FUNSO 5
Kodi m’Baibo Muli Uthenga Wotani?
“Ndidzaika cidani pakati pa iwe ndi mkaziyo, komanso pakati pa mbadwa yako ndi mbadwa yake. Mbadwa ya mkaziyo idzaphwanya mutu wako, ndipo iwe udzaivulaza cidendene.”
Genesis 3:15
“Kudzela mwa mbadwa yako, mitundu yonse yapadziko lapansi idzapeza madalitso cifukwa cakuti wamvela mau anga.”
Genesis 22:18
“Ufumu wanu ubwele. Cifunilo canu cicitike, monga kumwamba cimodzi-modzinso pansi pano.”
“Mulungu amene amapeleka mtendele adzaphwanya Satana pansi pa mapazi anu posacedwapa.”
“Koma zinthu zonse zikadzakhala pansi pake, Mwana nayenso adzaonetsa kuti ali pansi pa ulamulilo wa Mulungu, amene anaika zinthu zonse pansi pake, kuti Mulunguyo akhale zinthu zonse kwa aliyense.”
“Tsopano malonjezowo ananenedwa kwa Abulahamu ndi kwa mbadwa yake . . . , kutanthauza munthu mmodziyo, Khristu. Ndipo, ngati ndinu ake a Khristu, ndiye kuti ndinudi mbadwa za Abulahamu, olandila colowa malinga ndi lonjezolo.”
“Ufumu wa dziko wakhala Ufumu wa Ambuye wathu ndi wa Khristu wake, ndipo iye adzalamulila monga mfumu mpaka muyaya.”
“Conco cinjokaco anaciponya pansi, njoka yakale ija, iye wochedwa Mdyelekezi ndi Satana, amene akusoceletsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu. Anaponyedwa padziko lapansi limodzi ndi angelo ake.”
“Kenako anagwila cinjoka, njoka yakale ija, amene ndi Mdyelekezi komanso Satana, n’kumumanga kwa zaka 1,000.”

