BAIBO YA DZIKO LATSOPANO

Kodi mungacipeze bwanji cimwemwe?

Cinyanja
Kodi mungacipeze bwanji cimwemwe?
https://cms-imgp.jw-cdn.org/img/p/1001061100/univ/wpub/1001061100_univ_sqr_xl.jpg
nwt masa. 26-27

FUNSO 15

Kodi mungacipeze bwanji cimwemwe?

“Ndi bwino kudya zamasamba koma pali cikondi, kusiyana ndi kudya nyama ya ngʼombe yamphongo yonenepa koma pali cidani.”

Miyambo 15:17

“Ine Yehova ndine Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendeleni bwino, amene ndimakutsogolelani mʼnjila imene mukuyenela kuyenda.”

Yesaya 48:17

“Acimwemwe ndi anthu ozindikila zosowa zao zauzimu, cifukwa Ufumu wa kumwamba ndi wao.”

Mateyo 5:3

“Uzikonda mnzako mmene umadzikondela wekha.”

Mateyo 22:39

“Zimene mumafuna kuti anthu akucitileni, inunso muwacitile zomwezo.”

Luka 6:31

“Acimwemwe ndi anthu amene akumva mau a Mulungu ndi kuwasunga!”

Luka 11:28

“Munthu atakhala ndi zoculuka motani, moyo wake sucokela m’zinthu zimene ali nazo.”

Luka 12:15

“Conco, ngati tili ndi cakudya, zobvala, ndi pogona, tizikhala okhutila ndi zinthu zimenezi.”

1 Timoteyo 6:8

“Kupatsa kumabweletsa cimwemwe cacikulu kuposa kulandila.”

Macitidwe 20:35