FUNSO 18
Kodi Mungacite Ciani Kuti Mumuyandikile Mulungu?
“Inu Wakumva pemphelo, anthu a mitundu yonse adzabwela kwa inu.”
Salimo 65:2
“Uzikhulupilila Yehova ndi mtima wako wonse, ndipo usamadalile luso lako lomvetsa zinthu. Uzimukumbukila mʼnjila zako zonse, ndipo iye adzawongola njila zako.”
Miyambo 3:5, 6
“Iwo adzapeza moyo wosatha akamadziwa za inu Mulungu yekhayo woona, komanso za Yesu Khristu amene inu munamutuma.”
“[Mulungu] kwenikweni sali kutali ndi aliyense wa ife.”
“Ine ndikupitiliza kupemphela kuti cikondi canu cizipita cikukulila-kulila, limodzi ndi cidziwitso colondola, komanso luso lanu lozindikila zinthu.”
“Ngati wina akusowa nzelu, azipempha kwa Mulungu ndipo adzam’patsa, pakuti iye amapeleka kwa onse moolowa manja komanso mosatonza.”
“Yandikilani Mulungu ndipo iyenso adzakuyandikilani. Yeletsani manja anu ocimwa inu, ndipo yeletsani mitima yanu okaika-kaika inu.”
“Kukonda Mulungu kumatanthauza kutsatila malamulo ake, ndipo malamulo akewo si olemetsa.”

