Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Mateyo 5:1-48

  • ULALIKI WA PA PHILI (1-48)

    • Yesu ayamba kuphunzitsa pa phili (1, 2)

    • Zinthu 9 zopangitsa anthu kukhala acimwemwe (3-12)

    • Mcele ndi nyale (13-16)

    • Yesu anabwela kudzakwanilitsa Cilamulo (17-20)

    • Uphungu pa nkhani ya mkwiyo (21-26), cigololo (27-30), kusudzulana (31, 32), malumbilo (33-37), kubwezela (38-42), kukonda adani athu (43-48)

5  Ataona khamu la anthulo, anakwela m’phili. Ndipo atakhala pansi, ophunzila ake anabwela kwa iye. 2  Kenako anayamba kuwaphunzitsa kuti: 3  “Acimwemwe ndi anthu ozindikila zosowa zao zauzimu, cifukwa Ufumu wa kumwamba ndi wao. 4  “Acimwemwe ndi anthu amene akumva cisoni, cifukwa adzatonthozedwa. 5  “Acimwemwe ndi anthu ofatsa, cifukwa adzalandila dziko lapansi. 6  “Acimwemwe ndi anthu amene ali ndi njala komanso ludzu lofuna cilungamo, cifukwa adzakhuta. 7  “Acimwemwe ndi anthu acifundo, cifukwa adzacitilidwa cifundo. 8  “Acimwemwe ndi anthu oyela mtima, cifukwa adzaona Mulungu. 9  “Acimwemwe ndi anthu obweletsa mtendele, cifukwa adzachedwa ana a Mulungu. 10  “Acimwemwe ndi anthu amene azunzidwa cifukwa ca cilungamo, pakuti Ufumu wa kumwamba ndi wao. 11  “Ndinu acimwemwe anthu akamakunyozani, kukuzunzani, ndi kukunamizilani zoipa za mtundu ulionse cifukwa ca ine. 12  Kondwelani ndi kusangalala kwambili, cifukwa mphoto yanu ndi yaikulu kumwamba. Pakuti umu ndi mmene anazunzila aneneli amene analipo inu musanakhaleko. 13  “Inu ndinu mcele wa dziko lapansi, koma ngati mcele watha mphamvu yake, kodi mphamvu yake ingabwezeletsedwe motani? Umakhala wopanda nchito iliyonse, ndipo umangotaidwa kunja kumene anthu amauponda-ponda. 14  “Inu ndinu kuwala kwa dziko. Mzinda wokhala pa phili sungabisike. 15  Anthu akayatsa nyale, saibwinikila ndi thadza,* koma amaiika pa coikapo nyale, ndipo imaunikila onse m’nyumbamo. 16  Mofananamo, onetsani kuwala kwanu pamaso pa anthu, kuti aone nchito zanu zabwino ndi kulemekeza Atate wanu wa kumwamba. 17  “Musaganize kuti n’nabwela kudzaononga Cilamulo kapena zolemba za aneneli. Sin’nabwele kudzaziononga ai, koma kudzazikwanilitsa. 18  Ndithudi ndikukuuzani kuti ngakhale kumwamba ndi dziko lapansi zitacoka, kacilembo kocepetsetsa kapena kambali kakang’ono ka cilembo ca m’Cilamulo sikadzacoka mpaka zonse zitakwanilitsidwa. 19  Cotelo aliyense wophwanya limodzi mwa malamulo aang’ono kwambili amenewa, ndi kuphunzitsa ena kucita zimenezo, adzakhala wosayenela kulowa mu Ufumu wa kumwamba. Koma aliyense wowatsatila ndi kuphunzitsa ena malamulowa, adzakhala woyenela kulowa mu Ufumu wa kumwamba. 20  Pakuti ndikukuuzani kuti ngati cilungamo canu siciposa ca alembi ndi Afarisi, ndithu simudzalowa mu Ufumu wa kumwamba. 21  “Munamva kuti anthu akale anauzidwa kuti: ‘Usaphe munthu, aliyense wapha munthu wapalamula mlandu wa kukhoti.’ 22  Komabe ine ndikukuuzani kuti aliyense wopitiliza kukwiila m’bale wake, wapalamula mlandu wa ku khoti. Ndipo aliyense wonena m’bale wake ndi mau acipongwe, wapalamula mlandu wa ku Khoti Yaikulu. Koma aliyense wonena mnzake kuti, ‘Ndiwe citsilu!’ adzapita ku Gehena* wa moto. 23  “Conco ngati wabweletsa mphatso yako ku guwa la nsembe, ndipo uli komweko wakumbukila kuti m’bale wako ali nawe cifukwa, 24  siya mphatso yako patsogolo pa guwa la nsembe pomwepo, ndipo pita ukayanjane naye m’bale wakoyo coyamba. Ndiyeno ubwelenso udzapeleke mphatso yako. 25  “Usacedwe kuthetsa nkhani ndi munthu wokuimba mlandu pamene uli naye pa ulendo wopita ku khoti, kuti mwina iye asakakupeleke kwa woweluza, komanso kuti woweluzayo asakakupeleke kwa msilikali wa pakhoti kuti akuponye m’ndende. 26  Ndithu ndikukuuza kuti sudzatulukamo mpaka utalipila kakhobili kothela.* 27  “Munamva kuti anati: ‘Usacite cigololo.’ 28  Koma ine ndikukuuzani kuti aliyense woyang’anitsitsa mkazi mpaka kufika pomulakalaka, wacita naye kale cigololo mu mtima mwake. 29  Tsopano ngati diso lako lakumanja likukucimwitsa, ulikolowole ndi kulitaya. Pakuti ndi bwino kuti ukhale wopanda ciwalo cimodzi kusiyana n’kuti thupi lako lonse likaponyedwe ku Gehena.* 30  Komanso ngati dzanja lako lakumanja likukucimwitsa, ulidule ndi kulitaya. Pakuti ndi bwino kuti ukhale wopanda ciwalo cimodzi kusiyana n’kuti thupi lako lonse likaponyedwe ku Gehena.* 31  “Komanso paja anati: ‘Aliyense wosudzula mkazi wake ayenela kumupatsa cikalata ca cisudzulo.’ 32  Koma ine ndikukuuzani kuti, aliyense wosudzula mkazi wake pa cifukwa cosakhala ciwelewele,* amapangitsa mkaziyo kukhala pa mayeselo ocita cigololo, ndipo aliyense wokwatila mkazi wotelo akucita cigololo. 33  “Munamvanso kuti anthu akale anauzidwa kuti: ‘Usamalumbile koma osacita zimene walumbilazo. M’malomwake, uzikwanilitsa malumbilo ako kwa Yehova.’* 34  Koma ine ndikukuuzani kuti: Musamalumbile n’komwe, kaya mwa kuchula kumwamba cifukwa n’kumene kuli mpando wacifumu wa Mulungu, 35  kapena mwa kuchula dziko lapansi, cifukwa ndi copondapo mapazi ake, kapenanso mwa kuchula Yerusalemu cifukwa ndi mzinda wa Mfumu yaikulu. 36  Usamalumbile mwa kuchula mutu wako, cifukwa sungakwanitse kusandutsa ngakhale tsitsi limodzi kukhala loyela kapena lakuda. 37  Muzingotsimikiza kuti mukati ‘Inde,’ akhaledi inde, mukati ‘Ai,’ akhaledi ai, cifukwa mau oonjezela pamenepa amacokela kwa woipayo. 38  “Munamva kuti anati: ‘Diso kulipila diso, dzino kulipila dzino.’ 39  Koma ine ndikukuuzani kuti: Usalimbane naye munthu woipa. M’malo mwake, aliyense akakumenya mbama kutsaya lakumanja, mutembenuzilenso linalo. 40  Ndipo ngati munthu afuna kukupeleka ku khoti kuti atenge cobvala cako camkati, mulole kuti atengenso cobvala cako cakunja. 41  Ndipo ngati winawake waudindo wakulamula kuti umunyamulile katundu kwa mtunda wa kilomita imodzi, munyamulile kwa mtunda wa makilomita awili. 42  Munthu akakupempha cinthu mupatse, ndipo amene afuna kubweleka* cinacake kwa iwe usamumane. 43  “Munamva kuti anati: ‘Uzikonda mnzako ndi kudana naye mdani wako.’ 44  Koma ine ndikukuuzani kuti: Pitilizani kukonda adani anu ndi kupemphelela amene amakuzunzani, 45  kuti muonetse kuti ndinudi ana a Atate wanu wa kumwamba, cifukwa iye amawalitsila dzuwa lake pa anthu abwino ndi oipa omwe. Komanso amagwetsela mvula anthu olungama ndi osalungama omwe. 46  Nanga pali phindu lanji ngati mumakonda anthu okhawo amene amakukondani? Kodi si zimene okhometsa misonkho amacita? 47  Ndipo ngati mumapatsa moni abale anu okha, n’ciani capadela cimene mukucita? Kodi si zimenenso anthu a mitundu ina amacita? 48  Conco inu muyenela kukhala angwilo,* mmene Atate wanu wa kumwamba alili wangwilo.

Mau a m'Munsi

^ Kapena kuti, “thadza lopimila.”
^ Malo amene anali kutenthelako zinyalala kunja kwa Yerusalemu. Onani Matanthauzo a Mau Ena.
^ Kucokela ku Cigiriki, “utalipila leputoni yothela.” Onani Zakumapeto B14.
^ M’Cigiriki, por nei’a. Onani Matanthauzo a Mau Ena.
^ Kutanthauza kubweleka popanda ciongoladzanja.
^ Kapena kuti, “kukhala okwanila.”