Cinyanja
Mukapezekepo pa Msonkhano wa 2026 wakuti: “Cimwemwe Camuyaya”
https://cms-imgp.jw-cdn.org/img/p/1102026198/univ/art/1102026198_univ_sqr_xl.jpg

Tikukuitanani

Cimwemwe Camuyaya

Msonkhano Wacigao wa Mboni za Yehova wa 2026

Pezani Msonkhano Kufupi ndi Kwanu

Simudzalipila kuti mulowe Sikudzakhala kuyendetsa mbale ya zopeleka

Zomwe Zili Pamsonkhanowu

Tsiku Loyamba: Mudzaphunzila zimene Baibo imakamba zotsimikizila kuti Mulungu ndi Mwana wake, Yesu, amafuna kuti mukhale acimwemwe.

Tsiku Laciwili: Mudzaona mmene mungakhalile ndi cimwemwe cosatha mwa kuphunzila za ulaliki wochuka wa Yesu wa pa phili.

Tsiku Lothela: M’nkhani yakuti “Kodi Munacipeza Cuma ca Mtengo Wapatali?” mudzaona mmene coonadi ca m’Baibo cathandizila anthu mamiliyoni kupeza cimwemwe cacikulu.

Sewelo Lalikulu

Mbili ya Umoyo wa Yesu: Gao 4, 5 ndi 6

Mudzaona Yesu akuphunzitsa anthu, kucilitsa odwala, ndi kuukitsa akufa. Pa tsiku lililonse la msonkhanowu, tizionelela gao limodzi la mavidiyo ocititsa cidwi amenewa.

Pitani pa jw.org kuti muone pulogilamu yonse ndi kuonelela mavidiyo otsatila:

N’ciyani Cimacitika pa Msonkhano Wathu Wacigawo?

Onani zomwe zimacitika pamisonkhano ikulu-ikulu ya Mboni za Yehova.

Onani zina zomwe zili pamsonkhano wa caka cino.

Ndi motani mmene Yesu anagwilitsila nchito mphatso zake kuti athandize ena?

Onelelani magao a seweloli amene anaonetsedwa pa misonkhano ya mu 2024 ndi 2025.