FUNSO 3
Kodi Ndani Analemba Baibo?
“Mose analemba mau onse a Yehova.”
Ekisodo 24:4
“Danieli analota maloto ndipo anaona masomphenya atagona pabedi lake. Ndiyeno analemba zimene analotazo ndipo anafotokoza nkhani yonseyo.”
Danieli 7:1
“Pamene munalandila mau a Mulungu amene munamva kwa ife, simunawalandile monga mau a anthu ai, koma mmene alilidi, monga mau a Mulungu.”
“Malemba onse anauzilidwa ndi Mulungu, ndipo ndi othandiza pa kuphunzitsa.”
“Ulosi sunayambe wanenedwapo mwa kufuna kwa munthu, koma anthu analankhula mau ocokela kwa Mulungu motsogoleledwa ndi mzimu woyela.”

