B1
Uthenga wa m’Baibo
Yehova Mulungu ndiye woyenela kulamulila. Iye amalamulila m’njila yabwino koposa. Colinga cake cokhudza dziko lapansi komanso anthu cidzakwanilitsika.
|
Pambuyo pa 4026 B.C.E. “Njoka” itsutsa kuti Yehova ndiye woyenela kulamulila. Yehova alonjeza kubweletsa “mbadwa” kapena kuti “mbeu” imene m’kupita kwa nthawi idzaonongelatu njokayo yomwe ndi Satana. (Genesis 3:1-5, 15, mau a m’munsi) Komabe, Yehova akulola nthawi kupitapo kuti anthu adzilamulile okha motsogoleledwa ndi Satana. |
|
Mu 1943 B.C.E. Yehova auza Abulahamu kuti “mbadwa” yolonjezedwayo idzacokela mwa ana ake.—Genesis 22:18. |
|
Pambuyo pa 1070 B.C.E. Yehova atsimikizila Mfumu Davide, ndipo pambuyo pake atsimikizilanso Solomo mwana wake kuti “mbadwa” yolonjezedwayo idzacokela m’banja lao.—2 Samueli 7:12, 16; 1 Mafumu 9:3-5; Yesaya 9:6, 7. |
|
Mu 29 C.E. Yehova asankha Yesu kukhala “mbadwa” yolonjezedwayo, amene adzakhala woyenela kukhala pa mpando wacifumu wa Davide.—Agalatiya 3:16; Luka 1:31-33; 3:21, 22. |
|
Mu 33 C.E. Njokayo, amene ndi Satana, abvulaza “mbadwa” yolonjezedwayo kwa nthawi yocepa mwa kupha Yesu. Yehova anaukitsa Yesu, amene pambuyo pake anapita kumwamba. Kumeneko, Yehova analandila moyo wangwilo wa Yesu, umene umathandiza kuti anthu azikhululukidwa macimo ao komanso kuti mbadwa za Adamu zikalandile moyo wosatha.—Genesis 3:15; Macitidwe 2:32-36; 1 Akorinto 15:21, 22. |
|
Ca m’ma 1914 C.E. Yesu aponya njokayo, Satana, ku dziko lapansi kuti akhale kumeneko kwa nthawi yocepa.—Cibvumbulutso 12:7-9, 12. |
|
Mtsogolo Yesu adzamanga Satana kwa zaka 1,000, kenako adzamuononga, zimene zikuimila kuphwanya mutu wa Satana. Colinga ca Yehova capoyamba cokhudza dziko lapansi ndi anthu cidzakwanilitsika, dzina lake lidzayeletsedwa ku zitonzo zonse, ndipo pamapeto pake, ulamulilo wake udzaonekela kuti ndio wabwino koposa.—Cibvumbulutso 20:1-3, 10; 21:3, 4. |

