Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Mateyo 2:1-23

  • Okhulupilila nyenyezi apita kukaona Yesu (1-12)

  • Athawila ku Iguputo (13-15)

  • Herode akupha ana aamuna (16-18)

  • Abwelela ku Nazareti (19-23)

2  Yesu atabadwa ku Betelehemu wa ku Yudeya m’masiku a Herode* mfumu, okhulupilila nyenyezi ocokela Kum’mawa anabwela ku Yerusalemu. 2  Iwo anati: “Kodi mfumu ya Ayuda imene yabadwa ili kuti? Cifukwa tinaona nyenyezi yake pamene tinali Kum’mawa, ndipo tabwela kuti tiiwelamile.” 3  Mfumu Herode itamva zimenezi inavutika maganizo pamodzi ndi onse okhala mu Yerusalemu. 4  Kenako Herode anasonkhanitsa ansembe aakulu onse ndi alembi a anthu, n’kuwafunsa za kumene Khristu* adzabadwila. 5  Iwo anamuyankha kuti: “Ku Betelehemu wa Yudeya, pakuti izi n’zimene zinalembedwa kudzela mwa mneneli kuti: 6  ‘Ndipo iwe Betelehemu wa m’dziko la Yuda, sindiwe mzinda waung’ono kwambili pakati pa olamulila a Yuda, cifukwa mwa iwe mudzatuluka wolamulila amene adzaweta anthu anga Aisiraeli.’” 7  Ndiyeno Herode anaitanitsa okhulupilila nyenyezi aja mwamseli n’kuwafunsa mosamala kuti adziwe nthawi yeniyeni imene nyenyeziyo inaonekela. 8  Powatumiza ku Betelehemu, iye anawauza kuti: “Pitani mukamufune-fune mosamala mwanayo, ndipo mukakamupeza mudzabwelenso kudzandiuza, kuti inenso ndikapite kukamuwelamila.” 9  Atamva zimene mfumuyo inakamba, ananyamuka n’kumapita. Atanyamuka, nyenyezi ija imene anaiona ali Kum’mawa inaonekelanso. Ndipo inayamba kuyenda kutsogolo kwao mpaka inakaima pamwamba pa nyumba imene munali mwanayo. 10  Ataona kuti nyenyeziyo yaima anakondwela kwambili. 11  Pamene analowa m’nyumbamo, anamuona mwanayo ali ndi mai ake Mariya, ndipo anagwada pansi ndi kumuwelamila. Anamasulanso cuma cao n’kumupatsa mphatso mwanayo. Anamupatsa golide, lubani, ndi mule. 12  Koma popeza Mulungu anawacenjeza kudzela m’maloto kuti asabwelele kwa Herode, iwo anadzela njila ina pobwelela ku dziko lao. 13  Iwo atacoka, mngelo wa Yehova* anaonekela kwa Yosefe m’maloto n’kumuuza kuti: “Nyamuka, tenga mwanayu pamodzi ndi mai ake uthawile ku Iguputo. Ukakhale kumeneko mpaka n’dzakuuze zocita, cifukwa Herode posacedwa adzayamba kufuna-funa mwanayu kuti amuphe.” 14  Conco Yosefe anauka usiku womwewo n’kutenga mwanayo ndi mai ake n’kupita ku Iguputo. 15  Anakhalabe kumeneko mpaka pamene Herode anamwalila. Izi zinakwanilitsa mau amene Yehova* anakamba mwa mneneli wake kuti: “N’naitana mwana wanga kuti atuluke mu Iguputo.” 16  Herode atazindikila kuti okhulupilila nyenyezi aja amupusitsa, anakwiya koopsya. Conco anatumiza anthu kuti akaphe ana onse aamuna ku Betelehemu ndi m’madela onse ozungulila, kuyambila a zaka ziwili kubwela pansi mogwilizana ndi nthawi imene okhulupilila nyenyezi aja anamuuza. 17  Izi zinakwanilitsa mau amene ananenedwa kudzela mwa mneneli Yeremiya akuti: 18  “Mau olila mokweza anamveka ku Rama. Anali Rakele kulila ana ake, ndipo sanafune kutonthozedwa cifukwa anawo kunalibenso.” 19  Herode atamwalila, mngelo wa Yehova* anaonekela kwa Yosefe ku Iguputo 20  ndipo anati: “Nyamuka, tenga mwanayu ndi mai ake, ubwelele ku dziko la Isiraeli, cifukwa amene anali kufuna-funa moyo wa mwanayu anafa.” 21  Conco ananyamuka ndi kutenga mwanayo ndi mai ake, n’kupita ku dziko la Isiraeli. 22  Koma atamva kuti Arikelao ndiye akulamulila ku Yudeya, m’malo mwa Herode tate wake, anaopa kupita kumeneko. Kuonjezela apo, Mulungu atamucenjeza kudzela m’maloto, anacoka n’kupita ku dela la Galileya. 23  Ndipo anapita kukakhala mu mzinda wa Nazareti. Izi zinakwanilitsa mau amene ananenedwa kudzela mwa aneneli, akuti: “Iye adzachedwa Mnazareti.”*

Mau a m'Munsi

Kapena kuti, “Mesiya; Wodzozedwa.”
Cioneka kuti dzinali linacokela ku liu la Ciheberi lotanthauza kuti “mphukila.”