Cinyanja
Zocitika Zikulu-zikulu mu Umoyo wa Yesu ali Padziko Lapansi—Zimene Zinacitika Yesu Asanayambe Utumiki Wake
https://cms-imgp.jw-cdn.org/img/p/1001061100/univ/wpub/1001061100_univ_sqr_xl.jpg
nwt masa. 548-549

A7-A

Zocitika Zikulu-zikulu mu Umoyo wa Yesu Ali Padziko Lapansi—Zimene Zinacitika Yesu Asanayambe Utumiki Wake

Zocitika za m’mabuku a Uthenga Wabwino Zandandalikidwa Motsatila Nthawi Imene Zinacitika

Machati otsatila ali ndi mapu oonetsa mmene Yesu anayendela komanso malo kumene analalikilako. Zizindikilo za ngati mivi pa mapu, sizikuonetsa njila zenizeni zimene anadutsa, koma zikuonetsa madela kumene anafikako. Cizindikilo ca “c.” citanthauza “ca m’ma.”

Zimene Zinacitika Yesu Asanayambe Utumiki Wake

NTHAWI

MALO

COCITIKA

MATEYO

MALIKO

LUKA

YOHANE

3 B.C.E.

Yerusalemu, m’kacisi

Mngelo Gabirieli auzilatu Zekariya za kubadwa kwa Yohane M’batizi

   

1:5-25

 

c. 2 B.C.E.

Nazareti; Yudeya

Mngelo Gabirieli auzilatu Mariya za kubadwa kwa Yesu; Mariya apita kukaona Elizabeti

   

1:26-56

 

2 B.C.E.

Dela lamapili la Yudeya

Kubadwa kwa Yohane M’batizi komanso kupatsidwa dzina; Zekariya alosela; Yohane apita ku cipululu

   

1:57-80

 

2 B.C.E., c. Oct. 1

Betelehemu

Yesu abadwa; “Mauyo anakhala munthu”

1:1-25

 

2:1-7

1:14

Kufupi ndi Betelehemu; Betelehemu

Mngelo alengeza uthenga wabwino kwa abusa; angelo atamanda Mulungu; abusa apita kukaona mwana

   

2:8-20

 

Betelehemu; Yerusalemu

Yesu adulidwa (pa tsiku la 8); makolo apita naye ku kacisi (pambuyo pa masiku 40)

   

2:21-38

 

1 B.C.E. kapena 1 C.E.

Yerusalemu; Betelehemu; Iguputo; Nazareti

Okhulupilila nyenyezi apita kukaona Yesu; banja lithawila ku Iguputo; Herode akupha ana aamuna; banja libwelako ku Iguputo ndipo likhazikika ku Nazareti

2:1-23

 

2:39, 40

 

12 C.E., Pasika

Yerusalemu

Yesu ali ndi zaka 12 ndipo ali mu kacisi kufunsa mafunso aphunzitsi

   

2:41-50

 
 

Nazareti

Abwelela ku Nazareti; apitiliza kumvela makolo ake; aphunzila nchito yaukalipentala; Mariya abeleka ana ena anai aamuna komanso aakazi (Mt 13:55, 56; Mko 6:3)

   

2:51, 52

 

29, cakumayambililo kwa caka

Cipululu, Mtsinje wa Yorodano

Yohane M’batizi ayamba utumiki wake

3:1-12

1:1-8

3:1-18

1:6-8