Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Mateyo 21:1-46
21 Iwo atayandikila ku Yerusalemu, anafika ku Betifage pa Phili la Maolivi. Kenako Yesu anatuma ophunzila ake awili
2 n’kuwauza kuti: “Pitani m’mudzi uwo, ndipo mukakangolowamo, mukapeza bulu atam’mangilila pamodzi ndi mwana wake wamphongo. Mukawamasule n’kuwabweletsa kwa ine.
3 Munthu aliyense akakakufunsani ciliconse, mukanene kuti, ‘Ambuye akuwafuna.’ Ndipo nthawi yomweyo akawatumiza.”
4 Zimenezi zinacitikadi kuti mau amene ananenedwa kudzela mwa mneneli akwanilitsidwe, akuti:
5 “Uza mwana wamkazi wa Ziyoni kuti: ‘Taona! Mfumu yako ikubwela kwa iwe. Ndi yofatsa, ndipo yakwela pa bulu, inde, mwana wamphongo wa bulu, mwana wa nyama yonyamula katundu.’”
6 Conco ophunzilawo anapita, ndipo anacita ndendende zimene Yesu anawauza.
7 Anabwela naye buluyo pamodzi ndi mwana wake. Kenako anayanzika zobvala zao zakunja pa abuluwo, ndipo Yesu anakwelapo.
8 Anthu ambili m’khamulo anayanzika zobvala zao zakunja mu mseu, ndipo ena anali kudula nthambi za mitengo n’kuziyala mu mseu.
9 Komanso khamu la anthu limene linali patsogolo ndi pambuyo pake linali kupfuula kuti: “M’pulumutseni Mwana wa Davide! Wodalitsika ndi iye wobwela m’dzina la Yehova!* M’pulumutseni inu amene muli kumwambamwambako!”
10 Ndiyeno atalowa mu Yerusalemu, mumzinda wonsewo munakhala ciphokoso. Ena anali kufunsa kuti: “Ndani ameneyu?”
11 Khamulo linali kuyankha kuti: “Ameneyu ndi mneneli Yesu, wocokela ku Nazareti, ku Galileya!”
12 Yesu analowa m’kacisi ndi kupitikitsila panja onse omwe anali kugulitsa ndi kugula zinthu m’kacisimo. Komanso anagudubula matebulo a osintha ndalama ndi mabenchi a ogulitsa nkhunda.
13 Ndipo anawauza kuti: “Malemba amati, ‘Nyumba yanga idzachedwa nyumba yopemphelelamo,’ koma inu mwaisandutsa phanga la acifwamba.”
14 Komanso anthu akhungu ndi olemala anabwela kwa iye m’kacisimo, ndipo anawacilitsa.
15 Ansembe aakulu ndi alembi ataona zinthu zodabwitsa zimene iye anacita, ndiponso ataona anyamata amene anali kupfuula kuti, “M’pulumutseni Mwana wa Davide!” anakwiya kwambili,
16 ndipo anamufunsa kuti: “Kodi ukumva zimene awa akukamba?” Yesu anawayankha kuti: “Inde. Kodi simunawelengepo mau akuti, ‘Mwacititsa pakamwa pa ana ndi makanda kulankhula mau acitamando’?”
17 Ndiyeno anawasiya n’kutuluka mu mzindawo kupita ku Betaniya, ndipo anagona kumeneko.
18 Akubwelela ku mzinda wa Yerusalemu m’mamawa, anamva njala.
19 Ataona mtengo wa mkuyu m’mbali mwa mseu, anapita komweko, koma sanapezemo ciliconse. Anangopezamo masamba okha-okha. Conco anauza mtengowo kuti: “Kuyambila lelo sudzabalanso zipatso.” Ndipo mtengo wa mkuyuwo unafota nthawi yomweyo.
20 Ophunzilawo ataona zimenezi anadabwa kwambili, ndipo anati: “Zatheka bwanji kuti mtengo wa mkuyuwu ufote nthawi yomweyi?”
21 Poyankha Yesu anawauza kuti: “Ndithu ndikukuuzani kuti ngati muli ndi cikhulupililo ndipo simukaika, mudzatha kucita zimene nacita ku mtengo wa mkuyuwu. Ndiponso kuposa pamenepa mudzatha kuuza phili ili kuti, ‘Nyamuka ukadziponye m’nyanja,’ ndipo zidzacitikadi.
22 Zilizonse zimene mudzapempha m’mapemphelo anu, mudzalandila ngati muli ndi cikhulupililo.”
23 Yesu atalowa m’kacisi, ansembe aakulu ndi akulu anabwela kwa iye pamene anali kuphunzitsa n’kumufunsa kuti: “Kodi ulamulilo wocita zimenezi munautenga kuti? Nanga ndani anakupatsani ulamulilo umenewu?”
24 Yesu anawayankha kuti: “Inenso ndikufunsani cinthu cimodzi. Mukandiyankha, inenso ndikuuzani kumene n’natenga ulamulilo wocita zimenezi:
25 Kodi ubatizo wa Yohane unacokela kuti? Kumwamba kapena kwa anthu?”* Koma iwo anayamba kukambilana, n’kumati: “Tikanena kuti, ‘Unacokela kumwamba,’ atifunsa kuti, ‘Nanga n’cifukwa ciani simunamukhulupilile?’
26 Komanso sitingakambe kuti, ‘Unacokela kwa anthu,’ cifukwa tikuopa khamu la anthuli popeza onse amakhulupilila kuti Yohane anali mneneli.”
27 Conco pomuyankha Yesu, iwo anati: “Sitidziwa.” Yesu anati: “Inenso sindikuuzani kumene ndinatenga ulamulilo wocita zimenezi.
28 “Muganiza bwanji? Munthu wina anali ndi ana awili. Ndipo anapita kwa mwana woyamba n’kumuuza kuti, ‘Mwanawe, lelo upite kukagwila nchito m’munda wa mpesa.’
29 Poyankha iye anati, ‘Sinipita,’ koma pambuyo pake anamva cisoni ndipo anapita.
30 Anapita kwa waciwili n’kumuuzanso cimodzimodzi. Iye poyankha anati, ‘Nipita atate,’ koma sanapite.
31 Pa ana awiliwa, ndani anacita cifunilo ca atate ake?” Iwo anati: “Woyamba uja.” Ndiyeno Yesu anati: “Ndithu ndikukuuzani kuti okhometsa misonkho ndi mahule akukusiyani m’mbuyo n’kukalowa mu Ufumu wa Mulungu.
32 Pakuti Yohane anabwela kwa inu n’kukuonetsani njila ya cilungamo, koma simunam’khulupilile. Komabe, okhometsa misonkho ndi mahule anam’khulupilila. Koma ngakhale kuti inu munaona zimenezi, simunamve cisoni pambuyo pake n’kusintha maganizo anu kuti mum’khulupilile.
33 “Mvelani fanizo lina: Panali munthu wina amene anali ndi munda. M’mundawo analimamo mphesa n’kumanga mpanda kuzungulila mundawo, komanso anakumbamo copondelamo mphesa ndi kumanga nsanja. Kenako anausiya m’manja mwa alimi n’kupita ku dziko lina.
34 Nyengo yokolola zipatso itafika, iye anatuma akapolo ake kwa alimi aja kuti akatengeko zipatso zake.
35 Koma alimiwo anagwila akapolo aja. Mmodzi anamumenya, wina anamupha, ndipo wina anamuponya miyala.
36 Anatumanso akapolo ena ambili kuposa gulu loyamba lija. Koma amenewanso anawacita cimodzi-modzi.
37 Pamapeto pake anatuma mwana wake kwa iwo, n’kunena kuti, ‘Mwana wangayu akamulemekeza.’
38 Alimiwo ataona mwanayo anayamba kukambilana kuti, ‘Eya! Uyu ndiye wolandila colowa. Bwelani, tiyeni timuphe ndi kutenga colowa cake!’
39 Conco anamugwila ndi kumuponya kunja kwa munda wampesawo n’kumupha.
40 Ndiye kodi mwinimundayo akadzabwela, adzacita nao ciani alimiwo?”
41 Iwo anayankha kuti: “Cifukwa cakuti ndi oipa, adzawaononga koopsya ndipo adzapeleka munda wa mpesawo kwa alimi ena, amene angamupatse zipatso nthawi yokolola ikakwana.”
42 Ndiyeno Yesu anawafunsa kuti: “Kodi simunawelengepo m’Malemba kuti, ‘Mwala umene omanga anaukana, wakhala mwala wapakona* wofunika kwambili. Umenewu wacokela kwa Yehova,* ndipo ndi wodabwitsa m’maso mwathu’?
43 Ndiye cifukwa cake ndikukuuzani kuti, Ufumu wa Mulungu udzacotsedwa kwa inu ndi kupelekedwa kwa mtundu wobala zipatso zake.
44 Komanso munthu wogwela pa mwala umenewu adzaphwanyika. Ndipo aliyense amene mwalawo udzamugwele udzamupelelatu.”
45 Ansembe aakulu ndi Afalisi atamva mafanizo akewa, anadziwa kuti anali kukamba za iwo.
46 Ngakhale kuti iwo anali kufuna kumugwila* anaopa khamu la anthu, cifukwa anthuwo anali kumuona kuti ndi mneneli.
Mau a m'Munsi
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Kapena kuti, “kapena unayambitsidwa ndi anthu?”
^ Kucokela ku Cigiriki, “wakhala mutu wakona.” Mwala umenewu anali kuuika pa kona ya nyumba, pomwe zipupa ziwili zimakumana.
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Kapena kuti, “kumumanga.”

