Cinyanja
Zokhudza Mboni za Yehova?
https://cms-imgp.jw-cdn.org/img/p/1011228/univ/art/1011228_univ_sqr_xl.jpg

Zokhudza Ife

Kodi Mboni za Yehova Ndani?

Mboni za Yehova ndi cipembedzo cogwilizana pa dziko lonse. Timalambila Yehova amene ndi Mlengi komanso Mulungu wa Mphamvu zonse. (Masalimo 83:18; Cibvumbulutso 4:11) Ndife Akhristu amene timakhulupilila kuti Yesu Khristu ndi Mwana wa Mulungu komanso Mpulumutsi wathu. (Yohane 3:16; Macitidwe 4:10-12) Zonse zimene timakhulupilila zimacokela m’Baibo. (2 Timoteyo 3:16) Tikupemphani kuti mufufuze zimene timakhulupilila pogwilitsila nchito webusaiti ino komanso Baibo yanu.

Kuti mudziwe zambili zokhudza ife onelelani Vidiyo ya mutu wakuti Mboni za Yehova—Kodi Ndife Anthu Otani?

Ziwelengelo

Zocitika m’madela

Mafunso Ofunsidwa Kawili-kawili

Kodi Mboni za Yehova ndi Akristu?

Dziŵani zimene zimatisiyanitsa ndi zipembedzo zina zimene zimati n’zacikristu.

Tilembeleni Kapena Tumani Foni

Pemphani kuti wa Mboni adzakucezeleni

Kambilanani nkhani ya m’Baibo na Mboni za Yehova, kapena laŵani maphunzilo a Baibo amene timapeleka.

Kapezekemponi pa Misonkhano ya Mboni za Yehova

Fufuzani kumene timakumana komanso mmene timalambilila. Onse ni olandilidwa ndipo sipakhala kuyendetsa mbale ya zopeleka.

Dziŵitsani Mboni za Yehova

Maadilesi ndi manambala a foni a maofesi athu a pa dziko lonse.

Kukaona Malo pa Beteli

Fufuzani kumene mungayende kukaona malo pa Beteli kufupi na kwanu.