FUNSO 13
Kodi Baibo Imakambapo Ciani pa Nkhani ya Nchito?
“Kodi wamuona munthu waluso pa nchito yake? Iye adzaima pamaso pa mafumu. Sadzaima pamaso pa anthu wamba.”
Miyambo 22:29
“Munthu wakuba asiye kubako, koma azigwila nchito mwakhama. Azigwila nchito yabwino ndi manja ake kuti azikwanitsa kupeza zinthu zimene angagawane ndi munthu wosowa.”
“Munthu aliyense adye ndi kumwa nʼkumasangalala ndi zinthu zabwino, cifukwa ca nchito yake yonse imene waigwila mwakhama. Imeneyi ndi mphatso yocokela kwa Mulungu.”
Mlaliki 3:13

