Yoswa 24:1-33

  • Yoswa anafotokoza mbiri ya Aisiraeli (1-13)

  • Anawalimbikitsa kutumikira Yehova (14-24)

    • “Ine ndi banja langa tizitumikira Yehova” (15)

  • Yoswa anachita pangano ndi Aisiraeli (25-28)

  • Yoswa anamwalira nʼkuikidwa mʼmanda (29-31)

  • Mafupa a Yosefe anaikidwa mʼmanda ku Sekemu (32)

  • Eliezara anamwalira nʼkuikidwa mʼmanda (33)

24  Kenako Yoswa anasonkhanitsa mafuko onse a Isiraeli ku Sekemu. Iye anaitanitsa akulu a Isiraeli, atsogoleri, oweruza ndi akapitawo+ ndipo onse anaima pamaso pa Mulungu woona.  Yoswa anauza anthuwo kuti: “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Kale makolo anu,+ kuphatikizapo Tera, bambo ake a Abulahamu ndi Nahori, ankakhala kutsidya lina la Mtsinje,*+ ndipo ankatumikira milungu ina.+  Patapita nthawi, ndinatenga kholo lanu Abulahamu+ kuchokera kutsidya lina la Mtsinje.* Ndinamuyendetsa mʼdziko lonse la Kanani ndipo ndinachulukitsa mbadwa zake.*+ Ndinamʼpatsa Isaki+  ndipo Isaki ndinamʼpatsa Yakobo ndi Esau.+ Pambuyo pake Esau ndinamʼpatsa phiri la Seiri kuti likhale lake.+ Kenako Yakobo ndi ana ake anapita ku Iguputo.+  Patapita nthawi ndinatumiza Mose ndi Aroni+ ndipo ndinachititsa kuti ku Iguputo kugwe miliri.+ Kenako ndinakutulutsani ku Iguputoko.  Pamene ndinkatulutsa makolo anu ku Iguputo,+ atatsala pangʼono kufika kunyanja, Aiguputo anawathamangira ndi magaleta ankhondo ndiponso amuna okwera pamahatchi, mpaka ku Nyanja Yofiira.+  Iwo anayamba kufuulira Yehova.+ Choncho ndinaika mdima pakati pa iwo ndi Aiguputuwo, ndipo ndinawamiza ndi madzi amʼnyanja.+ Munaona ndi maso anu zimene ndinachita ku Iguputo.+ Kenako inu munakhala mʼchipululu zaka zambiri.*+  Ndipo ndinakufikitsani kudziko la Aamori amene ankakhala kutsidya lina* la Yorodano. Iwo anayamba kumenyana nanu+ koma ndinawapereka mʼmanja mwanu kuti mutenge dziko lawo kukhala lanu moti ndinawafafaniza pamaso panu.+  Kenako Balaki mwana wa Zipori, mfumu ya Mowabu, ananyamuka kukamenyana ndi Aisiraeli. Iye anaitanitsa Balamu, mwana wa Beori kuti akutemberereni.+ 10  Koma ine sindinafune kumvera Balamu.+ Choncho iye anakudalitsani mobwerezabwereza+ ndipo ndinakulanditsani mʼmanja mwake.+ 11  Kenako munawoloka Yorodano+ nʼkufika ku Yeriko.+ Atsogoleri a* ku Yeriko, omwe ndi Aamori, Aperezi, Akanani, Ahiti, Agirigasi, Ahivi ndi Ayebusi, anayamba kumenyana nanu, koma ine ndinawapereka mʼmanja mwanu.+ 12  Ndinawachititsa mantha inu musanafike, choncho anakuthawani+ ngati mmene anachitira mafumu awiri a Aamori. Iwo sanathawe chifukwa cha lupanga lanu kapena chifukwa cha uta wanu.+ 13  Ndinakupatsani dziko limene simunalikhetsere thukuta komanso mizinda imene simunaimange,+ ndipo munayamba kukhalamo. Mukudyanso zipatso za mitengo ya mpesa ndi mitengo ya maolivi imene simunadzale.’+ 14  Choncho muziopa Yehova ndi kumʼtumikira ndi mtima wathunthu* komanso mokhulupirika.*+ Chotsani milungu imene makolo anu ankatumikira kutsidya lina la Mtsinje* ndi ku Iguputo,+ ndipo muzitumikira Yehova. 15  Ngati kutumikira Yehova kukukunyansani, sankhani lero amene mukufuna kumʼtumikira,+ kaya milungu imene makolo anu ankaitumikira kutsidya lina la Mtsinje,*+ kapena milungu ya Aamori amene mukukhala mʼdziko lawo.+ Koma ine ndi banja langa tizitumikira Yehova.” 16  Anthuwo anayankha kuti: “Sitingayerekeze kusiya Yehova nʼkumatumikira milungu ina. 17  Yehova Mulungu wathu ndi amene anatitulutsa mʼdziko la Iguputo pamodzi ndi makolo athu,+ kutichotsa kudziko lomwe tinali akapolo.+ Iye anachita zizindikiro zazikulu pamaso pathu+ ndi kutiteteza njira yonse. Anatitetezanso kwa anthu onse amene tinadutsa pakati pawo.+ 18  Yehova anathamangitsa mitundu yonse ya anthu pamaso pathu, kuphatikizapo Aamori amene ankakhala mʼdzikoli. Choncho nafenso tipitiriza kutumikira Yehova chifukwa iye ndi Mulungu wathu.” 19  Ndiyeno Yoswa anauza anthuwo kuti: “Simungathe kutumikira Yehova, chifukwa iye ndi Mulungu woyera.+ Iye ndi Mulungu amene amafuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha.+ Sadzakhululuka zolakwa zanu* ndi machimo anu.+ 20  Mukasiya Yehova nʼkuyamba kutumikira milungu yachilendo, iyenso adzakutembenukirani nʼkukuchitirani zoipa ndi kukufafanizani pambuyo pokuchitirani zabwino.”+ 21  Koma anthuwo anayankha Yoswa kuti: “Ayi! Ife tizitumikira Yehova.”+ 22  Choncho Yoswa anauza anthuwo kuti: “Mukudzichitira umboni wotsimikizira kuti mwasankha nokha kutumikira Yehova.”+ Ndiyeno anthuwo anati: “Inde! Ndife mboni.” 23  “Choncho chotsani milungu yachilendo imene ili pakati panu ndipo perekani mitima yanu kwa Yehova Mulungu wa Isiraeli.” 24  Anthuwo anayankha Yoswa kuti: “Tizitumikira Yehova Mulungu wathu komanso kumumvera.” 25  Ndiyeno Yoswa anachita pangano ndi anthuwo ndipo anapereka lamulo ndi chigamulo ku Sekemu. 26  Kenako Yoswa analemba mawu amenewa mʼbuku la Chilamulo cha Mulungu.+ Atatero anatenga mwala waukulu+ ndi kuuika pansi pa mtengo waukulu kwambiri umene uli pafupi ndi malo opatulika a Yehova. 27  Yoswa anauza anthu onsewo kuti: “Mwauona mwalawu? Mwala umenewu ukhala mboni yathu,+ chifukwa wamva mawu onse amene Yehova watiuza, ndipo ukhala mboni yanu kuti musadzakane Mulungu wanu.” 28  Atatero, Yoswa anauza anthuwo kuti azipita, aliyense kucholowa chake.+ 29  Patapita nthawi, Yoswa mwana wa Nuni, mtumiki wa Yehova, anamwalira ali ndi zaka 110.+ 30  Kenako anamuika mʼmanda mʼgawo la cholowa chake ku Timinati-sera,+ kudera lamapiri la Efuraimu, kumpoto kwa phiri la Gaasi. 31  Aisiraeli anapitiriza kutumikira Yehova masiku onse amene Yoswa anali ndi moyo komanso masiku onse a akulu amene anakhalabe ndi moyo Yoswa atamwalira, omwe ankadziwa zinthu zonse zimene Yehova anachitira Aisiraeli.+ 32  Mafupa a Yosefe,+ amene Aisiraeli anabweretsa kuchokera ku Iguputo anawaika mʼmanda ku Sekemu, pamalo amene Yakobo anagula kwa ana a Hamori,+ bambo wa Sekemu. Malowo anawagula ndi ndalama zasiliva zokwana 100,+ ndipo anakhala cholowa cha ana a Yosefe.+ 33  Nayenso Eleazara mwana wa Aroni anamwalira.+ Choncho anamuika mʼmanda mʼphiri la Pinihasi mwana wake,+ limene anapatsidwa mʼdera lamapiri la Efuraimu.

Mawu a M'munsi

Umenewu ndi mtsinje wa Firate.
Umenewu ndi mtsinje wa Firate.
Kapena kuti, “mbewu yake.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “masiku ambiri.”
Imeneyi ndi mbali yakumʼmwawa.
Mabaibulo ena amati, “Nzika za.”
Kapena kuti, “mosalakwitsa.”
Kapena kuti, “mʼchoonadi.”
Umenewu ndi mtsinje wa Firate.
Umenewu ndi mtsinje wa Firate.
Kapena kuti, “Sadzakhululuka kugalukira kwanu.”