Ngakhale kuti timacokela kosiyana-siyana ndipo timakamba zinenelo zosiyana-siyana, timagwilizana cifukwa tili ndi colinga cimodzi. Cimene timafuna kwambili ndi kulemekeza Yehova, Mwiniwake Baibulo ndi Mlengi wa zinthu zonse. Timalimbikila kutsatila Yesu Kristu ndipo timanyadila kukhala Akristu. Aliyense wa ife amapatula nthawi yothandiza anthu kudziŵa Baibulo ndi Ufumu wa Mulungu. Cifukwa cakuti timalalikila za Yehova Mulungu ndi Ufumu wake, timachedwa Mboni za Yehova.

Onani zili pa webusaiti yathu.Ŵelengani Baibulo pa intaneti. Tidziŵeni bwino ife ndi zimene timakhulupilila