Cinyanja
Dzina la Mulungu m’Malemba a Cigiriki a Cikhristu
https://cms-imgp.jw-cdn.org/img/p/1001061100/univ/wpub/1001061100_univ_sqr_xl.jpg
nwt masa. 540-547

A5

Dzina la Mulungu m’Malemba a Cigiriki a Cikhristu

Akatswili a Baibo amabvomeleza kuti dzina la Mulungu, lolembedwa ndi zilembo zinai za Ciheberi (יהוה), limapezeka maulendo okwana 7,000 mʼmipukutu yoyambilila ya Malemba a Ciheberi. Komabe ena amaona kuti dzinali silinali kupezeka mʼmipukutu yoyambilila ya Malemba a Cigiriki. Cifukwa ca zimenezi, omasulila ma Baibo a Cingelezi ambili masiku ano, saikamo dzina lakuti Yehova akamamasulila Malemba amene amati ndi Cipangano Catsopano. Ngakhale akamagwila mau Malemba a Ciheberi omwe ali ndi zilembo zinai zoimila dzina la Mulungu, omasulila ambili amasewenzetsa mau akuti “Ambuye” mʼmalo mwa dzina lenileni la Mulungu.

Koma omasulila Baibo ya Dziko Latsopano ya Malemba Opatulika, sanacite zimenezi. MʼBaibo imeneyi, anabwezeletsa dzina lakuti Yehova ndipo limapezeka maulendo okwana 237 mʼMalemba a Cigiriki a Cikhristu. Posankha kucita zimenezi, omasulila Baibo imeneyi anaganizila mfundo ziwili zofunika izi: (1) Mipukutu ya Cigiriki yomwe tili nayo masiku ano si mipukutu yoyambilila. Pa mipukutu masauzande ambili yomwe ilipo masiku ano, yambili inalembedwa patadutsa zaka pafupifupi 200 pambuyo pa mipukutu yoyambilila. (2) Pa nthawi imeneyo, anthu amene anali kukopela mipukutu anacotsa dzina la Mulungu limene linali kulembedwa ndi zilembo zinai za Ciheberi nʼkuikamo mau a Cigiriki akuti Kyʹri·os, amene amatanthauza “Ambuye,” kapena anali kukopela kucokela mʼmipukutu yomwe dzinali linali litacotsedwamo kale.

Komiti Yomasulila Baibo ya Dziko Latsopano inali ndi umboni wotsimikizila kuti dzina la Mulungu limene linali kulembedwa ndi zilembo zinai za Ciheberi linali kupezekadi mʼmipukutu yoyambilila ya Cigiriki. Izi zili conco cifukwa ca mfundo zotsatilazi:

  • Mʼmipukutu ya Malemba a Ciheberi yomwe anali kusewenzetsa m’nthawi ya Yesu ndi atumwi, munali kupezeka dzina la Mulungu limene linali kulembedwa ndi zilembo zinai za Ciheberi. Mʼmbuyomu, anthu ena anali kutsutsa zimenezi. Koma popeza anthu apeza mipukutu ya Malemba a Ciheberi mʼdela la Qumran, yomwe anali kusewenzetsa m’nthawi ya atumwi, panopa palibenso amene akukaikila zimenezi.

  • M’nthawi ya Yesu ndi atumwi ake, dzina la Mulungu limene limalembedwa ndi zilembo zinai za Ciheberi, linali kupezekanso mʼmipukutu ya Cigiriki yomasulila Malemba a Ciheberi. Kwa zaka zambili, akatswili a Baibo anali kuganiza kuti mʼBaibo ya Cigiriki ya Septuagint, lomasulila Malemba a Ciheberi, simunali kupezeka dzina la Mulungu lakuti Yehova. Kenako capakati pa zaka za mʼma 1900, akatswiliwa anapeza zidutswa zakale za Baibo ya Cigiriki ya Septuagint yomwe inali kugwilitsidwa nchito m’nthawi ya Yesu. Zidutswazi zinali ndi dzina la Mulungu limene analilemba ndi zilembo za Ciheberi. Conco m’nthawi ya Yesu dzina la Mulungu linali kupezeka mʼmipukutu ya Cigiriki. Komabe pofika mʼzaka za mʼma 300 C.E., mipukutu yodziwika bwino ya Baibo ya Cigiriki ya Septuagint, monga ya Codex Vaticanus ndi Codex Sinaiticus, simunali kupezeka dzina la Mulungu kuyambila mʼbuku la Genesis mpaka Malaki (mʼmalo omwe linali kupezeka mʼmipukutu yoyambilila). Conco nʼzosadabwitsa kuti mipukutu imene inasungidwa kuyambila nthawi imeneyo mulibe dzina la Mulungu mʼMalemba amene amati ndi Cipangano Catsopano kapena kuti Malemba a Cigiriki a mʼBaibo.

    Yesu ananena momveka bwino kuti: “Ine ndabwela m’dzina la Atate wanga.” Iye anatsindikanso kuti nchito zimene anali kucita, anali kuzicita “m’dzina la Atate” wake

  • Malemba a Cigiriki omwewo amafotokoza momveka bwino kuti nthawi zambili Yesu anali kuchula dzina la Mulungu ndiponso anali kudziwitsa anthu ena za dzinali. (Yohane 17:6, 11, 12, 26) Yesu ananena momveka bwino kuti: “Ine ndabwela m’dzina la Atate wanga.” Anatsindikanso kuti zonse zomwe anali kucita, anali kuzicita “mʼdzina la Atate” wake.—Yohane 5:43; 10:25.

  • Popeza kuti Malemba a Cigiriki ndi ouzilidwa ngati mmene zilili ndi Malemba a Ciheberi, dzina la Mulungu lakuti Yehova lifunika lizipezekanso mʼMalemba a Cigirikiwo. Capakati pa zaka za mʼma 100 C.E., wophunzila Yakobo anauza akulu a ku Yerusalemu kuti: “Sumiyoni wafotokoza bwino kwambili mmene Mulungu anaceukila anthu a mitundu ina kwa nthawi yoyamba, kuti pakati pao atengepo anthu ena odziwika ndi dzina lake.” (Macitidwe 15:14) Ndiye zikanakhala zosamveka kuti Yakobo akambe mau amenewa, ngati pa nthawi imeneyo panalibe aliyense amene anali kusewenzetsa kapena kudziwika ndi dzina la Mulungu.

  • MʼCigiriki mulinso cidule ca dzina la Mulungu. Pa Cibvumbulutso 19:1, 3, 4, 6, pali cidule ca dzina la Mulungu comwe cikupezeka mʼmau akuti “Aleluya.” Mauwa akucokela ku mau a Ciheberi omwe amatanthauza kuti “Tamandani Ya.” Mau akuti “Ya” ndi cidule ca dzina lakuti Yehova. Maina ambili a mʼMalemba a Cigiriki a Cikhristu ndi ocokela pa dzina la Mulungu. Ndipo mabuku ambili amaonetsa kuti dzina la Yesu, limatanthauza kuti “Yehova ndi cipulumutso.”

  • Zolemba zoyambilila za Ayuda zimaonetsa kuti Akhristu a Ciyuda anali kusewenzetsa dzina la Mulungu. Buku lina la malamulo a Ayuda lomwe anamaliza kulilemba ca mʼma 300 C.E., lochedwa Tosefta, limanena mau otsatilawa pofotokoza za mabuku a Akhristu omwe anali kuochedwa pa tsiku la Sabata ndi anthu otsutsa Cikhristu: “Mabuku a anthu olengeza uthenga wabwino ndiponso mabuku a anthu ochedwa a minim [anthu ena amaganiza kuti anthu amenewa anali Akhristu a Ciyuda] anali kuochedwa ndi moto. Anali kupsyela pamalo amene awapezepo ndipo anali kuwaleka mpaka atanyeka moti mabuku onsewo pamodzi ndi masamba onse ochula dzina la Mulungu anali kupsyela limodzi.” Buku lomweli limagwilanso mau a Yosé, Rabi wa ku Galileya, amene anakhalako cakumayambililo kwa zaka za mʼma 100 C.E. Limati Rabiyo ananena kuti ngati tsiku limenelo si la Sabata, “tinali kungocotsako masamba [a Malemba a Cikhristu] amene ali ndi dzina la Mulungu ndipo ena onsewo anali kuochedwa.”

  • Akatswili ena a Baibo amabvomeleza kuti nʼzomveka kunena kuti dzina la Mulungu linali kupezeka mʼMalemba a Cigiriki omwe anagwila mau Malemba a Ciheberi. Nʼzocititsa cidwi kuti pansi pa kamutu kakuti “Zilembo Zinai Zoimila Dzina la Mulungu m’Cipangano Catsopano,” kopezeka m’buku lakuti The Anchor Bible Dictionary pamanena kuti: “Pali umboni woonetsa kuti olemba mabuku a Cipangano Catsopano, anali kulemba zilembo zinai zoimila dzina la Mulungu lakuti Yahweh, mʼMalemba ena kapena onse a mʼCipangano Catsopano amene mau ake akucokela m’Cipangano Cakale.” Ndipo katswili wina wa Baibo, dzina lake George Howard, anati: “Mʼpomveka kunena kuti olemba Cipangano Catsopano, sanali kucotsa zilembo zinai zoimila dzina la Mulungu mʼMalemba amene akucokela m’Cipangano Cakale. Tikutelo cifukwa cakuti pa nthawiyo zilembo zimenezi zinali kupezekabe mʼma Baibo a Cigiriki [a Septuagint] omwe Akhristu anali kusewenzetsa.”

  • Omasulila Baibo odziwika bwino anasewenzetsa dzina la Mulungu mʼMalemba a Cigiriki a Cikhristu. Ena mwa omasulila amenewa anacita zimenezi Baibo ya Dziko Latsopano isanatuluke. Ena mwa ma Baibo amene dzinali likupezekamo ndi awa: A Literal Translation of the New Testament . . . From the Text of the Vatican Manuscript, ya Herman Heinfetter (1863); The Emphatic Diaglott, ya Benjamin Wilson (1864); The Epistles of Paul in Modern English, ya George Barker Stevens (1898); St. Paulʼs Epistle to the Romans, la W. G. Rutherford (1900); komanso The New Testament Letters, ya J.W.C. Wand, Bishopu wa ku London (1946). Kuonjezela pamenepa, cakumayambililo kwa zaka za mʼma 1900, Pablo Besson anamasulila Baibo mʼCisipanishi. MʼBaibo imeneyi muli dzina lakuti “Yehova” pa Luka 2:15 ndi pa Yuda 14, ndiponso mau a mʼmunsi mʼmalo pafupifupi 100 oonetsa kuti pa lembalo pangaikidwenso dzina la Mulungu. Koma ma Baibo amenewa asanamasulilidwe, Malemba a Cigiriki amene anawamasulila mʼCiheberi ndipo anali kuwasewenzetsa kuyambila mʼzaka za mʼma 1500 C.E, anali kukhala ndi dzina la Mulungu mʼmalo ambili. Mʼcinenelo ca Cijeremani cokha, pafupifupi ma Baibo 11 osiyana-siyana anasewenzetsa dzina lakuti “Yehova” (kapena mau a Ciheberi akuti “Yahweh”) mʼMalemba a Cigiriki a Cikhristu. Koma omasulila ena anai anali kuonjezela dzinalo mʼmabulaketi akapeza dzina lakuti “Ambuye.” Ma Baibo oposa 70 omasulilidwa mʼCijeremani anasewenzetsa dzina la Mulungu mʼmau a mʼmunsi kapena mʼmau ofotokozela.

    Dzina la Mulungu pa Macitidwe 2:34 m’Baibo ya The Emphatic Diaglott, ya Benjamin Wilson (1864)

  • Ma Baibo a zinenelo zosiyana-siyana zoposa 300 mumapezeka dzina la Mulungu mʼMalemba a Cigiriki. Zinenelo zambili za ku Africa, America, Asia, Europe, komanso Pacific-islands zimasewenzetsa dzina la Mulungu mʼma Baibo ao. (Onani zina mwa zinenelozi  patsamba 546 ndi 547.) Omasulila ambili anacita zimenezi pa zifukwa zimene zachulidwa kale m’nkhani ino. Ena mwa ma Baibo omasulila Malemba a Cigirikiwa ayamba kupezeka caposacedwapa monga Baibo ya Chirotumani (1999), lomwe anasewenzetsa dzina lakuti “Jihova” maulendo okwana 51 mʼmavesi 48. Baibo ina ndi ya Cibataki (Citoba) (1989) ya ku Indonesia, lomwe anasewenzetsa dzina lakuti “Jahowa” maulendo okwana 110.

    Dzina la Mulungu pa Maliko 12:29, 30 m’Baibo yomasulilidwa m’cinenelo ca ku Hawai

Conco nʼzoonekelatu kuti pali zifukwa zomveka zobwezeletsela dzina la Mulungu lakuti Yehova mʼMalemba a Cigiriki a Cikhristu. Izi nʼzimene omasulila Baibo ya Dziko Latsopano anacita. Omasulilawo amalemekeza kwambili dzina la Mulungu ndipo sanafune kucotsa kalikonse pa mau omwe anali mʼmipukutu yoyambilila.—Cibvumbulutso 22:18, 19.