikoli ndi mizinda yawo.” 22  “Ine ndidzawaukira,”+ akutero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. “Ndipo mʼBabulo ndidzachotsamo dzina, anthu otsala, ana komanso mbadwa,”+ akutero Yehova. 23  “Babulo ndidzamusandutsa malo okhala nungu* ndiponso malo a zithaphwi. Ndidzamusesa ndi tsache la chiwonongeko,”+ akutero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. 24  Yehova wa magulu ankhondo akumwamba walumbira kuti: “Zimene ndikufuna kuchita, zidzachitika mmene ndikufunira,Ndipo zimene ndasankha, ndi zimene zidzachitike. 25  Ndidzaphwanya Msuri mʼdziko langa,Ndipo ndidzamupondaponda pamapiri anga.+ Goli lake lidzachotsedwa pa iwoNdipo katundu wake adzachotsedwa pamapewa awo.”+ 26  Izi nʼzimene zakonzedwa kuti zidzachitikire dziko lonse lapansi,Ndipo ili ndi dzanja limene latambasulidwa* kuti lilange mitundu yonse ya anthu. 27  Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wasankha zoti achite,Ndiye ndi ndani amene angazilepheretse?+ Dzanja lake latambasulidwa,Ndi ndani amene angalibweze?+ 28  Mʼchaka chimene Mfumu Ahazi inamwalira,+ uthenga wamphamvu uwu unaperekedwa: 29  “Usasangalale iwe Filisitiya, kapena aliyense wokhala mwa iweChifukwa chakuti ndodo ya amene ankakumenya yathyoka. Chifukwa pamuzu wa njoka+ padzatuluka njoka yapoizoni,+Ndipo mwana wake adzakhala njoka youluka, yaululu wamoto.* 30  Ana oyamba kubadwa a anthu onyozeka adzadya nʼkukhutaNdipo anthu osauka adzagona motetezeka,Koma ndidzapha anthu ako* ndi njala,Ndipo amene adzatsale mwa iwe adzaphedwa.+ 31  Lira mofuula geti iwe! Lira mokweza mzinda iwe! Nonsenu mudzataya mtima, inu anthu a ku Filisitiya! Chifukwa utsi ukubwera kuchokera kumpoto,Ndipo palibe msilikali amene akutsalira pa magulu ake ankhondo.” 32  Kodi iwo adzawayankha chiyani amithenga ochokera ku mtundu wina? Adzawayankha kuti, Yehova waika maziko a Ziyoni,+Ndipo anthu onyozeka pakati pa anthu ake adzathawira mmenemo.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “adzawapatsa mpumulo.”
Mtengo wa junipa ndi wofanana ndi mtengo wa mkungudza.
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “atonde.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼnyumba.”
Kapena kuti, “nthambi.”
“Nungu” ndi nyama yamʼtchire yomwe ili ndi minga zodzitetezera thupi lonse.
Kapena kuti, “dzanja lakonzekera.”
Kapena kuti, “njoka yapoizoni yothamanga kwambiri.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “muzu wako.”