Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Mateyo 7:1-29

  • ULALIKI WA PA PHILI (1-27)

    • Lekani kuweluza ena (1-6)

    • Pemphanibe, pitilizani kufuna-funa, gogodanibe (7-11)

    • Khalidwe Lopambana (12)

    • Geti yopanikiza (13, 14)

    • Mudzawadziwa ndi zipatso zao (15-23)

    • Nyumba yomangidwa pa thanthwe, nyumba yomangidwa pa mcenga (24-27)

  • Khamu la anthu lidabwa ndi kaphunzitsidwe ka Yesu (28, 29)

7  “Lekani kuweluza ena kuopela kuti inunso mungaweluzidwe; 2  cifukwa ciweluzo cimene mukuweluza naco ena, inunso mudzaweluzidwa naco, ndipo muyeso umene mukupimila ena, inunso adzakupimilani womwewo. 3  Nanga n’cifukwa ciani ukuyang’ana kacitsotso m’diso la m’bale wako, koma osaona mtanda wa mtenje wa nyumba umene uli m’diso lako? 4  Kapena ungauze bwanji m’bale wako kuti, ‘Leka ndikucotse kacitsotso m’diso lako,’ pamene iwe m’diso lako muli mtanda wa mtenje wa nyumba? 5  Wonyenga iwe! Coyamba cotsa mtanda wa nyumba umene uli m’diso lakowo. Ukatelo, udzatha kuona bwino-bwino mmene ungacotsele kacitsotso m’diso la m’bale wako. 6  “Musamapatse agalu zinthu zopatulika kapena kuponyela nkhumba ngale zanu, kuopela kuti zingaponde-ponde ngalezo ndi kutembenuka n’kukukhadzulani. 7  “Pemphanibe, ndipo adzakupatsani; pitilizani kufuna-funa, ndipo mudzapeza; gogodanibe ndipo adzakutsegulilani; 8  pakuti aliyense wopempha amalandila, ndipo aliyense wofuna-funa amapeza, ndiponso aliyense wogogoda adzamutsegulila. 9  Ndani wa inu amene mwana wake akamupempha mkate, angamupatse mwala? 10  Kapena akamupempha nsomba, kodi angamupatse njoka? 11  Cotelo ngati inu, ngakhale kuti ndinu oipa, mumadziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kuli bwanji Atate wanu wa kumwamba? Ndithudi, iye adzapeleka zinthu zabwino kwa amene amamupempha! 12  “Conco, zinthu zonse zimene mumafuna kuti anthu akucitileni, inunso muwacitile zomwezo. Ndipo izi n’zimene Cilamulo ndi zolemba za aneneli zimaphunzitsa. 13  “Lowani pa geti yopanikiza, cifukwa mseu wotakasuka ukupita ku cionongeko, ndipo geti yake ndi yaikulu, komanso anthu ambili akuyenda mmenemo; 14  koma geti yolowela ku moyo ndi yopanikiza, ndiponso mseu wake ndi wopanikiza, komanso amene akuyendamo ndi ocepa. 15  “Samalani ndi aneneli abodza amene amabwela kwa inu atabvala ngati nkhosa, koma mkati mwao ndi mimbulu yolusa. 16  Mudzawazindikila ndi zipatso zao. Anthu sathyola mphesa mu mtengo wa minga, kapena nkhuyu pa citsamba ca minga, amatelo kodi? 17  Mofananamo, mtengo ulionse wabwino umabala zipatso zabwino, koma mtengo ulionse woipa umabala zipatso zoipa. 18  Mtengo wabwino sungabale zipatso zoipa, ndipo mtengo woipa sungabale zipatso zabwino. 19  Mtengo ulionse wosabala zipatso zabwino, amaudula n’kuuponya pa moto. 20  Cotelo, anthu amenewo mudzawazindikila mwa zipatso zao. 21  “Sikuti aliyense wonena kwa ine kuti, ‘Ambuye, Ambuye,’ adzalowa mu Ufumu wa kumwamba ai, koma yekhayo wocita cifunilo ca Atate wanga amene ali kumwamba. 22  Pa tsikulo, ambili adzati kwa ine: ‘Ambuye, Ambuye, kodi sitinanenele m’dzina lanu, kutulutsa ziwanda m’dzina lanu, ndi kucita nchito zambili zamphamvu m’dzina lanunso?’ 23  Koma ine ndidzawauza kuti: ‘Sindikudziwani m’pang’ono pomwe! Cokani pamaso panga, anthu osamvela malamulo inu!’ 24  “Conco, aliyense womva mau anga ndi kuwacita, adzakhala ngati munthu wanzelu amene anamanga nyumba yake pa thanthwe. 25  Ndiyeno kunagwa cimvula camphamvu ndipo madzi anasefukila. Kenako kunabwela cimphepo ndipo cinaomba nyumbayo mwamphamvu, koma sinagwe cifukwa maziko ake anali pa thanthwe. 26  Aliyense womva mau angawa koma osawacita, adzakhala ngati munthu wopusa amene anamanga nyumba yake pa mcenga. 27  Ndiyeno kunagwa cimvula camphamvu, ndipo madzi anasefukila. Kenako kunabwela cimphepo cimene cinaomba nyumbayo mwamphamvu, ndipo inagwa ndi kuonongeka kothelatu.” 28  Yesu atatsiliza kukamba mau amenewa, khamu la anthulo linadabwa kwambili ndi kaphunzitsidwe kake, 29  cifukwa anali kuwaphunzitsa monga munthu waulamulilo, osati monga alembi ao.

Mau a m'Munsi