BAIBO YA DZIKO LATSOPANO

N’cifukwa Ciani Anthu Amabvutika?

Cinyanja
N’cifukwa Ciani Anthu Amabvutika?
https://cms-imgp.jw-cdn.org/img/p/1001061100/univ/wpub/1001061100_univ_sqr_xl.jpg
nwt tsa. 19

FUNSO 9

N’cifukwa Ciani Anthu Amabvutika?

“Si nthawi zonse pamene anthu othamanga kwambili amapambana pampikisano komanso pamene amphamvu amapambana pankhondo. Si nthawi zonse pamene anthu ocenjela amapeza cakudya, ndiponso si nthawi zonse pamene anthu anzelu amakhala ndi cuma. Komanso anthu odziwa zinthu, si nthawi zonse pamene zinthu zimawayendela bwino, cifukwa nthawi yatsoka komanso zinthu zosayembekezeleka zimagwela onsewo.”

Mlaliki 9:11

“Monga mmene ucimo unalowela m’dziko kudzela mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzela mwa ucimo, imfayo inafalikila kwa anthu onse cifukwa onse anacimwa—.”

Aroma 5:12

“N’cifukwa cake Mwana wa Mulungu anaonekela kuti aononge nchito za Mdyelekezi.”

1 Yohane 3:8

“Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.”

1 Yohane 5:19