Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Mateyo 9:1-38
9 Conco Yesu anakwela bwato n’kuolokela ku tsidya lina, ndipo analowa mu mzinda wakwao.
2 Kumeneko, anthu anamubweletsela munthu wofa ziwalo atamugoneka pa macila. Ataona cikhulupililo cao, Yesu anauza wofa ziwaloyo kuti: “Limba mtima mwanawe, macimo ako akhululukidwa.”
3 Tsopano alembi ena mumtima anati: “Munthu uyu akunyoza Mulungu.”
4 Podziwa maganizo ao, Yesu anati, “N’cifukwa ciani mukuganiza zinthu zoipa m’mitima mwanu?
5 Mwacitsanzo, capafupi n’citi, kukamba kuti, ‘Macimo ako akhululukidwa,’ kapena kukamba kuti, ‘Nyamuka uyambe kuyenda’?
6 Koma kuti mudziwe kuti Mwana wa munthu ali ndi mphamvu zokhululukila macimo pa dziko lapansi . . .” Kenako anauza wofa ziwaloyo kuti, “Nyamuka, nyamula macila akowa, pita ku nyumba kwanu.”
7 Iye ananyamuka n’kumapita kwao.
8 Khamu la anthulo litaona zimenezi linagwidwa ndi mantha, ndipo linatamanda Mulungu amene anapeleka mphamvu zotelo kwa anthu.
9 Atacoka pamenepo, Yesu anaona munthu wina dzina lake Mateyo, atakhala pansi mu ofesi yokhomelamo misonkho. Ndipo anamuuza kuti: “Khala wotsatila wanga.” Nthawi yomweyo iye ananyamuka ndi kumutsatila.
10 Patapita nthawi, Yesu anali kudya m’nyumba, ndipo okhometsa misonkho ambili komanso anthu ocimwa, anabwela n’kuyamba kudya naye pamodzi ndi ophunzila ake.
11 Koma Afarisi ataona zimenezi anafunsa ophunzila ake kuti: “N’cifukwa ciani mphunzitsi wanu amadya ndi okhometsa misonkho komanso ocimwa?”
12 Yesu atamva zimenezi anati: “Anthu athanzi safunikila dokotala, koma odwala ndio amamufuna.
13 Cotelo, pitani mukamvetsetse tanthauzo la mau akuti: ‘Ndifuna cifundo osati nsembe.’ Pakuti n’nabwela kudzaitana anthu ocimwa osati olungama.”
14 Kenako ophunzila a Yohane anabwela kwa iye n’kumufunsa kuti: “N’cifukwa ciani ife ndi Afarisi timasala kudya, koma ophunzila anu sasala kudya?”
15 Yesu anawayankha kuti: “Anzake a mkwati sakhala acisoni ngati mkwatiyo ali nao limodzi, amatelo kodi? Koma masiku adzafika pamene mkwatiyo adzacotsedwa pakati pao, ndipo panthawiyo adzasala kudya.
16 Palibe munthu amene amasokelela cigamba ca nsalu yatsopano pa cobvala cakunja cakale, cifukwa akatelo cigamba catsopanoco cimaguza cobvalaco, ndipo pong’ambikapo pamakula kwambili.
17 Ndiponso anthu sathila vinyo watsopano m’matumba acikumba akale. Akatelo, matumba a vinyowo amaphulika, ndipo vinyoyo amataika matumbawo n’kuonongeka. Koma anthu amathila vinyo watsopano m’matumba acikumba atsopano, ndipo zonse ziwili zimasungika bwino.”
18 Pamene iye anali kuwauza zimenezi, kunafika wolamulila wina amene anamugwadila ndi kumuuza kuti: “Pano ndikukamba, mwana wanga wamkazi ayenela kuti wamwalila. Koma tiyeni mukaike dzanja lanu pa iye, ndipo akhalanso ndi moyo.”
19 Pamenepo Yesu ananyamuka pamodzi ndi ophunzila ake n’kumutsatila.
20 Tsopano mai wina wodwala matenda otaya magazi kwa zaka 12, anamuyandikila kumbuyo kwake n’kugwila ulusi wopota wa cobvala cake cakunja,
21 cifukwa mumtima mwake anali kunena kuti: “Ndikangogwila cobvala cake cakunja ndicila ndithu.”
22 Pamenepo Yesu anatembenuka, ndipo atamuona anati: “Limba mtima mwanawe! Cikhulupililo cako cakucilitsa.” Kucokela ola limenelo, maiyo anacila.
23 Ndiyeno Yesu atalowa m’nyumba ya wolamulila uja, anaona anthu oliza zitolilo, komanso anthu ambili akulila mokweza.
24 Ndiyeno Yesu anati: “Tulukani, cifukwa mtsikana wamng’onoyu sanamwalile koma wagona.” Anthuwo atamva zimenezi anayamba kumuseka monyodola.
25 Atangowatulutsa panja anthuwo, Yesu analowa n’kugwila dzanja la mtsikanayo, ndipo iye anauka.
26 Nkhani imeneyi inafala m’dela lonselo.
27 Yesu pocoka kumeneko, amuna awili akhungu anam’tsatila. Iwo anali kupfuula kuti: “Ticitileni cifundo inu Mwana wa Davide.”
28 Atalowa m’nyumba, akhungu aja anafika kwa Yesu, ndipo iye anawafunsa kuti: “Kodi muli ndi cikhulupililo cakuti ndingacite zimenezi?” Iwo anamuyankha kuti: “Inde Ambuye.”
29 Kenako anawagwila m’maso ndi kuwauza kuti: “Zicitike mogwilizana ndi cikhulupililo canu.”
30 Pamenepo anayamba kuona. Ndiyeno Yesu anawacenjeza mwamphamvu kuti: “Samalani kuti aliyense asadziwe zimenezi.”
31 Koma atatuluka panja, anafalitsa za iye m’dela lonselo.
32 Pamene iwo anali kucoka, anthu anamubweletsela munthu wosalankhula wogwidwa ndi ciwanda.
33 Ciwandaco atacitulutsa, munthu wosalankhulayo anayamba kulankhula. Khamu la anthulo litaona zimenezi, linadabwa kwambili ndipo linati: “Zotelezi sitinazionepo mu Isiraeli.”
34 Koma Afarisi anali kunena kuti: “Ameneyu amatulutsa ziwanda ndi mphamvu za wolamulila ziwanda.”
35 Ndiyeno Yesu anayamba ulendo woyendela mizinda ndi midzi yonse. Anali kuphunzitsa m’masunagoge ao, kulalikila uthenga wabwino, ndi kucilitsa matenda a mtundu ulionse komanso zofooka zilizonse.
36 Ataona cikhamu ca anthuwo, anawamvela cisoni cifukwa anali omyuka-myuka komanso otaika ngati nkhosa zopanda m’busa.
37 Kenako iye anauza ophunzila ake kuti: “Zoonadi, zokolola n’zoculuka koma anchito ndi ocepa.
38 Conco pemphani Mwini zokolola kuti atumize anchito okakolola.”

