BAIBO YA DZIKO LATSOPANO

Kodi Mungathane Nazo Motani Nkhawa?

Cinyanja
Kodi Mungathane Nazo Motani Nkhawa?
https://cms-imgp.jw-cdn.org/img/p/1001061100/univ/wpub/1001061100_univ_sqr_xl.jpg
nwt masa. 28-29

FUNSO 16

Kodi Mungathane Nazo Motani Nkhawa?

“Umutulile Yehova nkhawa zako, ndipo iye adzakuthandiza. Iye sadzalola kuti munthu wolungama agwe.”

Salimo 55:22

“Mapulani a munthu wakhama amamuthandiza kuti zinthu zimuyendele bwino, koma onse amene amacita zinthu mopupuluma amasauka.”

Miyambo 21:5

“Usacite mantha, cifukwa ndili ndi iwe. Usade nkhawa cifukwa ine ndine Mulungu wako. Ndikulimbitsa, ndithu ndikuthandiza, ndikugwila mwamphamvu ndi dzanja langa lamanja lacilungamo.”

Yesaya 41:10

“Ndani wa inu angatalikitse moyo wake ngakhale pang’ono pokha mwa kuda nkhawa?”

Mateyo 6:27

“Conco musamade nkhawa ndi za mawa, cifukwa mawa lidzakhala ndi nkhawa zake. Zobvuta za tsiku lililonse n’zokwanila pa tsikulo.”

Mateyo 6:34

“Muzitsimikizila ndi kusankha zinthu zomwe ndi zofunika kwambili.”

Afilipi 1:10

“Musamade nkhawa ndi cinthu ciliconse. Koma pa ciliconse, mwa pemphelo ndi pembedzelo, pamodzi ndi ciyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Mukatelo, mtendele wa Mulungu umene umapambana kumvetsa zinthu kwa mtundu ulionse, udzateteza mitima yanu komanso maganizo anu mwa Khristu Yesu.”

Afilipi 4:6, 7