FUNSO 14
Kodi Cuma Canu Mungacisamalile Bwanji?
“Munthu amene amakonda zosangalatsa adzasauka. Amene amakonda vinyo ndi mafuta sadzalemela.”
Miyambo 21:17
“Wobweleka amakhala kapolo wa wobweleketsa.”
Miyambo 22:7
“Ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja, sayamba wakhala pansi n’kuwelengela mtengo wake, kuti aone ngati ali ndi ndalama zokwanila zotsilizila nsanjayo? Cifukwa ngati sangacite zimenezo, angayale maziko ake koma osakwanitsa kuitsiliza, ndipo onse oona angayambe kumuseka n’kumanena kuti: ‘Munthu uyu anayamba bwino-bwino kumanga, koma camukanga kuti atsilize.’”
“Anthuwo atadya n’kukhuta, iye anauza ophunzila ake kuti: ‘Sonkhanitsani zonse zotsala kuti pasaonongeke ciliconse.’”

