July

Lachitatu, July 1

July

Sindinaonepo munthu aliyense wolungama atasiyidwa.—Sal. 37:25.

Atumiki a Yehova ena amavutika chifukwa cha matenda, ukalamba kapena mavuto ena okhudza thanzi lawo. Izi zingachititse kuti azikayikira ngati Yehova amawaonabe kuti ndi amtengo wapatali. Angamadzifunse kuti, ‘Kodi Yehova amaonabe kuti ndine wofunika?’ Wolemba Salimo 71 ankakayikiranso ngati Yehova amamuona kuti ndi wofunika. Iye anapemphera kuti: “Musandisiye pa nthawi imene mphamvu zanga zatha.” (Sal. 71:​9, 18) Koma iye sankakayikira kuti ngati angapitirize kutumikira Mulungu mokhulupirika, Yehova adzamutsogolera komanso kumuthandiza. Wolemba salimoyu anazindikira kuti Yehova amasangalala ndi anthu amene amapitiriza kumutumikira ngakhale pamene sakutha kuchita zambiri. (Sal. 37:​23-25) Ngati ndinu wachikulire, muyenera kuganizira mmene Yehova amakuonerani. Ngakhale kuti mphamvu zanu zikuchepa iye angakuthandizeni kuti mukhale amphamvu mwauzimu. (Sal. 92:​12-15) M’malo moganizira zimene simungathe kuchita, muziganizira zimene mungakwanitse. w24.10 28 ¶14-16

Pa nkhani ya kudya zakudya zoperekedwa kwa mafano, timadziwa kuti fano si kanthu.1 Akor. 8:4.

Akhristu osakhwima mwauzimu amavutika pakachitika nkhani imene ikufunika kuganizira mfundo za m’Baibulo n’kuzitsatira. Anthu ena amaganiza kuti ngati palibe lamulo la m’Baibulo pa nkhani inayake ndiye kuti akhoza kuchita zilizonse zimene akufuna. Ena amafuna kuti achite kupatsidwa lamulo pa nkhani zimene palibe lamulo. Mwachitsanzo, zikuoneka kuti Akhristu a ku Korinto ankafuna kuti mtumwi Paulo awaikire lamulo pa nkhani ya chakudya chimene chaperekedwa ku mafano. M’malo mongowauza zochita, Paulo anawafotokozera kuti aliyense ali ndi ‘ufulu wosankha’ mogwirizana ndi chikumbumtima chake. Iye anakambirana nawo mfundo zimene zingathandize kuti chikumbumtima cha aliyense chisamamuvutitse komanso asamakhumudwitse ena. (1 Akor. 8:​7-9) Choncho Paulo anathandiza Akhristu a ku Korinto kuti akule mwauzimu n’cholinga choti azigwiritsa ntchito luso lawo la kuganiza m’malo modalira anthu ena kapena kumafuna kuti pa nkhani iliyonse pakhale lamulo. w24.04 5 ¶14

Ine Yehova ndimafufuza mtima, . . . kuti munthu aliyense ndimuchitire zinthu mogwirizana ndi zochita zake.—Yer. 17:10.

M’nthawi ya Yona, anthu a ku Nineve anali ndi mwayi wolapa. Komanso kumbukirani zimene Yesu ananena zokhudza anthu amene ‘adzaukitsidwe kuti aweruzidwe.’ Ankaphatikizapo anthu “amene ankachita zoipa.” (Yoh. 5:29) Choncho zikuoneka kuti anthu ena a ku Sodomu ndi Gomora akhozanso kudzaukitsidwa. N’kutheka kuti ena mwa anthuwo adzaukitsidwa ndipo tingadzakhale ndi mwayi wowaphunzitsa za Yehova ndi Yesu Khristu. Nthawi zonse Yehova ‘amafufuza mtima, amafufuza maganizo a mkati mwa mtima wa munthu.’ Choncho pa nkhani ya kuukitsa anthu, Yehova adzachitira munthu aliyense “mogwirizana ndi zochita zake.” Adzachita zinthu mwamphamvu komanso mwachifundo ngati pakufunika kutero. Choncho tisamafulumire kuganiza kuti munthu winawake alibe chiyembekezo choti adzaukitsidwa, pokhapokha ngati tatsimikiza kuti Baibulo limanena zimenezo. w24.05 5-6 ¶15-16

Usachite mantha. Ineyo ndikuthandiza.—Yes. 41:13.

Kuyambira kale, Mawu a Mulungu akhala akulimbikitsa atumiki ake kuti athe kugwira ntchito zovuta. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mneneri Yeremiya. Iye ankachita mantha Mulungu atamutuma kuti akalalikire. Yeremiya anati: “Ine sinditha kulankhula chifukwa ndine mwana.” (Yer. 1:6) Ndiye kodi iye anatani kuti asiye kudzikayikira? Anapeza mphamvu kuchokera m’Mawu a Mulungu. Iye anati: “Mawu ake anali ngati moto woyaka umene watsekeredwa mʼmafupa anga, ndipo ndinatopa ndi kudziletsa kuti ndisalankhule.” (Yer. 20:​8, 9) Ngakhale kuti Yeremiya ankalalikira m’gawo lovuta, uthenga womwe ankalalikira unamupatsa mphamvu zoti agwirire ntchitoyo. Akhristu amapeza mphamvu kuchokera m’Mawu a Mulungu. Mtumwi Paulo ananena kuti kudziwa zinthu molondola kungalimbikitse abale akewo kuti ‘akhale ndi khalidwe logwirizana ndi zimene Yehova amafuna’ ndiponso kuti ‘apitirize kubala zipatso pantchito iliyonse yabwino.’—Akol. 1:​9, 10. w24.04 14-15 ¶2-4

Zadoki wansembe . . . anadzoza Solomo.—1 Maf. 1:39.

Zadoki anakhalabe wokhulupirika kwa Yehova ngakhale kuti Abiyatara yemwe anali mkulu wa ansembe ankathandiza Adoniya mwana wa Davide amene anakonza zolanda Ufumu. Davide sanasiye kumukhulupirira Zadoki. Chiwembu cha Adoniya chitadziwika, Davide anasankha Zadoki, Natani ndi Benaya kuti akadzoze Solomo kukhala mfumu. (1 Maf. 1:​32-34) Kukhala pakati pa atumiki a Yehova okhulupirika monga Natani ndi ena omwe anali kumbali ya Mfumu Davide, kuyenera kuti ndi kumene kunamulimbikitsa Zadoki. Solomo atakhala mfumu, anasankha “wansembe Zadoki kuti alowe m’malo mwa Abiyatara.” (1 Maf. 2:35) Kodi tingamutsanzire bwanji Zadoki? Ngati munthu amene mumamukonda wasiya kutumikira Yehova, inuyo muzisonyeza kuti mukufuna kukhalabe wokhulupirika. (Yos. 24:15) Yehova adzakupatsani mphamvu komanso kukulimbikitsani. Muzimudalira popemphera kwa iye komanso kupitiriza kukhala pa ubwenzi ndi Akhristu anzanu okhulupirika. Yehova amaona kukhulupirika kwanu ndipo adzakupatsani mphoto.—2 Sam. 22:26. w24.07 6-7 ¶16-17

Tisasiye kuchita zabwino.Agal. 6:9.

Lemba la Salimo 15: 2 limanena kuti mnzake wa Mulungu ayenera ‘kuyenda mosalakwitsa zinthu, ndipo amachita zinthu zabwino.’ Mawu akuti ‘kuyenda’ komanso ‘kuchita’ akutanthauza kuchita zinazake mosalekeza. Koma kodi n’zothekadi ‘kuyenda mosalakwitsa zinthu’? Inde. Ngakhale kuti palibe munthu wangwiro, Yehova angatione kuti ndife munthu ‘wosalakwitsa zinthu’ ngati timayesetsa kumumvera. Tikadzipereka n’kubatizidwa timakhala kuti tangoyambapo kuyenda ndi Mulungu. Kumbukirani kuti kale kungokhala Mwisiraeli sikunkapangitsa munthu kukhala mlendo wa Yehova. Panali anthu ena omwe sankachita zinthu ‘kuchokera pansi pa mtima ndipo sankachita zoyenera.’ (Yes. 48:1) Mwisiraeli wokhulupirika ankafunika kuphunzira malamulo a Yehova n’kumawatsatira. Masiku anonso kuti Mulungu azisangalala nafe, pamafunika zambiri kuposa kungobatizidwa n’kumasonkhana ndi mpingo. Timafunika kupitiriza ‘kuchita zinthu zabwino.’ w24.06 9 ¶4; 10 ¶6

Muzitsanzira Mulungu.—Aef. 5:1.

Kodi Yehova wasonyeza m’njira ziti kuti ndi wopatsa? Tiyeni tikambirane zitsanzo zingapo. Yehova amatipatsa zinthu zofunika pa moyo. N’zoona kuti sitingakhale ndi zinthu zonse zimene timalakalaka. Koma Yehova amatipatsa zinthu zofunika kwambiri pa moyo. Mwachitsanzo, amatipatsa chakudya, zovala komanso pogona. (Sal. 4:8; Mat. 6:​31-33; 1 Tim. 6:​6-8) Kodi Yehova amangotipatsa zinthuzi chifukwa chakuti ndi udindo wake? Ayi. Taganizirani mawu amene Yesu ananena pa Mateyu 6:​25, 26. Ponena za mbalame, Yesu anati: “Pajatu sizifesa mbewu kapena kukolola kapenanso kusunga chakudya mʼnyumba zosungiramo zinthu.” Kenako iye ananena kuti: “Koma Atate wanu wakumwamba amazidyetsa.” Ndiyeno anafunsa kuti: “Kodi inu si amtengo wapatali kuposa mbalame?” Apa mfundo ndi yakuti Yehova amaona kuti atumiki ake ndi amtengo wapatali kuposa zinyama. Ndiye ngati Yehova amasamalira zinyama, sitiyenera kukayikira kuti adzatithandizanso kupeza zinthu zofunika. Iye ali ngati bambo wachikondi amene amayesetsa kupeza zofunika m’banja lake chifukwa cha chikondi.—Sal. 145:16; Mat. 6:32. w24.09 26-27 ¶4-6

Amuna amene amatumikira bwino amakhala ndi mbiri yabwino ndi ufulu waukulu wolankhula za chikhulupiriro.—1 Tim. 3:13.

Mtumiki wothandiza amakhala m’bale wobatizidwa yemwe amaikidwa ndi akulu kuti aziwathandiza pa ntchito zina mumpingo. Atumiki othandiza ayenera kukhala anthu amene amakonda Yehova ndiponso kutsatira mfundo zake zolungama. Iwo amafunikanso kukonda kwambiri abale ndi alongo awo. (Mat. 22:​37-39) Kodi m’bale wobatizidwa angatani kuti akhale mtumiki wothandiza? Baibulo limafotokoza makhalidwe amene munthu ayenera kukhala nawo kuti akhale mtumiki wothandiza. (1 Tim. 3:​8-10, 12) Kuti mukhale mtumiki wothandiza muyenera kuphunzira makhalidwe amenewa n’kumayesetsa kuwasonyeza. Koma choyamba, muyenera kufufuza chimene chikukuchititsani kufuna kukhala mtumiki wothandiza. w24.11 15 ¶4-5

Simunawalandire monga mawu a anthu, koma mmene alilidi, monga mawu a Mulungu.—1 Ates. 2:13.

Anthu ena amanena kuti awerengapo Baibulo maulendo ambirimbiri. Koma kodi amakhulupirira zimene limanena? Kodi amagwiritsa ntchito zimene awerenga komanso kulola kuti zisinthe moyo wawo? N’zomvetsa chisoni kuti satero. Izitu ndi zosiyana kwambiri ndi zimene anthu a Yehovafe timachita. Timayesetsa kutsatira malangizo ake pa moyo wathu. Komabe si nthawi zonse pamene zimakhala zophweka kuwerenga komanso kugwiritsa ntchito zimene tawerenga m’Mawu a Mulungu. Nthawi zina zingamativute kuti tipeze nthawi yoti tiwerenge. Apo ayi tikhoza kumawerenga mofulumira kwambiri n’kulephera kupeza nthawi yoganizira zimene tawerenga. Mwinanso tikhoza kukhumudwa tikaganizira kuchuluka kwa zinthu zimene tikufunika kusintha. Choncho kaya inu mukulimbana ndi vuto lotani, dziwani kuti mungathe kuligonjetsa. Yehova angakuthandizeni. Choncho tiyeni tizilola kuti atithandize kuti tisakhale anthu ongomva n’kuiwala koma amene amachita zimene Mawu a Mulungu amanena. N’zosachita kufunsa kuti tikamawerenga kwambiri komanso kugwiritsa ntchito Mawu a Mulungu pa moyo wathu, m’pamenenso timakhala osangalala kwambiri.—Yak. 1:25. w24.09 7 ¶15-16

Pitirizani kupempha ndipo adzakupatsani.—Luka 11:9.

Zinthu zoipa zikatichitikira, Yehova amatitonthoza pogwiritsa ntchito mzimu wake woyera. Ngati inunso mukulimbana ndi mayesero amene achititsa kuti musweke mtima, muzimufotokozera Yehova mmene mukumvera. Muzichita zimenezi nthawi iliyonse komanso kwa nthawi yaitali mmene mukufunira. (Sal. 86:3; 88:1) Muzipempha Yehova mobwerezabwereza kuti akupatseni mzimu wake woyera ndipo nthawi zonse iye adzakuthandizani. Kodi mwafooka chifukwa cha zinthu zinazake zoipa zimene zakuchitikirani? Mzimu woyera ungakupatseni mphamvu kuti mupitirize kutumikira Yehova mokhulupirika. (Aef. 3:16) Kodi mungatani kuti muzichita zinthu mogwirizana ndi pemphero lanu lopempha mzimu woyera? Muzichita nawo zinthu zimene zingachititse kuti mzimu woyera uzikuthandizani. Zinthu zimenezi zikuphatikizapo kupezeka pamisonkhano komanso kulalikira. Muziwerenga Baibulo tsiku lililonse kuti muziyendera maganizo a Yehova. (Afil. 4:​8, 9) Mukamawerenga, muziona anthu otchulidwa m’Baibulo amene anakumana ndi mavuto osiyanasiyana ndipo muziganizira mmene Yehova anawathandizira kupirira. w24.10 9 ¶12-14

Mulungu anakonda kwambiri dziko.Yoh. 3:16.

Mofanana ndi Yehova ndi Mwana wake, nafenso timakonda anthu. (Miy. 8:31) Timamvera chisoni anthu omwe “sadziwa Mulungu” ndiponso “alibe chiyembekezo.” (Aef. 2:12) Iwo akukumana ndi mavuto ambiri ndipo zimakhala ngati ali m’dzenje lakuya. Koma ife tili ndi chingwe chomwe tingawaponyere kuti tiwatulutsemo, chomwe ndi uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Chifukwa chakuti timawakonda komanso kuwamvera chisoni, timayesetsa kuti tiwauze uthenga wabwinowu. Uthengawu umawapatsa chiyembekezo, kuwathandiza kuti akhale ndi moyo wabwino panopa komanso umawapatsa chiyembekezo chodzapeza “moyo weniweniwo,” umene ndi moyo wosatha m’dziko latsopano la Mulungu. (1 Tim. 6:19) Kukonda anthu kumatichititsanso kuti tiziwachenjeza kuti mapeto a dziko loipali ali pafupi. (Ezek. 33:​7, 8) Timafuna kuti iwo adziwe zimene zichitike pa nthawi ya chisautso chachikulu, pamene choyamba zipembedzo zonse zabodza zidzachotsedwa ndipo kenako maboma onse adzawonongedwa pa nkhondo ya Aramagedo.—Chiv. 16:​14, 16; 17:​16, 17; 19:​11, 19, 20. w24.05 16-17 ¶8-9

Okondedwa, musamabwezere zoipa, koma siyirani malo mkwiyo wa Mulungu. Chifukwa Malemba amati: “‘Kubwezera ndi kwanga, ndidzawabwezera ndine,’ watero Yehova.”—Aroma 12:19.

Mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu kuti ‘azisiyira malo mkwiyo wa Mulungu.’ Timasiyira malo mkwiyo wa Mulungu tikamalola kuti iye achite chilungamo pa nthawi komanso m’njira imene akuona kuti ndi yoyenera. M’bale wina dzina lake John atachitiridwa zopanda chilungamo ananena kuti: “Ndinkalimbana ndi mtima wofuna kuti ndikonze zinthu pandekha. Koma lemba la Aroma 12:19 linandithandiza kuti ndiziyembekezera Yehova.” Zinthu zimatiyendera bwino tikamayembekezera Yehova kuti akonze zinthu. Tikatero timakhala ngati tatula mtolo wofuna kuyesa kuti tikonze tokha zinthu. Yehova ndi wokonzeka kutithandiza. Zimakhala ngati iye akunena kuti, ‘Ndisiyire zinthu zopanda chilungamozo. Ndithana nazo.’ Tikamvera lonjezo lake lakuti “ndidzawabwezera ndine,” timasiya nkhaniyo m’manja mwake ndipo timakhulupirira kuti athetsa nkhaniyo m’njira yabwino kwambiri. w24.11 6 ¶14-15

Mutipatse chakudya chalero mogwirizana ndi chakudya chofunika pa tsikuli.Luka 11:3.

Tiyenera kusamala kuti tisamaone zinthu kapena ndalama ngati zofunika kwambiri pa moyo wathu. Paulo anafotokozanso bwino mfundo imeneyi pamene analembera Akhristu a Chiyuda. Iye anafotokoza zimene zinachitikira Aisiraeli kuphatikizapo zomwe zinachitika pafupi ndi phiri la Sinai. Anachenjeza Akhristu kuti ‘asamalakelake zinthu zoipa ngati mmene [Aisiraeli] anachitira.’ (1 Akor. 10:​6, 7, 11) Aisiraeli analola kuti dyera lawo lolakalaka chakudya lichititse zinthu zimene Yehova anawapatsa modabwitsa kukhala “zinthu zoipa.” (Num. 11:​4-6, 31-34) Komanso pamene ankalambira mwana wa ng’ombe iwo anasonyeza kuti chomwe chinali chofunika kwambiri kwa iwo ndi kudya, kumwa komanso kusangalala. (Eks. 32:​4-6) Paulo anatchula zimenezi pomwe ankachenjeza Aisiraeli omwe ankayembekezera kuwonongedwa kwa Yerusalemu mu 70 C.E. Ifenso tikukhala m’nthawi ya mapeto, choncho tingachite bwino kuganizira malangizo a Paulowa. w24.12 6 ¶13

Uzisangalala ndi mkazi amene unamukwatira udakali wachinyamata.—Miy. 5:18.

Yehova ndi “Mulungu wachimwemwe,” ndipo amafuna kuti ifenso tizisangalala. (1 Tim. 1:11) Watipatsa mphatso zambiri zotithandiza kuti tizisangalala. (Yak. 1:17) Imodzi mwa mphatso zimenezi ndi banja. Mwamuna ndi mkazi akakwatirana amalonjezana kuti azikondana, kulemekezana komanso kusamalirana. Iwo akamagwirizana amakhala osangalala kwambiri. Anthu ambiri amaiwala zimene analonjeza patsiku laukwati. Ndipo zotsatira zake ndi zoti sakhala osangalala. Koma kodi Yehova amafuna kuti amuna azichita bwanji zinthu ndi akazi awo? Yehova amalamula amuna kuti azilemekeza akazi awo. Mwamuna amene amalekeza mkazi wake amachita naye zinthu mokoma mtima komanso mwachikondi.—1 Pet. 3:7. w25.01 8 ¶1-2; 9 ¶4-5

Yehova ndi amene amandithandiza. Sindidzaopa.—Aheb. 13:6.

Sitikukayikira kuti kalata imene mtumwi Paulo analembera Akhristu a Chiheberi inathandiza Akhristuwo kukonzekera chisautso chimene chinkabwera. Paulo analimbikitsa abale ake kuti ayenera kuphunzira Malemba mozama komanso kuwamvetsa. Kuchita zimenezi kukanawathandiza kuti azizindikira komanso kupewa mfundo zomwe zikanasokoneza chikhulupiriro chawo. Anawalimbikitsanso kuti ayenera kulimbitsa chikhulupiriro chawo kuti adzatsatire malangizo a Yesu komanso a amene ankatsogolera mumpingo. Iye anathandiza Akhristuwo kuti azikhala ndi maganizo oyenera pa nkhani ya mayesero n’cholinga choti awapirire komanso kuti aziona mayeserowo ngati njira imene Atate wawo wachikondi akuwaphunzitsira. Tiyeni nafenso tizitsatira malangizo ouziridwa amenewa. Tikatero tidzatha kupirira mpaka mapeto.—Aheb. 3:14. w24.09 13 ¶17, 19

Tayeretsedwa . . . kudzera mʼthupi la Yesu Khristu limene analipereka nsembe kamodzi kokha.—Aheb. 10:10.

Mogwirizana ndi zimene Baibulo limanena, dipo ndi malipiro amene amaperekedwa pofuna kuphimba machimo komanso kugwirizanitsa anthu ndi Yehova. Yehova amaona kuti dipo ndi limene limathandiza kubwezeretsa zimene zinatayika. Kumbukirani kuti Adamu ndi Hava anataya moyo wangwiro komanso mwayi wokhala ndi moyo wosatha. Choncho dipo linayenera kukhala malipiro ofanana ndi zimene zinatayikazo. (1 Tim. 2:6) Linayenera kuperekedwa ndi munthu wamkulu yemwe (1) anali wangwiro, (2) anali ndi mwayi woti akanatha kukhala ndi moyo padziko lapansi mpaka kalekale komanso (3) anali wofunitsitsa kupereka moyo wake ngati nsembe. Taonani zifukwa zitatu zimene zikuchititsa Yesu kukhala woyenera kupereka dipoli. (1) Iye anali wangwiro ndipo “sanachite tchimo.” (1 Pet. 2:22) (2) Popeza anali wangwiro, akanatha kukhala ndi moyo mpaka kalekale padziko lapansi. (3) Iye analolera kufa n’kupereka moyo wake chifukwa cha ifeyo.—Aheb. 10:9. w25.02 4-5 ¶11-12

Iye akafuna kupereka mzimu sapereka moumira.Yoh. 3:34.

Yehova amakukondani ndipo amafuna kuti mukhale m’banja lake. Izitu zili choncho ngakhale kuti mukukumana ndi mavuto omwe angakulepheretseni kubatizidwa. Pa nthawi ina Yesu anauza kagulu ka ophunzira ake kuti: “Ngati mutakhala ndi chikhulupiriro chofanana ndi kanjere ka mpiru kuchepa kwake, mudzatha kuuza phiri ili kuti, ‘Choka pano upite apo,’ ndipo lidzachokadi. Palibe chimene chidzakhale chosatheka kwa inu.” (Mat. 17:20) Anthu amene anamva zimenezi anali atakhala ndi Yesu kwa zaka zochepa chabe, choncho chikhulupiriro chawo chinali chikukulabe. Koma Yesu anawatsimikizira kuti ngati atakhala ndi chikhulupiriro chokwanira, Yehova adzawathandiza kulimbana ndi mavuto okhala ngati mapiri. Ndipotu Yehova angakuthandizeni inunso kuchita zimenezi. Ngati mwazindikira kuti pali mavuto ena omwe akukulepheretsani kubatizidwa, yesetsani kuti muwathetse mofulumira. Dziperekeni kwa Yehova ndi kubatizidwa. Mukachita zimenezi mudzakhala kuti mwasankha bwino kwambiri. w25.03 7 ¶18-20

Yehova ali kumbali yanga, sindidzaopa.—Sal. 118:6.

Tingathe kupirira mayesero ngati timakumbukira kuti Mulungu wamoyo ndi wokonzeka kutithandiza. Tingamakhulupirire kwambiri zimenezi tikaganizira zimene anachitapo kale. (Yes. 37:​17, 33-37) Komanso muziwerenga ndi kuonera malipoti a pa jw.org osonyeza mmene Yehova akuthandizira abale ndi alongo athu masiku ano. Kuwonjezera pamenepo, muziganiziranso mmene anakuthandizirani inuyo. Zilibe kanthu kuti simungatchule mavuto akuluakulu. Tikutero chifukwa Yehova wakhala akukuchitirani zambiri pa moyo wanu. Anakukokani kuti mukhale naye pa ubwenzi. (Yoh. 6:44) Choncho mungachite bwino kumupempha kuti akukumbutseni nthawi imene anayankha mapemphero anu, kukuthandizani pa nthawi yoyenera komanso kukusamalirani pa nthawi yovuta. Kuganizira zimenezi kungakuthandizeni kuti muzikhulupirira kwambiri kuti Yehova adzapitiriza kukuthandizani. w24.06 21 ¶8

“Imfayo inafalikira kwa anthu onse chifukwa onse anachimwa”.—Aroma 5:12.

Timafunitsitsa kuti tisachite chilichonse chomwe chingakhumudwitse Yehova. Komabe si ife angwiro choncho tikhoza kuyesedwa kuti tichite zoipa. (Aroma 7:​21-23) Mosayembekezera, tingapezeke kuti tayamba kuona zinthu zinazake zoipa ngati zabwino. Kuti tikhalebe okhulupirika kwa Yehova ndi Yesu, tiyenera kutsatira malangizo a Yesu oti tikhalebe maso. Tonsefe timayesedwa kuti tichite zoipa. Koma aliyense ali ndi zofooka zake, kaya zomwe zingachititse kuti achite tchimo lalikulu, ayambe kuchita makhalidwe oipa kapena agwere mumsampha woyamba kuganiza ngati anthu a m’dzikoli. Wina angakhale ndi chilakolako champhamvu chofuna kuchita zoipa monga kuseweretsa maliseche kapena kuonera zolaula. Pamene wina angamalimbane ndi vuto la kuopa anthu, kufuna kumangoyendera maganizo ake okha, kukwiya msanga ndi zina. w24.07 14 ¶3; 15 ¶5

Mukhululukireni ndi mtima wonse ndiponso kumutonthoza, kuopera kuti iye angakhale ndi chisoni chopitirira malire mpaka kutaya mtima.—2 Akor. 2:7.

Taganizirani zimene zikanachitika ngati akulu akanakana kulandiranso munthu wina wolapa mumpingo kapenanso ngati pambuyo pobwerera, Akhristu anzake akanakana kumusonyeza chikondi. Iye akanakhala ndi “chisoni chopitirira malire.” Akanamaona kuti sangatumikirenso Yehova. Zikanamuvutanso kuti apitirize kukonza ubwenzi wake ndi Mulungu. Choopsa kwambiri ndi chakuti ngati abale ndi alongowo akanakana kukhululukira munthu wolapayo akanasokoneza ubwenzi wawo ndi Yehova. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa m’malo motsanzira Yehova yemwe amakhululukira anthu ochimwa omwe alapa, akanatsanzira Satana yemwe ndi wopanda chifundo komanso wankhanza. Iwo akanakhala ngati zida zimene Mdyerekezi akugwiritsa ntchito pofuna kulepheretsa munthuyo kuti ayambirenso kutumikira Yehova.—2 Akor. 2:​10, 11; Aef. 4:27. w24.08 17 ¶7, 10-11

Atakwera pamalo apamwamba, . . . anapereka amuna kuti akhale mphatso.—Aef. 4:8.

Yesu Khristu anapereka akulu ena ngati “mphatso” kuti azithandiza mipingo m’njira ina. Motsogoleredwa ndi Yesu, akulu ku Yerusalemu anatumiza Paulo, Baranaba ndi ena monga oyang’anira oyendayenda. (Mac. 11:22) Anachita zimenezi kuti azikalimbikitsa mipingo ngati mmenenso akulu ndi atumiki othandiza amachitira. (Mac. 15:​40, 41) Nthawi zambiri oyang’anira madera amakhala akuyendayenda. Ena amayenda makilomita ambirimbiri kuti akafike kumipingo ina. Mlungu uliwonse, woyang’anira dera amakamba nkhani zingapo komanso kuchita maulendo a ubusa. Amachititsa msonkhano wa apainiya, wa akulu komanso misonkhano yokonzekera utumiki. Amathandizana ndi akulu pokonzekera misonkhano yadera ndi yachigawo ndiponso kukamba nkhani pamisonkhanoyo. Amaphunzitsa sukulu za apainiya komanso kukonza msonkhano wapadera wa apainiya m’dera lawo ndipo nthawi zina amagwira ntchito zimene apemphedwa ndi ofesi ya nthambi. w24.10 21 ¶12-13

Ine ndidzawakhululukira zolakwa zawo ndipo machimo awo sindidzawakumbukiranso.—Yer. 31:34.

Yehova anauza mneneri Yeremiya kuti alembe mawu a mulemba lalerowa. Mtumwi Paulo anafotokozanso zofanana ndi zimenezi pamene analemba kuti: “Sindidzakumbukiranso machimo awo.” (Aheb. 8:12) Koma kodi mawu amenewa akutanthauza chiyani? M’Baibulo mawu akuti “kukumbukira” samangotanthauza kuganizira zinthu zina zimene zinachitika. Koma amatanthauza kuchita zinazake. Mwachitsanzo, chigawenga chimene chinapachikidwa pafupi ndi Yesu chinapempha kuti: “Yesu, mukandikumbukire mukakalowa mu Ufumu wanu.” (Luka 23:​42, 43) Iye sankangopempha Yesu kuti amuganizire pa nthawiyo. Yankho la Yesu linasonyeza kuti iye adzachitapo kanthu poukitsa munthuyu. Choncho Yehova akamatiuza kuti sakumbukiranso machimo athu, zimatanthauza kuti sadzatiimba mlandu chifukwa cha machimowo. Komanso m’tsogolo sadzatilanga chifukwa cha machimo amene anatikhululukira. w25.02 10-11 ¶14-15

Ngati ungadziwe Mulungu, yemwe ndi Woyera Koposa, udzakhala womvetsa zinthu.—Miy. 9:10.

Kuti munthu akhale womvetsa zinthu, ayenera kudziwa bwino makhalidwe a Yehova, cholinga chake komanso zimene amakonda ndi zimene amadana nazo. Dzifunseni kuti, ‘Mogwirizana ndi zomwe ndikudziwa zokhudza Yehova, kodi ndingasankhe kuchita zinthu ziti zomwe zingamusangalatse?’( Aef. 5:17) Kuti tisangalatse Yehova, nthawi zina timafunika kusankha zinthu zomwe zingakhumudwitse anthu omwe amatikonda. Mwachitsanzo, makolo angalimbikitse mwana wawo kuti akwatiwe ndi mwamuna wopeza bwino kapena amene akuona kuti angawapatse ndalama zambiri zolowolera ngakhale kuti mwamunayo sali pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. N’zoona kuti iwo amafuna kuti mwana wawo azisamalidwa bwino koma ndi ndani amene adzamuthandize kulimbitsa ubwenzi wake ndi Yehova? Kodi Yehova amaiona bwanji nkhaniyi? Tingapeze yankho la funso limeneli pa Mateyu 6:33. Palembali, Akhristu amalimbikitsidwa kuti ‘aziika Ufumu pamalo oyamba pa moyo wawo.’ Ngakhale kuti timalemekeza makolo komanso anthu a m’dera lathu, chofunika kwambiri kwa ife ndi kusangalatsa Yehova. w25.01 17 ¶9-10

Ambuye anaima nane pafupi nʼkundipatsa mphamvu.—2 Tim. 4:17.

Masiku ano timafunikira kuti Yehova azitithandiza kuti tizilalikira mwakhama ngakhale tikutsutsidwa. (Chiv. 12:17) N’chifukwa chiyani sitiyenera kukayikira kuti Yehova adzatithandiza? Taganizirani pemphero la Yesu lomwe limapezeka mu Yohane chaputala 17. Yesu anapempha Yehova kuti aziyang’anira atumwi ake, ndipo Yehova anayankha pempheroli. Buku la Machitidwe limafotokoza mmene Yehova anathandizira atumwi kuti azilalikira mwakhama ngakhale pamene ankazunzidwa. M’pemphero lake, Yesu anapemphanso Yehova kuti aziyang’anira anthu omwe angakhulupirire uthenga womwe atumwi ankalalikira. Anthu amenewa akuphatikizapo inuyo. Yehova sanasiye kuyankha pemphero la Yesu. Iye adzakuthandizani inuyo ngati mmene anathandizira atumwi. (Yoh. 17:​11, 15, 20) Pamene mapeto akuyandikira, nthawi zina zizikhala zovuta kulalikira uthenga wabwino mwakhama. Ngakhale zili choncho, tingapeze thandizo lomwe timafunikira.—Luka 21:​12-15. w25.03 18 ¶13-14

Atumiki anga adzafuula mosangalala.—Yes. 65:14.

Anthu a Mulungu ‘amafuula mosangalala’ chifukwa choyamikira zimene Yehova wawachitira. Timakhala ndi “chimwemwe mumtima” chifukwa cha mfundo zolimbitsa chikhulupiriro, malonjezo opezeka m’Mawu a Mulungu komanso chiyembekezo chomwe chimatheka chifukwa cha nsembe ya dipo ya Khristu. Timasangalala kwambiri tikamakambirana zimenezi. (Sal. 34:8; 133:​1-3) Chikondi komanso mgwirizano pakati pa anthu a Yehova ndi makhalidwe akuluakulu amene amapezeka m’paradaiso wauzimu. Mgwirizano umenewu umasonyeza mmene moyo udzakhalire m’dziko latsopano, pamene atumiki a Yehova azidzakondana kwambiri komanso kugwirizana kuposa panopa. (Akol. 3:14) Aliyense amene akufuna kukhala wosangalala komanso wokhutira ayenera kulowa m’paradaiso wauzimu. Kaya anthu amaganiza zotani zokhudza atumiki a Yehova, iwo ali ndi mbiri yabwino kwa Yehovayo komanso onse amene amamulambira.—Yes. 65:15. w24.04 21 ¶7-8

Pitirizani . . . kulimbikitsana.—1 Ates. 5:11.

Kodi tonsefe tingathandize bwanji Akhristu amene akufuna kulowa m’banja? Njira imodzi ndi kukhala osamala ndi zimene timalankhula. (Aef. 4:29) Tingadzifunse kuti: ‘Kodi ndimakonda kuseleula anthu amene sali pa banja? Kodi ndikaona m’bale ndi mlongo amene sali pa banja akucheza ndimafulumira kuganiza kuti akufunana?’ (1 Tim. 5:13) Kuwonjezera apo, si bwino kuchititsa Akhristu ena kuganiza kuti akuperewera chifukwa chakuti sali pa banja. Tingachitetu bwino kuyesetsa kupeza mpata woti tiziyamikira Akhristu amene sali pa banja. Kodi mungatani ngati mukuona kuti zingakhale bwino m’bale ndi mlongo wina atakwatirana? Baibulo limatiuza kuti tiziganizira mmene anthu ena akumvera. (Aroma 15:2) Anthu ambiri amene sali pa banja safuna kuti ena awauze munthu woti akwatirane naye ndipo tiyenera kulemekeza maganizo awo. (2 Ates. 3:11) Pomwe ena amafuna kuti anthu awathandize koma sitiyenera kuchita zimenezi ngati sanatipemphe.—Miy. 3:27. w24.05 24-25 ¶14-15

Thanthwe lawo si lofanana ndi Thanthwe lathu.—Deut. 32:31.

Mavuto adzidzidzi akhoza kusokoneza kapena kusinthiratu moyo wathu. Koma mtima wathu umakhala m’malo podziwa kuti tili ndi Yehova Mulungu amene angatithandize. Iye akatithandiza zimatitsimikizira kuti “Yehova ndi wamoyo.” (Sal. 18:46) Koma atangonena kuti Yehova ndi wamoyo, Davide anatchulanso Mulungu kuti “Thanthwe langa.” N’chifukwa chiyani iye anayerekezera Yehova ndi thanthwe lomwe ndi lopanda moyo? Baibulo limayerekezera Yehova ndi “thanthwe” pofuna kutithandiza kumvetsa makhalidwe amene ali nawo. Nthawi zambiri mawuwa amapezeka munkhani zomutamanda zosonyeza kuti palibe wofanana naye. Malo oyamba pamene Yehova amatchulidwa kuti “Thanthwe” ndi pa Deuteronomo 32:4. Komanso popemphera, Hana ananena kuti “palibe thanthwe lofanana ndi Mulungu wathu.” (1 Sam. 2:2) Habakuku anatchulanso Yehova kuti “Thanthwe langa.” (Hab. 1:12) Amene analemba Salimo 73 anatchulanso Mulungu kuti “thanthwe la mtima wanga.” (Sal. 73:26) Ndiponso Yehova mwiniwakeyo anadzitchula kuti Thanthwe.—Yes. 44:8. w24.06 26 ¶1, 3

Yehosafati . . . anafunafuna Yehova ndi mtima wake wonse.—2 Mbiri 22:9.

Mafumu a Chiisiraeli omwe Yehova anasangalala nawo ankamutumikira ndi mtima wonse. Pofotokoza za Yosiya, Baibulo limati: “Iye asanakhale mfumu, panalibe mfumu ina imene inabwerera kwa Yehova ndi mtima wake wonse.” (2 Maf. 23:25) Nanga bwanji za Solomo yemwe pamapeto pake anachita zoipa? Baibulo limati: “Sanatumikire Yehova Mulungu wake ndi mtima wathunthu.” (1 Maf. 11:4) Ndipo ponena za Abiyamu, yemwenso anali mfumu yosakhulupirika, Baibulo limati: “Sanatumikire Yehova Mulungu wake ndi mtima wonse.” (1 Maf. 15:3) Nthawi zambiri Baibulo limagwiritsa ntchito mawu akuti “mtima” pofotokoza mmene munthu alili, zomwe zikuphatikizapo zimene amalakalaka, zimene amaganiza, khalidwe lake, luso, komanso zolinga zake. Ndiye kodi kutumikira Yehova ndi mtima wonse kumatanthauza chiyani? Munthu amene amatumikira Mulungu ndi mtima wake wonse samangomulambira chifukwa chakuti ndi zimene akuyenera kuchita. M’malomwake, amamutumikira chifukwa cha chikondi komanso mtima wodzipereka. w24.07 21 ¶4-5

Fufutani zolakwa zanga zonse.—Sal. 51:9.

Yehova amagwiritsa ntchito fanizo pofotokoza mmene amafafanizira machimo. Iye ananena kuti: “Ndidzafafaniza zolakwa zako ndipo zidzakhala ngati ndaziphimba ndi mtambo ndipo machimo ako adzakhala ngati ndawaphimba ndi mtambo waukulu.” (Yes. 44:22) Yehova akatikhululukira zimakhala ngati waphimba machimo athu ndi mtambo waukulu moti sangaonekenso. Kodi tikuphunzira chiyani pa mafanizowa? Yehova akatikhululukira machimo athu sitiyenera kudziimba mlandu kwa moyo wathu wonse. Magazi a Yesu Khristu anachititsa kuti ngongole yathu yonse ifafanizidwe. Zili ngati pamene panalembedwa ngongoleyo sipakuonekanso chilichonse. Umu ndi mmene Yehova amatikhululukira ndi mtima wonse tikalapa machimo athu. Chifundo cha Yehova chimatithandiza kuti tikhale nayenso pa ubwenzi wabwino ndiponso kuti tisapitirize kudziimba mlandu chifukwa cha machimo athu. w25.02 10 ¶11-14

Mulungu akukusonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu, . . . nʼcholinga choti ulape.—Aroma 2:4.

Akulu omwe ali m’komiti amakhala ndi udindo pamaso pa Yehova wothandiza kuti mpingo ukhale woyera. (1 Akor. 5:7) Amafunanso kuthandiza anthu ochimwa kuti alape ngati n’kotheka. Kuti zimenezi zitheke iwo ayenera kukhala ndi maganizo abwino, n’kumayembekezera kuti munthuyo akhoza kusintha. Chifukwa chiyani? Chifukwa iwo amafuna kutsanzira Yehova yemwe ndi “wachikondi chachikulu komanso wachifundo.” (Yak. 5:11) Mtumwi Yohane nayenso ankakonda abale ndi alongo ake. Iye analemba kuti: “Ana anga okondedwa, ndikukulemberani zinthu izi kuti musachite tchimo. Komabe, wina akachita tchimo, tili ndi wotithandiza wolungama, Yesu Khristu, amene ali ndi Atate.” (1 Yoh. 2:1) N’zomvetsa chisoni kuti nthawi zina Mkhristu sangafune kulapa. Zikatero amayenera kuchotsedwa mumpingo. w24.08 25 ¶19-20

Khalani ndi chikhulupiriro cholimba.—1 Akor. 16:13.

Nthawi zina mungayambe kuyerekezera zimene mumachita ndi zimene ena amachita. N’chifukwa chiyani muyenera kupewa zimenezi? Chifukwa chakuti Yehova samakuyerekezerani ndi ena. (Agal. 6:4) Mwachitsanzo, Mariya anapatsa Yesu mphatso ya mafuta amtengo wapatali. (Yoh. 12:​3-5) Koma mkazi wina wamasiye anapereka kukachisi tindalama tiwiri tochepa mphamvu. (Luka 21:​1-4) Koma Yesu anaona kuti akazi onsewa anasonyeza chikhulupiriro. Ndipo Atate wake Yehova, amayamikira zilizonse zimene mumachita chifukwa choti munadzipereka kwa iye ndipo mumamukonda, kaya zikhale zochepa bwanji. Tonsefe nthawi zina timakayikira zinthu zina. Koma Mawu a Mulungu angatithandize kuti tisiye kukayikira. Choncho muzichita zonse zimene mungathe kuti musiye kukayikira ndipo mukatero mtima wanu udzakhala m’malo. Yehova amaona kuti inuyo panokha ndinu ofunika. Iye amayamikira zonse zimene mumachita kuti muzimutumikira ndipo adzakupatsani mphoto. Yehova amakonda komanso kuganizira atumiki ake onse okhulupirika. w24.10 25 ¶3; 29 ¶17-18