Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Mateyo 8:1-34

  • Wakhate acilitsidwa (1-4)

  • Cikhulupililo ca kapitawo wa asilikali (5-13)

  • Yesu acilitsa anthu ambili ku Kaperenao (14-17)

  • Mmene tingatsatilile Yesu (18-22)

  • Yesu aleketsa cimphepo ca mkuntho pa nyanja (23-27)

  • Yesu atumiza ziwanda m’nkhumba (28-34)

8  Atatsika m’philimo, cikhamu ca anthu cinamutsatila. 2  Ndiyeno kunabwela munthu wakhate, ndipo anamuwelamila n’kunena kuti: “Ambuye, ngati mufuna mungandiyeletse.” 3  Pamenepo Yesu anatambasula dzanja lake n’kumukhudza, ndipo anati: “Ndifuna! Khala woyela.” Nthawi yomweyo khate lakelo linatha. 4  Ndiyeno Yesu anamuuza kuti: “Samala kuti usauze aliyense zimenezi. Koma pita ukadzionetse kwa wansembe, ndipo ukapeleke mphatso imene Mose analamula, kuti ukhale umboni kwa iwo.” 5  Atalowa mu mzinda wa Kaperenao, kapitawo wa asilikali anabwela kwa iye, n’kuyamba kumucondelela 6  kuti: “Bambo, wanchito wanga ali gone m’nyumba, akudwala matenda ofa ziwalo, ndipo akuzunzika koopsya.” 7  Iye anamuuza kuti: “Ndikafika kumeneko, ndikam’cilitsa.” 8  Kapitawo uja anamuyankha kuti: “Bambo, ine sindine woyenela kuti inu mukalowe m’nyumba mwanga. Koma mungokamba mau, ndipo wanchito wanga acila. 9  Pakuti inenso ndili ndi akulu-akulu amene amandilamulila, ndipo ndili ndi asilikali amene ndimawalamulila. Ndikauza uyu kuti, ‘Pita!’ amapita, ndikauza wina kuti, ‘Bwela!’ amabwela, ndipo ndikauza kapolo wanga kuti, ‘Cita ici!’ amacita.” 10  Yesu atamva zimenezi anadabwa kwambili, ndipo anauza amene anali kumutsatila aja kuti: “Kukuuzani zoona, mu Isiraeli sin’napezemo munthu wa cikhulupililo cacikulu ngati ici. 11  Koma ndikukuuzani kuti ambili ocokela kum’mawa ndi kumadzulo, adzabwela kudzakhala pa thebulo pamodzi ndi Abulahamu, Isaki, komanso Yakobo mu Ufumu wa kumwamba. 12  Koma ana a Ufumuwo adzaponyedwa kunja ku mdima. Kumeneko azikalila ndi kukukuta mano.” 13  Kenako Yesu anauza kapitawo wa asilikaliyo kuti: “Pita. Popeza waonetsa cikhulupililo, zimene wapempha zicitike.” Ndipo mu ola limenelo wanchito uja anacila. 14  Tsopano Yesu atalowa m’nyumba ya Petulo, anaona apongozi aakazi a Petulo ali cigonele cifukwa codwala malungo.* 15  Iye anagwila dzanja lao, ndipo anacila malungowo, moti anauka n’kuyamba kumukonzela cakudya. 16  Koma madzulo anthu anamubweletsela anthu ambili ogwidwa ndi ziwanda, ndipo iye anatulutsa mizimuyo ndi mau cabe, komanso anacilitsa onse amene anali kudwala, 17  kuti mau amene ananenedwa kudzela mwa mneneli Yesaya akwanilitsidwe akuti: “Iyeyo anacotsa matenda athu ndi kunyamula zowawa zathu.” 18  Yesu ataona kuti khamu la anthu lamuzungulila, analamula ophunzila ake kuti anyamuke n’kupita naye ku tsidya lina. 19  Tsopano mlembi wina anabwela n’kumuuza kuti: “Mphunzitsi, ndikutsatilani kulikonse kumene mungapite.” 20  Koma Yesu anamuyankha kuti: “Nkhandwe zili ndi mapanga ao, ndipo mbalame za mumlengalenga zili ndi zisa, koma Mwana wa munthu alibe ngakhale posamila mutu.”* 21  Kenako wina mwa ophunzila ake anamuuza kuti: “Ambuye, ndiloleni coyamba ndipite ndikaike malilo a atate anga.” 22  Yesu anamuyankha kuti: “Pitiliza kunditsatila, aleke akufa aike akufa ao.” 23  Atakwela bwato, ophunzila ake anamutsatila. 24  Ndiyeno pa nyanjapo panauka namondwe woopsya! moti madzi anayamba kulowa m’bwatomo cifukwa ca kukula kwa mafunde; koma iye anali mtulo. 25  Kenako iwo anapita kukamuutsa n’kumuuza kuti: “Ambuye, tipulumutseni tikufa!” 26  Koma iye anawafunsa kuti: “N’cifukwa ciani mukucita mantha conci, a cikhulupililo cocepa inu?” Kenako iye anauka n’kudzudzula mphepo ndi nyanjayo, ndipo panakhala bata lalikulu. 27  Poona izi, ophunzilawo anadabwa ndipo anati: “Kodi munthu ameneyu ndi wotani? Ngakhale mphepo ndi nyanja zikumumvela!” 28  Yesu atafika kutsidya lina la nyanja m’cigao ca Agadara, anakumana ndi amuna awili ogwidwa ndi ziwanda akucokela ku manda.* Iwo anali aukali kwambili, moti panalibe munthu anali kulimba mtima kupitila njila imeneyo. 29  Pamenepo iwo anayamba kupfuula kuti: “Mufuna ciani kwa ife inu Mwana wa Mulungu? Kodi mwabwela kudzatizunza nthawi yoikika isanakwane?” 30  Capatali ndithu kucokela pamenepo, panali gulu la nkhumba zambili zimene zinali kudya. 31  Cotelo ziwandazo zinayamba kumucondelela kuti: “Ngati mudzatitulutsa, mutitumize tikalowe m’nkhumba izo.” 32  Ndipo Yesu anaziuza kuti: “Pitani!” Pamenepo ziwandazo zinatuluka n’kupita kukalowa m’nkhumbazo. Zitatelo, nkhumbazo zinathamangila ku phompho mpaka kukagwela m’nyanja, ndipo zinafela momwemo. 33  Koma owetela nkhumbazo anathawa. Atalowa mu mzinda, anafotokozela anthu zonse zimene zinacitika, kuphatikizapo za amuna ogwidwa ndi ziwanda aja. 34  Pamenepo anthu onse a mu mzindawo anapita kukakumana ndi Yesu, ndipo atamuona anamupempha kuti acoke m’dela lao.

Mau a m'Munsi

^ Kucokela ku Cigiriki, “cifukwa ca kutentha thupi.”
^ Kucokela ku Cigiriki, “alibe kulikonse kumene angasamile mutu wake.”
^ Kapena kuti, “manda acikumbutso.”