FUNSO 1
Kodi Mulungu Ndani?
“Anthu adziwe kuti inu, amene dzina lanu ndinu Yehova, inu nokha ndinu Wamʼmwambamwamba, woyenela kulamulila dziko lonse lapansi.”
Salimo 83:18
“Dziwani kuti Yehova ndi Mulungu. Iye ndi amene anatipanga, ndipo ndife ake. Ndife anthu ake komanso nkhosa zimene akuweta.”
Salimo 100:3
“Ine ndine Yehova. Dzina langa ndi limeneli. Sindipeleka ulemelelo wanga kwa wina aliyense ndipo sindifuna kuti aliyense azitamanda zifanizilo zogoba mʼmalo mwa ine.”
Yesaya 42:8
“Aliyense woitanila pa dzina la Yehova adzapulumuka.”
“Nyumba iliyonse imacita kumangidwa ndi winawake, koma amene anapanga zinthu zonse ndi Mulungu..”
“Kwezani maso anu kumwamba ndipo muone. Kodi ndi ndani amene analenga zinthu zimenezi? Ndi amene akutsogolela gulu lonse la nyenyezi ndipo zonse amaziwelenga. Iliyonse amaiitana poichula dzina lake. Cifukwa ca kuculuka kwa mphamvu zake zoopsa ndiponso cifukwa cakuti ali ndi mphamvu zambili zocitila zinthu, palibe iliyonse imene imasowa.”
Yesaya 40:26

