Matanthauzo a Mau Ena a m’Baibo
A B C D F G H I J K L M N O P S T U W Y Z
A
-
Acipani ca Herode.—
Onani ANTHU OTSATILA HERODE.
-
Aepikureya.
Anthu amene anali kutsatila katswili wina wa nzelu za anthu, dzina lake Epicurus (341-270 B.C.E.). Aepikureya anali kulimbikitsa mfundo yakuti cofunika kwambili pa moyo wa munthu ndi kusangalala.—Mac 17:18.
-
Afarisi.
Kagulu kochuka ka cipembedzo ca Ciyuda ka m’nthawi ya atumwi. Afarisi sanali a m’banja la ansembe, koma anali kutsatila kwambili Cilamulo, kuphatikizapo tumfundo tung’ono-tung’ono twa m’Cilamulo. Iwo anali kuona miyambo ya makolo kukhala yofunika kwambili mofanana ndi Cilamulo, ndipo anali kuitsatilanso mosamalitsa kwambili. (Mt 23:23) Sanali kulola kutengela cikhalidwe ca Agiriki mwanjila ina iliyonse. Ndipo popeza anali akatswili a Cilamulo komanso miyambo, anali ndi ulamulilo waukulu pa anthu. (Mt 23:2-6) Afarisi ena anali mamembala a Khoti Yaikulu ya Ayuda (Sanihedirini). Nthawi zambili iwo anali kutsutsa Yesu pa nkhani yosunga Sabata, miyambo, ndiponso pa nkhani ya kugwilizana ndi ocimwa komanso okhometsa misonkho. Afarisi ena pambuyo pake anakhala Akhristu, kuphatikizapo Saulo wa ku Tariso.—Mt 9:11; 12:14; Mko 7:5; Lu 6:2; Mac 26:5.
-
Akaya.
MʼMalemba a Cigiriki a Cikhristu, mauwa amanena za malo amene anali m’cigao ca kumʼmwela kwa Girisi comwe cinali kulamulilidwa ndi Aroma ndipo likulu lake linali ku Korinto.—Mac 18:12.
-
Akerubi.
Angelo audindo wapamwamba omwenso amagwila nchito zapadela. Ndi osiyana ndi aserafi.—Ge 3:24; Eks 25:20; Yes 37:16; Ahe 9:5.
-
Akulu-akulu a zamalamulo.
Mʼzigao zolamulidwa ndi Aroma, anthu amenewa anali kukhala akulu-akulu a boma. Nchito zina zimene anali kugwila zinali kukhazikitsa bata, kuyangʼanila za ndalama, kuweluza ophwanya malamulo, komanso kulamula kuti anthu alangidwe.—Mac 16:20.
-
Alabasitala.
Dzina la timabotolo ta mafuta onunkhila timene tinali kupangidwa kucokela ku miyala yomwe inali kupezeka kufupi ndi ku Alabastron, mʼdziko la Iguputo. Nthawi zambili mabotolowa anali kukhala ndi khosi loningʼa lomwe anali kulimata kuti mafuta a mtengo wapataliwa asamataike. Kenako mwalawu unayamba kudziwikanso ndi dzina lomweli.—Mko 14:3.
-
Alefa ndi Omega.
-
Amedi.
Mbadwa za mwana wa Yafeti dzina lake Madai. Iwo anakhala kudela lamapili la ku Iran ndipo dziko lao linayamba kutchedwa Mediya. Amedi ena analipo ku Yerusalemu pa Pentekosite mu 33 C.E.—Mac 2:9.
-
Ameni.
“Zikhale momwemo,” kapena “ndithu.” Mauwa akucokela ku mau a Ciheberi akuti ’a·manʹ, omwe amatanthauza “kukhulupilika, kudalilika.” “Ameni” anali kunenedwa pobvomeleza lumbilo, pemphelo, kapena mfundo inayake. Mʼbuku la Cibvumbulutso, mauwa amagwilitsidwa nchito ngati dzina laudindo la Yesu.—De 27:26; 1Mb 16:36; Aro 1:25; Civ 3:14.
-
Angelo.
Pa Ciheberi ndi mal·ʼakhʹ, pa Cigiriki agʹge·los. Mau onsewa amatanthauza “opeleka uthenga,” koma akamanena za mizimu yopeleka uthenga amasewenzetsa mau akuti “angelo.” (Ge 16:7; 32:3; Yak 2:25; Civ 22:8) Angelo ndi mizimu yamphamvu yomwe inalengedwa ndi Mulungu kale kwambili anthu asanalengedwe. MʼBaibo amachulidwanso kuti “oyela masauzande masauzande,” “ana a Mulungu,” komanso “nyenyezi zamʼmawa.” (De 33:2; Yob 1:6; 38:7; Yuda 14) Anawalenga mmodzi-mmodzi ndipo sanawalenge kuti azibeleka ana. Alipo oposa 100 miliyoni. (Da 7:10) Baibo imaonetsa kuti angelo ali ndi makhalidwe osiyana-siyana ndipo aliyense ali ndi dzina. Iwo ndi odzicepetsa, salola kuti azilambilidwa, ndipo nthawi zambili sakamba maina ao. (Ge 32:29; Lu 1:26; Civ 22:8, 9) Ali ndi maudindo osiyana-siyana ndipo amagwila nchito zosiyana-siyana monga kutumikila kumpando wa Yehova, kupeleka mauthenga, kuthandiza atumiki a Yehova apadziko lapansi, kupeleka ziweluzo za Mulungu, komanso kuthandiza pa nchito yolalikila uthenga wabwino. (2Mf 19:35; Sl 34:7; Mt 4:11; Lu 1:30, 31; Civ 5:11; 14:6) Mtsogolomu adzathandiza Yesu kumenya nkhondo ya Aramagedo.—Civ 19:14, 15.
-
Anthu otsatila nzelu za Sitoiki.
Anthu amene anali kuphunzila nzelu za Sitoiki ndipo anali kukhulupilila kuti munthu amakhala wosangalala ngati amasewenzetsa luso lake la kuganiza kuti amvetse malamulo amʼcilengedwe nʼkumawatsatila. Anali kuonanso kuti munthu wanzelu saonetsa kwenikweni kuti akumva ululu kapena wasangalala.—Mac 17:18.
-
Aramagedo.
Pa Ciheberi Har Meghid·dohnʹ, kutanthauza “Phili la Megido.” Mauwa amasewenzetsedwa ponena za “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuzonse” pamene “mafumu a dziko lonse lapansi kumene kuli anthu” adzasonkhane kuti amenyane ndi Yehova. (Civ 16:14, 16; 19:11-21)—Onani CISAUTSO CACIKULU.
-
Areopagi.
Phili lalitali ku Atene, kumpoto cakumadzulo kwa Akuropolisi. Linalinso dzina la khoti limene anthu anali kukumanako. Anthu ena a nzelu za Sitoiki ndi Epikureya anatenga Paulo nʼkupita naye kumeneko kuti akafotokoze zimene amakhulupilila.—Mac 17:19.
-
Asaduki.
Kagulu kochuka ka Ciyuda ka anthu olemela, olemekezeka, komanso ansembe amene anali ndi ulamulilo waukulu pa zocitika za pa kacisi. Iwo anali kukana miyambo yambili ya makolo imene Afarisi anali kutsatila komanso zikhulupililo zina za Afarisi. Sanali kukhulupilila kuti akufa adzauka kapena kuti kuli angelo. Asaduki anali kutsutsa Yesu.—Mt 16:1; Mac 23:8.
-
Asamariya.
Poyamba dzinali linali la Aisiraeli a mu ufumu wa kumpoto wa mafuko 10 koma pambuyo pogonjetsedwa ndi Asuri mu 740 B.C.E., dzinali linayamba kuphatikizaponso anthu a mitundu ina amene Asuri anawabweletsa kudelali. M’nthawi ya Yesu, dzinali silinali kukambanso za mtundu wa anthu kapena zokhudza ndale koma linali kunena za anthu acipembedzo ca mbali ya kumene kunali Sekemu ndi Samariya. Anthu acipembedzo cimeneci anali kukhulupilila zinthu zosiyana ndi zimene Ayuda anali kukhulupilila.—Yoh 8:48.
-
A·selʹgei·a.—
Onani KHALIDWE LOPANDA MANYAZI.
-
Asia.
MʼMalemba a Cigiriki a Cikhristu, dzinali limanena za cigao cimene cinali kulamulilidwa ndi Aroma, ndipo masiku ano ndi mbali yakumadzulo kwa dziko la Türkey komanso madela a zilumba za Samo ndi Patmo. Likulu lake linali ku Efeso.—Mac 20:16; Civ 1:4.
-
Asilikali Oteteza Mfumu.
Gulu la asilikali a Ciroma limene linakhazikitsidwa kuti liziteteza mfumu ya Aroma. Asilikaliwa anali ndi mphamvu zambili pothandiza kuti mfumu izilamulila kapena kuicotsa pampando.—Afi 1:13.
B
-
Baala.
Mulungu wa Akanani amene anali kuonedwa kuti ndi wobweletsa mvula, wobeleketsa, komanso mwini wa mlengalenga. Dzina lakuti “Baala” linali kugwilitsidwanso nchito ponena za milungu ina ingʼono-ingʼono. Mauwa m’Ciheberi amatanthauza “Mwiniwake; Mbuye.”—1Mf 18:21; Aro 11:4.
-
Bango.
-
Belezebule.
Dzina lina la Satana, kalonga kapena kuti wolamulila wa ziwanda. N’kutheka kuti dzinali linacokela ku dzina la Baala wochedwa Baala-zebabu, mulungu amene Afilisiti anali kulambila ku Ekironi.—2Mf 1:3; Mt 12:24.
-
Bwalo.
Malo a mkati mwa mpanda wa cihema ndipo anali kuzungulila cihema conse. Kenako anadzakhala malo a mkati mwa mpanda ozungulila nyumba yaikulu pa kacisi. Guwa la nsembe zopsyeleza linali mʼbwalo la cihema komanso mʼbwalo lamkati la kacisi. Baibo imanenanso za mabwalo a nyumba za anthu ndi nyumba zacifumu.—Eks 8:13; 27:9; 1Mf 7:12; Mt 26:3; Mko 15:16; Civ 11:2.
-
Bwanamkubwa.
C
-
Cakhumi.
Limodzi mwa magao 10 kapena kuti 10 pelesenti ya zinthu, imene inali kupelekedwa ngati mphatso maka-maka pa zinthu zokhudza kulambila. (Mki 3:10; De 26:12; Mt 23:23; Ahe 7:5) MʼCilamulo ca Mose, cakhumi ca zokolola kapena ziweto cinali kupelekedwa kwa Alevi caka ciliconse kuti azigwilitsa nchito pa umoyo wao. Naonso Alevi anali kutenga cakhumi pa zimene alandilazo nʼkupeleka kwa ansembe amʼbanja la Aroni kuti azigwilitsa nchito pa umoyo wao. Panali kukhalanso zakhumi zina zimene anthu anali kupeleka. Akhristu sanalamulidwe kuti azipeleka cakhumi.
-
Cakudya Camadzulo ca Ambuye.
Cakudya ceniceni, comwe ndi mikate yopanda zofufumitsa ndiponso vinyo, zomwe zimaimila thupi ndi magazi a Yesu; mwambo wokumbukila imfa ya Yesu. Mwambowu umachedwanso “Cikumbutso” cifukwa cakuti Malemba amalamula Akhristu kuti aziucita caka ciliconse.”—1Ak 11:20, 23-26.
-
Ciaramu.
Cinenelo cofanana ndi Ciheberi ndipo afabeti yakenso ndi yofanana ndi ya Ciheberi. Poyamba cinali kulankhulidwa ndi anthu a ku Aramu, koma kenako cinali kugwilitsidwanso nchito ndi anthu a mu ufumu wa Asuri ndi wa Babulo pa nkhani zamalonda. Cinalinso cinenelo ca boma mu ufumu wa Perisiya. (Eza 4:7) Mbali zina za buku la Ezara, Yeremiya, ndi Danieli zinalembedwa mʼCiaramu.—Eza 4:8–6:18; 7:12-26; Yer 10:11; Da 2:4b–7:28; Mko 14:36; Mac 9:36.
-
Cibvundikilo cophimba macimo.
Cinthu cophimbila likasa la pangano cimene mkulu wa ansembe anali kuciwaza magazi pa Tsiku la Mwambo Wophimba Macimo. Mau ake a Ciheberi amanena za “kuphimba (macimo)” kapena “kufufuta (macimo).” Cibvundikiloci cinali ca golide ndipo cinali ndi kerubi mmodzi mbali ina wina mbali ina. Nthawi zina cimangochedwa “cibvundikilo.”—Eks 25:17-22; 1Mb 28:11; Ahe 9:5.
-
Cidindo.
Cipangizo codindila (padothi ndi zinthu zina) comwe cinali kuonetsa kuti cinthuco ndi ceniceni. Cinali kuonetsanso umwini komanso mgwilizano, ndipo zinali kulepheletsa munthu kusintha zimene zalembedwa pa pepala kapena zinthu zina zimene zadindidwa, kuphatikizapo pa zitseko ndi pa manda. Zidindo zakale zinali kukhala zolimba (za mwala, minyanga, kapena mtengo) ndipo zojambula zake kapena zilembo zake anali kuzilemba cobwelela mʼmbuyo. Mau akuti cidindo amagwilitsidwanso nchito mophiphilitsa poonetsa kuti cinthu ndi ceniceni kapena cili ndi mwiniwake, kapenanso pofuna kuonetsa kuti cinthu cabisidwa mwinanso ndi cacinsinsi.—Mt 27:66; Yoh 6:27; Aef 1:13; Civ 5:1; 9:4.
-
Cigiriki.
Cilankhulo ca anthu a ku Girisi, ndipo anthu akumeneko kapena amene makolo awo anacokela kumeneko amachedwa Agiriki. MʼMalemba a Cigiriki a Cikhristu mau akuti Agiriki amakambanso za anthu onse omwe si Ayuda kapena amene anali kutengela cilankhulo ndi cikhalidwe ca Agiriki.—Yow 3:6; Yoh 12:20.
-
Cigololo.
-
Ciguduli.
Nsalu yokhuthala (yamtika) yopangila masaka osungila mbeu. Ciguduli cinali kupangidwa kucokela ku ubweya wakuda wa mbuzi ndipo cinali cobvala cimene anthu anali kubvala polila, malinga ndi cikhalidwe cao.—Ge 37:34; Lu 10:13.
-
Cikondwelelo ca Mikate Yopanda Zofufumitsa.
Cimodzi mwa zikondwelelo zitatu zikulu-zikulu zimene Aisiraeli anali kucita caka ciliconse. Cinali kuyamba pa Nisani 15, pambuyo pa tsiku la Pasika ndipo cinali kucitika kwa masiku 7. Anthu anali kudya mikate yopanda zofufumitsa yokha pokumbukila ulendo wao wocoka ku Iguputo.—Eks 23:15; Mko 14:1.
-
Cikondwelelo ca Misasa.
Cinali kuchedwanso kuti Cikondwelelo ca Mahema kapena Cikondwelelo ca Zokolola. Cinali kucitika mʼmwezi wa Etanimu kuyambila pa 15 mpaka pa 21. Aisiraeli anali kucita cikondweleloci akamaliza kukolola zinthu zao mʼmunda ndipo inali nthawi yacisangalalo komanso yoyamika Yehova cifukwa cowapatsa zokolola. Pa nthawi ya cikondweleloci anthu anali kukhala mʼmisasa kuti azikumbukila ulendo wao wocoka ku Iguputo. Cinali cimodzi mwa zikondwelelo zitatu zimene amuna anali kufunika kupita kukacita nao ku Yerusalemu.—Le 23:34; Eza 3:4; Yoh 7:2.
-
Cikondwelelo Copeleka Kacisi kwa Mulungu.
Caka ciliconse pa tsikuli, anali kukumbukila kuyeletsedwa kwa kacisi pambuyo poti anadetsedwa ndi Antiochus Epiphanes. Cinali kuyamba pa 25 mʼmwezi wa Kisilevi ndipo cinali kucitika kwa masiku 8.—Yoh 10:22.
-
Cikumba.
Khungu la nkhosa, mbuzi, ndi ana a ngʼombe yomwe anali kukonza kuti azilembapo. Zinali zolimba kusiyana ndi gumbwa ndipo anazisewenzetsa popanga mipukutu ya Baibo. Mipukutu yazikumba imene Paulo anapempha Timoteyo kuti amupelekele iyenela kuti panalembedwa mbali ina ya Malemba a Ciheberi. Mipukutu ina ya ku Nyanja Yakufa inali yacikumba.—2Ti 4:13.
-
Cilamulo ca Mose.
-
Cilamulo.
-
Cilungamo.
M’Malemba, mauwa amasewenzetsedwa pokamba za cinthu coyenela malinga ndi miyezo ya Mulungu pa nkhani ya cabwino ndi coipa.—Ge 15:6; De 6:25; Zef 2:3; Mt 6:33.
-
Cimalizilo ca nthawi ino.
Nthawi yokatifikitsa pa mapeto a dongosolo lino la zinthu, lolamulidwa ndi Satana. Nthawi imeneyi ndiyonso nthawi ya kukhalapo kwa Khristu. Motsogoleledwa ndi Yesu, angelo adzapita “kukacotsa oipa pakati pa olungama” n’kuwaononga. (Mt 13:40-42, 49) Ophunzila a Yesu anali kufuna kudziwa kuti nthawi ya “cimalizilo” imeneyi idzakhalapo liti. (Mt 24:3) Yesu asanabwelele kumwamba, analonjeza otsatila ake kuti adzakhala nao mpaka nthawi imeneyi.—Mt 28:20.
-
Cinsinsi copatulika.
-
Cipangano.
Mgwilizano wa pakati pa Mulungu ndi anthu kapena wa pakati pa anthu okha-okha. Amagwilizana kuti adzacita kapena sadzacita zinazake. Nthawi zina, amene ali mbali imodzi ya cipanganoco ndi amene anali kuyenela kucita zimene zikufunikazo ndipo limeneli kwenikweni linali kukhala lonjezo. Nthawi zina mbali zonse ziwili zinali kufunika kucita zinazake. Kupatula pa zipangano za pakati pa Mulungu ndi anthu, Baibo imanenanso za zipangano za pakati pa anthu, mapfuko, mitundu, kapena magulu a anthu. Zipangano zina, zimene zotsatila zake ndi za nthawi yaitali, ndi za pakati pa Mulungu ndi Abulahamu, Mulungu ndi Davide, Mulungu ndi mtundu wa Isiraeli (cipangano ca Cilamulo), ndiponso pakati pa Mulungu ndi Isiraeli wa Mulungu (cipangano catsopano).—Ge 9:11; 15:18; 21:27; Eks 24:7; 2Mb 21:7; Lu 22:29; Mac 3:25; 2Ak 3:6; Ahe 8:6.
-
Cisautso cacikulu.
Mau a Cigiriki amene anamasulilidwa kuti “cisautso,” amanena za kubvutika kapena kusowa mtendele cifukwa copanikizika ndi mabvuto enaake. Yesu ananena kuti ku Yerusalemu kudzakhala “cisautso cacikulu” cimene sicinacitikepo. Koma ananenanso maka-maka za “cisautso cacikulu” cimene cidzacitike padzikoli iyeyo atatsala pangʼono ‘kubwela ndi ulemelelo waukulu.’ (Mt 24:21, 29-31) Paulo ananena kuti cisautsoci cidzakhala ciweluzo colungama cimene Mulungu adzapeleke kwa anthu “osadziwa Mulungu komanso kwa anthu amene samvela uthenga wabwino” wonena za Yesu Khristu. Caputala 19 ca Cibvumbulutso cimaonetsa kuti Yesu ndi amene adzatsogolele magulu ankhondo akumwamba pomenyana ndi “cilombo, mafumu a dziko lapansi ndi asilikali ao.” (2At 1:6-8; Civ 19:11-21) Baibo imaonetsa kuti a “khamu lalikulu” adzapulumuka cisautso cimeneci. (Civ 7:9, 14)—Onani ARAMAGEDO.
-
Cisomo.
Mau ake a Cigiriki kwenikweni amanena za cinthu cobvomelezeka komanso cosangalatsa. Nthawi zambili mauwa amasewenzetsedwa ponena za mphatso yopelekedwa cifukwa ca kukoma mtima komanso mtima wopatsa. Akamanena za cisomo ca Mulungu, mauwa amanena za mphatso yaulele yopelekedwa moolowa manja ndi Mulungu, popanda kuyembekezela kuti wolandilayo abweze kenakake. Conco ndi umboni wa kuolowa manja, cikondi, komanso kukoma mtima kumene Mulungu amaonetsa anthu. Mau ake a Cigiriki nthawi zina amamasulilidwanso kuti “cifundo” komanso “mphatso yopelekedwa cifukwa ca kukoma mtima.” Wopelekayo sayembekezela kubwezeledwa ndipo sayangʼana ngati munthuyo ndi woyenela kupatsidwa mphatsoyo. Koma amangopeleka cifukwa coti ndi woolowa manja.—2Ak 6:1; Aef 1:7.
-
Cisonga cotosela.
Ndodo yosongoka kumapeto imene alimi anali kugwilitsa nchito potsogolela nyama. Mauwa amagwilitsidwanso nchito ponena za mau a munthu wanzelu amene amalimbikitsa munthu kutsatila malangizo othandiza. Mau akuti “kuponya miyendo nʼkumamenya zisonga zotosela” akucokela pa zimene ngʼombe yamakani inali kucita posafuna kutsogoleledwa. Inali kuponya miyendo kuti imenye ndodoyi, koma zotsatila zake zinali zoti inali kudzibvulaza.—Mac 26:14; Owe 3:31.
-
Citsamba cowawa.
Zitsamba zowawa kwambili koma zonunkhila bwino. Pa Cibvumbulutso 8:11, mau akuti “citsamba cowawa” amakamba za cakumwa cina cowawa kwambili komanso capoizoni cochedwa absinthe.
-
Ciwelewele.
Liu lomasulilidwa kucokela ku liu la Cigiriki lakuti por·neiʹa. M’Malemba, liuli limagwilitsidwa nchito ponena za mcitidwe ulionse wa zakugonana umene Mulungu amaletsa. Ciwelewele cimaphatikizapo cigololo, uhule, kugonana kwa anthu osakwatilana, mathanyula, komanso kugona nyama. M’buku la Cibvumbulutso, liu limeneli limagwilitsidwa nchito mophiphilitsa ponena za hule lauzimu lochedwa “Babulo Wamkulu” cifukwa cogwilizana ndi olamulila a dzikoli pofuna kukhala ndi ulamulilo komanso cuma. (Civ 14:8; 17:2; 18:3; Mt 5:32; Mac 15:29; Aga 5:19)—Onani HULE.
-
Cizindikilo.
-
Codetsedwa.
Mauwa anganene za kuda kwenikweni kapena kusakhala ndi makhalidwe abwino. Komabe mʼBaibo, nthawi zambili mauwa amanena za cinthu cosabvomelezeka komanso comwe si coyela malinga ndi Cilamulo ca Mose. (Le 5:2; 13:45; Mt 10:1; Mac 10:14; Aef 5:5)—Onani KUYELA.
-
Coyela.
D
-
Dalakima.
MʼMalemba a Cigiriki a Cikhristu, imeneyi inali ndalama yasiliva yomwe inali kulemela magalamu 3.4.—Mt 17:24.
-
Dekapole.
Dzina la mizinda ya Agiriki yomwe inalipo 10 (kucokela ku mau a Cigiriki akuti deʹka, kutanthauza “10,” ndi poʹlis, kutanthauza “mzinda”). Linalinso dzina la dela lakumʼmawa kwa Nyanja ya Galileya ndi Mtsinje wa Yorodano kumene kunali ina mwa mizindayi. Anthu a cikhalidwe ca Agiriki anali kukhala mʼmizinda imeneyi komanso kucitilamo malonda. Yesu anadutsapo mʼdela limeneli koma palibe umboni wakuti analowa mʼmizindayi.—Mt 4:25; Mko 5:20.
-
Dinari.
-
Dipo.
Malipilo opelekedwa kuti munthu amasulidwe ku ukapolo, ku mabvuto, komanso ku ucimo. Dipo lingatanthauzenso malipilo opelekedwa kuti munthu amasuke ku udindo wocita zinazake, kapenanso kuti munthu woyenela kulandila cilango asalangidwe. Malipilowo sanali kukhala ndalama nthawi zonse. (Yes 43:3) Dipo linali kupelekedwa pa zocitika zosiyana-siyana. Mwacitsanzo, ana onse aamuna oyamba kubadwa a anthu kapena a ziweto mu Isiraeli anali a Yehova, ndipo anali kufunika kumagwila nchito yake basi. Conco, anali kufunika kuwapelekela dipo kuti amasuke ku utumiki umenewo. (Nu 3:45, 46; 18:15, 16) Ngati ng’ombe yaikali sinayang’anilidwe bwino ndipo yapha munthu, mwiniwake ng’ombeyo anali kufunika kupeleka dipo kuti asaphedwe. (Eks 21:29, 30) Koma panalibe dipo lowombolela munthu wopha mnzake mwadala. (Num. 35:31) Baibo imakamba za dipo lofunika kwambili limene Khristu anapeleka pololela kufa kuti amasule anthu omvela ku ucimo ndi imfa.—Sl 49:7, 8; Mt 20:28; Aef 1:7.
-
Dzombe.
Mtundu wa ziwala zimene zimayenda m’magulu akulu-akulu. M’Cilamulo ca Mose, dzombe linali cakudya cosadetsedwa. Nthawi zina, dzombe linali kuononga zinthu kwambili mwa kudya zomela zilizonse zimene lapeza. Zikakhala telo, anthu anali kuona kuti umenewo ndi mlili wa dzombe.—Eks 10:14; Mt 3:4.
F
-
Fano; Kulambila mafano.
Fano ndi cifanizilo ca cinthu ceniceni kapena congoyelekezela cimene anthu amasewenzetsa polambila. Kulambila mafano kumatanthauza kupeleka ulemu, kukonda, komanso kulambila cifanizilo.—Sl 115:4; Mac 17:16; 1Ak 10:14.
-
Farao.
Dzina laudindo la mafumu a ku Iguputo. Baibo imachula maina a Afarao asanu (Sisaki, So, Tirihaka, Neko, ndi Hofira) koma Afarao ena sanachulidwe maina. Ena omwe sanachulidwe mainawo ndi amene nkhani zao zimakhudza Abulahamu, Mose, ndi Yosefe.—Eks 15:4; Aro 9:17.
-
Firate.
Mtsinje wautali komanso wofunika kwambili wakumʼmwela kwa Asia ndipo unali umodzi mwa mitsinje ikulu-ikulu ya ku Mesopotamia. Mtsinjewu umachulidwa koyamba pa Genesis 2:14 kuti unali umodzi mwa mitsinje inai ya mu Edeni. Nthawi zambili umangochulidwa kuti “Mtsinje.” (Ge 31:21) Mtsinjewu unali malile akumpoto kwa dziko limene Aisiraeli anapatsidwa.—Ge 15:18; Civ 9:14; 16:12.
G
-
Galeta.
-
Gehena.
Dzina la Cigiriki la Cigwa ca Hinomu, comwe cinali kum’mwela koma cakumadzulo kwa mzinda wamakedzana wa Yerusalemu. (Yer 7:31) Ulosi wina unakamba kuti mitembo idzaponyedwa kumeneko. (Yer 7:32; 19:6) Palibe umboni ulionse wakuti nyama kapena anthu anali kuponyedwa ku Gehena kuti atenthedwe kapena kuzunzika ali amoyo. Conco Gehena sitanthauza malo osaoneka kumene anthu amoyo amakazunzika m’moto weniweni kwamuyaya. Koma Yesu ndi ophunzila ake anagwilitsa nchito mau akuti Gehena mophiphilitsa pokamba za cilango ca “imfa yaciwili,” kutanthauza cionongeko cothelatu.—Civ 20:14; Mt 5:22; 10:28.
-
Gulu lampatuko.
Gulu la anthu limene limatsatila mfundo zinazake kapena mtsogoleli winawake ndipo limakhala ndi zikhulupililo zake. Mauwa amasewenzetsedwa ponena za magulu awili a Ciyuda, Afarisi ndi Asaduki. Anthu omwe sanali Akhristu anali kunena kuti Akhristu ndi “gulu lampatuko” kapena “gulu lampatuko la anthu a ku Nazareti” mwina poona kuti linacoka mʼcipembedzo ca Ciyuda. Patapita nthawi, magulu ampatuko anayambika mumpingo wa Cikhristu. Mwacitsanzo, buku la Cibvumbulutso limanena za “mpatuko wa Nikolao.”—Mac 5:17; 15:5; 24:5; 28:22; Civ 2:6; 2Pe 2:1.
-
Guwa.
Malo okwela opangidwa ndi dothi, miyala, cimwala kapena mitengo yokutidwa ndi citsulo amene anali kuwagwilitsa nchito polambila. Pa malowa anali kupelekelapo nsembe zonunkhila komanso nsembe zina. Mʼcipinda coyamba ca cihema komanso ca kacisi munali “guwa lansembe lagolide” lalingʼono lopelekelapo nsembe zonunkhila. Linapangidwa ndi matabwa okutidwa ndi golide. “Guwa lansembe lakopa” lalikulu lopelekelapo nsembe zina linali pabwalo.—Eks 39:38, 39; 1Mf 6:20; Mt 5:23, 24; Lu 1:11; Mac 17:23.
H
-
Hade.
Mau a Cigiriki amene amafanana tanthauzo ndi mau a Ciheberi akuti “Sheol.” Amamasulilidwa kuti “Manda” (“M” wamkulu), pofuna kuonetsa kuti amenewa ndi manda a anthu onse.—Onani MANDA.
-
Heme.
Mulungu wa Agiriki, mwana wa Zeu. Anthu a ku Lusitara analakwitsa nʼkumachula Paulo kuti Heme poganiza kuti iye ndi mulungu wao. Iwo anali kukhulupilila kuti mulungu ameneyu anali kupeleka uthenga wocokela kwa milungu komanso anali kuthandiza anthu kuti azilankhula mwaluso.—Mac 14:12.
-
Herode.
Dzina la mafumu a kubanja limene linasankhidwa ndi Aroma kuti lizilamulila Ayuda. Herode Wamkulu anachuka cifukwa comanganso kacisi wa ku Yerusalemu komanso cifukwa colamula kuti ana aphedwe pofuna kupha Yesu. (Mt 2:16; Lu 1:5) Herode Arikelawo ndi Herode Antipa anali ana a Herode Wamkulu ndipo anapatsidwa zigao zina za ufumu wa atate wao kuti azilamulila. (Mt 2:22) Antipa anali bwanamkubwa amene anali kuchulidwanso kuti “mfumu” ndipo ndi amene anali kulamulila pa zaka zitatu ndi hafu zimene Yesu anacita utumiki wake padzikoli, mpaka nthawi ya zocitika za mʼMacitidwe caputala 12. (Mko 6:14-17; Lu 3:1, 19, 20; 13:31, 32; 23:6-15; Mac 4:27; 13:1) Kenako Herode Agiripa Woyamba, mdzukulu wa Herode Wamkulu, anaphedwa ndi mngelo wa Mulungu atangolamulila kwa nthawi yocepa. (Mac 12:1-6, 18-23) Zitatelo mwana wake, Herode Agiripa Waciwili, anayamba kulamulila ndipo analamulila mpaka nthawi imene Ayuda anapandukila Aroma.—Mac 23:35; 25:13, 22-27; 26:1, 2, 19-32.
-
Hisope.
Comela ca nthambi komanso masamba ofewa comwe anali kusewenzetsa powaza magazi kapena madzi pamwambo woyeletsa. Nʼkutheka kuti cinali ca marjoram (Origanum maru; Origanum syriacum). Koma cimene cachulidwa pa Yohane 19:29, ciyenela kuti cinali marjoram amene anamumangilila kunthambi ya mtengo kapena mtundu winawake wa mapila wochedwa durra (Sorghum vulgare). Tikutelo cifukwa cakuti mapila a mtundu umenewu anali kukhala ndi phesi lalitali ndipo zinali zotheka kutengela vinyo wosasa nʼkuika pakamwa pa Yesu.—Ahe 9:19.
-
Hule.
Munthu amene amagonana ndi anthu ena omwe sanakwatilane nao, maka-maka pofuna kupeza ndalama. (Mau a Cigiriki amene anamasulilidwa kuti “hule” ndi porʹne, ndipo amacokela ku mau otanthauza “kugulitsa.”) Nthawi zambili mauwa amanena za akazi ngakhale kuti Baibo imakambanso za mahule aamuna. Cilamulo ca Mose cinali kuletsa uhule ndipo sicinali kulola kutenga malipilo auhule nʼkukapeleka kumalo opatulika a Yehova. Izi zinali zosiyana ndi anthu a mitundu ina, amene anali kugwilitsa nchito mahule apakachisi kuti apeze ndalama zamsonkho. (De 23:17, 18; 1Mf 14:24) Baibo imasewenzetsanso mauwa ponena za anthu, mitundu, kapena mabungwe amene amalambila mafano kwinaku akukamba kuti akulambilanso Mulungu. Mwacitsanzo, zipembedzo zonse zimene zimachedwa “Babulo Wamkulu,” zofotokozedwa m’buku la Cibvumbulutso zimanenedwa kuti ndi hule cifukwa cakuti zimagwilizana ndi olamulila a dzikoli kuti zipeze cuma komanso mphamvu.—Civ 17:1-5; 18:3; 1Mb 5:25.
I
-
Iluriko.
Cigao cimene cinali kulamulidwa ndi Aroma kumpoto cakumadzulo kwa Girisi. Paulo anafikako pa utumiki wake, koma Baibo silinena ngati analalikilako kapena anangofikako basi.—Aro 15:19.
-
Isiraeli.
Dzina limene Mulungu anapatsa Yakobo. Kenako dzinali linali kuimila mbadwa zonse za Yakobo. Mbadwa za ana 12 a Yakobo zinali kuchedwanso ana a Isiraeli, nyumba ya Isiraeli, amuna a Isiraeli, kapena Aisiraeli. Dzina lakuti Isiraeli linali kugwilitsidwanso ntchito ponena za ufumu wakumpoto wa mafuko 10 umene unapandukila ufumu wakumʼmwela. Patapita nthawi, dzinali linayambanso kuimila Akhristu odzozedwa omwe amachedwa “Isiraeli wa Mulungu.”—Aga 6:16; Ge 32:28; Mac 4:10; Aro 9:6.
J
-
Joko.
Mtengo umene anthu anali kunyamula paphewa nʼkukoloweka katundu mbali zonse. Nthawi zina unali kukhala mtengo umene anali kuika pakhosi pa nyama (nthawi zambili zinali kukhala ngʼombe) kuti zizikoka ngolo kapena zinthu zina. Popeza akapolo anali kusewenzetsa joko ponyamula katundu wolemela, mau akuti joko amawasewenzetsanso mophiphilitsa ponena za ukapolo, kugonjela munthu wina, kupondelezedwa, komanso kubvutika. Mau akuti kucotsa kapena kuthyola joko anali kutanthauza kumasula munthu kuti asakhalenso kapolo, asapondelezedwenso, kapena asamudyelenso masuku pamutu.—Le 26:13; Mt 11:29, 30.
K
-
Kacisi.
Nyumba ya ku Yerusalemu imene inalowa mʼmalo mwa cihema ndipo Aisiraeli anali kukumana kumeneko kuti alambile Mulungu. Kacisi woyamba anamangidwa ndi Solomo ndipo anaonongedwa ndi Ababulo. Waciwili anamangidwa ndi Zerubabele pambuyo poti Aisiraeli abwelako ku ukapolo wa ku Babulo ndipo kenako anamangidwanso ndi Herode Wamkulu. MʼMalemba, kacisiyu nthawi zambili amachedwa “nyumba.”—Mt 21:13; Lu 11:51; 1Mb 29:1; 2Mb 2:4; Mt 24:1.
-
Kaisara.
Dzina la kubanja lina la Ciroma lomwe linadzakhala dzina laudindo la olamulila a ku Roma. Ena mwa olamulila ochulidwa mʼBaibo amene anali kudziwika ndi dzinali ndi Augusto, Tiberiyo, ndi Kalaudiyo. Nayenso Nero anali Kaisara ngakhale kuti sachulidwa mʼBaibo. MʼMalemba a Cigiriki a Cikhristu, mauwa amagwilitsidwanso nchito pofotokoza za ulamulilo wa boma kapena wa dziko.—Mko 12:17; Mac 25:12.
-
Khalidwe lopanda manyazi.
Kucokela ku mau a Cigiriki akuti a·selʹgei·a, ndipo amanena za khalidwe lililonse lophwanya kwambili malamulo a Mulungu. Munthu wake amaonetsa kuti alibiletu manyazi, ndi wacipongwe, wopanda ulemu, ndiponso amadelela mwinanso kunyansidwa ndi olamulila, malamulo, komanso mfundo zoyenela kutsatila. Mauwa sanena za kulakwitsa zinthu zingʼono-zingʼono.—Aga 5:19; 2Pe 2:7.
-
Khate; Wakhate.
Matenda oopsya apakhungu. MʼMalemba, mau akuti khate samangokamba za matenda akhate amene anthu amawadziwa masiku ano cifukwa sanali kungogwila anthu okha, koma anali kugwilanso zobvala ndi nyumba. Munthu wodwala khate amadziwika kuti wakhate.—Le 14:54, 55; Lu 5:12.
-
Khonde Lazipilala la Solomo.
Mʼnthawi ya Yesu, amenewa anali malo okhala ndi mtenje mmene anthu anali kutha kudutsamo ndipo anali cakumʼmawa kwa bwalo lakunja. Anthu ambili amakhulupilila kuti imeneyi inali mbali yotsala ya kacisi wa Solomo. Yesu anayenda pamalo amenewa ‘mʼnyengo yozizilaʼ komanso Akhristu oyambilila anali kukumana pamalowa kuti alambile Mulungu.—Yoh 10:22, 23; Mac 5:12.
-
Khristu.
-
Kudzipeleka kwa Mulungu.
-
Kudzoza.
Mau ake a Ciheberi amatanthauza “kupaka zinthu zamadzi-madzi.” Anthu anali kuthila munthu kapena zinthu mafuta poonetsa kuti zasankhidwa kuti zigwile nchito yapadela. MʼMalemba a Cigiriki a Cikhristu, mauwa amagwilitsidwanso nchito ponena za kupeleka mzimu woyela kwa anthu amene ali ndi ciyembekezo copita kumwamba.—Eks 28:41; 1Sa 16:13; Lu 4:18; Mac 10:38; 2Ak 1:21.
-
Kuika manja.
-
Kukhalapo.
M’mavesi ena a Malemba a Cigiriki a Cikhristu, liu limeneli limakamba za nthawi ya kukhalapo kwa Yesu Khristu monga mfumu, kucokela pamene anaikidwa kukhala Mfumu kumwamba mpaka pa mapeto a masiku otsiliza a nthawi ino. Nthawi ya kukhalapo kwa Khristu si nthawi yocepa imene iye adzabwela n’kubwelelanso mwamsanga ai, koma ndi nthawi yaitali.—Mt 24:3.
-
Kukhulupilila zamizimu.
Cikhulupililo cakuti munthu akafa, cinacake cimakhalabe ndi moyo ndipo amatha kulankhulana ndi anthu amoyo kudzela mwa wolankhula ndi mizimu. Mau a Cigiriki amene anawamasulila kuti “kucita zamizimu” ndi akuti phar·ma·kiʹa, ndipo amatanthauza “kupeleka mankhwala.” Anali kusewenzetsa mauwa cifukwa cakuti kalelo anthu anali kusewenzetsa mankhwala akafuna kupeza mphamvu ya ziwanda kuti azicita zamizimu.—Aga 5:20; Civ 21:8.
-
Kukwapula.
MʼMalemba a Cigiriki a Cikhristu mauwa amanena za kumenya munthu ndi ndodo kapena ndi mkwapu wazingwe wokhala ndi timfundo kapena tinthu tolasa—Yoh 19:1.
-
Kulapa.
-
Kulila.
Kuonetsa cisoni moonekela cifukwa cakuti munthu wafeledwa kapena wakumana ndi mabvuto enaake. Kale anthu anali kulila kwa nthawi yaitali. Kuonjezela pamenepo, anali kulila mokweza, kubvala zovala zapadela, kudzithila phulusa mʼmutu, kungʼamba zobvala, komanso kudziguguda pacifuwa. Nthawi zina pamalilo, anthu anali kuitana olila aganyu.—Est 4:3; Mt 11:17; Mko 5:38; Yoh 11:33; Civ 21:4.
-
Kusala kudya.
Kukhala osadya cakudya ciliconse kwa nthawi inayake. Aisiraeli anali kusala kudya pa tsiku la Mwambo Wophimba Macimo, pa nthawi ya mabvuto, komanso akamafuna kuti Mulungu awatsogolele. Ayuda anakhazikitsa nthawi zinai zoti azisala kudya pacaka pokumbukila nthawi yobvuta pa umoyo wao. Akhristu sanalamulidwe kuti azisala kudya.—Eza 8:21; Yes 58:6; Mt 4:2; 9:14; Lu 18:12; Mac 13:2, 3; 27:9.
-
Kuuka kwa akufa.
Mau ake a Cigiriki ndi akuti a·naʹsta·sis ndipo amatanthauza “kuuka” kapena “kuimilila.” Baibo imachula anthu 9 amene anaukitsidwa ndipo wina ndi Yesu amene anaukitsidwa ndi Yehova Mulungu. Ngakhale kuti anthu enawo anaukitsidwa ndi Eliya, Elisa, Yesu, Petulo, ndi Paulo, zoona zake n’zakuti onsewa anaukitsidwa ndi mphamvu za Mulungu. Mfundo yakuti “Mulungu adzaukitsa olungama ndi osalungama omwe” padzikoli imagwilizana ndi colinga cake. (Mac 24:15) Baibo imakambanso za kuuka “koyamba” kopita kumwamba kumene kudzacitika kwa abale ake a Yesu odzozedwa ndi mzimu.—Afi 3:11; Civ 20:5, 6; Yoh 5:28, 29; 11:25.
-
Kuyela; Ciyelo.
Yehova ndi woyela. Mau akuti kuyela amatanthauza kukhala ndi makhalidwe osadetsedwa komanso kupatulika. (Eks 28:36; 1Sa 2:2; Miy 9:10; Yes 6:3) Mau a Ciheberi ndi a Cigiriki amene anawamasulila kuti kuyela, ngati akukamba za anthu (Eks 19:6; 2Mf 4:9), nyama (Nu 18:17), zinthu (Eks 28:38; 30:25; Le 27:14), malo (Eks 3:5; Yes 27:13), nthawi (Eks 16:23; Le 25:12,) kapena zocitika zina (Eks 36:4), amatanthauza kuti cinthuco n’capadela, copatulika, coyeletsedwa kuti cikhale ca Mulungu, kapena coikidwa padela kuti cigwilitsidwe nchito potumikila Yehova. MʼMalemba a Cigiriki a Cikhristu mau akuti “kuyela” amatanthauzanso kuikidwa padela kuti cikhale ca Mulungu. Mauwa amagwilitsidwanso nchito ponena za kukhala ndi makhalidwe osadetsedwa.—2Ak 7:1; 1Pe 1:15, 16.
L
-
Leputoni.
Pomwe Malemba a Cigiriki a Cikhristu anali kulembedwa, lepitoni kanali kandalama kakopa kakangʼono kwambili ka Ayuda. Ma Baibo ena amamasulila mauwa kuti “mite”.—Mko 12:42; Lu 21:2; mau a m’munsi.
-
Levi; Mlevi.
Mwana wacitatu wa Yakobo ndipo mai ake anali Leya. Komanso ndi dzina la pfuko la Levi. Ana ake atatu anadzakhala atsogoleli a magulu atatu akulu-akulu a Alevi. Nthawi zina mau akuti “Alevi” amanena za pfuko lonse, koma nthawi zambili amapatulapo banja la Aroni lomwe munali kucokela ansembe. Pfuko la Levi silinalandile malo mʼDziko Lolonjezedwa, koma linapatsidwa mizinda 48 ya mʼmalo amene anapelekedwa kwa mapfuko ena.—De 10:8; 1Mb 6:1; Ahe 7:11.
-
Likasa la cipangano.
Bokosi lopangidwa ndi matabwa a mtengo wa mthethe ndipo analikuta ndi golide. Linali kusungidwa mʼMalo Opatulika Koposa a cihema ndipo kenako mʼMalo Opatulika Koposa a kacisi wa Solomo. Linali ndi cibvundikilo cagolide colimba cokhala ndi akerubi awili oyangʼanizana. Mkati mwake munali miyala iwili ya Malamulo Khumi ndi zinthu zina.—De 31:26; 1Mf 6:19; Ahe 9:4.
-
Lipenga.
Cipangizo cocita kufuzilila copangidwa ndi citsulo cimene anali kusewenzetsa poimba komanso pofuna kupeleka cizindikilo. Nthawi zambili, kulila kwa lipenga mophiphilitsa kumayendela limodzi ndi kulengeza ziweluzo za Yehova kapena zinthu zina zapadela zocokela kwa Mulungu.—1Ak 15:52; Civ 8:7–11:15.
-
Lubani.
Utomoni wouma wa mitengo kapena zitsamba zina za mʼgulu la Boswellia. Lubani akawochedwa amanunkhila bwino kwambili. Anali mʼgulu la zinthu zopangila zonunkhila zopatulika za pacihema komanso za mʼkachisi. Anali kumupeleka limodzi ndi nsembe ya ufa komanso anali kumuika pakati pa mikate yoonetsa kwa Mulungu mʼMalo Opatulika.—Eks 30:34-36; Le 2:1; 24:7; Mt 2:11.
-
Lumbilo.
Mau amene munthu amanena pofuna kutsimikizila kuti zinazake ndi zoona kapena lonjezo lotsimikizila kuti munthu adzacita kapena sadzacita zinazake. Nthawi zambili linali kukhala lonjezo limene munthu anali kupanga kwa winawake wamkulu, maka-maka kwa Mulungu. Yehova anatsimikizila cipangano cake kwa Abulahamu mwa kulumbila.—Ge 14:22; Ahe 6:16, 17.
M
-
Maele.
-
Makedoniya.
Cigao ca kumpoto kwa Girisi ndipo cinali cochuka mu ulamulilo wa Alekizanda Wamkulu. Cigaoci cinali coima pacokha mpaka nthawi imene cinagonjetsedwa ndi Aroma. Pa nthawi imene Paulo anapita ku Europe, cigao ca Makedoniya cinali kulamulidwa ndi Aroma. Paulo anafika ku Makedoniya maulendo atatu.—Mac 16:9.
-
Malemba.
-
Malo Opatulika.
Cipinda coyamba komanso cacikulu ca cihema kapena kacisi ndipo nʼcosiyana ndi cipinda camkati kwambili cochedwa Malo Opatulika Koposa. Mʼcihema, mʼMalo Opatulika munali kukhala coikapo nyale cagolide, guwa lansembe zofukiza lagolide, thebulo la mikate yacionetselo, komanso ziwiya zagolide. MʼMalo Opatulika amʼkacisi munali kupezeka guwa lagolide, zoikapo nyale 10 zagolide, komanso mathebulo 10 a mikate yacionetselo.—Eks 26:33; Ahe 9:2.
-
Malo Opatulika Koposa.
Cipinda camkati kwambili mwa cihema komanso kacisi kumene anali kusungilako likasa la cipangano. Anali kuchedwanso kuti Malo Oyela Koposa. Malinga ndi Cilamulo ca Mose, mkulu wa ansembe yekha ndiye anali kuloledwa kulowa mʼMalo Opatulika Koposa ndipo anali kuyenela kulowamo pa Tsiku la Mwambo Wophimba Macimo basi.—Eks 26:33; Le 16:2, 17; 1Mf 6:16; Ahe 9:3.
-
Manda acikumbutso.
Malo amene amaikamo thupi la munthu amene wamwalila. Mauwa anamasulilidwa kucokela ku mau a Cigiriki akuti mne·meiʹon. Mau a Cigirikiwa amacokela ku mau otanthauza “kukumbutsa” poonetsa kuti munthu womwalilayo akukumbukilidwa.—Yoh 5:28, 29.
-
Manda.
Akalembedwa ndi “m” wamngʼono amanena za manda amodzi, koma akalembedwa ndi “M” wamkulu amanena za manda a anthu onse omwe pa Ciheberi ndi “Sheol” ndipo pa Cigiriki ndi “Hade.” Baibo imafotokoza kuti Manda ndi malo ophiphilitsa kumene munthu sangacite ciliconse ndipo sadziwa kalikonse.—Ge 47:30; Mla 9:10; Mt 27:61; Mac 2:31.
-
Mankhusu.
Makoko a mbeu monga mpunga kapena tiligu amene amacotsedwa popuntha kapena pouluza mbeuzo. Liu lakuti mankhusu amalisewenzetsa mophiphilitsa potanthauza zinthu zopanda nchito komanso zosafunika.—Sl 1:4; Mt 3:12.
-
Mana.
Cakudya cimene Aisiraeli anali kudya mʼcipululu kwa zaka 40. Yehova ndiye anali kuwapatsa cakudyaci. Tsiku lililonse mʼmawa kupatulapo la Sabata, mana anali kupezeka pansi atakutidwa ndi mame. Aisiraeli ataona mana kwa nthawi yoyamba anali kufunsa kuti, “Ici nʼciani?” kapena mʼCiheberi “man huʼ?” (Eks 16:13-15, 35) Yesu anagwilitsanso nchito mau oti mana mophiphilitsa.—Yoh 6:49, 50.
-
Masiku otsiliza.
Mau amenewa amasewenzetsedwa mʼmaulosi a mʼBaibo pofotokoza nthawi imene zocitika za padzikoli zidzafike pacimake. (Eze 38:16; Da 10:14; Mac 2:17) Malinga ndi zimene ulosi umanena, nthawi imeneyi ikhoza kukhala zaka zocepa kapena zambili. Nthawi zambili, Baibo imasewenzetsa mauwa ponena za masiku otsiliza a dziko loipali omwe akuyendela limodzi ndi nthawi ya kukhalapo kwa Yesu kosaonekela.—2Ti 3:1; Yak 5:3; 2Pe 3:3.
-
Matangadza.
Cinthu cimene anali kuikamo munthu pofuna kumulanga. Mʼmatangadza ena, munthu anali kumulowetsa mapazi okha pomwe ena anali kumulowetsa mapazi, manja, ndi khosi moti thupi linali kupindika.—Yer 20:2; Mac 16:24.
-
Matumba azikumba.
Matumba opangidwa ndi zikumba za nyama monga nkhosa kapena mbuzi omwe anali kusungilamo vinyo. Vinyo watsopano anali kuikidwa mʼmatumba atsopano cifukwa cakuti vinyoyo akayamba kuwila anali kutulutsa mpweya wa carbon dioxide womwe unali kucititsa kuti matumba afufume. Koma matumbawo akakhala kuti ndi akale anali kungophulika.—Yos 9:4; Mt 9:17.
-
Mdulidwe.
-
Mdyelekezi.
-
Mesiya.
Mauwa anacokela ku mau a Ciheberi otanthauza “kudzozedwa” kapena “wodzozedwa.” Mau a Cigiriki ofanana nao ndi akuti “Khristu.”—Da 9:25; Yoh 1:41.
-
Mfulu; Munthu womasulidwa.
Mu ulamulilo wa Aroma, anthu ena anali kubadwa ndi ufulu wonse monga nzika pomwe ena anali kukhala ndi ufulu akamasulidwa ku ukapolo. Ena akamasulidwa anali kukhala nzika koma sanali kugwila nao nchito mʼboma pomwe ena akamasulidwa sanali kupatsidwa ufulu wonse umene nzika zinali kukhala nao.—1Ak 7:22.
-
Mheberi.
Abulamu (Abulahamu) ndi amene anali woyamba kuchulidwa ndi dzina limeneli ndipo linali kumusiyanitsa ndi anthu a Ciamori amene anayandikana nao. Kenako mbadwa za Abulahamu, kudzela mwa mdzukulu wake Yakobo, zinali kuchedwa Aheberi ndipo cinenelo cao cinali kuchedwa Ciheberi. Pamene Yesu anali padzikoli, Ciheberi cinali ndi mau ambili a Ciaramu ndipo ndi cinenelo cimene iye ndi ophunzila ake anali kulankhula.—Ge 14:13; Eks 5:3; Mac 26:14.
-
Mikate yacionetselo.
Mitanda 12 ya mkate imene inali kuikidwa mʼMalo Opatulika a pacihema kapena mʼkachisi. Inali kuikidwa pathebulo, mbali ina 6 mbali ina 6. Inali kuchedwanso kuti “mikate yosanjikiza,” komanso “mikate yoonetsa kwa Mulungu.” Pa tsiku la Sabata, mikateyi anali kuicotsapo nʼkuikapo yatsopano. Ansembe okha ndi amene anali kuyenela kudya mikate yomwe yacotsedwayo.—2Mb 2:4; Eks 25:30; Le 24:5-9; Mt 12:4; Ahe 9:2.
-
Mina.
MʼMalemba a Cigiriki a Cikhristu, ndalama ya mina inali yofanana ndi madalakima 100 ndipo inali kulemela magalamu 340.—Lu 19:13.
-
Mkhalapati.
-
Mkhristu.
Dzina limene Mulungu anapatsa otsatila a Yesu Khristu.—Mac 11:26; 26:28.
-
Mkono.
Muyezo wodziwila kutalika kwa cinthu ndipo anali kuyeza kucokela pa cigongono kufika pamapeto pa cala capakati. Kwa Aisiraeli, muyezo wa mkono unali pafupifupi masentimita 44.5, koma analinso ndi muyezo wina wotalikilapo umene unali pafupifupi masentimita 51.8.—Ge 6:15; Mt 6:27; Lu 12:25; Civ 21:17.
-
Mkulu wa angelo.
-
Mkulu wa ansembe.
M’Cilamulo ca Mose, ameneyu anali wansembe wamkulu amene anali kuimila anthu pamaso pa Mulungu komanso kuyang’anila ansembe anzake. Anali kuchedwanso “wansembe wamkulu.” (2Mb 26:20; Eza 7:5) Iye yekha ndiye anali kuloledwa kulowa m’Malo Opatulika Koposa, kutanthauza m’cipinda camkatikati ca cihema, ndipo pambuyo pake m’cipinda camkatikati ca kacisi. Iye anali kulowamo kamodzi cabe pa caka pa Tsiku Lophimba Macimo. Yesu Khristu nayenso amachedwa “mkulu wa ansembe.”—Le 16:2, 17; 21:10; Mt 26:3; Ahe 4:14.
-
Mkulu; Wacikulile.
Mwamuna wamkulu msinkhu. Koma mʼMalemba, mauwa amakamba za munthu amene ali ndi udindo kudela kapena mʼdziko. Mʼbuku la Cibvumbulutso mauwa amakambanso za zolengedwa zakumwamba. Mau a Cigiriki akuti pre·sbyʹte·ros amamasulilidwa kuti “mkulu” akamakamba za anthu amene ali ndi udindo wotsogolela mumpingo wa Cikhristu.—Eks 4:29; Miy 31:23; 1Ti 5:17; Civ 4:4.
-
Mlembi.
Munthu wokopela Malemba a Ciheberi. M’nthawi ya Yesu, mauwa anali kukamba za anthu amene anali ophunzila Cilamulo omwenso anali kutsutsa Yesu.—Eza 7:6 mau amʼmunsi; Mko 12:38, 39; 14:1.
-
Mlili.
Matenda alionse amene anali kufalikila mofulumila komanso kupha anthu ambili.—Lu 21:11.
-
Mlonda.
Munthu amene amalondela anthu kapena katundu ndipo nthawi zambili amacita zimenezi usiku. Alonda akale anali kuliza lipenga akaona zoopsya. Iwo anali kukonda kukhala pamwamba pa mipanda ya mzinda kapena pansanja kuti aziona anthu amene akubwela asanafike pafupi. Asilikali a nkhondo naonso anali kukhala ndi alonda.—Mt 27:65; 28:4.
-
Mnazareti.
-
Moloki.
Mulungu wa Aamoni ndipo zikuoneka kuti amachedwanso Malikamu, Milikomu, ndi Moleki.—Mac 7:43.
-
Mopondela mphesa.
Nthawi zambili anali kukhala maenje awili opangidwa pamwala walaimu. Dzenje lina linali kukhala pamwamba, lina m’munsi ndipo panali kukhala kangalande kolumikiza maenjewo. Anthu akamaponda mphesa mʼdzenje lalikululo, madzi ake anali kupita mʼdzenje lalingʼono. Mauwa amagwilitsidwanso nchito mophiphilitsa ponena za ciweluzo ca Mulungu.—Civ 19:15.
-
Mpando woweluzila milandu.
Nthawi zambili, malowa anali kukhala pa malo okwela ndipo anali ndi masitepe. Anthu audindo anali kukhala pa malo amenewa kuti alankhule ndi anthu kapena kupeleka ciweluzo. Mau akuti “mpando woweluzila wa Mulungu” kapena “mpando woweluzila milandu wa Khristu” ndi ophiphilitsa ndipo amaimila zimene Yehova wakonza kuti adzaweluze anthu onse.—Aro 14:10; 2Ak 5:10; Yoh 19:13.
-
Mpatuko.
Mau ake a Cigiriki (a·po·sta·siʹa) amacokela ku mau otanthauza “kucoka.” Mauwa amatanthauza “kusiya” kapena “kugalukila.” MʼMalemba a Cigiriki a Cikhristu, amasewenzetsa mauwa ponena za anthu amene asiya kulambila koona.—Miy 11:9; Mac 21:21; 2At 2:3.
-
Mphatso zacifundo.
Mphatso zopelekedwa kwa wosauka kuti zimuthandize. Mphatso zimenezi sizichulidwa mwacindunji m’Malemba a Ciheberi. Koma kupitila m’Cilamulo, Mulungu anapeleka malangizo omveka bwino kwa Aisiraeli ofotokoza udindo wao pothandiza osauka.—Mt 6:2.
-
Mphelo.
Mwala wozungulila umene anali kuuika pamwamba pa mwala unzake ndipo anali kuusewenzetsa popela ufa. Panali cikhomo cimene anali kuciika pakati pa mwala wapansi comwe cinali kuthandiza kuti mphelo izizungulila. M’nthawi za m’Baibo, anthu ambili anali kukhala ndi mphelo zazing’ono ndipo azimai ndi amene anali kuzigwilitsa nchito. Popeza banja linali kudalila mphelo kuti lipeze cakudya, Cilamulo ca Mose cinali kuletsa kutenga mphelo ngati cikole ca nkhongole. Mphelo zikulu-zikulu zinali kuyendetsedwa ndi nyama.—De 24:6; Mko 9:42.
-
Mpingo.
Gulu la anthu limene lasonkhana pamodzi kuti licite zinazake. MʼMalemba a Ciheberi, mauwa nthawi zambili amanena za mtundu wa Aisiraeli. MʼMalemba a Cigiriki a Cikhristu, mauwa amanena za mipingo yosiyana-siyana ya Akhristu, koma nthawi zambili, amanena za Akhristu onse monga mpingo.—1Mf 8:22; Mac 9:31; Aro 16:5.
-
Mpukutu.
Colembapo cacitali copangidwa kucokela ku cikumba kapena gumbwa ndipo anali kulemba mbali imodzi yokha. Nthawi zambili anali kuukulunga pakandodo. Malemba anali kukopeledwa pamipukutu ndipo pamene Baibo inali kulembedwa, mabuku a nthawi imeneyo anali amenewa.—Lu 4:17-20; 2Ti 4:13.
-
Mtengo.
Mtengo woongoka umene anali kupacikapo munthu amene ali ndi mlandu. Anthu a mitundu ina anali kuphela munthu pamtengo kapena kupacika mtembo wake kuti acenjeze anthu ena kapena amucititse manyazi. Asuri anali kucita nkhanza kwambili pankhondo cifukwa akagwila adani ao, anali kuwapacika powaboola ndi mtengo pamimba womwe unali kufika mʼcifuwa. Koma Ayuda, malinga ndi malamulo ao, munthu amene wapalamula mlandu waukulu monga kunyoza Mulungu kapena kulambila mafano, anali kumupha mwa kumuponya miyala coyamba kapena mwa njila inayake, kenako nʼkupacika mtembo wake pamtengo kuti ena atengelepo phunzilo. (De 21:22, 23; 2Sa 21:6, 9) Nthawi zina, Aroma anali kungomangilila munthu pamtengo moti anali kukhala masiku angapo kenako nʼkufa cifukwa ca ululu, ludzu, njala, kapena kutentha kwa dzuwa. Koma nthawi zina anali kumukhomelela manja ndi mapazi pamtengo ngati mmene anacitila ndi Yesu. (Lu 24:20; Yoh 19:14-16; 20:25; Mac 2:23, 36)—Onani MTENGO WOZUNZIKILAPO.
-
Mtengo wa moyo.
Mtengo wamʼmunda wa Edeni. Baibo silionetsa kuti zipatso za mtengowu zinali ndi mphamvu yopatsa moyo. Koma unali cizindikilo cakuti Yehova angapeleke moyo wosatha kwa anthu amene waalola kudya zipatso za mtengowo. M’buku la Cibvumbulutso, umafotokozedwa ngati cizindikilo ca makonzedwe a Mulungu codzapeleka moyo wosatha.—Ge 2:9; 3:22; Civ 2:7; 22:19.
-
Mtengo wozunzikilapo.
Mau amenewa anamasulilidwa kucokela ku liu la Cigiriki lakuti stau·rosʹ, limene limatanthauza mtengo woongoka monga umene anaphelapo Yesu. Palibe umboni ulionse wakuti liu la Cigiriki limeneli limatanthauza mtanda, monga umene anthu akunja anali kuusewenzetsa ngati cizindikilo ca cipembedzo kwa zaka mahandiledi Yesu asanabwele pa dziko lapansi. Mau akuti “mtengo wozunzikilapo” amamveketsa bwino tanthauzo la liu la Cigiriki lakuti stau·rosʹ, cifukwa cakuti liuli limagwilitsidwanso nchito poonetsa kuti otsatila a Yesu adzazunzidwa, kubvutika, ndi kucititsidwa manyazi. (Mt 16:24; Ahe 12:2)—Onani MTENGO.
-
Mtumiki Wamkulu.
-
Mtumiki wothandiza.
Mau ake a Cigiriki ndi akuti di·aʹko·nos, ndipo nthawi zambili amamasulilidwa kuti “mtumiki.” “Mtumiki wothandiza” ndi munthu amene amatumikila mothandiza akulu mumpingo. Kuti munthu akhale mtumiki amafunika kukwanilitsa mfundo zina za mʼBaibo.—1Ti 3:8-10, 12.
-
Mtumwi.
-
Mule.
Utomoni wonunkhila wocokela ku zitsamba zosiyana-siyana komanso mitengo ingʼono-ingʼono ya mʼgulu la Commiphora. Mule anali mʼgulu la zinthu zopangila mafuta opatulika odzozela. Anali kumusewenzetsa ponunkhilitsa zinthu monga zobvala kapena mabedi komanso anali kumuphatikiza ndi mafuta odzola. Mule anali kumusewenzetsanso pokonza thupi la munthu wakufa kuti akaliike mʼmanda.—Eks 30:23; Miy 7:17; Mko 15:23; Yoh 19:39.
-
Mwala wapakona.
Mwala umene unali kuikidwa pakona polumikiza makoma awili ndipo unali kuthandiza kuti makonawo alimbe. Mwala wapakona wofunika kwambili unali kukhala pamaziko. Anthu akafuna kumanga nyumba zikulu-zikulu kapena mpanda wa mzinda, anali kusankha mwala wolimba kwambili. Mauwa amagwilitsidwanso nchito mophiphilitsila ponena za kukhazikitsidwa kwa dziko. Yesu amanenedwa kuti ndi “mwala wapakona wa maziko” a mpingo wa Cikhristu womwe umayelekezeledwa ndi nyumba yauzimu.—Aef 2:20; Yob 38:6.
-
Mwambi.
Mau anzelu kapena nthano imene imaphunzitsa anthu kapenanso kukamba mfundo yoona mʼmau ocepa. Miyambi ya mʼBaibo itha kukhala mau okuluwika kapena cilapi. Mfundo za coonadi zimafotokozedwa mʼmiyambi mʼnjila yomveka bwino kapena moyelekezela ndi zinthu zina. Koma miyambi ina imakhala mau ofala onyozela anthu ena.—Mla 12:9; 2Pe 2:22.
-
Mwana wa Davide.
-
Mwana wa munthu.
Mau amenewa amapezeka maulendo pafupifupi 80 m’mabuku a Uthenga Wabwino. Amakamba za Yesu Khristu, ndipo amaonetsa kuti iye atabadwa anakhala munthu weniweni, osati mngelo wobvala thupi la munthu. Mauwa amaonetsanso kuti Yesu anali kudzakwanilitsa ulosi wa pa Danieli 7:13, 14. M’Malemba a Ciheberi, mau akuti mwana wa munthu anagwilitsidwa nchito pochula Ezekieli ndi Danieli pofuna kuonetsa kuti iwo anali cabe anthu olankhulilako Mulungu polengeza uthenga wake.—Eze 3:17; Da 8:17; Mt 19:28; 20:28.
-
Mwana woyamba kubadwa.
Nthawi zambili mauwa anali kukamba za mwana wamwamuna wamkulu wa tate (osati wa mai). M’nthawi za Baibo, mwana wamwamuna woyamba kubadwa anali kulemekezedwa kwambili mʼbanja ndipo ndiye anali kutsogolela banjalo atate ake akamwalila. Kuonjezela pa kukhala woyamba kubadwa wa Yehova, Yesu ndiye anali woyamba kubadwa wa cilengedwe conse kucoka kwa akufa.—Ge 25:33; Eks 11:5; Akl 1:15; Civ 1:5.
-
Mwiitopiya.
Munthu wocokela ku dziko la Itiyopiya. Dziko lakale lakumʼmwela kwa Iguputo. Dela la dzikoli linali kufika kumʼmwela kwenikweni kwa dziko la Iguputo komanso hafu ya kumpoto kwa dziko la Sudan.—Mac 8:27.
-
Myuda.
Dzina limene linali kugwilitsidwa nchito ponena za munthu wa fuko la Yuda pambuyo poti ufumu wa mafuko 10 a Isiraeli wagonjetsedwa. (2Mf 16:6) Aisiraeli atabwela ku ukapolo wa ku Babulo, dzina lakuti Ayuda linali kusewenzetsedwa ponena za Aisiraeli a mafuko osiyana-siyana amene anabwelela ku Isiraeli. (Eza 4:12) Patapita nthawi, dzinali linali kugwilitsidwa nchito padziko lonse posiyanitsa Aisiraeli ndi anthu a mitundu ina. (Est 3:6) Paulo anagwilitsanso nchito dzinali mophiphilitsa pofuna kuonetsa kuti mtundu wa munthu si nkhani yaikulu mumpingo wa Cikhristu.—Aro 2:28, 29; Aga 3:28.
-
Mzati.
Cinthu coimilila cimene cinali kuthandiza kuti cinthu comangidwa ciimilile. Mizati inagwilitsidwa nchito m’kacisi komanso pa nyumba yacifumu imene Solomo anamanga. M’Malemba a Cigiriki a Cikhristu, liuli limagwilitsidwanso nchito mophiphilitsa potanthauza kucilikiza (1Ti 3:15) kapena kukhazikika pa malo enaake (Civ 3:12).—Owe 16:29; 1Mf 7:21.
-
Mzimu.
Mau a Ciheberi akuti ruʹach komanso a Cigiriki akuti pneuʹma, amene amamasulilidwa kuti mzimu amatanthauza zambili. Matanthauzo onsewo amanena za cinthu cosaoneka koma mphamvu yake imaoneka. Mau a Ciheberi komanso a Cigirikiwa amanena za (1) mphepo, (2) mphamvu ya moyo ya mʼzolengedwa zapadziko lapansi, (3) mphamvu yocokela mumtima wophiphilitsa wa munthu imene imamucititsa kuti azicita kapena kulankhula mʼnjila inayake, (4) mau ouzilidwa ocokela kwa winawake wosaoneka, (5) zolengedwa zauzimu, komanso (6) mphamvu yogwila nchito ya Mulungu kapena kuti mzimu woyela.—Eks 35:21; Sl 104:29; Mt 12:43; Lu 11:13.
-
Mzimu woyela.
N
-
Nado.
Mafuta onunkhila komanso odula kwambili. Anali kukhala ofiilila ndipo anali kucokela ku zomela zochedwa Nardostachys jatamansi. Popeza anali odula, nthawi zina anali kuwasakaniza ndi mafuta ena otsikilapo ndipo nado wina sanali kukhala weniweni. Mpake kuti Maliko ndi Yohane ananena kuti mafuta amene Yesu anathilidwa anali “nado weniweni.”—Mko 14:3; Yoh 12:3.
-
Ndodo yacifumu.
Ndodo imene wolamulila anali kunyamula poonetsa kuti ndi mfumu komanso ali ndi mphamvu.—Ge 49:10; Ahe 1:8.
-
Nisani.
Dzina latsopano limene anapatsa mwezi wa Abibu pambuyo poti Aisiraeli abwelako ku ukapolo wa ku Babulo. Unali mwezi woyamba pa kalenda yopatulika ya Ayuda komanso mwezi wa 7 pa kalenda ya anthu onse. Unali kuyamba pakati pa mwezi wa March mpaka pakati pa April. (Ne 2:1) Ayuda anali kukondwelela Pasika pa Nisani 14, ndipo ndi pa tsiku limeneli, pamene Yesu anayambitsa Mwambo wa Cakudya Camadzulo ca Ambuye. (Lu 22:15, 19, 20) Iye anaphedwa pa mtengo wozunzikilapo pa tsiku limeneli.—Lu 23:44-46.
-
Njila.
MʼMalemba, mauwa amasewenzetsedwa mophiphilitsa ponena za njila yocitila zinthu kapena khalidwe linalake lomwe ndi lobvomelezeka kapena losabvomelezeka kwa Yehova. Anthu amene anakhala otsatila a Yesu Khristu anali kunenedwa kuti amatsatila “Njilayo,” kutanthauza kuti anali kukhulupilila Yesu Khristu komanso kutengela citsanzo cake pa umoyo wao.—Mac 19:9.
-
Nsalu yochinga.
-
Nsembe yacakumwa.
Nsembe ya vinyo imene anali kuithila paguwa ndipo anali kuipeleka limodzi ndi nsembe zina zambili. Paulo anagwilitsa nchito mauwa mophiphilitsa poonetsa kuti anali kufunitsitsa kuthandiza Akhristu anzake.—Nu 15:5, 7; Afi 2:17.
-
Nsembe yamacimo.
Nsembe imene munthu anali kupeleka cifukwa cakuti wacita chimo mosadziwa cifukwa cakuti anali wopanda ungwilo. Panali nyama zosiyana-siyana zimene anali kupeleka malinga ndi udindo wa munthuyo komanso mmene zinthu zilili pa umoyo wake. Anali kukwanitsa kupeleka nyama yaikulu monga ngʼombe kapena nyama yaingʼono monga njiwa.—Le 4:27, 29; Ahe 10:8.
-
Nsembe yopsyeleza.
Nyama imene inali kutenthedwa paguwa la nsembe ngati nsembe yathunthu yopeleka kwa Mulungu. Palibe mbali iliyonse ya nyamayo (ngʼombe yaimuna, nkhosa yaimuna, mbuzi yaimuna, njiwa, kapena nkhunda) imene inali kutengedwa ndi wopeleka nsembeyo.—Eks 29:18; Le 6:9; Mko 12:33; Ahe 10:6.
-
Nsembe.
Zinthu zimene munthu amapeleka kwa Mulungu pofuna kumuthokoza, kubvomeleza kuti walakwitsa, komanso pofuna kuti akhalenso naye pa ubwenzi. Kuyambila nthawi ya Abele, anthu anali kupeleka nsembe zosiyana-siyana mwa kufuna kwao ndipo nsembe zina zinali kukhala za nyama. Cilamulo ca Mose citapelekedwa, kupeleka nsembe linali lamulo. Yesu atapeleka moyo wake ngati nsembe yangwilo, nsembe za nyama sizinali zofunikilanso. Komabe Akhristu amapeleka nsembe zauzimu kwa Mulungu.—Ge 4:4; Ahe 13:15, 16; 1Yo 4:10.
-
Nthanda.
Mauwa angatanthauzenso “nyenyezi yamʼmawa.” Imeneyi ndi nyenyezi yomalizila kutuluka imene imaonekela cakumʼmawa dzuwa lisanatuluke ndipo imaonetsa kuti kukuca.—Civ 22:16; 2Pe 1:19.
-
Nthawi.
Liu limeneli linamasulilidwa kucokela ku liu la Cigiriki lakuti ai·onʹ likamanena za zinthu kapena zocitika za pa nyengo inayake zimene zimapangitsa nyengoyo kukhala yapadela. Baibo imagwilitsa nchito mau akuti “nthawi ino” pofotokoza mmene zinthu zikuyendela padzikoli kuphatikizapo makhalidwe ndi zocita za anthu a m’dzikoli. (2Ti 4:10) Kudzela m’Cipangano ca Cilamulo, Mulungu anayambitsa nthawi imene ena angaiche nthawi ya Aisiraeli kapena kuti ya Ayuda. Pamene Yesu Khristu anapeleka moyo wake monga nsembe ya dipo, Mulungu anamugwilitsa nchito poyambitsa nthawi ina yosiyana, imene imakhudza kwambili mpingo wa Akhristu odzozedwa. Ici cinali ciyambi ca nthawi yatsopano ya zinthu zenizeni zimene zinali kuimilidwa ndi zinthu za m’Cilamulo. Mau akuti nthawi angagwilitsidwenso nchito pofotokoza nyengo zosiyana-siyana, kapena mmene zinthu zakhala zikuyendela, mmene zilili palipano, komanso mmene zidzakhalila kutsogolo.—Mt 24:3; Mko 4:19; Aro 12:2; 1Ak 10:11.
-
Nyama za guwa lansembe.
Zinthu zooneka ngati nyanga zimene zinali kukhala mʼmakona anai a maguwa ena.—Le 8:15; 1Mf 2:28; Civ 9:13.
-
Nyanga.
Mauwa amanena za nyanga za nyama zomwe anali kusewenzetsa pomwela zinthu, kusungilamo zinthu monga mafuta, inki, ndi zodzikongoletsela. Nyanga anali kuzisewenzetsanso ngati zipangizo zoimbila kapena zopelekela uthenga. (1Sa 16:1, 13; 1Mf 1:39; Eze 9:2) Mau akuti “nyanga” nthawi zambili amagwilitsidwanso nchito mophiphilitsa ponena za mphamvu, kugonjetsa ,kapena kupambana.—De 33:17; Mik 4:13; Lu 1:69.
-
Nyanja ya moto.
Malo ophiphilitsila kumene ‘kumayaka moto ndi sulufule.’ Amachulidwanso kuti “imfa yaciwili.” Anthu ocimwa amene salapa, Mdyelekezi, imfa, komanso Manda (kapena kuti Hade) zidzaponyedwa mʼnyanjayi. Popeza kuti Mdyelekezi yemwe ndi mzimu, komanso imfa, ndi Manda zomwe sizipsya, zidzaponyedwa kumeneku, ndiye kuti nyanjayi ndi yophiphilitsa. Siikuimila kuzunza anthu kwamuyaya koma kuzionongelatu moti sizidzakhalakonso.—Civ 19:20; 20:14, 15; 21:8.
-
Nyenyezi yam’mawa.—
Onani NTHANDA.
-
Nyumba yopatulika.
Malo apadela amene anthu amalambililako, malo oyela. Koma nthawi zambili mauwa amakamba za cihema kapena kacisi wa ku Yerusalemu. Mauwa amakambanso za malo amene Mulungu amakhala kumwamba.—Eks 25:8, 9; 2Mf 10:25; 1Mb 28:10; Civ 11:19.
O
-
Otsatila a Herode.
Amadziwikanso kuti “a cipani ca Herode.” Anali a cipani amene anali kugwilizana ndi zolinga zandale za Aherode onse amene anali kulamulila pansi pa ufumu wa Aroma. Nʼkutheka kuti Asaduki ena anali mʼcipani cimeneci. Anthu a cipani ca Herodewa anagwilizana ndi Afarisi potsutsa Yesu.—Mko 3:6.
P
-
Paradaiso.
Paki yokongola kapena munda wokongola. Malo oyamba otelewa anali Edeni ndipo Yehova ndiye anakonza malo amenewo kuti anthu awili oyambilila azikhalamo. Yesu anaonetsa kuti dzikoli lidzakhala paradaiso pamene anali kulankhula ndi mmodzi mwa zigawenga zimene zinapacikidwa naye pafupi. Pa 2 Akorinto 12:4, mauwa amanena za paradaiso wamtsogolo, ndipo pa Cibvumbulutso 2:7 amakamba za paradaiso wakumwamba.—Nym 4:13; Lu 23:43.
-
Pasika.
Cikondwelelo ca pacaka cimene cinali kucitika pa 14 mʼmwezi wa Abibu (kenako unachedwa Nisani) pokumbukila kumasulidwa kwa Aisiraeli kucoka ku Iguputo. Pa mwambowu anali kupha mwana wa nkhosa (kapena wa mbuzi) nʼkumuocha ndipo anali kumudya pamodzi ndi masamba owawa komanso mikate yopanda zofufumitsa.—Eks 12:27; Yoh 6:4; 1Ak 5:7.
-
Pentekosite.
Cikondwelelo caciwili pa zikondwelelo zitatu zikulu-zikulu zimene amuna a Ciyuda anali kufunika kupita kukacita ku Yerusalemu. Mau akuti Pentekosite omwe amatanthauza “(tsiku) la 50,” amasewenzetsedwa mʼMalemba a Cigiriki ponena za Cikondwelelo ca Zokolola kapena Cikondwelelo ca Masabata cochulidwa mʼMalemba a Ciheberi. Cinali kucitika pa tsiku la 50 kucokela pa Nisani 16.—Eks 23:16; 34:22; Mac 2:1.
-
Phompho.
Liu la Cigiriki lakuti aʹbys·sos, limatanthauza “kuzama kwambili” kapena “kuzama kosayelekezeka, kopanda malile.” Mauwa amasewenzetsedwa m’Malemba a Cigiriki a Cikhristu pokamba za malo kapena umoyo wofanana ndi wa kundende. Mauwa angagwilitsidwe nchito ponena za manda kapena zinthu zina.—Lu 8:31; Aro 10:7; Civ 20:3.
-
Por·neiʹa.—
Onani CIWELEWELE.
S
-
Sabata.
Mauwa amacokela ku mau a Ciheberi amene amatanthauza “kupuma” kapena “kusiya.” Linali tsiku la 7 la mlungu wa Ayuda (linali kuyamba pa Cisanu dzuwa likalowa nʼkukatha pa Ciwelu dzuwa likalowanso). Caka ca 7, caka ca 50, ndiponso masiku ena a zikondwelelo anali kukhalanso a sabata. Pa Sabata, anthu sanali kuyenela kugwila nchito kupatula imene ansembe anali kugwila kumalo opatulika. Mʼcaka ca Sabata, anthu sanali kuyenela kulima minda yao komanso sanali kuyenela kukakamiza Aheberi anzawo kuti abweze nkhongole. MʼCilamulo ca Mose, malamulo okhudza Sabata anali abwino-bwino koma kenako atsogoleli acipembedzo anaonjezelapo mfundo zina moti pofika nthawi ya Yesu kusunga Sabata kunali kobvuta kwambili.—Eks 20:8; Le 25:4; Lu 13:14-16; Akl 2:16.
-
Salimo.
Nyimbo yotamanda Mulungu. Masalimo ambili anakonzedwa ngati nyimbo zoti anthu olambila Mulungu aziimba, ndipo nthawi zina anali kuimba pagulu la anthu polambila Yehova Mulungu kukacisi wa ku Yerusalemu.—Lu 20:42; Mac 13:33; Yak 5:13.
-
Sanihedirini.
Khoti Yaikulu ya Ayuda yomwe inali ku Yerusalemu. M’nthawi ya Yesu, oweluza a mʼkhotiyi anali kukhala mkulu wa ansembe, anthu ena amene anakhalapo akulu a ansembe, anthu a kubanja la mkulu wa ansembe, akulu, mitu ya mafuko, mitu ya mabanja, komanso alembi. Onse pamodzi anali kukwana 71.—Mko 15:1; Mac 5:34; 23:1, 6.
-
Satana.
-
Siriya; Asiriya.
M’Malemba a Cigiriki a Cikhristu, Siriya linali cigao cimene cinali kulamulilidwa ndi Aroma ndipo likulu lake linali mzinda wa Antiokeya. Cigaoci cinali kuphatikizapo ambili mwa malo amene amachedwa Siriya (omwe amachedwanso Aramu) m’Malemba a Ciheberi. Bwanamkubwa wa Siriya anali kuyang’anila dela lonse la Palesitina.—Lu 2:2; Mac 18:18; Aga 1:21.
-
Sunagoge.
Mauwa amatanthauza “kubweletsa pamodzi” kapena “msonkhano.” Koma mʼmalemba ambili mauwa amakamba za nyumba kapena malo amene Ayuda anali kusonkhana kuti awelenge Malemba, alandile malangizo, alalikile, komanso apemphele. Pa nthawi ya Yesu, tauni iliyonse yaikulu bwino ku Isiraeli inali kukhala ndi sunagoge ndipo mizinda ikulu-ikulu inali kukhala ndi masunagoge oposa mmodzi.—Lu 4:16; Mac 13:14, 15.
-
Suriti.
Magombe awili akulu-akulu osazama akumpoto kwa Africa mʼdziko la Libya. Anthu oyenda panyanja anali kuopako cifukwa cakuti mcenga unali kusuntha-suntha cifukwa ca mphepo.—Mac 27:17.
T
-
Talente.
Muyezo waukulu kwambili wa kulemela kwa zinthu komanso ndalama yaikulu kwambili ya Aheberi. Ndalama zokwana talente imodzi zinali kukhala zolemela makilogalamu 34.2. Talente ya Cigiriki inali yocepelapo ndipo inali kulemela makilogalamu 20.4.—1Mb 22:14; Mt 18:24.
-
Tatalasi.
MʼMalemba a Cigiriki a Cikhristu, mauwa amanena za umoyo wokhala ngati wakundende ndipo angelo a mʼmasiku a Nowa anapatsidwa cilango cokhala umoyo umenewo. Pa 2 Petulo 2:4, mau amene anasewenzetsa akuti tar·ta·roʹo (“kuponya ku Tatalasi”) satanthauza kuti angelo amene anacimwa anaponyedwa ku Tatalasi wochulidwa m’nthano zambili zacikunja (yomwe ndi ndende yapansi pa nthaka komanso malo amdima kumene milungu ingʼono-ingʼono imakhala). Koma amatanthauza kuti Mulungu anawacotsa kumwamba, kuwalanda maudindo ao, ndiponso kuti anawacititsa kuti azikhala umoyo ngati kuti ali mumdima wandiweyani moti sangadziwe zolinga zilizonse za Mulungu. Mdimawu umaonetsanso kuti tsogolo lao si lowala cifukwa Malemba amanena kuti angelo amenewa adzaonongedwa pamodzi ndi mtsogoleli wao Satana Mdyelekezi ndipo sadzakhalaponso. Conco mau akuti Tatalasi amanena za umoyo wotsika kwambili umene angelo opandukawa akukhala. Mauwa ndi osiyana ndi “phompho” lochulidwa pa Cibvumbulutso 20:1-3.
-
Tembelelo.
Kuopsyeza kapena kunena kuti zoipa zinazake zidzacitikila munthu kapena cinthu. Koma sizitanthauza zimene munthu amanena potukwana kapena akapsya mtima kwambili. Tembelelo ndi kulengeza kapena kunenelatu zoipa zimene zidzacitikila munthu ndipo ngati yemwe watembelelayo ndi Mulungu kapena munthu waudindo, mau ake amakhala ngati ulosi ndipo zimacitikadi.—Ge 12:3; Nu 22:12; Mko 11:21; Mac 23:12; Aro 12:14; Aga 3:10.
-
Tsiku la Ciweluzo.
Tsiku kapena nthawi imene magulu a anthu, mitundu, kapena anthu onse adzaweluzidwa ndi Mulungu. Ingakhale nthawi pamene anthu oweluzidwa kuti ayenela kuphedwa, adzaonongedwa, kapena pamene anthu ena adzapatsidwa mwai wopulumuka kuti akhale ndi moyo wosatha. Yesu Khristu ndi atumwi ake anakamba za “Tsiku la Ciweluzo” la kutsogolo, limene ndi nthawi pamene anthu amoyo komanso amene anafa adzaweluzidwa.—Mt 12:36.
-
Tsiku la Mwambo Wophimba Macimo.
Tsiku lofunika kwambili kwa Aisiraeli ndipo linali kuchedwanso kuti Yom Kippur (kucokela ku mau a Ciheberi akuti yohm hak·kip·pu·rimʹ, kutanthauza “tsiku lophimba”). Tsikuli linali pa 10 mu mwezi wa Etanimu. Ndi pa tsiku lokhali pacaka pomwe mkulu wa ansembe anali kulowa mʼMalo Opatulika Koposa a cihema ndipo kenako a kacisi. Akalowa, anali kupeleka magazi a nyama kuti ikhale nsembe ya macimo ake, macimo a Alevi ena, komanso a anthu ena onse. Nsembezo zinali kuimila nsembe ya Yesu imene anapeleka kamodzi kokha ndipo inaphimbilatu macimo a mtundu wa anthu. Nsembeyo imathandiza anthu kuyanjananso ndi Yehova. Tsikuli linali kukhala la msonkhano wopatulika, losala kudya, komanso la sabata lomwe anthu sanali kugwila nchito zao za tsiku ndi tsiku.—Le 23:27, 28; Mac 27:9; Akl 1:20; Ahe 9:12.
-
Tsiku lokhala mwezi watsopano.
Tsiku loyamba la mwezi ulionse pa kalenda ya Ayuda. Linali kukhalanso tsiku la msonkhano, la cikondwelelo, komanso lopeleka nsembe zapadela. Patapita nthawi, tsikuli linali tsiku la cikondwelelo ca dziko lonse ndipo anthu sanali kugwila nchito.—Nu 10:10; 2Mb 8:13; Akl 2:16.
-
Tsiku Lokonzekela.
Tsiku loti mawa lake ndi Sabata ndipo pa tsikuli Ayuda anali kucita zinthu zokonzekela Sabata. Tsikuli linali kutha pa Cisanu dzuwa likalowa ndipo pa nthawi imeneyo mʼpamenenso Sabata linali kuyamba. Tsiku la Ayuda linali kuyamba madzulo nʼkudzathanso m’madzulo a tsiku lotsatila.—Mko 15:42; Lu 23:54.
U
-
Ubatizo; Kubatiza.
-
Ufumu wa Mulungu.
-
Ulosi.
Uthenga wouzilidwa, woulula kapena kulengeza zimene Mulungu akufuna kucita. Ulosi unali kutha kuphunzitsa mfundo za makhalidwe abwino, kulamula anthu kuti acite zinazake, kulengeza ciweluzo ca Mulungu, kapena zinazake zimene zidzacitika.—Mt 13:14; 2Pe 1:20, 21.
-
Uthenga wabwino.
W
-
Wamatsenga.
Munthu amene amasewenzetsa mphamvu zocokela kwa mizimu yoipa.—Mac 13:6.
-
Wansembe.
Munthu amene anali kuimila Mulungu kwa anthu amene anali kuwatumikila, ndipo anali kulangiza anthuwo zokhudza Mulungu komanso malamulo ake. Ansembe anali kuimilanso anthu kwa Mulungu popeleka nsembe komanso popemphela mocondelela mʼmalo mwa anthuwo. Cilamulo ca Mose cisanapelekedwe, mutu wabanja ndiye anali kukhala wansembe wabanjalo. MʼCilamulo ca Mose amuna a mʼbanja la Aroni, omwe anali a pfuko la Levi, ndiwo anali kukhala ansembe. Amuna ena onse a pfuko la Levi anali kuwathandiza. Cipangano catsopano citakhazikitsidwa, Isiraeli wauzimu ndiye anakhala mtundu wa ansembe ndipo Yesu ndiye Mkulu wa Ansembe.—Eks 28:41; Ahe 9:24; Civ 5:10.
-
Wansembe wamkulu.
Mau ena otanthauza “mkulu wa ansembe” m’Malemba a Ciheberi. Zioneka kuti m’Malemba a Cigiriki a Cikhristu, mau akuti “ansembe aakulu” anali kutanthauza amuna audindo waukulu m’gulu la ansembe, mwina kuphatikizapo amene kale anali akulu a ansembe komanso atsogoleli a zigao 24 za ansembe.—2Mb 26:20; Eza 7:5; Mt 2:4; Mko 8:31.
-
Wofulidwa.
Amuna otelewa anali atumiki a mʼnyumba yacifumu kapena oyangʼanila mfumukazi ndi akazi aangʼono a mfumu. Panalinso anthu ena amene anali kupatsidwa udindo mʼnyumba yacifumu omwe sanali kukhala ofulidwa. Mau oti kufulidwa amagwilitsidwanso nchito mophiphilitsila ponena za anthu amene “sakwatila cifukwa ca Ufumu wakumwamba.” Iwo amadziletsa nʼcolinga cakuti azicita zambili potumikila Mulungu.—Mt 19:12; Est 2:15; Mac 8:27.
-
Woipayo.
-
Wokana Khristu.
Mau a Cigiriki amenewa ali ndi matanthauzo awili. Amatanthauza wotsutsana ndi Khristu kapena wonamizila kuti ndi Khristu. Anthu, mabungwe, kapena magulu amene amanamizila kuti amaimila Khristu kapena munthu amene amanamizila kukhala Mesiya kapena kutsutsa Khristu ndi ophunzila ake, anganenedwe kuti ndi okana Khristu.—1Yo 2:22.
-
Wokhulupilila nyenyezi.
Munthu amene amayang’ana kayendedwe ka dzuwa, mwezi, ndi nyenyezi pofuna kukambilatu zimene zidzacitika kutsogolo.—Da 2:27; Mt 2:1.
-
Wolosela za mtsogolo.
Munthu amene amanena kuti amatha kukambilatu za mtsogolo. Ansembe amatsenga, olankhula ndi mizimu, komanso okhulupilila nyenyezi, ndi ena mwa anthu amene ali mʼgulu la anthu amene Baibo imati ndi olosela za mtsogolo.—Le 19:31; De 18:11; Mac 16:16.
-
Wolowa Ciyuda.
-
Woumba mbiya.
Munthu amene anali kuumba zinthu zadothi monga miphika, mbale, ndi zina. Mau ake a Ciheberi amatanthauza “wopanga.” Ulamulilo umene woumba amakhala nao akamagwila nchitoyi, amauyelekezela ndi ulamulilo umene Yehova ali nao pa anthu komanso maiko.—Yes 64:8; Aro 9:21.
-
Woyang’anila.
Mwamuna amene udindo wake waukulu ndi kuyangʼanila komanso kuweta mpingo. Mau ake a Cigiriki akuti e·piʹsko·pos amanena za kuyangʼanila pofuna kuteteza. Ndipo mau akuti “woyangʼanila” komanso “mkulu” (pre·sbyʹte·ros), amanena za udindo wofanana, womwe munthu amakhala nao mumpingo wa Cikhristu. Mau akuti “mkulu” amaonetsa kuti munthu amene wapatsidwa udindowu amacita zinthu mwaucikulile ndipo mau akuti “woyangʼanila” amatsindika za nchito imene amagwila.—Mac 20:28; 1Ti 3:2-7; 1Pe 5:2.
Y
-
Yakobo.
Mwana wa Isaki ndi Rabeka. Kenako Mulungu anamupatsa dzina lakuti Isiraeli ndipo anali kholo la mtundu wa Isiraeli (womwe unali kuchedwanso Aisiraeli, kenako Ayuda). Iye anali bambo wa ana aamuna 12, omwe pamodzi ndi mbadwa zao, anapanga mafuko 12 a Isiraeli. Dzina lakuti Yakobo linapitiliza kugwilitsidwa nchito ponena za mtundu wa Isiraeli kapena kuti Aisiraeli.—Ge 32:28; Mt 22:32.
-
Yehova.
Mu Baibo ya Dziko Latsopano ya Malemba Opatulika muli dzina lakuti “Yehova” maulendo 237 mu Malemba a Cigiriki a Cikhristu. Maumboni otsatilawa apeleka zifukwa zimene anaikilamo dzina la Mulungu:
-
1. Mʼmipukutu ya Malemba a Ciheberi yomwe anali kusewenzetsa m’nthawi ya Yesu ndi atumwi, munali kupezeka dzina la Mulungu limene linali kulembedwa ndi zilembo zinai za Ciheberi (יהוה).
-
2. M’nthawi ya Yesu ndi atumwi ake, dzina la Mulungu limene limalembedwa ndi zilembo zinai za Ciheberi, linali kupezekanso mʼmipukutu ya Cigiriki yomasulila Malemba a Ciheberi.
-
3. Malemba a Cigiriki omwewo amafotokoza momveka bwino kuti nthawi zambili Yesu anali kuchula dzina la Mulungu ndiponso anali kudziwitsa anthu ena za dzinali.—Yohane 17:6, 11, 12, 26.
-
4. Popeza kuti Malemba a Cigiriki ndi ouzilidwa ngati mmene zilili ndi Malemba a Ciheberi, dzina la Mulungu lakuti Yehova lifunika lizipezekanso mʼMalemba a Cigirikiwo.
-
5. M’Cigiriki mulinso cidule ca dzina la Mulungu.—Cibvumbulutso 19:1, 3, 4, 6.
-
6. Zolemba zoyambilila za Ayuda zimaonetsa kuti Akhristu a Ciyuda anali kusewenzetsa dzina la Mulungu.
-
7. Akatswili ena a Baibo amabvomeleza kuti nʼzomveka kunena kuti dzina la Mulungu linali kupezeka mʼMalemba a Cigiriki omwe anagwila mau Malemba a Ciheberi.
-
8. Ma Baibo a zinenelo zosiyana-siyana zoposa 100 mumapezeka dzina la Mulungu mʼMalemba a Cigiriki.
Conco nʼzoonekelatu kuti pali zifukwa zomveka zobwezeletsela dzina la Mulungu lakuti Yehova mʼMalemba a Cigiriki. Izi nʼzimene omasulila Baibo ya Dziko Latsopano anacita. Omasulilawo amalemekeza kwambili dzina la Mulungu ndipo sanafune kucotsa kalikonse pa mau omwe anali mʼmipukutu yoyambilila.—Cibvumbulutso 22:18, 19.
-
-
Yuda.
Mwana wacinai wa Yakobo ndipo mai ake anali Leya. Yakobo atatsala pangʼono kumwalila, analosela kuti mfumu yamphamvu komanso imene idzalamulile kwa nthawi yaitali idzacokela mʼbanja la Yuda. Yesu anabadwa kucokela mʼbanja la Yuda. Dzina lakuti Yuda linalinso la pfuko ndipo kenako la ufumu.—Ge 29:35; 49:10; Ahe 7:14.
Z
-
Zeu.
Mulungu wamkulu pa milungu yambili imene Agiriki anali kulambila. Ku Lusitara, anthu anali kulakwitsa nʼkumanena kuti Baranaba ndi Zeu. Zolemba zina zomwe zinapezeka pafupi ndi ku Lusitara zinali ndi mau akuti “ansembe a Zeu” komanso “Zeu, mulungu wa dzuwa.” Ngalawa imene Paulo anakwela pocoka pa cilumba ca Melita inali ndi cizindikilo ca “Ana a Zeu” omwe anali ana amapasa ndipo maina ao anali Kasita ndi Polakisi.—Mac 14:12; 28:11.
-
Zipatso zoyambilila.
Mbeu kapena zipatso zoyambilila kukolola komanso cinthu ciliconse coyambilila. Yehova anali kufuna kuti Aisiraeli azimupatsa zinthu zoyambilila, kaya ndi mwana woyamba kubadwa wa munthu, wa nyama, kapenanso mbeu ndi zipatso zoyambilila. Mtundu wa Aisiraeli unali kupeleka zinthu zoyambilila pa Cikondwelelo ca Mikate Yopanda Zofufumitsa komanso pa Pentekosite. Mau akuti “zipatso zoyambilila” amagwilitsidwanso nchito mophiphilitsa pokamba za Khristu ndi otsatila ake odzozedwa.—1Ak 15:23; Nu 15:21; Miy 3:9; Civ 14:4.
-
Ziwanda.
Mizimu yoipa yosaoneka yomwe ndi yamphamvu kuposa anthu. Ziwanda zimenezi zimachulidwa kuti “ana a Mulungu woona” pa Genesis 6:2 komanso “angelo” pa Yuda 6. Angelowa sanalengedwe oipa, koma anadzipangitsa kukhala adani a Mulungu poonetsa kusamumvela mʼmasiku a Nowa komanso pogwilizana ndi Satana amene anapandukila Yehova.—De 32:17; Lu 8:30; Mac 16:16; Yak 2:19.
-
Ziwaya.
Ziwiya zagolide, zasiliva, kapena zakopa zimene anali kusewenzetsa pa cihema ndiponso mʼkacisi. Anali kuzigwilitsa nchito powocha nsembe, pocotsa makala paguwa lansembe, komanso pocotsa phulusa pa coikapo nyale cagolide. Zinali kudziwikanso kuti zopelekela nsembe.—Eks 37:23; 2Mb 26:19; Ahe 9:4.
-
Ziyoni; Phili la Ziyoni.
Dzina la mzinda wa Yebusi umene unali ndi mpanda wolimba ndipo unali kumpoto cakumadzulo kwa Yerusalemu. Davide atagonjetsa mzindawu, anamanga nyumba yake yacifumu pa malowa ndipo mzindawu unayamba kuchedwa “Mzinda wa Davide.” (2Sa 5:7, 9) Yehova anali kuona kuti Phili la Ziyoni ndi lopatulika maka-maka pamene Davide anabweletsa Likasa kumeneku. Kenako mau akuti Ziyoni anali kunena za malo amene kunali kacisi pa Phili la Moriya ndipo nthawi zina anali kunenanso za mzinda wonse wa Yerusalemu. Mauwa amagwilitsidwa nchito mophiphilitsa mʼMalemba a Cigiriki a Cikhristu.—Sl 2:6; 1Pe 2:6; Civ 14:1.
-
Zofufumitsa.
Zinthu zimene anali kuika mʼzinthu zamadzi-madzi kapena pokanda ufa kuti aufufumitse. Nthawi zambili anali kusewenzetsa ufa wokanda-kanda umene unafufuma kale. Kawili-kawili, Baibo imagwilitsa nchito mauwa mophiphilitsa ponena za ucimo kapena kuonongeka. Mauwa amagwilitsidwanso nchito poonetsa kukula kapena kuonjezeka kosaonekela.—Eks 12:20; Mt 13:33; Aga 5:9.
-
Zofukiza.
Zinthu zonunkhila zopangidwa kucokela kumitengo inayake zomwe zinali kupsya pangʼono-pangʼono nʼkumatulutsa kapfungo kabwino. Zonunkhila zina zapadela zinali kupangidwa posakaniza zinthu zinai ndipo zinali kugwilitsidwa nchito pacihema ndi pakacisi. Zinali kuochedwa mʼmawa ndi usiku paguwa la nsembe zofukiza la mʼMalo Opatulika. Pa tsiku la Mwambo Wophimba Macimo, zinali kuochedwa mʼMalo Opatulika Koposa. Mau akuti zofukiza anali kagwilitsidwanso nchito mophiphilitsa ponena za mapemphelo obvomelezeka a atumiki a Mulungu okhulupilika. Akhristu sanalamulidwe kuti azipeleka nsembe zofukiza.—Eks 30:34, 35; Le 16:13; Civ 5:8.
-
Zozizwitsa; Nchito zamphamvu.

