Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Mateyo 1:1-25

  • Mzele wa makolo a Yesu Khristu (1-17)

  • Kubadwa kwa Yesu (18-25)

1  Buku lofotokoza mbili ya* Yesu Khristu* mwana wa Davide, mwana wa Abulahamu:  2  Abulahamu anabeleka Isaki;Isaki anabeleka Yakobo;Yakobo anabeleka Yuda ndi abale ake;  3  Yuda anabeleka Perezi ndi Zera mwa Tamara;Perezi anabeleka Hezironi;Hezironi anabeleka Ramu;  4  Ramu anabeleka Aminadabu;Aminadabu anabeleka Naasoni;Naasoni anabeleka Salimoni;  5  Salimoni anabeleka Boazi mwa Rahabi;Boazi anabeleka Obedi mwa Rute;Obedi anabeleka Jese;  6  Jese anabeleka Davide mfumu. Davide anabeleka Solomo mwa mkazi yemwe anali wa Uriya;  7  Solomo anabeleka Rehobowamu;Rehobowamu anabeleka Abiya;Abiya anabeleka Asa;  8  Asa anabeleka Yehosafati;Yehosafati anabeleka Yehoramu;Yehoramu anabeleka Uziya;  9  Uziya anabeleka Yotamu;Yotamu anabeleka Ahazi;Ahazi anabeleka Hezekiya; 10  Hezekiya anabeleka Manase;Manase anabeleka Amoni;Amoni anabeleka Yosiya; 11  Yosiya anabeleka Yekoniya ndi abale ake, Ayuda atatsala pang’ono kutengedwa ukapolo kupita ku Babulo. 12  Ku Babuloko, Yekoniya anabeleka Salatiyeli;Salatiyeli anabeleka Zerubabele; 13  Zerubabele anabeleka Abiyudi;Abiyudi anabeleka Eliyakimu;Eliyakimu anabeleka Azoro; 14  Azoro anabeleka Zadoki;Zadoki anabeleka Akimu;Akimu anabeleka Eliyudi; 15  Eliyudi anabeleka Eliyezara;Eliyezara anabeleka Matani;Matani anabeleka Yakobo; 16  Yakobo anabeleka Yosefe mwamuna wa Mariya. Mariyayu ndiye anabeleka Yesu, wochedwa Khristu. 17  Conco mibadwo yonse, kucokela pa Abulahamu kukafika pa Davide inalipo 14; kucokela pa Davide mpaka pamene Ayuda anatengedwa ukapolo kupita ku Babulo, panali mibadwo 14; ndipo kucokela pamene Ayuda anatengedwa ukapolo kupita ku Babulo, mpaka kukafika pa Khristu panali mibadwo 14. 18  Koma kubadwa kwa Yesu Khristu kunali motele: Pa nthawi imene Mariya mai ake anali wotomeledwa kwa Yosefe, Mariyayo anapezeka kuti ali ndi pathupi mwa mzimu woyela* asanatengane. 19  Komabe, cifukwa Yosefe mwamuna* wake anali wolungama, anaganiza zomusudzula mwamseli kuti asamucititse manyazi kwa anthu. 20  Koma ataiganizila mofatsa nkhaniyi, mngelo wa Yehova* anaonekela kwa iye m’maloto, n’kumuuza kuti: “Yosefe, mwana wa Davide, usaope kutenga Mariya mkazi wako ndi kupita naye ku nyumba kwako, cifukwa pathupi pamene alinapo pakhala mwa mzimu woyela. 21  Iye adzabeleka mwana wamwamuna ndipo udzamuche Yesu,* cifukwa iyeyo adzapulumutsa anthu ake ku macimo ao.” 22  Zonsezi zinacitikadi, ndipo zinakwanilitsa mau amene Yehova* anakamba kudzela mwa mneneli wake, akuti: 23  “Tamvelani! Namwali adzakhala ndi pathupi n’kubeleka mwana wamwamuna, ndipo adzamupatsa dzina lakuti Emanuweli.” Dzinali polimasulila limatanthauza kuti “Mulungu ali nafe.” 24  Kenako Yosefe anauka n’kucita zimene mngelo wa Yehova* anamulangiza. Anatenga mkazi wakeyo n’kupita naye ku nyumba. 25  Koma sanagone naye mkaziyo kufikila atabeleka mwana wamwamuna, ndipo Yosefe anacha mwanayo dzina lakuti Yesu.

Mau a m'Munsi

^ Kapena kuti, “lofotokoza mzele wa makolo a.”
^ Kapena kuti, “Mesiya; Wodzozedwa.”
^ Kapena kuti, “mwa mphamvu ya Mulungu yogwila nchito.”
^ M’cikhalidwe ca Ayuda, anthu akatomelana anali kuwaona ngati okwatilana.
^ M’Baibo ino, awa ndi malo oyamba pa malo 237 m’Malemba a Cigiriki a Cikhristu pamene pakupezeka dzina la Mulungu lakuti Yehova. Onani Zakumapeto A5.
^ Dzinali m’Ciheberi ndi Yesuwa kapena kuti Yoswa, ndipo limatanthauza kuti “Yehova Ndiye Cipulumutso.”