Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Mateyo 24:1-51
24 Tsopano pamene Yesu anali kucoka pa kacisi, ophunzila ake anafika kwa iye kuti amuonetse zimango za pa kacisipo.
2 Iye anawauza kuti: “Kodi mukuziona zinthu zonsezi? Ndithu ndikukuuzani kuti, pano sipadzatsala mwala ulionse pamwamba pa unzake umene sudzagwetsedwa.”
3 Iye atakhala pansi m’Phili la Maolivi, ophunzila ake anamufikila mwamseli n’kumufunsa kuti: “Tiuzeni, kodi zinthu zimenezi zidzacitika liti, nanga cizindikilo ca kukhalapo* kwanu komanso ca cimalizilo ca nthawi ino* cidzakhala ciani?”
4 Poyankha Yesu anawauza kuti: “Samalani kuti munthu asakusoceletseni,
5 cifukwa ambili adzabwela m’dzina langa n’kumanena kuti, ‘Khristu uja ndine,’ ndipo adzasoceletsa anthu ambili.
6 Mudzamva phokoso la nkhondo komanso malipoti a nkhondo. Zimenezi zisadzakucititseni mantha. Pakuti ziyenela kucitika koma mapeto adzakhala asanafikebe.
7 “Mtundu udzaukilana ndi mtundu wina, ndipo ufumu udzaukilana ndi ufumu wina, komanso kudzakhala njala ndi zibvomezi m’malo osiyana-siyana.
8 Zinthu zonsezi ndi ciyambi ca masautso.*
9 “Ndiyeno anthu adzakupelekani kuti mukazunzidwe ndipo adzakuphani. Ndiponso mitundu yonse idzakudani cifukwa ca dzina langa.
10 Cina, anthu ambili adzapunthwa ndipo adzapelekana ndi kudana.
11 Kudzabwela aneneli ambili abodza ndipo adzasoceletsa anthu ambili.
12 Ndiponso cifukwa ca kuwonjezeka kwa kusamvela malamulo, cikondi ca anthu ambili cidzacepa.
13 Koma amene adzapilile* mpaka pa mapeto adzapulumuka.
14 Uthenga wabwino uwu wa Ufumu udzalalikidwa pa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti udzakhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.
15 “Cotelo, mukadzaona cinthu conyansa cobweletsa cionongeko, cimene mneneli Danieli ananena, citaimilila pa malo oyela (wowelenga adzazindikile).
16 Amene ali mu Yudeya adzayambe kuthawila ku mapili.
17 Munthu amene adzakhale pa mtenje asadzatsike kuti akatenge katundu m’nyumba mwake.
18 Ndipo munthu amene adzakhale ku munda, asadzabwelele kuti akatenge cobvala cake cakunja.
19 Tsoka kwa akazi apathupi komanso oyamwitsa m’masiku amenewo!
20 Pitilizani kupemphela kuti musadzathawe m’nyengo yozizila kapena pa tsiku la Sabata.
21 Cifukwa panthawiyo kudzakhala cisautso cacikulu cimene sicinacitikepo kucokela pa ciyambi ca dziko mpaka pano, ndipo sicidzacitikanso.
22 Kukamba zoona masikuwa akanapanda kucepetsedwa, palibe amene akanapulumuka. Koma cifukwa ca osankhidwawo masikuwo adzacepetsedwa.
23 “Cotelo munthu akadzakuuzani kuti, ‘Onani! Khristu uja ali kuno,’ kapena, ‘Ali uko!’ musakakhulupilile.
24 Pakuti kudzabwela anthu onamizila kukhala Khristu komanso aneneli abodza. Ndipo adzacita zizindikilo zamphamvu ndi zodabwitsa kuti asoceletse anthu, ndipo ngati n’kotheka ngakhale osankhidwawo.
25 Onani! Ine ndakucenjezelanitu.
26 Conco, anthu akadzakuuzani kuti, ‘Inu! Iye ali ku cipululu,’ musakapiteko. Akadzanena kuti ‘Ali m’zipinda zamkati,’ musadzakhulupilile.
27 Pakuti monga mmene mphenzi imang’animila kucokela kum’mawa mpaka kumadzulo, ndi mmenenso zidzakhalile ndi kukhalapo* kwa Mwana wa munthu.
28 Kulikonse kumene kuli thupi lakufa, ziombankhanga zimasonkhana kumeneko.
29 “Cisautso ca m’masiku amenewo cikadzangotha, dzuwa lidzacita mdima, ndipo mwezi sudzawala. Nyenyezi zidzagwa kucokela kumwamba, ndipo mphamvu zakumwamba zidzagwedezeka.
30 Kenako cizindikilo ca Mwana wa munthu cidzaonekela kumwamba. Ndipo mapfuko onse a padziko lapansi adzadziguguda pacifuwa cifukwa ca cisoni. Iwo adzaona Mwana wa munthu akubwela pa mitambo ya kumwamba ali ndi mphamvu komanso ulemelelo waukulu.
31 Iye adzatumiza angelo ake ndi kulila kwamphamvu kwa lipenga, ndipo adzasonkhanitsa osankhidwa ake kucokela ku mphepo zinai. Kucokela kumalekezelo a mlengalenga mpaka kumalekezelo ake ena.
32 “Tsopano phunzilamponi kanthu pa fanizo ili la mtengo wamkuyu. Mukangoona kuti nthambi yake yanthete yayamba kuphuka ndi kutulutsa masamba, mumadziwa kuti dzinja layandikila.
33 Mofananamo, inunso mukadzaona zinthu zonsezi, mukadziwe kuti iye ali pafupi, pa khomo penipeni.
34 Ndithu ndikukuuzani, m’badwo uwu sudzatha wonse mpaka zinthu zonsezi zitacitika.
35 Kumwamba ndi dziko lapansi zidzacoka, koma mau anga sadzacoka ai.
36 “Ponena za tsikulo ndi ola lake palibe amene adziwa, ngakhale angelo akumwamba kapena Mwanayo, koma Atate yekha basi.
37 Pakuti monga zinalili m’masiku a Nowa, ndi mmenenso zidzakhalile pa nthawi ya kukhalapo* kwa Mwana wa munthu.
38 M’masiku amenewo Cigumula cisanacitike, anthu anali kudya ndi kumwa, amuna anali kukwatila ndipo akazi anali kukwatiwa, kufikila tsiku limene Nowa analowa m’cingalawa.
39 Anthuwa ananyalanyaza zimene zinali kucitika mpaka Cigumula cinafika n’kuwakokolola onsewo. Umu ndi mmenenso zidzakhalile pa nthawi ya kukhalapo kwa Mwana wa munthu.
40 Pa nthawiyo amuna awili adzakhala m’munda, ndipo mmodzi adzatengedwa koma winayo adzasiidwa.
41 Akazi awili adzakhala akupela pa mphelo. Mmodzi adzatengedwa koma winayo adzasiidwa.
42 Conco khalanibe maso cifukwa simukudziwa tsiku limene Mbuye wanu adzabwela.
43 “Koma dziwani ici: Ngati mwininyumba angadziwe nthawi imene kawalala akubwela usiku,* angakhalebe maso ndipo sangalole kuti kawalalayo athyole n’kulowa m’nyumba mwake.
44 Mwa ici, inunso khalani okonzeka cifukwa Mwana wa munthu adzabwela pa ola limene inu simukuliganizila.
45 “Ndani kwenikweni amene ali kapolo wokhulupilika ndi wanzelu, amene mbuye wake anamuika kuti aziyang’anila anchito ake a pakhomo, ndi kuwapatsa cakudya cao pa nthawi yoyenela?
46 Kapoloyo adzakhala wacimwemwe ngati mbuye wake pobwela adzamupeza akucita zimenezo!
47 Ndithu ndikukuuzani, adzamuika kuti aziyang’anila zinthu zake zonse.
48 “Koma ngati kapolo woipayo mumtima mwake anganene kuti, ‘Mbuye wanga akucedwa,’
49 n’kuyamba kumenya akapolo anzake, ndiponso kudya ndi kumwa pamodzi ndi zidakwa zenizeni,
50 mbuye wa kapoloyo adzabwela pa tsiku limene iye sakuliyembekezela, komanso pa ola limene sakulidziwa.
51 Pamenepo adzamupatsa cilango cowawa zedi, ndipo adzamuika ku malo a anthu onyenga. Kumeneko azikalila ndi kukuta mano.
Mau a m'Munsi
^ Onani Matanthauzo a Mau Ena.
^ Onani Matanthauzo a Mau Ena.
^ Kucokela ku Cigiriki, “ca zowawa za pobeleka.”
^ Kapena kuti, “wapilila.”
^ Onani Matanthauzo a Mau Ena.
^ Onani Matanthauzo a Mau Ena.
^ Kapena kuti, “mwininyumba akanadziwa kuti mbala ibwela pa ulonda uti.”

