Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Mateyo 28:1-20

  • Yesu aukitsidwa (1-10)

  • Asilikali apatsidwa ndalama kuti azikamba zabodza (11-15)

  • Lamulo la kupanga ophunzila (16-20)

28  Pambuyo pa tsiku la Sabata, m’matandakuca pa tsiku loyamba la mlunguwo, Mariya Mmagadala ndi Mariya wina uja anapita kukaona mandawo. 2  Ndipo panali patacitika cibvomezi camphamvu, cifukwa mngelo wa Yehova* anali atatsika kumwamba ndi kubwela kudzagubuduzila kumbali cimwalaco n’kukhalapo. 3  Maonekedwe ake anali owala ngati mphenzi, ndipo zobvala zake zinali zoyela mbee! 4  Cifukwa coopa mngeloyo, alondawo ananjenjemela, ndipo anangouma gwa ngati akufa! 5  Koma mngeloyo anauza azimai aja kuti: “Musacite mantha cifukwa ndidziwa kuti mukufuna Yesu, amene anaphedwa pa mtengo. 6  Iye sali kuno cifukwa wauka kwa akufa, monga ananenela. Bwelani muone pamene panali mtembo wake. 7  Ndiyeno pitani mwamsanga mukauze ophunzila ake kuti iye wauka kwa akufa, ndipo watsogola kupita ku Galileya. Mukamuona kumeneko. Musaiwale zimene ndakuuzani.” 8  Nthawi yomweyo, azimaiwo anacoka pa mandapo ali ndi mantha komanso cisangalalo cosaneneka. Ndipo anathamanga kukauza ophunzila ake zimenezi. 9  Mwadzidzidzi Yesu anakumana nao n’kunena kuti, “Moni azimai!” Iwo anafika pafupi ndi iye. Ndiyeno anagwada ndi kugwila mapazi ake n’kumuwelamila. 10  Kenako Yesu anawauza kuti: “Musacite mantha! Pitani mukauze abale anga kuti apite ku Galileya, ndipo akandiona kumeneko.” 11  Ali m’njila, ena mwa asilikali olonda aja anapita mu mzinda kukafotokozela ansembe aakulu zonse zimene zinacitika. 12  Ansembe aakuluwo anakumana pamodzi ndi akulu n’kukambilana nkhaniyo. Kenako anapeleka ndalama zambili zasiliva kwa asilikaliwo 13  n’kuwauza kuti: “Muzinena kuti, ‘Ophunzila ake anabwela usiku n’kuba mtembo wake ife tili mtulo.’ 14  Ndipo bwanamkubwa akamva za nkhaniyi, tikamba naye.* Inu musade nkhawa.” 15  Conco, anatenga ndalama zasilivazo n’kucita mmene anawalangizila, ndipo nkhaniyi yakhala yofala pakati pa Ayuda mpaka lelo. 16  Koma ophunzila 11 aja anapita ku Galileya, ku phili, kumene Yesu anawauza kuti akakumane. 17  Atamuona, anamugwadila, koma ena anakaikila ngati analidi Yesu. 18  Yesu anafika pafupi n’kuwauza kuti: “Ulamulilo wonse wapelekedwa kwa ine, kumwamba ndi padziko lapansi. 19  Conco pitani mukapange anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzila. Muziwabatiza m’dzina la Atate, la Mwana, ndi la mzimu woyela, 20  ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene n’nakulamulani. Ndipo dziwani kuti ine ndili nanu pamodzi masiku onse mpaka cimalizilo ca nthawi ino.”*

Mau a m'Munsi

^ Kucokela ku Cigiriki, “nkhaniyi, tidzamunyengelela.”