Kufotokoza Mavesi a m’Baibo

Dziŵani tanthauzo lenileni la mavesi komanso mawu ena odziŵika bwino a m’Baibo. Ŵelengani mawuwo m’nkhani yake yonse na kudziŵa zimene zinapangitsa kuti alembedwe. Mbaliyi ikuthandizani kumvetsa mozama mawu a Mulungu pogwilitsa nchito mawu am’munsi komanso malifalensi.

Kufotokoza Salimo 37:4—“Udzikondweretsenso mwa Yehova”

Kodi salimoyi imatithandiza bwanji kukhala anthu anzelu komanso kukhala na makhalidwe amene Mulungu amavomeleza?

Salimo 46:10—“Khalani Chete, Ndipo Dziŵani Kuti Ine Ndine Mulungu”

Kodi vesili litanthauze kungokhala chete m’chalichi?

Miyambo 3:5, 6 Lafotokozedwa—“Usamadalile Luso Lako Lomvetsa Zinthu”

Mungaonetse bwanji kuti mumakhulupilila kwambili Mulungu kuposa inu mwini?

Kufotokoza Miyambo 16:3—“Peleka Zocita Zako kwa AMBUYE”

Ndi zifukwa ziwili ziti zimene zimapangitsa kuti anthu azipempha Mulungu kuwathandiza posankha zocita?

Kufotokoza Miyambo 17:17—“Bwenzi Lenileni Limakukonda Nthawi Zonse”

Mwambi uwu ufutokoza bwino tanthauzo la bwenzi lenileni.

Yesaya 41:10—“Usacite Mantha, Pakuti Ndili Nawe”

Yehova anagwilitsa nchito mfundo zitatu pofuna kutsimikizila anthu ake okhulupilika kuti adzawathandiza.

Kufotokoza Yeremiya 29:11—“Ndikudziwa Bwino Zimene Ndikuganiza Zokhudza Inu”

Kodi Mulungu anakonzelatu zokhudza munthu wina aliyense?

Kufotokoza Aroma 10:13—”Adzaitana pa Dzina la Ambuye”

Mulungu anapatsa anthu onse mwayi wopulumuluka na kupeza moyo wosatha. Koma kuti tikapulumuke, tifunika kuitana pa la Mulungu Wamphamvuyonse.