Yoswa 3:1-17

  • Aisiraeli anawoloka Yorodano (1-17)

3  Mʼmamawa kutacha, Yoswa ndi Aisiraeli* onse ananyamuka ku Sitimu+ nʼkuyenda kukafika kumtsinje wa Yorodano. Iwo anagona kumeneko asanawoloke.  Patatha masiku atatu, akapitawo+ a anthuwo anapita mumsasa wonse,  ndipo anauza anthuwo kuti: “Mukangoona likasa la pangano la Yehova Mulungu wanu litanyamulidwa ndi Alevi omwe anali ansembe,+ musamuke pamalo panu nʼkuyamba kulitsatira,  koma musaliyandikire. Pakati pa inu ndi likasalo pakhale mtunda wokwana mikono pafupifupi 2,000.* Mukatero mudzadziwa koyenera kupita, chifukwa kumeneko simunayambe mwapitako.”  Tsopano Yoswa anauza anthuwo kuti: “Mudziyeretse,+ chifukwa mawa Yehova akuchitirani zinthu zodabwitsa.”+  Kenako Yoswa anauza ansembe kuti: “Nyamulani likasa+ la pangano ndipo muziyenda patsogolo pa anthuwa.” Choncho ansembewo ananyamula likasa la panganolo nʼkumayenda patsogolo pa anthuwo.  Ndipo Yehova anauza Yoswa kuti: “Lero ndiyamba kukulemekeza pamaso pa Aisiraeli onse+ nʼcholinga choti adziwe kuti ndidzakhala nawe+ ngati mmene ndinkachitira ndi Mose.+  Ulamule ansembe onyamula likasa la pangano kuti: ‘Mukakafika mʼmbali mwa mtsinje wa Yorodano, mukalowe mʼmadzimo nʼkuima.’”+  Ndiyeno Yoswa anauza Aisiraeli kuti: “Bwerani kuno mudzamve mawu a Yehova Mulungu wanu.” 10  Kenako Yoswa anati: “Mukaona zimene zichitike pano, mudziwa kuti Mulungu wamoyo ali pakati panu+ ndipo adzathamangitsadi Akanani, Ahiti, Ahivi, Aperezi, Agirigasi, Aamori ndi Ayebusi.+ 11  Likasa la pangano la Ambuye wa dziko lonse lapansi liyenda patsogolo panu kulowa mumtsinje wa Yorodano. 12  Tsopano tengani amuna 12 mʼmafuko a Isiraeli, mwamuna mmodzi pafuko lililonse.+ 13  Zimene zichitike nʼzakuti, mapazi a ansembe onyamula likasa la Yehova, Ambuye wa dziko lonse lapansi, akangoponda mʼmadzi a mumtsinje wa Yorodano, madzi ochokera kumtunda aima nʼkukhala ngati khoma.”+ 14  Choncho anthuwo anachotsa mahema awo, nʼkunyamuka kuti awoloke Yorodano, ndipo ansembe onyamula likasa+ la pangano anali patsogolo pawo. 15  Onyamula Likasawo atangofika pamtsinje wa Yorodano, nʼkuponda madzi a mʼmphepete mwake (mtsinje wa Yorodano unkasefukira+ nyengo yonse yokolola), 16  madzi ochokera kumtunda anaima ngati khoma. Ndipo anakhala ngati damu lomwe linasefukira mpaka kukafika kutali kwambiri. Izi zinachitikira ku Adamu, mzinda woyandikana ndi mzinda wa Zeretani. Koma madzi akumunsi omwe ankapita kunyanja ya Araba, yomwe ndi Nyanja Yamchere,* anaphwa. Choncho, madzi a mtsinjewo anagawikana, ndipo anthuwo anawolokera kutsidya lina, pafupi ndi Yeriko. 17  Ansembe onyamula likasa la pangano la Yehova anaima panthaka youma+ pakati pa mtsinje wa Yorodano. Anaimabe choncho pamene Aisiraeli onse ankawoloka panthaka youmayo,+ mpaka mtundu wonse unawoloka mtsinje wa Yorodano.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira: “ana a Isiraeli.”
Umenewu ndi mtunda wa mamita 890. Onani Zakumapeto B14.
Imeneyi ndi Nyanja Yakufa.