Cinyanja
Kodi mungaphunzile bwanji zokhudza Mulungu?
https://cms-imgp.jw-cdn.org/img/p/1001061100/univ/wpub/1001061100_univ_sqr_xl.jpg
nwt masa. 8-9

FUNSO 2

Kodi mungaphunzile bwanji zokhudza Mulungu?

“Buku la Cilamulo ili lisacoke pakamwa pako. Uziliwelenga ndi kuganizila mozama masana ndi usiku, kuti uzitsatila bwino-bwino zonse zimene zalembedwamo. Ukamatelo, zizikuyendela bwino ndipo uzicita zinthu mwanzelu.”

Yoswa 1:8

“Iwo anapitiliza kuwelenga bukulo mokweza. Anapitiliza kuwelenga Cilamulo ca Mulungu woona, kucifotokoza momveka bwino ndi kumveketsa tanthauzo lake. Conco anathandiza anthuwo kumvetsa tanthauzo la zimene ankawelenga.”

Nehemiya 8:8

“Wosangalala ndi munthu amene sayenda motsatila malangizo a anthu oipa . . . , koma amakonda kwambili cilamulo ca Yehova, ndipo amawelenga ndi kuganizila mozama cilamuloco masana ndi usiku. . . . Ndipo zonse zimene amacita zimamuyendela bwino.”

Salimo 1:1-3

“Filipo anali kuthamanga m’mbali mwa galetalo, ndipo anamumva akuwelenga mokweza ulosi wa mneneli Yesaya. Ndiyeno Filipo anamufunsa kuti: ‘Kodi mukumvetsa zimene mukuwelengazo?’ Iye anayankha kuti: ‘Ndingamvetse bwanji popanda wina wondimasulila?’ Conco anapempha Filipo kuti akwele ndi kukhala naye m’galetamo.’”

Macitidwe 8:30, 31

“Kucokela pomwe dziko linalengedwa, makhalidwe a Mulungu osaoneka ndi maso akuonekela bwino. Makhalidwe akewo, ngakhalenso mphamvu zake zosatha komanso Umulungu wake, zikuonekela m’zinthu zimene anapanga, moti anthuwo alibenso cifukwa comveka cosakhulupilila kuti Mulungu aliko.”

Aroma 1:20

“Uzisinkhasinkha mozama zinthu zimenezi, ndipo uzizicita modzipeleka kuti anthu onse aone kuti ukupita patsogolo.”

1 Timoteyo 4:15

“Ndipo tiyeni tiganizilane kuti tilimbikitsane pa kukondana ndi kucita nchito zabwino. Tisaleke kusonkhana pamodzi monga mmene ena amene ali ndi cizolowezi cosafika pamisonkhano amacitila. Koma tiyeni tilimbikitsane, ndipo tionjezele kucita zimenezi, maka-maka pamene mukuona kuti tsikulo likuyandikila.”

Aheberi 10:24, 25

“Conco ngati wina akusowa nzelu, azipempha kwa Mulungu ndipo adzam’patsa, pakuti iye amapeleka moolowa manja kwa onse komanso mosatonza.”

Yakobo 1:5