Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Mateyo 3:1-17

  • Ulaliki wa Yohane M’batizi (1-12)

  • Ubatizo wa Yesu (13-17)

3  M’masiku amenewo, Yohane M’batizi anapita ku cipululu ca Yudeya, ndi kuyamba kulalikila. 2  Anali kulalikila kuti: “Lapani, cifukwa Ufumu wa kumwamba wayandikila.” 3  Mneneli Yesaya anali kukamba za ameneyu pamene anati: “Winawake akupfuula m’cipululu kuti: ‘Konzani njila ya Yehova!* Wongolani miseu yake.’” 4  Yohane anali kubvala cobvala caubweya wa ngamila ndi lamba wacikumba m’ciuno mwake. Cakudya cake cinali dzombe ndi uci. 5  Pa nthawiyo, anthu a mu Yerusalemu ndi mu Yudeya yense, komanso a m’madela onse ozungulila Yorodano anali kupita kwa iye. 6  Iye anali kuwabatiza* mu Mtsinje wa Yorodano, ndipo iwo anali kuulula macimo ao poyela. 7  Yohane ataona kuti Afarisi ndi Asaduki ambili akubwela ku ubatizowo, anawauza kuti: “Ana a njoka inu, ndani wakucenjezani kuti muthawe mkwiyo umene ukubwela? 8  Conco balani zipatso zoonetsa kulapa. 9  Musadzinamize n’kumati, ‘Tili ndi atate wathu Abulahamu.’ Pakuti ndikukuuzani kuti Mulungu angathe kusandutsa miyala iyi kukhala ana a Abulahamu. 10  Nkhwangwa yaikidwa kale pa mizu ya mitengo. Cotelo mtengo ulionse wosabala zipatso zabwino udzadulidwa ndi kuponyedwa pa moto. 11  Ine ndikukubatizani ndi madzi cifukwa mwalapa. Koma amene akubwela m’mbuyo mwanga ndi wamphamvu kuposa ine, ndipo sindine woyenela kumubvula nsapato. Ameneyo adzakubatizani ndi mzimu woyela komanso moto. 12  Fosholo yake youluzila ili m’manja mwake. Iye adzayeletsa kothelatu malo ake opunthila mbeu. Ndipo tiligu adzamututila m’nkhokwe, koma mankhusu* adzawatentha pa moto wosazimitsika.” 13  Kenako Yesu anacoka ku Galileya n’kupita kwa Yohane ku Yorodano kuti akamubatize. 14  Koma Yohaneyo anayesa kumuletsa pomuuza kuti: “Ndine amene ndiyenela kubatizidwa ndi inu, nanga bwanji inu mukubwela kwa ine?” 15  Yesu anamuyankha kuti: “Lola kuti zikhale telo pa nthawi ino, cifukwa kucita zimenezi n’koyenela kwa ife kuti tikwanilitse cilungamo conse.” Atatelo, analeka kumuletsa. 16  Yesu atabatizidwa, nthawi yomweyo anabvuuka m’madzimo. Atabvuuka, kumwamba kunatseguka, ndipo Yohane anaona mzimu wa Mulungu ukutsika ngati nkhunda kudzatela pa iye. 17  Kumwamba kunamvekanso mau akuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndimakondwela naye.”

Mau a m'Munsi

^ Kapena kuti, “kuwabviika; kuwamiza.”
^ “Mankhusu” ndi makoko amene amacotsa ku mbeu monga mpunga akapuntha, ndipo amatha kuwauluza.