Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Mateyo 22:1-46
22 Yesu anawauzanso mafanizo ena. Anati:
2 “Ufumu wa kumwamba uli ngati mfumu imene inakonza phwando la ukwati wa mwana wake wamwamuna.
3 Ndipo inatuma akapolo ake kuti akaitane anthu oitanidwa ku phwando la ukwatilo, koma iwo anakana.
4 Anatumanso akapolo ena n’kuwauza kuti, ‘Kauzeni oitanidwa aja kuti: “Taonani! Ndakonza cakudya ca masana, ndapha ng’ombe zanga ndi nyama zanga zonenepa, ndipo zonse zakonzedwa kale. Bwelani ku phwando la ukwati.”’
5 Koma oitanidwawo sanalabadile ndipo anacoka, wina anapita ku munda kwake, wina ku malonda ake.
6 Koma enawo anagwila akapolo aja, ndipo anawazunza n’kuwapha.
7 “Pamenepo mfumu ija inakwiya koopsya, ndipo inatuma asilikali ake kukapha anthu amene anapha akapolo ake aja n’kutentha mzinda wao.
8 Kenako anauza akapolo ake kuti, ‘Phwando la ukwati lakonzedwa, koma amene anaitanidwa aja sanali oyenela.
9 Conco, pitani m’miseu yotulukila mu mzinda uno, mukaitane aliyense amene mum’peze kuti abwele ku phwando la ukwatili.’
10 Conco akapolowo anapita m’miseu ndi kusonkhanitsa anthu onse amene anapeza, oipa ndi abwino omwe. Ndipo cipinda cocitilamo phwando la ukwatilo cinadzala ndi anthu olandila cakudya.
11 “Mfumu ija italowa m’cipindamo poyendela oitanidwawo, inaona munthu wina amene sanabvale cobvala ca ukwati.
12 Mfumuyo inamufunsa kuti, ‘Bwanawe, walowa bwanji muno popanda cobvala ca ukwati?’ Iye anasowa cokamba.
13 Basi mfumuyo inauza atumiki ake kuti, ‘Mumangeni manja ndi miyendo ndi kum’ponya kunja ku mdima. Kumeneko azikalila ndi kukukuta mano.’
14 “Pakuti oitanidwa ndi ambili koma osankhidwa ndi owelengeka.”
15 Pambuyo pake Afarisi anapita kukapangana zakuti amutape m’kamwa Yesu.
16 Conco iwo anamutumizila ophunzila ao pamodzi ndi a cipani ca Herode. Iwo anati: “Mphunzitsi, tidziwa kuti mumakamba zoona ndi kuphunzitsa njila ya Mulungu m’coonadi, komanso simukondela cifukwa simuyang’ana maonekedwe a anthu.
17 Ndiye tiuzeni, muganiza bwanji? Kodi n’kololeka* kupeleka msonkho kwa Kaisara kapena ai?”
18 Koma Yesu podziwa colinga cao coipa anati: “Onyenga inu, n’cifukwa ciani mukundiyesa?
19 Ndionetseni khobili la msonkhowo.” Iwo anamubweletsela khobili la dinari.
20 Kenako iye anawafunsa kuti: “Kodi cithunzi ici ndi mau awa n’zandani?”
21 Iwo anayankha kuti: “Ndi za Kaisara.” Ndiyeno iye anawauza kuti: “Conco pelekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara, koma za Mulungu kwa Mulungu.”
22 Atamva zimenezi anadabwa kwambili ndipo anamusiya n’kucoka.
23 Pa tsiku limenelo, Asaduki amene amati kulibe kuuka kwa akufa, anabwela n’kumufunsa kuti:
24 “Mphunzitsi, Mose anati: ‘Mwamuna akamwalila wopanda ana, m’bale wake wa munthuyo ayenela kukwatila mkazi wamasiyeyo ndi kumubelekela ana m’bale wake uja.’
25 Tsopano panali amuna 7 apacibale. Woyamba anakwatila kenako anamwalila. Koma popeza analibe ana, mkazi uja anakwatiwa ndi m’bale wa mwamuna wake.
26 Zinacitika cimodzi-modzi kwa waciwili ndi wacitatu mpaka kwa onse 7.
27 Pothela pake, mkazi uja nayenso anamwalila.
28 Ndiye pamene akufa adzauka, kodi mkaziyo adzakhala wa ndani popeza onse 7 anamukwatilapo?”
29 Yesu anawayankha kuti: “Mukulakwitsa, cifukwa simudziwa Malemba kapena mphamvu za Mulungu;
30 Pakuti pa kuuka kwa akufa, amuna sadzakwatila ndipo akazi sadzakwatiwa koma adzakhala ngati angelo akumwamba.
31 Ponena za kuuka kwa akufa, kodi simunawelenge zimene Mulungu anakuuzani pamene anati:
32 ‘Ine ndine Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki, komanso Mulungu wa Yakobo’? Iye si Mulungu wa akufa ai, koma wa anthu amoyo.”
33 Khamulo litamva zimenezi, linadabwa kwambili ndi kaphunzitsidwe kake.
34 Afarisi atamva kuti Yesu anawasowetsa conena Asaduki, anasonkhana pamodzi n’kubwela kwa iye.
35 Ndipo mmodzi wa iwo, wodziwa Cilamulo, anamuyesa mwa kumufunsa kuti:
36 “Mphunzitsi, kodi lamulo lalikulu kwambili m’Cilamulo ndi liti?”
37 Iye anamuyankha kuti: “‘Uzikonda Yehova* Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.’
38 Ili ndilo lamulo lalikulu kwambili komanso loyamba.
39 Laciwili lofanana nalo ndi ili: ‘Uzikonda mnzako mmene umadzikondela wekha.’
40 Cilamulo conse komanso zolemba za aneneli zagona pa malamulo awili amenewa.”
41 Ndiyeno Afarisi aja atasonkhana pamodzi, Yesu anawafunsa kuti:
42 “Muganiza bwanji za Khristu? Kodi ndi mwana wa ndani?” Iwo anamuyankha kuti: “Wa Davide.”
43 Iye anawafunsanso kuti: “Nanga n’cifukwa ciani Davide mouzilidwa anamuchula kuti Ambuye, pamene anati
44 ‘Yehova* anauza Ambuye wanga kuti: “Khala kudzanja langa lamanja, mpaka nditaika adani ako kunsi kwa mapazi ako”’?
45 Ngati Davide anamuchula kuti Ambuye, ndiye akhala bwanji mwana wake?”
46 Koma palibe anatha kumuyankha, ndipo kucokela tsiku limenelo palibe analimba mtima kumufunsanso mafunso.

