FUNSO 7
Kodi Baibo Inalosela Ciani za Nthawi Yathu Ino?
“Mtundu udzaukilana ndi mtundu wina, ndipo ufumu udzaukilana na ufumu wina . . . Zinthu zonsezi ndi ciyambi ca masautso.”
“Kudzabwela aneneli ambili abodza ndipo adzasoceletsa anthu ambili. Ndiponso cifukwa ca kuwonjezeka kwa kusamvela malamulo, cikondi ca anthu ambili cidzacepa.”
“Mukadzamva phokoso la nkhondo komanso malipoti a nkhondo, musadzacite mantha. Zimenezi ziyenela kucitika, koma mapeto adzakhala asanafikebe.”
“Kudzakhala zivomezi zamphamvu, ndipo kudzakhala njala ndi milili m’malo osiyana-siyana. Ndipo kudzaoneka zinthu zocititsa mantha, komanso kumwamba kudzaoneka zizindikilo zodabwitsa.”
“Masiku otsiliza adzakhala nthawi yosautsa komanso yobvuta. Pakuti anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, onyada, odzikuza, onyoza, osamvela makolo, osayamika, osakhulupilika, opanda cikondi, osafuna kugwilizana ndi anzao, amisece, osadziletsa, oopsya, osakonda zabwino, opeleka anzao kwa adani ao, osamva za ena, odzitukumula cifukwa ca kunyada, okonda zosangalatsa m’malo mokonda Mulungu, ndiponso onamizila kuti amapembedza Mulungu koma amakana kuti mphamvu ya kupembedzako iwasinthe.”

